Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 31

Kodi Mudzayembekezera Yehova Moleza Mtima?

Kodi Mudzayembekezera Yehova Moleza Mtima?

“Ndidzayembekezera moleza mtima.”​—MIKA 7:7.

NYIMBO NA. 128 Tizipirira Mpaka Mapeto

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

KODI mumamva bwanji ngati katundu amene mumafunika kulandira sanafike panthawi imene mumayembekezera? Kodi mungakhumudwe? Mwina mungamve ngati mmene lemba la Miyambo 13:12 limanenera kuti: “Chinthu chimene unali kuyembekeza chikalephereka, chimadwalitsa mtima.” Koma kodi mungamve bwanji mutadziwa kuti pali zifukwa zomveka zimene zachititsa kuti katunduyo asafike pa nthawi imene mumayembekezerayo? N’zosakayikitsa kuti mukhoza kudikirabe moleza mtima.

2 Munkhaniyi tikambirana mfundo za m’Baibulo zingapo zimene zingatithandize kuti tipitirizebe ‘kuyembekezera moleza mtima.’ (Mika 7:7). Kenako tikambirana mbali ziwiri zimene tiyenera kuyembekezera moleza mtima kuti Yehova achitepo kanthu. Pomaliza tikambirana madalitso amene anthu amene amayembekezera Yehova adzapeze.

MFUNDO ZA M’BAIBULO ZIMENE ZIMATITHANDIZA KUKHALA OLEZA MTIMA

3. Kodi tikuphunzira mfundo yotani pa Miyambo 13:11?

3 Pa Miyambo 13:11, pali chitsanzo chosonyeza kufunika kochita zinthu moleza mtima. Lembali limati: “Zinthu zamtengo wapatali zimene zimapezedwa m’njira yachinyengo zimacheperachepera, koma wozisonkhanitsa ndi dzanja lake ndi amene amazichulukitsa.” Kodi mfundo yake ndi yotani pamenepa? Munthu angasonyeze kuti ndi wanzeru ngati amachita zinthu moleza mtima komanso mwapang’onopang’ono.

4. Kodi tikuphunzira chiyani pa mfundo ya pa Miyambo 4:18?

4 Lemba la Miyambo 4:18 limatiuza kuti: “Njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka mpaka tsiku litakhazikika.” Mawuwa akutithandiza kumvetsa kuti Yehova amaulula cholinga chake kwa atumiki ake pang’onopang’ono. Koma mawu a palembali akutithandizanso kumvetsa mmene Mkhristu amasinthira zinthu pa moyo wake n’cholinga choti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. Komabe pangatenge nthawi kuti Mkhristu akhale wolimba mwauzimu. Koma ngati timachita khama kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito malangizo amene timapeza m’Mawu a Mulungu komanso m’gulu lake, pang’ono ndi pang’ono tidzayamba kukhala ndi makhalidwe ofanana ndi a Khristu ndipo tingamudziwe bwino Mulungu. Tiyeni tione fanizo limene Yesu anapereka pankhaniyi.

Mofanana ndi mbewu imene imakula pang’onopang’ono, munthu amene wamva komanso kukhulupirira uthenga wa Ufumu amasintha zinthu pang’onopang’ono pa moyo wake (Onani ndime 5)

5. Kodi Yesu anapereka fanizo lotani losonyeza kuti pamatenga nthawi kuti munthu asinthe zinthu pa moyo wake?

5 Yesu anagwiritsa ntchito fanizo pofotokoza mmene uthenga wa Ufumu umene timalalikira ulili ngati kambewu kamene kamakula pang’onopang’ono m’mitima ya anthu abwino. Iye anati: “Mbewuzo zimamera ndi kukula. Koma mmene zimenezi zimachitikira, mwiniwakeyo sadziwa ayi. Pang’onopang’ono, payokha nthaka ija imabala zipatso. Choyamba mmera umabiriwira, kenako umatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tirigu amaonekera m’ngalamo.” (Maliko 4:27, 28) Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamenepa? Iye ankatanthauza kuti mofanana ndi mbewu imene imakula pang’onopang’ono, pamatenga nthawi kuti munthu amene wamva uthenga wa Ufumu asinthe zinthu pa moyo wake. Mwachitsanzo, anthu amene timaphunzira nawo Baibulo akayamba kukhala pa ubwenzi ndi Yehova timaona mmene asinthira zinthu zambiri pa moyo wawo. (Aef. 4:22-24) Koma tizikumbukira kuti Yehova ndi amene amachititsa kuti mbewu ya choonadi ikule mumtima mwa munthu.​—1 Akor. 3:7.

6-7. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yehova anachita polenga dziko lapansi?

6 Pa zonse zimene amachita, Yehova amaleza mtima komanso amadzipatsa nthawi yokwanira kuti amalize ntchito imene akugwira. Iye amachita zimenezi kuti dzina lake lilemekezedwe komanso pofuna kuthandiza anthu ena. Mwachitsanzo taganizirani zimene anachita pokonza dziko lapansili pang’onopang’ono.

7 Pofotokoza mmene Yehova analengera dziko lapansili, Baibulo limanena kuti iye “anaika miyezo yake,” anazika “maziko ake” komanso anaika “mwala wake wapakona.” (Yobu 38:5, 6) Iye ankapeza nthawi yoonanso mmene zinthu zimene analenga zinkaonekera. (Gen. 1:10, 12) Tangoganizani mmene angelo ankamvera akaona chinthu chatsopano chilichonse chimene Yehova walenga. Iwo ayenera kuti ankasangalala kwambiri. Tikutero chifukwa pa nthawi ina, “anayamba kufuula ndi chisangalalo.” (Yobu 38:7) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Panatenga zaka zambiri kuti Yehova amalize ntchito yake yolenga zinthu, koma ataona zinthu zonse zimene analenga, iye ananena kuti “zinali zabwino kwambiri.”​—Gen. 1:31

8. Kodi tsopano tikambirana chiyani?

8 Monga momwe taonera mu zitsanzo zimenezi, tingapeze mfundo zambiri m’Mawu a Mulungu zosonyeza kufunika koleza mtima. Tsopano tiyeni tikambirane mbali ziwiri zimene tiyenera kuyembekezera Yehova moleza mtima.

KODI NDI PA NTHAWI ZITI PAMENE TIYENERA KUYEMBEKEZERA YEHOVA?

9. Kodi ndi mbali ina iti imene tingafunike kuyembekezera Yehova?

9 Tingafunike kuyembekezera Yehova kuti ayankhe mapemphero athu. Nthawi zina tikapempha Yehova kuti atithandize kulimbana ndi mayesero amene takumana nawo, kapena kusiya khalidwe linalake limene iye sasangalala nalo, tingaone kuti akuchedwa kuyankha mapemphero athu. N’chifukwa chiyani Yehova sayankha mapemphero athu onse nthawi yomweyo?

10. N’chifukwa chiyani timafunika kuyembekezera moleza mtima kuti Yehova ayankhe mapemphero athu?

10 Yehova amamvetsera mosamala mapemphero athu. (Sal. 65:2) Amaona mapemphero athu ochokera pansi pamtima ngati umboni wosonyeza kuti timamukhulupirira. (Aheb. 11:6) Iye amafuna aone ngati tatsimikiza mtima kuchita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athu komanso zimene amafuna. (1 Yoh. 3:22) Choncho tiyenera kuyembekezera moleza mtima komanso kuchita zonse zomwe tingathe kuti tisiye khalidwe limene iye sasangalala nalo. Yesu anasonyeza kuti mapemphero athu ena sangayankhidwe nthawi yomweyo. Iye anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani. Pakuti aliyense wopempha amalandira, aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira.” (Mat. 7:7, 8) Tikamatsatira malangizo amenewa komanso ‘kulimbikira kupemphera,’ tingakhale otsimikiza kuti Atate wathu wakumwamba adzamva komanso kuyankha mapemphero athu.​—Akol. 4:2.

Pamene tikuyembekezera Yehova, timapemphera kwa iye ndi chikhulupiriro (Onani ndime 11) *

11. Kodi lemba la Aheberi 4:16, lingatithandize bwanji ngati tikuona kuti Mulungu akuchedwa kuyankha mapemphero athu?

11 Ngakhale tingaone ngati akuchedwa kuyankha mapemphero athu, Yehova akulonjeza kuti adzatiyankha “pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Werengani Aheberi 4:16.) N’chifukwa chake sitikuyenera kumuimba mlandu ngati zinazake sizinachitike msanga ngati mmene timaganizira. Mwachitsanzo anthu ambiri akhala akupemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere kuti udzathetse dziko loipali. Ndipotu Yesu anatiuza kuti tizitchula zimenezi m’mapemphero athu. (Mat. 6:10) Choncho kungakhaletu kupusa kwambiri ngati munthu angalole kuti chikhulupiriro chake chichepe chifukwa chakuti mapeto sanafike pa nthawi imene anthu amayembekezera. (Hab. 2:3; Mat. 24:44) Tingasonyeze kuti ndife anzeru tikamayembekezera Yehova moleza mtima komanso kupemphera kwa iye n’kumakhulupirira kuti ayankha mapemphero athu. Mapeto adzafika pa nthawi yoyenera chifukwa Yehova anasankha kale ‘tsiku ndi ola’ limene mapetowa adzafike. Ndipo nthawi imeneyo idzakhala yabwino kwambiri kwa aliyense.​—Mat. 24:36; 2 Pet. 3:15.

Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yosefe pa nkhani ya kuleza mtima? (Onani ndime 12-14)

12. Kodi ndi pa nthawi iti pamene mwina zingativute kuyembekezera moleza mtima?

12 Tingafunike kuyembekezera moleza mtima kuti chilungamo chichitike. Nthawi zambiri anthu m’dzikoli, amachitira zinthu zoipa anthu amene ndi osiyana nawo mtundu, chikhalidwe, kochokera komanso omwe si amuna kapena akazi anzawo. Enanso amachitiridwa zoipa chifukwa choti ndi olumala kapenanso chifukwa choti ali ndi mavuto a muubongo. Komanso a Mboni ambiri amachitiridwa zinthu zopanda chilungamo chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Tikakumana ndi zinthu zoterezi tizikumbukira mawu a Yesu. Iye anati: “Amene adzapirire mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.” (Mat. 24:13) Koma kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwazindikira kuti wina mumpingo wachita tchimo lalikulu? Ngati akulu adziwa za nkhaniyo, kodi mudzaisiya m’manja mwawo komanso kuyembekezera moleza mtima kuti aisamalire mogwirizana ndi malangizo a Yehova? Ndiye kodi akulu amatani akadziwa kuti wina wachita tchimo lalikulu?

13. Kodi Yehova amafuna kuti akulu azichita chiyani ngati wina wachita tchimo lalikulu?

13 Akulu akazindikira kuti wina mumpingo wachita tchimo lalikulu, amapempha “nzeru yochokera kumwamba” n’cholinga choti adziwe maganizo a Yehova pa nkhaniyo. (Yak. 3:17) Cholinga chawo chimakhala chakuti ngati n’kotheka, ‘abweze wochimwa panjira yake yoipa.’ (Yak. 5:19, 20) Komanso amayesetsa kuchita zonse zomwe angathe kuti ateteze mpingo komanso kulimbikitsa amene alakwiridwa. (2 Akor. 1:3, 4) Akulu akamaweruza nkhani yokhudza munthu amene wachita tchimo lalikulu, amafunika kufufuza zimene zachitika ndipo pangafunike nthawi yokwanira kuti achite zimenezi. Kenako iwo amapemphera, kupereka mosamala malangizo a m’Malemba komanso kuwongolera wochimwayo “pa mlingo woyenera.” (Yer. 30:11) Ngakhale kuti iwo sachita zinthu mozengereza sikuti amangothamangira kupereka chiweruzo. Akulu akatsatira malangizo a Yehova, anthu onse mumpingo amapindula. Komabe ngakhale kuti akulu angachite zonse zofunika potsatira malangizo, nthawi zina munthu amene walakwiridwayo angakhalebe wokhumudwa chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene zinamuchitikira. Ngati inunso zimenezi zinakuchitikirani, kodi mungatani kuti musapitirize kukhala wokhumudwa?

14. Kodi ndi chitsanzo chiti cha m’Baibulo chimene chingakuthandizeni kupirira Mkhristu mnzanu akakukhumudwitsani kwambiri?

14 Kodi munthu wina kapena Mkhristu mnzanu anayamba wakukhumudwitsanipo kwambiri? M’Baibulo muli zitsanzo zabwino kwambiri zimene zingatithandize kuti tiziyembekezera Yehova kuti akonze zinthu. Abale ake enieni atamuchitira zinthu zopanda chilungamo, Yosefe sanalole kuti zimene abale ake anamulakwira zimuchititse kukhala wokwiya. M’malomwake iye ankaganizira kwambiri zotumikira Yehova yemwe anamudalitsa chifukwa choyembekezerabe mopirira. (Gen. 39:21) N’kupita kwa nthawi Yosefe anakhululukira abale ake omwe anamulakwirawo ndipo anaona mmene Yehova anamudalitsira. (Gen. 45:5) Mofanana ndi Yosefe, timalimbikitsidwa tikakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova n’kumayembekezera kuti akonze zinthu pa nthawi yake.​—Sal. 7:17; 73:28.

15. Kodi n’chiyani chinathandiza mlongo wina kupirira zinthu zopanda chilungamo zimene mnzake ankamuchitira?

15 N’zoona kuti si nthawi zonse pamene tingachitiridwe zinthu zopanda chilungamo ngati zimene Yosefe anakumana nazo, komabe nthawi zina zimene ena angatichitire zingatikhumudwitse. Ngati tasemphana zochita ndi munthu wina, kuphatikizapo amene salambira Yehova, kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kungatithandize. (Afil. 2:3, 4) Taganizirani chitsanzo cha mlongo wina yemwe anazindikira kuti mnzake amene ankagwira naye ntchito ankamunenera zoipa kwa anthu ena. M’malo mochita zinthu mopupuluma, mlongoyo anaganizira chitsanzo cha Yesu. Pamene ankanenedwa zachipongwe, Yesu sanabwezere. (1 Pet. 2:21, 23) Poganizira zimenezi iye sanafune kuti akulitse nkhaniyo. Pambuyo pake iye anazindikira kuti mnzake wa kuntchitoyo anali ndi matenda aakulu ndipo ankada nkhawa kwambiri. Iye anazindikira kuti sichinali cholinga cha mnzakeyo kuti amuipitsire mbiri. Choncho mlongoyo anasangalala kuti anapirira moleza mtima zimene mnzakeyo ankamunenera ndipo anapeza mtendere wa mumtima.

16. Kodi n’chiyani chimene chingakulimbikitseni ngati mukukumana ndi zinthu zopanda chilungamo? (1 Pet. 3:12)

16 Ngati mukupirira zinthu zina zopanda chilungamo kapena zokhumudwitsa muzikumbukira kuti Yehova ali pafupi ndi anthu “a mtima wosweka.” (Sal. 34:18) Amakukondani chifukwa mumaleza mtima komanso kumutulira nkhawa zanu. (Sal. 55:22) Iye ndi Woweruza wa dziko lonse. Ndipo amaona zonse zimene zikuchitika. (Werengani 1 Petulo 3:12.) Ndiye ngati mukukumana ndi mavuto amene simungathe kuwathetsa, kodi mudzayembekezera Yehova kuti achitepo kanthu?

ANTHU OYEMBEKEZERA YEHOVA ADZAPEZA MADALITSO OMWE SADZATHA

17. Mogwirizana ndi Yesaya 30:18, kodi Yehova amatilonjeza chiyani?

17 Posachedwapa Atate wathu wakumwamba adzatipatsa madalitso ambiri pogwiritsa ntchito Ufumu wake. Lemba la Yesaya 30:18, limati: “Yehova azidzayembekezera kuti akukomereni mtima ndipo adzanyamuka kuti akuchitireni chifundo, pakuti Yehova ndi Mulungu amene amaweruza mwachilungamo. Odala ndi anthu onse amene amamuyembekezera.” Anthu amene amayembekezera Yehova amapeza madalitso panopa komanso adzapeza madalitso ochuluka m’dziko limene likubweralo.

18. Kodi tikuyembekezera madalitso otani?

18 Anthu a Mulungu akadzalowa m’dziko latsopano sadzafunikanso kupirira mavuto ndi zinthu zodetsa nkhawa zimene amakumana nazo masiku ano. Zinthu zopanda chilungamo zidzakhala mbiri yakale ndipo zopweteka sizidzakhalaponso. (Chiv. 21:4) Sitidzadandaulanso kuti tipeza bwanji zimene timafunikira chifukwa aliyense adzakhala ndi zinthu zochuluka. (Sal. 72:16; Yes. 54:13) Awatu adzakhala madalitso osaneneka.

19. Kodi Yehova akutikonzekeretsa chiyani?

19 Panopa Yehova akutikonzekeretsa kuti tidzakhale mu Ufumu wake potithandiza kuthetsa makhalidwe amene sasangalala nawo, n’kumakhala ndi makhalidwe abwino. Choncho sitiyenera kutaya mtima kapena kufooka. Moyo wabwino ukubwera posachedwapa. Podikira tsogolo labwinoli, tiyeni tipitirize kuyembekezera moleza mtima kuti Yehova amalize kugwira ntchito yake.

NYIMBO NA. 118 “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”

^ ndime 5 Kodi munayamba mwamvapo Mkhristu amene watumikira Yehova kwa nthawi yayitali akunena kuti, ‘Sindinkayembekezera kuti dziko loipali likhala lilipobe mpaka pano.’ Tonsefe timafunitsitsa Yehova atawononga dziko loipali makamaka munthawi yovutayi. Komabe tiyenera kuphunzira kukhala oleza mtima. Munkhaniyi tikambirana mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuyembekezera nthawi imene Yehova adzachitepo kanthu. Tikambirananso mbali ziwiri zimene tiyenera kuyembekezera Yehova moleza mtima komanso madalitso amene anthu omwe amamuyembekezera adzapeze.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo wakhala akupemphera kwa Yehova nthawi zonse kuyambira ali wamng’ono. Ali mwana makolo ake anamuphunzitsa kupemphera. Ali mtsikana anayamba upainiya ndipo nthawi ndi nthawi ankapempha Yehova kuti adalitse utumiki wake. Patapita zaka mwamuna wake atayamba kudwala kwambiri, iye ankapempha Yehova kuti amuthandize kupirira mayesero amenewo. Panopa ndi wamasiye ndipo amapemphera nthawi zonse n’kumakhulupirira kuti Atate wake wakumwamba ayankha mapemphero ake monga mmene wakhala akuchitira m’mbuyo monsemu.