Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 32

Limbitsani Cikhulupililo Canu mwa Mlengi

Limbitsani Cikhulupililo Canu mwa Mlengi

“Cikhulupililo ndico . . . umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.”—AHEB. 11:1.

NYIMBO 11 Cilengedwe Citamanda Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi munaphunzila zotani ponena za Mlengi wathu?

NGATI munakulila m’banja la Mboni za Yehova, ndiye kuti mwina munaphunzila za Yehova muli wamng’ono. Munaphunzila kuti iye ni Mlengi, ali na makhalidwe abwino, komanso kuti ali na colinga cabwino kwa anthu.—Gen. 1:1; Mac. 17:24-27.

2. Kodi anthu ena amawaona bwanji awo amene amakhulupilila mwa Mlengi?

2 Anthu ambili sakhulupilila kuti Mulungu aliko, kapena kuti iye ndiye Mlengi. M’malo mwake, iwo amakhulupilila kuti moyo unangoyambika wokha. Kenako pang’ono-m’pang’ono, zamoyo zing’ono-zing’ono zinayamba kusandulika kukhala zamoyo zamitundu yosiyana-siyana. Ndipo ena mwa anthu amenewo amakhala ophunzila kwambili. Iwo amati sayansi yatsimikizila kuti zimene Baibo imakamba si zoona, komanso kuti anthu amene amakhulupilila mwa Mlengi ni mbuli, opanda nzelu, komanso otengeka mosavuta.

3. N’cifukwa ciani kulimbitsa cikhulupililo cathu n’kofunika?

3 Kodi n’zotheka kuti zimene ophunzila amakamba zitipangitse kuyamba kukaikila kuti Yehova ni Mlengi wathu wacikondi? Zimadalila kwambili pa cifukwa cake timakhulupilila kuti Yehova ni Mlengi. Kodi tinacita kuuzidwa kuti tikhulupilile zimenezi, kapena tinacita kutayilapo nthawi kufufuza na kudzipezela tekha umboni wake? (1 Akor. 3:12-15) Kaya takhala Mboni ya Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tiyenela kupitiliza kulimbitsa cikhulupililo cathu. Tikatelo, sitidzasoceletsedwa na “nzelu za anthu ndi cinyengo copanda pake,” zimene anthu otsutsa Mawu a Mulungu amaphunzitsa. (Akol. 2:8; Aheb. 11:6) Pofuna kutithandiza, m’nkhani ino tikambilana (1) cifukwa cake anthu ambili sakhulupilila mwa Mlengi, (2) mmene mungalimbitsile cikhulupililo canu mwa Yehova, Mlengi wanu, komanso (3) zimene mungacite kuti cikhulupililo canuco cikhalebe colimba.

CIFUKWA CAKE ANTHU AMBILI SAKHULUPILILA MWA MLENGI

4. Malinga na Aheberi 11:1, kodi cikhulupililo ca zoona cimatsamila pa ciani?

4 Anthu ena amaganiza kuti kukhala na cikhulupililo kumatanthauza kungokhulupilila cina cake popanda umboni. Koma malinga na zimene Baibo imaphunzitsa, ici sindico cikhulupililo ca zoona. (Ŵelengani Aheberi 11:1.) Onani kuti kukhulupilila zosaoneka monga Yehova, Yesu, na Ufumu wakumwamba, n’kozikidwa pa umboni weniweni. (Aheb. 11:3) Wasayansi wina amene anakhala Mboni anati: “Mboni za Yehova zili na umboni wa zimene zimakhulupilila. Ngakhale n’conco, iwo sanyalanyaza zimene asayansi amakamba.”

5. N’cifukwa ciani anthu ambili amakhulupilila kuti moyo unangoyambika wokha popanda Mlengi?

5 Tingadzifunse kuti, ‘Ngati pali umboni wakuti Mlengi alikodi, n’cifukwa ciani anthu ambili sakhulupilila kuti Mulungu ndiye analenga zinthu?’ Ena sanayesepo n’komwe kupeza umboni wa zimenezi pa iwo okha. Robert, amene tsopano ni Mboni anati: “Popeza kuti ku sukulu sanaphunzitsepo zacilengedwe, n’nali kuganiza kuti kulibe Mlengi. Koma n’tafika zaka za m’ma 20, Mboni za Yehova zinanifikila. Iwo ananionetsa umboni wosatsutsika wa m’Baibo wakuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse.” *—Onani bokosi lakuti “Mawu kwa Makolo.”

6. N’cifukwa ciani anthu ena sakhulupilila mwa Mlengi?

6 Ena sakhulupilila mwa Mlengi cifukwa amakamba kuti amakhulupilila cabe zinthu zooneka na maso. Komabe, iwo amakhulupilila kuti kuli mphamvu yokoka zinthu kuti zigwe pansi ngakhale kuti samatha kuiona. Cikhulupililo cochulidwa m’Baibo cimaphatikizapo ‘umboni wa zinthu zenizeni zosaoneka.’ (Aheb. 11:1) Zimatenga nthawi, komanso zimafuna khama kuti tiphunzile maumboni amenewo patokha. Ndipo anthu ambili alibe cidwi cocita zimenezo. Munthu amene sapenda maumboni payekha, angayambe kukhulupilila kuti kulibe Mulungu.

7. Kodi anthu onse ophunzila amatsutsa zakuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse? Fotokozani.

7 Pambuyo popenda maumboni, asayansi ena afika pokhulupilila kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse. * Monga zinalili kwa Robert, amene tam’chula poyamba, ena anali kuganiza kuti kulibe Mlengi cifukwa sanaphunzilepo za cilengedwe ku mayunivesiti. Komabe, asayansi ambili afika podziŵa Yehova na kum’konda. Mofanana na asayansi amenewa, tonsefe tiyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Mulungu, mosasamala kanthu za maphunzilo amene tili nawo. Palibe wina angaticitile zimenezi.

MMENE MUNGALIMBITSILE CIKHULUPILILO CANU MWA MLENGI

8-9. (a) Tikambilane funso liti tsopano? (b) Kodi kuphunzila za cilengedwe kungakupindulitseni bwanji?

8 Kodi mungalimbitse bwanji cikhulupililo canu mwa Mlengi? Tiyeni tikambilane njila zinayi.

9 Muziphunzila za cilengedwe. Mungalimbitse cikhulupililo canu mwa kuyang’anitsitsa nyama, zomela, na nyenyezi. (Sal. 19:1; Yes. 40:26) Pamene muphunzila kwambili zinthu zimenezi, m’pamenenso cikhulupililo canu cakuti Yehova ndiye Mlengi cidzalimba kwambili. Kambili, mabuku athu amakhala na nkhani zofotokoza mwatsatane-tsatane zinthu za cilengedwe. Simuyenela kulumphila kuŵelenga nkhanizi, ngakhale muona kuti n’zovuta kuzimvetsetsa. Phunzilani zambili mmene mungathele. Cina, mungapenyelelenso mavidiyo okamba za cilengedwe pa webusaiti yathu, amene tinapenyelela pa misonkhano yacigawo pa zaka zaposacedwa.

10. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene cilengedwe cimapelekela umboni wakuti Mlengi alikodi. (Aroma 1:20)

10 Pamene muyang’ana cilengedwe, muzikhala chelu kuti muphunzile zinthu zokhudza Mlengi wathu. (Ŵelengani Aroma 1:20.) Mwacitsanzo, mungaphunzile kuti kuwonjezela pa kucilikiza zamoyo padziko, dzuŵa limatulutsanso mphamvu ya kuwala kwake yowononga. Ife anthu timatetezedwa ku mphamvu yowononga imeneyo. Motani? M’mlenga-lenga muli mpweya umene umacepetsako mphamvu yowononga yocokela ku dzuŵa. Pamene mphamvuyo iculukila-culukila, nawonso mpweya umenewo umaculukila-culukila. Ndiye, kodi simungavomeleze kuti pali wina wake amene amacititsa zimenezi, ndiponso kuti iye ni Mlengi wacikondi komanso wanzelu?

11. Ni kuti kumene mungapeze mfundo zolimbitsa cikhulupililo pa nkhani ya cilengedwe? (Onani bokosi lakuti, “ Zida Zothandiza Kulimbitsa Cikhulupililo.”)

11 Mungapeze mfundo zambili zolimbitsa cikhulupililo pa nkhani ya cilengedwe, mwa kufufuza m’buku la Watch Tower Publications Index, komanso pa jw.org. Mwina mungayambe na kuŵelenga nkhani, komanso kutamba mavidiyo pa mbali yakuti “Kodi Zinangocitika Zokha?” Nkhani zake na mavidiyo ake ni aafupi, ndipo ali na mfundo zocititsa cidwi zokhudza nyama na zolengedwa zina. Mulinso zitsanzo zoonetsa mmene asayansi ayesela kupanga zinthu mokopela zimene aona m’cilengedwe.

12. Pamene muŵelenga Baibo, ni zinthu zina ziti zimene muyenela kuganizila?

12 Muziŵelenga Baibo. Wasayansi amene tam’chula kuciyambi kwa nkhani ino, poyamba sanali kukhulupilila za Mlengi. Koma m’kupita kwa nthawi, anafika pokhulupilila kuti Mlengi alikodi. Iye anati: “Cikhulupililo canga sicinali cozikidwa cabe pa zimene n’naphunzila zokhudza sayansi. Koma cinali cozikidwanso pa zimene n’naphunzila m’Baibo.” Mwina muli kale na cidziŵitso colondola pa Baibo. Ngakhale n’telo, kuti mulimbitse cikhulupililo canu mwa Mlengi, muyenela kupitiliza kuphunzila Mawu a Mulungu. (Yos. 1:8; Sal. 119:97) Muziona mmene Baibo imafotokozela molondola mbili yakale. Onani mmene maulosi a m’Baibo anakwanilitsidwila, komanso mmene mfundo za m’Baibo zimagwilizanila. Kucita zimenezi, kudzalimbitsa cikhulupililo canu cakuti Mlengi wathu wacikondi komanso wanzelu ndiye anatilenga, ndiponso kuti ndiye anauzila Baibo. *2 Tim. 3:14; 2 Pet. 1:21.

13. Ni citsanzo citi coonetsa kuti m’Mawu a Mulungu muli malangizo anzelu?

13 Pamene muŵelenga Mawu a Mulungu, muziona mmene uphungu wake ungakuthandizileni. Mwacitsanzo, kale kwambili Baibo inaticenjeza kuti kukonda ndalama n’koipa, ndipo kumabweletsa “zopweteka zambili.” (1 Tim. 6:9, 10; Miy. 28:20; Mat. 6:24) Kodi mfundo imeneyi ikali yothandizabe masiku ano? Buku lina (The Narcissism Epidemic) linati: “Pa avaleji, anthu okonda cuma sakhala acimwemwe, ndipo amakhala opsinjika maganizo. Amakhalanso na mavuto ena okhudza thanzi.” Ndiye cifukwa cake, n’kothandiza ngako kumvela cenjezo la m’Baibo lakuti tipewe kukonda ndalama. Kodi mungaganizileko mfundo zina za m’Baibo zimene zakhala zothandiza? Tikaona mmene mfundo za m’Baibo zilili zothandiza, m’pamenenso tidzayamba kudalila kwambili malangizo anzelu a Mlengi wathu wacikondi. (Yak. 1:5) Zotulukapo n’zakuti, tidzakhala na umoyo wacimwemwe.—Yes. 48:17, 18.

14. Kodi kuŵelenga Baibo kudzatiphunzitsa ciani za Yehova?

14 Muziŵelenga Baibo na colinga cofuna kudziŵa Yehova. (Yoh. 17:3) Mukamaŵelenga Baibo, mudzaona kuti makhalidwe amene Yehova ali nawo, ni amenenso amaonekela bwino m’zinthu zimene analenga. Makhalidwe ake amenewo amatithandiza kukhulupilila kuti iye alikodi. (Eks. 34:6, 7; Sal. 145:8, 9) Mukafika pom’dziŵa bwino Yehova, cikhulupililo canu mwa iye cidzalimba, cikondi canu pa iye cidzakulilako, komanso ubale wanu na iye udzalimbilako.

15. Kodi mudzapindula bwanji mukamauzako ena za cikhulupililo canu?

15 Muziuzako ena za cikhulupililo canu mwa Mulungu. Mukamacita zimenezi, cikhulupililo canuco cidzalimbilako. Koma kodi mungacite ciani ngati munthu amene mwam’lalikila, wakufunsani funso lokhudza kukhalapo kwa Mulungu, ndipo simudziŵa mmene mungamuyankhile? Yesani kupeza yankho la m’Malemba lofotokozedwa m’zofalitsa zathu, ndiyeno kambilanani naye yankholo. (1 Pet. 3:15) Mungapemphenso wofalitsa wa cidziŵitso cokulilapo kuti akuthandizeni. Kaya munthuyo avomeleze mayankho a m’Baibo kapena ayi, mudzakhala mutapindulabe na kufufuza kwanu. Ndipo cikhulupililo canu cidzalimbilako. Zotulukapo n’zakuti, simudzakhulupilila anthu ooneka kuti ni anzelu, kapena ophunzila kwambili amene amakamba kuti kulibe Mlengi.

PITILIZANI KULIMBITSA CIKHULUPILILO CANU

16. Cingacitike n’ciani tikaleka kulimbitsa cikhulupililo cathu?

16 Kaya tatumikila Yehova kwa nthawi yaitali motani, tiyenela kupitiliza kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa iye. Cifukwa ciani? Cifukwa ngati sitingasamale, cikhulupililo cathu cingayambe kucepa. Monga taphunzilila, cikhulupililo cimaphatikizapo umboni weniweni wa zinthu zosaoneka. Zinthu zimene sitingathe kuziona, tingaziiŵale mosavuta. Ndiye cifukwa cake, Paulo anati kupanda cikhulupililo ni “chimo limene limatikola mosavuta.” (Aheb. 12:1) Ndiye tingacite ciani kuti tipewe msampha umenewu?—2 Ates. 1:3.

17. N’ciani cingatithandize kukhalabe na cikhulupililo colimba?

17 Coyamba, muzipempha mzimu woyela wa Yehova nthawi zonse. Cifukwa ciani? Cifukwa cikhulupililo ni khalidwe limene mzimu woyela umabala. (Agal. 5:22, 23) Sitingalimbitse cikhulupililo cathu mwa Mlengi wathu popanda thandizo la mzimu wake woyela. Ngati tipitiliza kupempha Yehova mzimu wake, iye adzatipatsa. (Luka 11:13) Ndipo tingam’pemphe mwacindunji kuti: “Tiwonjezeleni cikhulupililo.”—Luka 17:5.

18. Malinga na Salimo 1:2, 3, kodi tili na mwayi wotani?

18 Cinanso, muziŵelenga Mawu a Mulungu nthawi zonse. (Ŵelengani Salimo 1:2, 3.) Pamene Salimo limeneli linali kulembedwa, ni Aisiraeli ocepa amene anali na kope lathunthu la Cilamulo ca Mulungu. Ngakhale n’telo, panali makonzedwe akuti kumapeto kwa zaka 7 zilizonse, mafumu na ansembe azitenga makope athunthu a Cilamulo ca Mulungu, na kuŵelengela “amuna, akazi, ana,” na alendo okhala mu Isiraeli. (Deut. 31:10-12) M’nthawi ya Yesu, mipukutu ya Malemba inali kupezeka na anthu ocepa cabe. Mipukutu yambili anali kuisungila m’masunagoge. Mosiyana na zimenezi, masiku ano anthu ambili ali na Baibo lathunthu kapena mbali yake. Ni mwayi waukulu cotani nanga! Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila mphatso imeneyi?

19. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tikhalebe na cikhulupililo colimba?

19 Tingaonetse kuti timayamikila mphatso ya Mawu a Mulungu mwa kuwaŵelenga nthawi zonse. Tizikhala na pulogilamu yocita phunzilo laumwini. Tisamangocita phunzilo laumwini pamene tapezela mpata. Tikamatsatila pulogilamu yathu yocita phunzilo laumwini, cikhulupililo cathu cidzapitiliza kukhala colimba.

20. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciani?

20 Mosiyana na “anthu anzelu ndi ozindikila” a m’dzikoli, ife tili na cikhulupililo colimba cozikidwa pa Mawu a Mulungu. (Mat. 11:25, 26) Cifukwa coŵelenga buku lopatulika limeneli, ife tidziŵa cifukwa cake zinthu zikuipilaipila padzikoli, komanso zimene Yehova adzacita posacedwa. Conco, tiyeni tiyesetse kulimbitsa cikhulupililo cathu, komanso kuthandiza anthu ambili kuti akhale na cikhulupililo mwa Mlengi wathu. (1 Tim. 2:3, 4) Ndipo tiyeni tipitilize kuyang’ana kutsogolo panthawi imene onse padziko lapansi adzatamanda Yehova mwa kukamba mawu apa Chivumbulutso 4:11 akuti: “Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo . . . cifukwa munalenga zinthu zonse.”

NYIMBO 2 Dzina Lanu Ndimwe Yehova

^ ndime 5 Baibo imakamba momveka bwino kuti Yehova Mulungu ni Mlengi. Koma anthu ambili sakhulupilila zimenezi. Iwo amakhulupilila kuti moyo unangokhalako wokha. Zimene amakamba zingatipangitse kuyamba kukayikila kuti moyo unacita kulengedwa. Koma tingapewe zimenezi ngati tiyesetsa kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Mulungu, komanso pa Baibo. Nkhani ino ifotokoze mmene tingacitile zimenezi.

^ ndime 5 M’masukulu ambili, ana saphunzitsidwa zakuti zinthu zonse zinacita kulengedwa. Aphunzitsi ena samatelo posafuna kukakamiza mwana wa sukulu aliyense kukhulupilila mwa Mulungu.

^ ndime 7 Akatswili ambili kuphatikizapo asayansi, amakhulupilila cilengedwe. Onani zimene ena akambapo mu Galamukani! ya September 2006, pansi pa mutu wakuti, “Cifukwa Cimene Timakhulupilila Kuti Kuli Mlengi.”

^ ndime 12 Mwacitsanzo onani nkhani yakuti “Kodi Sayansi ndi Baibo Zimagwilizana?,” mu Galamukani! ya Chichewa ya February 2011, komanso yakuti “Zimene Yehova Amalosela Zimakwanilitsidwa,” mu Nsanja ya Olonda ya Chichewa ya January 1, 2008.