Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 29

Kondwelani na Mmene Mukupitila Patsogolo!

Kondwelani na Mmene Mukupitila Patsogolo!

Aliyense payekha . . . akhale ndi cifukwa cosangalalila ndi nchito yake, osati modziyelekezela ndi munthu wina.’—AGAL. 6:4.

NYIMBO 34 N’dzayenda mu Umphumphu Wanga

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciani Yehova satiyelekezela na ŵena?

YEHOVA amasangalala na kusiyana-siyana kwa zinthu. Izi zimaonekela bwino m’zolengedwa zake zokongola, kuphatikizapo mtundu wa anthu. Aliyense wa ife ni wosiyana. Pa cifukwa cimeneci, Yehova satiyelekezela na ŵena. Amasanthula mtima wathu na umunthu wathu wamkati. (1 Sam. 16:7) Iye amadziŵanso zimene tingakwanitse kucita, zifooko zathu, komanso mmene tinakulila. Ndipo satiuza kucita zimene sitingakwanitse. Conco tiyenela kudziona mmene Yehova amationela. Tikatelo, tidzakhala ‘oganiza bwino,’ posadziona ngati apamwamba kapena ngati osanunkha kanthu.—Aroma 12:3.

2. N’cifukwa ciani si kwabwino kudziyelekezela na ŵena?

2 N’zoona kuti tingapindule kwambili ngati titengela citsanzo ca m’bale kapena mlongo wokhulupilika amene amacita bwino mu ulaliki. (Aheb. 13:7) Tingaphunzileko mmene tingakulitsile maluso athu mu ulaliki. (Afil. 3:17) Kutengela citsanzo cabwino ca munthu wina kulibe vuto. Koma kudzilinganiza na munthuyo ndiye kolakwika. Kudziyelekezela koteloko, kungatipangitse kucita kaduka, kulefuka, kapena kudziona acabe-cabe. Cinanso, malinga na zimene tinaphunzila m’nkhani yapita, kupikisana na ŵena mu mpingo kungativulazenso mwauzimu. Conco, mwacikondi Yehova akutilangiza kuti: “Aliyense payekha ayese nchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatelo adzakhala ndi cifukwa cosangalalila ndi nchito yake, osati modziyelekezela ndi munthu wina.”—Agal. 6:4.

3. Kodi mwapita patsogolo kuuzimu m’njila ziti zimene zakubweletselani cimwemwe?

3 Yehova amafuna kuti muzikondwela na mmene mukupitila patsogolo mwauzimu. Mwacitsanzo, ngati munabatizika mungakondwele kuti munakwanilitsa colinga canu! Munapanga cisankho cocita zimenezi pa inu nokha. Munacita izi cifukwa ca cikondi canu pa Mulungu. Tangoganizani mmene mwapitila patsogolo kucokela pamene munabatizika. Mwacitsanzo, kodi mwakulitsa cikondi canu pa kuŵelenga Baibo na kucita phunzilo laumwini? Kodi tsopano mumapeleka mapemphelo ocokela pansi pa mtima? (Sal. 141:2) Kodi mwanola luso lanu la kuyambitsa makambilano mu ulaliki, na kuseŵenzetsa zida zathu zophunzitsila? Ngati muli pabanja, kodi Yehova wakuthandizani kukhala mwamuna wabwino, mkazi wabwino, kapena kholo labwino? Mungakhale acimwemwe komanso okhutila ngati muona mmene mwapitila patsogolo pa mbali ngati zimenezi.

4. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

4 Tingathandize ena kusangalala na kupita kwawo patsogolo. Tingaŵathandizenso kupewa kudzilinganiza na ŵena. M’nkhani ino, tiona mmene makolo angathandizile ana awo, mmene okwatilana angathandizilane, komanso mmene akulu na ŵena angathandizile abale na alongo mu mpingo. Cotsilizila, tikambilana mfundo za m’Baibo zimene zingatithandize kudziikila zolinga zimene tingakwanilitse, malinga na mmene zinthu zili kwa ife.

ZIMENE MAKOLO KOMANSO AM’CIKWATI ANGACITE

Makolo, muziyamikila mwana aliyense pa zimene amakwanitsa kucita (Onani ndime 5-6 5-6) *

5. Malinga na Aefeso 6:4, kodi makolo ayenela kupewa ciani?

5 Makolo ayenela kusamala kuti asamayelekezele mwana wina na wina, kapena kufuna kuti ana azicita zimene sangakwanitse. Ngati makolo amacita zimenezi, angalefule ana awo. (Ŵelengani Aefeso 6:4.) Mlongo wina dzina lake Sachiko * anati: “Aphunzitsi anga anali kufuna kuti nizicita bwino kwambili kuposa anzanga m’kalasi. Ndiponso, amayi nawonso anali kufuna kuti niziphasa ku sukulu, n’colinga cakuti nikhale na mbili yabwino monga Mboni kwa aphunzitsi anga, komanso kwa atate anga amene si mboni. Iwo anali kufuna kuti nizikhoza zonse pa mayeso, zimene zinali zosatheka kwa ine. Ngakhale kuti papita zaka zingapo ndithu kucokela pamene n’natsiliza sukulu, nthawi zina nimakayikilabe ngati zimene nimacita kwa Yehova n’zokwanila.”

6. Kodi makolo aphunzilapo ciani pa Salimo 131:1, 2?

6 Phunzilo lofunika kwambili kwa makolo lipezeka pa Salimo 131:1, 2. (Ŵelengani.) Mfumu Davide anakamba kuti ‘sanafune zinthu zapamwamba kwambili,’ kapena zinthu zimene sakanakwanitsa kucita. Cifukwa cakuti anali wodzicepetsa, anakhala wokhutila komanso ‘anakhazika mtima wake pansi.’ Kodi makolo akuphunzilapo ciani pa mawu a Davide? Makolo angaonetse kuti ni odzicepetsa ngati sayembekezela kucita zinthu zimene sangathe, kapena zimene ana awo sangakwanitse. Iwo angathandize ana awo kuona kuti ni ofunika mwa kuzindikila zimene anawo angathe kucita na zimene sangathe. Akatelo, anawo adzadziikila zolinga zimene angakwanilitse. Mlongo wina dzina lake Marina anati: “Amayi sanali kunilinganiza na azibale anga kapena ana ŵena. Ananiphunzitsa kuti munthu aliyense ali na mphatso zosiyana-siyana, ndiponso kuti ni wa mtengo wapatali kwa Yehova. Cifukwa ca zimene ananiphunzitsa, si kaŵili-kaŵili kudziyelekezela na ŵena.”

7-8. Kodi mwamuna angaonetse bwanji kuti amalemekeza mkazi wake?

7 Mwamuna wacikhristu ayenela kulemekeza mkazi wake. (1 Pet. 3:7) Kulemekeza munthu kumatanthauza kumuona kukhala wofunika na kum’patsa ulemu. Mwacitsanzo, mwamuna amalemekeza mkazi wake mwa kucita naye zinthu mwaulemu. Sayembekezela kuti mkazi wake azicita zimene sangakwanitse. Komanso amapewa kumuyelekezela na akazi ena. Kodi mkazi angamvele bwanji ngati mwamuna wake amamuyelekezela na akazi ena? Mlongo wina dzina lake Rosa, mwamuna wake amene si Mboni, amakonda kumuyelekezela na akazi ena. Mawu ankhanza a mwamuna wake amam’pangitsa kuona ngati ngakhale anthu ena samukonda. Mlongoyu anati: “Nthawi zambili n’nali kufuna wonithandiza kuona kuti Yehova amanikonda.” Koma mwamuna wacikhristu amalemekeza mkazi wake. Amadziŵa kuti zocita zake zimakhudza mkazi wake komanso ubale wake na Yehova. *

8 Mwamuna amene amalemekeza mkazi wake amakamba zabwino za iye, amamuonetsa cikondi, komanso amamuyamikila. (Miy. 31:28) Izi n’zimene mwamuna wa mlongo Katerina, amene tinamuchula m’nkhani yapita, amacita pothandiza mkazi wake akakhala na maganizo odziona wacabe-cabe. Katerina ali mwana, amayi ake anali kumupeputsa na kumuyelekezela na atsikana ŵena. Izi zinapangitsa kuti iye ayambe kudziyelekezela na ŵena, ngakhale pambuyo pophunzila coonadi. Komabe, mwamuna wake wacikhristu anam’thandiza kuthetsa vuto limeneli, ndipo anayamba kudziona moyenela. Iye anati: “Mwamuna wanga amanikonda, amaniyamikila nikacita zabwino, ndiponso amapemphela nane. Cina, amanikumbutsa makhalidwe abwino a Yehova na kunithandiza kuwongolela maganizo anga olakwika.”

ZIMENE AKULU ACIKONDI KOMANSO ENA ANGACITE

9-10. Kodi akulu acikondi anam’thandiza bwanji mlongo wina kuleka kudziyelekezela na ŵena?

9 Kodi akulu angathandize bwanji aja amene amakonda kudziyelekezela na ŵena? Ganizilani citsanzo ca mlongo wina dzina lake Hanuni. Iye ali mwana sanali kuyamikilidwa. Anati: “N’nali wamanyazi, ndipo n’nali kuona kuti ana ŵena anali kucita bwino kuposa ine. Kucokela panthawiyo, n’nayamba kudziyelekezela na ŵena.” Ngakhale pambuyo pophunzila coonadi, Hanuni sanaleke kudziyelekezela na ŵena. Zotsatilapo n’zakuti anali kudziona kuti ni wosafunika mu mpingo. Koma tsopano, akutumikila mwacimwemwe monga mpainiya. N’ciani cinam’thandiza kusintha maganizo ake osayenela?

10 Mlongo Hanuni anati akulu acikondi ndiwo anam’thandiza. Iwo anamuuza kuti iye ni ciwalo cofunika mu mpingo, ndipo anamuyamikila kaamba ka citsanzo cake cabwino. Iye analemba kuti: “Kangapo konse, akulu ananipempha kuti nilimbikitse alongo ena ofunikila thandizo. Utumiki umenewu, unanipangitsa kudziona kuti ndine wofunika ngako. Nikumbukila pamene akulu ananiyamikila cifukwa colimbikitsa alongo acicepele. Ndiyeno, anaŵelenga nane 1 Atesalonika 1:2, 3. Lembali linanifika pamtima kwambili! Cifukwa ca akulu acikondi amenewo, tsopano nimayamikila kudziŵa kuti ndine wofunika mu mpingo.”

11. Kodi tingawathandize bwanji anthu ‘opsinjika ndi a mtima wodzicepetsa’ ochulidwa pa Yesaya 57:15?

11 Ŵelengani Yesaya 57:15. Yehova amasamala za anthu ‘opsinjika ndi a mtima wodzicepetsa.’ Tonsefe, osati akulu okha, tingawalimbikitse abale na alongo okondedwa amenewa. Njila imodzi imene tingawalimbikitsile ni kuwaonetsa cidwi ceniceni. Yehova amafuna tizionetsa cikondi cake ku nkhosa zake za mtengo wapatali. (Miy. 19:17) Tingathandizenso abale na alongo athu mwa kukhala odzicepetsa. Sitifuna kudzipezela ulemelelo cifukwa ca maluso athu, zimene zingapangitse ena kuyamba kuticitila kaduka. M’malo mwake, tiyenela kuseŵenzetsa maluso na cidziŵitso cathu kuti tilimbikitsane.—1 Pet. 4:10, 11.

Ophunzila a Yesu anali kum’konda cifukwa sanali kudziona kukhala woposa iwo. Anali kukonda kuceza na mabwenzi ake (Onani ndime 12)

12. N’cifukwa ciani anthu wamba anali kum’konda Yesu? (Onani cithunzi pacikuto.)

12 Tingaphunzile zambili za mokhalila na ŵena poona mmene Yesu anacitila zinthu na otsatila ake. Anali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako. Ngakhale n’conco, iye anali “wofatsa ndi wodzicepetsa.” (Mat. 11:28-30) Sanadzitukumule cifukwa ca nzelu zake za pamwamba, komanso cidziŵitso cake coculuka. Pophunzitsa, anali kuseŵenzetsa mawu osavuta kumva na mafanizo ogwila mtima kuti afike pa mtima anthu odzicepetsa. (Luka 10:21) Mosiyana na atsogoleli acipembedzo onyada, Yesu sanapangitse anthu kumvela kuti ni osanunkha kanthu kwa Mulungu. (Yoh. 6:37) M’malo mwake, iye anali kuwalemekeza anthu wamba.

13. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kukoma mtima na cikondi kwa ophunzila ake?

13 Kukoma mtima kwa Yesu na cikondi cake, zinaonekela bwino na mmene anali kucitila zinthu kwa ophunzila ake. Anadziŵa kuti maluso na mikhalidwe yawo pa umoyo zinali zosiyana. Iwo sanali na maudindo ofanana, komanso sakanacita zofanana mu ulaliki. Komabe, Yesu anali kuyamikila aliyense cifukwa cocita zimene akanatha. Fanizo la matalente lionetsa bwino khalidwe la Yesu limeneli. M’fanizo limenelo, mbuye anagaŵila kapolo aliyense nchito “malinga ndi luso lake.” Mmodzi wa akapolo aŵili akhama anapindula zambili kuposa mnzake. Koma mbuye wawo anayamikila onse aŵili na mawu ofanana akuti: “Wacita bwino kwambili, kapolo wabwino ndi wokhulupilika iwe!”—Mat. 25:14-23.

14. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu pocita zinthu na ŵena?

14 Masiku anonso, Yesu amacita nafe zinthu mwacikondi komanso mokoma mtima. Amadziŵa kuti maluso na mikhalidwe ya anthu pa umoyo imasiyana, ndipo amayamikila tikacita zimene tingakwanitse. Tiyenela kutengela citsanzo ca Yesu pocita zinthu na ŵena. Sitiyenela kupangitsa alambili anzathu kumva kuti ni osafunika, kapena kuwacititsa manyazi cifukwa sakwanitsa kucita zambili monga ena. M’malo mwake, tizifunafuna mipata yoyamikila abale na alongo athu cifukwa coyesetsa kucita zimene angathe potumikila Yehova.

DZIIKILENI ZOLINGA ZIMENE MUNGAKWANITSE

Pezani cimwemwe mwa kudziikila zolinga zimene mungazikwanilitse (Onani ndime 15-16) *

15-16. Kodi mlongo wina anapindula bwanji cifukwa codziikila zolinga zimene angakwanitse?

15 Zolinga zathu zauzimu zimapangitsa umoyo wathu kukhala waphindu. Komabe, cinsinsi cake cagona pa kudziikila zolinga potengela maluso athu na mikhalidwe yathu, osati zolinga za ŵena. Kudziikila zolinga zimene sitingakwanitse kungatigwilitse mwala ndipo tingalefuke. (Luka 14:28) Ganizilani citsanzo ca mlongo wina dzina lake Midori.

16 Ali mwana, atate ake a Midori amene si Mboni, anali kum’cititsa manyazi pomuyelekezela na azibale ake, komanso anzake a m’kalasi. Midori anati: “N’nadziona wacabe-cabe.” Komabe, pamene anali kukula anayamba kudziona moyenela. Anati: “Nimaŵelenga Baibo tsiku lililonse kuti nikhale na mtendele wamaganizo, ndipo nimaona kuti Yehova amanikonda.” Kuwonjezela apo, anadziikila zolinga zimene angakwanitse, ndipo anapemphela kuti Mulungu am’thandize kuzikwanilitsa. Cotulukapo cake n’cakuti Midori amakondwela na mmene akupitila patsogolo kuuzimu.

PITILIZANI KUPATSA YEHOVA ZABWINO KOPOSA

17. Kodi tingapitilize bwanji kukhala atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo athu? Nanga padzakhala zotulukapo zotani?

17 Zimatenga nthawi kuti tithetse maganizo odziona kukhala wosafunika. N’cifukwa cake Yehova akutilimbikitsa kuti: ‘[Pitilizani] kukhala atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu.’ (Aef. 4:23, 24) Kuti ticite zimenezi, tiyenela kupemphela, kuŵelenga Mawu a Mulungu, na kusinkhasinkha. Conco pitilizani kucita zimenezi, ndipo muzipempha Yehova kuti akupatseni nyonga. Mzimu wake woyela udzakuthandizani kuthetsa cizolowezi canu codzilinganiza na ŵena. Yehova adzakuthandizani kuzindikila ngati mwayamba mzimu wa kaduka na kudzikuza. Adzakuthandizaninso kuwazula mwamsanga makhalidwe oipa amenewa.

18. Kodi mawu apa 2 Mbiri 6:29, 30 angakulimbikitseni bwanji?

18 Ŵelengani 2 Mbiri 6:29, 30. Yehova amadziŵa za mu mtima mwathu. Amadziŵanso kuti timalimbana na mzimu wa dziko komanso zophophonya zathu. Yehova akamationa tikuyesetsa kugwebana na zoipa ngati zimenezi, cikondi cake pa ife cimakulilako.

19. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene Yehova amatikondela.

19 Yehova potionetsa kuti amatikonda kwambili, amagwilitsa nchito citsanzo ca mmene mayi amakondela mwana wake. (Yes. 49:15) Mayi wina dzina lake Rachel anakamba kuti: “Mwana wanga Stephanie anabadwa miyezi isanakwane. N’tamuona kwa nthawi yoyamba kanali kakang’ono kwambili. Koma mwezi woyamba pamene mwana wanga anali ku malaiti, adokotala anali kunilola kumunyamulako tsiku lililonse. Izi zinapangitsa kuti cikondi pakati pa ine na mwana wanga cikulileko. Apa lomba ali na zaka 6, koma amaonekabe wamng’ono kuposa anzake a msinkhu wake. Ngakhale n’telo, nimam’konda ngako cifukwa zinali zovuta kwa iye kuti akhale na moyo. Iye wanibweletsela cimwemwe cacikulu mu umoyo wanga.” N’zolimbikitsa cotani nanga kudziŵa kuti Yehova amatikonda kwambili akationa tikulimbana na zoipa kuti tim’tumikile na mtima wonse!

20. Monga mtumiki wa Yehova wodzipatulila, kodi muli na cifukwa citi cokhalila wosangalala?

20 Mtumiki aliyense wa Yehova ni wosiyana, koma ni wofunika kwambili m’banja lake. Yehova sanakukokeleni kwa iye cifukwa munali kucita bwino kuposa ena. Anakukokelani kwa iye cifukwa anayang’ana mu mtima wanu na kuona kuti ndimwe wofatsa, komanso wofunitsitsa kuphunzila kwa iye kuti musinthe. (Sal. 25:9) Dziŵani kuti iye amayamikila mukamacita zonse zotheka kuti mum’tumikile. Kupilila na kukhulupilika kwanu ni umboni wakuti muli na “mtima woona komanso wabwino.” (Luka 8:15) Conco, pitilizani kupatsa Yehova zabwino koposa. Mukatelo, mudzakhala na cifukwa cosangalalila na ‘nchito [yanu].’

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

^ ndime 5 Yehova satiyelekezela na ŵena. Komabe, tingayambe kudziyelekezela na ŵena na kuyamba kuona kuti siticita bwino. M’nkhani ino, tikambilana cifukwa cake si kwabwino kudziyelekezela na ŵena. Tionenso mmene tingathandizile a m’banja lathu na ŵena mu mpingo kudziona mmene Yehova amawaonela.

^ ndime 5 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 7 Ngakhale kuti malangizo awa akupita kwa amuna, mfundo zake zigwilanso nchito kwa akazi.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pa kulambila kwa pabanja, makolo akusangalala poona zimene mwana aliyense wapanga zolowetsa mu cingalawa ca Nowa.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo amene akulela yekha mwana akulinganiza zinthu pa umoyo wake kuti aciteko upainiya wothandiza. Ndipo iye ni wokondwa kuti wakwanilitsa colinga cake