Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 34

Kodi Tingatani Kuti ‘Tilawe’ Ubwino wa Yehova?

Kodi Tingatani Kuti ‘Tilawe’ Ubwino wa Yehova?

“Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino. Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawira kwa iye.”​—SAL. 34:8.

NYIMBO NA. 117 Ubwino wa Yehova

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Mogwirizana ndi Salimo 34:8, kodi tingatani kuti tilawe ubwino wa Yehova?

YEREKEZERANI kuti munthu wina wakupatsani chakudya chimene simunachilawepo. Mukhoza kudziwa zambiri zokhudza chakudyacho pongochiyang’ana, kuchinunkhiza, kudziwa zinthu zina zimene aikamo komanso pofunsa anthu ena amene amachidziwa. Koma njira yabwino yodziwira mmene chakudyacho chimakomera ndi kuchilawa nokha.

2 Mofanana ndi zimenezi, tikhoza kuphunzira za ubwino wa Yehova powerenga Baibulo kapena mabuku athu, kapenanso pomvetsera pamene anthu ena akufotokoza madalitso amene Yehova wawapatsa. Komabe, timamvetsa ubwino wa Yehova ‘tikalawa’ tokha ubwino wakewo. (Werengani Salimo 34:8.) Tiyeni tione chitsanzo cha mmene tingachitire zimenezi. Tiyerekeze kuti tikufuna kuchita utumiki winawake wanthawi zonse, koma kuti tikwanitse cholinga chimenechi, tiyenera kusintha zinthu zina pa moyo wathu. N’kutheka kuti takhala tikuwerengapo za lonjezo la Yesu lakuti tikamayika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba, Yehova adzatipatsa zimene timafunikira. (Mat. 6:33) Koma ifeyo patokha, sitinaonepo kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli. Ngakhale zili choncho, pokhulupirira lonjezo la Yesuli, tachepetsa zimene timagula komanso nthawi imene timagwira ntchito n’cholinga choti tizichita zambiri pa ntchito yolalikira. Pamene tikuchita zimenezi, tikufika podzionera tokha kuti Yehova amatipatsadi zinthu zimene timafunikira. Zikatero timakhala kuti ‘talawa’ tokha ubwino wa Yehova.

3. Mogwirizana ndi Salimo 16:1, 2, kodi ndi ndani amasangalala ndi ubwino wa Yehova?

3 Yehova ndi wabwino, kapena kuti “amakomera mtima aliyense,” kuphatikizapo amene samudziwa. (Sal. 145:9; Mat. 5:45) Komabe iye amapereka madalitso ambiri kwa anthu amene amamukonda komanso kumutumikira ndi mtima wonse. (Werengani Salimo 16:1, 2.) Tiyeni tione zinthu zina zabwino zimene Yehova amatichitira.

4. Kodi Yehova amasonyeza bwanji ubwino wake kwa anthu amene ayamba kukhala naye pa ubwenzi?

4 Nthawi iliyonse imene taphunzira komanso kugwiritsa ntchito zomwe taphunzira zokhudza Yehova, timaona ubwino wa zimenezi pa moyo wathu. Titayamba kuphunzira za iye komanso kumukonda, anatithandiza kusiya maganizo olakwika komanso makhalidwe amene sasangalala nawo. (Akol. 1:21) Ndipo titadzipereka n’kubatizidwa, tinayamba kuona ubwino wake mowonjezereka pamene anatipatsa chikumbumtima chabwino komanso kutithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba.​—1 Pet. 3:21.

5. Kodi timaona bwanji ubwino wa Yehova tikamagwira ntchito yolalikira?

5 Timapitiriza kuona ubwino wa Yehova tikamagwira ntchito yolalikira. Kodi ndinu munthu wamanyazi? Atumiki enanso ambiri a Yehova ndi amanyazi. N’kutheka kuti musanakhale mtumiki wa Yehova, simunkaganizira n’komwe kuti tsiku lina mungadzagogode pakhomo la munthu yemwe simukumudziwa n’kumamufotokozera uthenga wa m’Baibulo. Koma masiku ano mumachita zimenezi nthawi zonse. Ndipo Yehova wakuthandizani kuti muzisangalala kwambiri mukamagwira ntchito yolalikira. N’kutheka mwaona kuti iye wakuthandizaninso m’njira zina. Wakuthandizani kuti muziugwira mtima mukakumana ndi otsutsa, muzikumbukira lemba loyenera loti mukambirane ndi munthu amene wasonyeza chidwi komanso wakupatsani mphamvu kuti muzipitirizabe kulalikira, ngakhale pamene mwakumana ndi anthu amene sakufuna kumvetsera.​—Yer. 20:7-9.

6. Kodi maphunziro amene Yehova amatipatsa amasonyeza bwanji kuti iye ndi wabwino?

6 Yehova amatisonyezanso ubwino wake potiphunzitsa mmene tingagwirire ntchito yolalikira. (Yoh. 6:45) Pamisonkhano yamkati mwa mlungu, timamvetsera zitsanzo za ulaliki zokonzedwa bwino ndipo timalimbikitsidwa kuzigwiritsa ntchito tikamalalikira. Poyamba tikhoza kumachita mantha kuti tiyesere zinthu zatsopano. Koma tikamagwiritsa ntchito malangizowo, tingayambe kuona kuti uthenga wathu ukuwafika pamtima anthu a m’gawo lathu. Pamisonkhano yampingo komanso yachigawo, timalimbikitsidwanso kuti tiziyesa kugwiritsa ntchito njira zina zolalikirira zomwe sitinaziyesepo. Zimenezinso zingamatidetse nkhawa. Komabe tikamazichita, Yehova amatidalitsa. Tsopano tiyeni tikambirane ena mwa madalitso amene timapeza chifukwa choyesa kugwiritsa ntchito njira zatsopano potumikira Yehova, posatengera mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Kenako tikambirana njira zinanso zimene tingawonjezerere utumiki wathu.

YEHOVA AMADALITSA ANTHU AMENE AMAMUKHULUPIRIRA

7. Kodi timapeza madalitso otani tikamachita khama kuwonjezera utumiki wathu?

7 Timakhala pa ubwenzi wolimba kwambiri ndi Yehova. Taganizirani zimene zinachitikira mkulu wina dzina lake Samuel, * yemwe ndi mkazi wake amatumikira ku Colombia. Banjali linkasangalala kuchita upainiya mumpingo wakwawo. Komabe, ankafuna kuwonjezera zochita pa utumiki wawo pokathandiza mpingo wina womwe kunkafunika olalikira ambiri. Kuti akwaniritse cholinga chimenechi, iwo ankafunika kusintha zinthu zina pa moyo wawo. Samuel ananena kuti: “Poganizira zimene zili pa Mateyu 6:33, tinasiya kugula zinthu zina zosafunika. Koma chovuta kwambiri chinali kusamuka m’nyumba yathu. Nyumbayi tinkaikonda chifukwa inamangidwa m’njira imene ifeyo tinkafuna ndipo tinalibe ngongole iliyonse yokhudza nyumbayi.” Iwo atayamba utumiki watsopanowu, anaona kuti ankagwiritsa ntchito ndalama zochepa kwambiri poyerekeza ndi zimene ankagwiritsa ntchito m’mbuyomo. Samuel ananenanso kuti: “Taona Yehova akutitsogolera komanso kuyankha mapemphero athu. Panopa tazindikira kuti Yehova amatikonda kwambiri kuposa mmene takhala tikuonera m’mbuyomu.” Kodi inunso mungawonjezere zochita pa utumiki wanu? Ngati ndi choncho, dziwani kuti mudzakhala pa ubwenzi wolimba kwambiri ndi Yehova ndipo iye adzakusamalirani.​—Sal. 18:25.

8. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Ivan ndi Viktoria ananena?

8 Timasangalala ndi utumiki wathu. Taonani zimene ananena Ivan ndi Viktoria, banja lomwe likuchita upainiya ku Kyrgyzstan. Iwo anasintha zinthu zina pa moyo wawo n’cholinga choti adzipereke pochita utumiki uliwonse, kuphatikizapo wa zomangamanga. Ivan ananena kuti: “Tinkagwira mwakhama ntchito iliyonse. Ngakhale kuti tinkatopa tsiku likamatha, tinkakhala ndi mtendere wamumtima komanso okhutira podziwa kuti tagwiritsa ntchito mphamvu zathu pa ntchito za Ufumu. Tinkasangalalanso chifukwa tinapeza anzathu atsopano ndipo tinali ndi zinthu zabwino zambiri zimene tinkazikumbukira.”​—Maliko 10:29, 30.

9. Kodi mlongo wina yemwe akukumana ndi mavuto osiyanasiyana wachita chiyani kuti awonjezere utumiki wake, ndipo pakhala zotsatira zotani?

9 Tingamasangalale potumikira Yehova ngakhale tikukumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, mlongo wina wachikulire komanso wamasiye wa ku West Africa dzina lake Mirreh, anayamba upainiya atapuma pa ntchito yake ya udokotala. Panopa Mirreh amavutika ndi nyamakazi ndipo amangolalikira kwa ola limodzi akamalalikira kunyumba ndi nyumba. Komabe iye amatha kulalikira kwa nthawi yaitali akamalalikira m’malo opezeka anthu ambiri. Iye ali ndi maulendo obwereza komanso maphunziro ambiri ndipo ena mwa iwo amakambirana nawo kudzera patelefoni. Kodi n’chiyani chinalimbikitsa Mirreh kuti azichita zambiri potumikira Yehova? Iye anati: “Ndimakonda kwambiri Yehova ndi Khristu Yesu ndipo nthawi zonse ndimapempha Yehova kuti azindithandiza kuchita zambiri pomutumikira.”​—Mat. 22:36, 37.

10. Mogwirizana ndi 1 Petulo 5:10, kodi Yehova amawachitira zotani anthu amene amawonjezera zochita pomutumikira?

10 Timalandira maphunziro owonjezereka kuchokera kwa Yehova. Kenny, yemwe ndi mpainiya ku Mauritius, anaona kuti zimenezi ndi zoona. Ataphunzira choonadi, anasiya maphunziro a kuyunivesite n’kubatizidwa ndipo kenako anayamba utumiki wanthawi zonse. Iye ananena kuti, “Ndimayesetsa kutengera chitsanzo cha mneneri Yesaya yemwe anati: ‘Ine ndilipo! Nditumizeni.’” (Yes. 6:8) Iye wathandizapo nawo ntchito zingapo zomangamanga komanso kumasulira mabuku ofotokoza Baibulo m’chilankhulo chake. Kenny ananena kuti: “Ndinalandira maphunziro amene anandithandiza kukhala ndi luso limene ndinkafunikira pa ma utumiki osiyanasiyana.” Koma iye anaphunzira zambiri, osati chabe luso logwirira ntchito inayake. Iye ananenanso kuti, “Ndadziwa zimene ndingakwanitse ndi zimene sindingakwanitse komanso makhalidwe amene ndiyenera kukulitsa n’cholinga choti ndikhale mtumiki wabwino wa Yehova.” (Werengani 1 Petulo 5:10.) Bwanji inunso osaganizira mmene zinthu zilili pa moyo wanu n’kuona ngati mungadzipereke kuti mulandire maphunziro owonjezereka kuchokera kwa Yehova?

Banja likulalikira kumene kukufunika olalikira ambiri, mlongo wachitsikana akuthandiza pantchito yomanga Nyumba ya Ufumu, banja lachikulire likulalikira pa telefoni. Onsewa akusangalala ndi zimene akuchita pa utumiki wawo (Onani ndime 11)

11. Kodi alongo ena a ku South Korea anachita chiyani kuti azilalikira, nanga zotsatira zake zinali zotani? (Onani chithunzi chapachikuto.)

11 A Mboni amene akhala akutumikira Yehova kwa nthawi yaitali, amapindulanso ndi maphunziro omwe amapatsidwa akamayesa kuchita utumiki watsopano. Pa nthawi ya mliri wa COVID-19, akulu a mumpingo wina ku South Korea analemba kuti: “Anthu ena omwe poyamba ankaganiza kuti sangamalalikire chifukwa cha thanzi lawo, panopa amalalikira kudzera pa vidiyokonferensi. Alongo atatu azaka za m’ma 80 anaphunzira mmene angamagwiritsire ntchito zipangizo zamakono ndipo anayamba kulalikira nawo pafupifupi tsiku lililonse.” (Sal. 92:14, 15) Kodi inunso mungakonde kuwonjezera utumiki wanu kuti mulawe ubwino wa Yehova mowonjezereka? Tiyeni tione zinthu zina zomwe mungachite kuti mukwaniritse cholinga chanu.

KODI MUNGATANI KUTI MUZICHITA ZAMBIRI?

12. Kodi Yehova amalonjeza chiyani anthu amene amamudalira?

12 Muzidalira Yehova. Iye amalonjeza kuti azitipatsa madalitso ochuluka tikamamudalira komanso kuchita zonse zomwe tingathe pomutumikira. (Mal. 3:10) Mlongo wina wa ku Colombia, dzina lake Fabiola, anaona mmene Yehova anakwaniritsira lonjezo limeneli pa moyo wake. Iye atangobatizidwa, ankafuna atachita upainiya wokhazikika. Koma ankafunika kumagwira ntchito kuti azisamalira mwamuna wake komanso ana ake atatu. Choncho itafika nthawi yoti akhoza kupuma pantchito, anapemphera kwambiri kwa Yehova kuti amuthandize. Iye anati: “Nthawi zambiri pamatenga nthawi yaitali kuti munthu ayambe kulandira ndalama za penshoni. Koma ine ndinayamba kulandira patangotha mwezi umodzi. Zinali zodabwitsa kwambiri!” Patangotha miyezi iwiri, iye anayamba upainiya. Panopa ali ndi zaka za m’ma 70 ndipo wakhala akuchita upainiya kwa zaka zoposa 20. Pa nthawi imeneyi, mlongoyu wathandiza anthu okwana 8 kubatizidwa. Iye ananena kuti: “Ngakhale kuti nthawi zina ndimafooka, Yehova amandithandiza tsiku lililonse kuti ndipitirizebe kuchita upainiya.”

Kodi Abulahamu ndi Sara, Yakobo komanso ansembe omwe anawoloka mtsinje wa Yorodano anasonyeza bwanji kuti ankadalira Yehova? (Onani ndime 13)

13-14. Kodi ndi zitsanzo ziti zomwe zingatithandize kuti tizidalira Yehova n’kumachita zambiri pomutumikira?

13 Muziphunzira kwa anthu amene anasonyeza kudalira Yehova. M’Baibulo muli zitsanzo za anthu ambiri omwe anachita khama potumikira Yehova. Nthawi zambiri, atumiki a Yehovawa ankafunika kuchita kaye zinazake zosonyeza kuti akumudalira kuti iye awadalitse. Mwachitsanzo, panali pambuyo poti Abulahamu wachoka kwawo, “ngakhale sanadziwe kumene anali kupita,” pamene Yehova anamudalitsa. (Aheb. 11:8) Yakobo analandiranso madalitso apadera pambuyo poti walimbana ndi mngelo. (Gen. 32:24-30) Komanso Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, panali pamene ansembe anaponda mumtsinje wa Yorodano pomwe anthu anatha kuwoloka.​—Yos. 3:14-16.

14 Mukhozanso kuphunzira zambiri kwa a Mboni za Yehova amasiku ano, omwe asonyeza kudalira Yehova n’kudzipereka kuti achite zambiri pomutumikira. Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Payton ndi mkazi wake Diana, ankasangalala kuwerenga nkhani za abale ndi alongo amene anawonjezera zochita potumikira Yehova, monga omwe afotokozedwa munkhani zakuti, “Anadzipereka ndi Mtima Wonse.” * Payton ananena kuti: “Tikamawerenga nkhani zimenezi, zinkangokhala ngati tikuona munthu wina amene akudya chakudya chokoma. Pamene tinkawerenga kwambiri nkhani zimenezi, m’pamenenso tinkafunitsitsa ‘kulawa ndi kuona kuti Yehova ndi wabwino.’” Pasanapite nthawi, Payton ndi Diana anasamukira kumene kunkafunikira olalikira Ufumu ambiri. Kodi inunso munawerengapo nkhani zimenezi? Ndiponso kodi mwaonerapo mavidiyo akuti, Kulalikira M’dera Lakutali​—Australia komanso Kulalikira M’dera Lakutali M’dziko la Ireland, omwe akupezeka pa jw.org? Mavidiyo amenewa angakuthandizeni kuona zimene mungachite kuti muwonjezere utumiki wanu.

15. Kodi kugwirizana ndi anthu oyenera kungatithandize bwanji?

15 Muzigwirizana ndi anthu oyenera. Anthufe timafunitsitsa kudya chakudya chinachake tikamakonda kucheza ndi anthu amene amakonda kudya chakudyacho. Mofanana ndi zimenezi, tikamakonda kucheza ndi anthu amene amaona kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri, ifenso timayamba kufufuza zimene tingachite kuti tiwonjezere zochita potumikira Mulungu. Kent ndi Veronica, omwe ndi banja, anaona kuti zimenezi n’zoona. Kent ananena kuti: “Anzathu komanso achibale athu anatilimbikitsa kuti tiyesere kuchita utumiki watsopano. Tinazindikira kuti kucheza ndi anthu amene amaika patsogolo zinthu za Ufumu kunatithandiza kuona kuti tingawonjezere utumiki wathu.” Panopa Kent ndi Veronica akutumikira ngati apainiya ku Serbia.

16. Mogwirizana ndi fanizo la Yesu la pa Luka 12:16-21, n’chifukwa chiyani tiyenera kudzimana zinthu zina potumikira Yehova?

16 Muzilolera kudzimana kuti mutumikire Yehova. Sikuti timafunika kusiya zinthu zonse zabwino kuti tizisangalatsa Yehova. (Mlal. 5:19, 20) Komabe ngati titalephera kuchita zambiri potumikira Yehova, mwina pongofuna kusadzimana zinthu zina, tikhoza kukhala tikulakwitsa ngati munthu wamufanizo la Yesu. Iye anachita khama kuti azikhala moyo wawofuwofu koma sankaganizira za Mulungu. (Werengani Luka 12:16-21.) M’bale wina dzina lake Christian, yemwe amakhala ku France, ananena kuti, “Sindinkachita zonse zomwe ndingathe potumikira Yehova komanso kuthandiza banja langa.” Iye ndi mkazi wake anaganiza zoyamba upainiya. Koma kuti akwaniritse cholinga chawochi, ankafunika kusiya ntchito zawo. Kuti azipeza zinthu zofunikira pa moyo, iwo anayamba bizinezi yaing’ono yoyeretsa ma ofesi ndi nyumba za anthu ndipo anaphunzira kukhala okhutira ndi zochepa zimene ali nazo. Kodi iwo anayamba kusangalala chifukwa cha zimene anachitazi? Christian anati, “Timasangalala kwambiri ndi utumiki komanso kuona ophunzira Baibulo athu ndi maulendo obwereza akuphunzira za Yehova.”

17. N’chiyani chingatilepheretse kuyeserera njira zatsopano zolalikirira?

17 Muzikhala ofunitsitsa kuyeserera njira zatsopano zolalikirira. (Mac. 17:16, 17; 20:20, 21) Shirley, yemwe ndi mpainiya ku United States, ankafunika kusintha njira zolalikirira pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Poyamba, iye ankazengereza kuti ayambe kulalikira pogwiritsa ntchito telefoni. Koma pa mlungu wina wapadera ataphunzitsidwa mmene angachitire zimenezi, iye anayamba kugwiritsa ntchito njirayi nthawi zonse. Shirley anati: “Poyamba ndinkachita mantha, koma tsopano ndimasangalala kulalikira pafoni. Panopa timalalikira anthu ambiri kuposa mmene tinkachitira tikamalalikira kunyumba ndi nyumba.”

18. Kodi n’chiyani chomwe chingatithandize kulimbana ndi mavuto omwe angatilepheretse kuchita zambiri pa utumiki wathu?

18 Muzidziikira cholinga n’kumayesetsa kuchikwaniritsa. Tikakumana ndi mavuto, tizipempha Yehova kuti atithandize ndipo tiziyesetsa kuganizira zimene tingachite kuti tithane ndi mavuto athuwo. (Miy. 3:21) Sonia, yemwe ndi mpainiya wokhazikika m’kagulu ka Chiromani ku Europe, ananena kuti: “Ndimalemba zolinga zanga papepala n’kulisiya poonekera. Patebulo langa ndinajambula chithunzi cha misewu iwiri yomwe ikulowera kosiyana. Ndikafuna kusankha zochita, ndimayang’ana pamisewu iwiriyo n’kuganizira kuti zimene ndisankhezo zindifikitsa pati.” Sonia amayesetsa kumaona moyenera mavuto amene amakumana nawo. Iye ananena kuti: “Chilichonse chomwe chachitika pa moyo wanga chingakhale ngati khoma londitsekereza kuti ndisakwaniritse zolinga zanga kapena buliji londithandiza kuti ndikwaniritse zolingazo. Zimangodalira mmene ndikuonera zinthu.”

19. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zinthu zabwino zimene Yehova watipatsa?

19 Yehova amatidalitsa m’njira zambiri. Tingasonyeze kuti timayamikira kwambiri zimene amatichitira, pochita zonse zimene tingathe pomutamanda. (Aheb. 13:15) Zimenezi zikuphatikizapo kupeza njira zatsopano zowonjezera utumiki wathu zomwe zimachititsanso kuti Yehova atidalitse kwambiri. Tsiku lililonse, tiyeni tiziyesetsa kupeza njira zotithandiza kuti ‘tilawe ndi kuona kuti Yehova ndi wabwino.’ Tikamachita zimenezi, tingafanane ndi Yesu, yemwe ananena kuti: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.”​—Yoh. 4:34.

NYIMBO NA. 80 “Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova Ndi Wabwino”

^ ndime 5 Zinthu zonse zabwino zimachokera kwa Yehova. Iye amapereka zinthu zabwino kwa aliyense, ngakhalenso kwa anthu oipa. Koma iye amakonda kuchitira zinthu zabwino makamaka atumiki ake okhulupirika. Munkhaniyi, tiona mmene Yehova amaperekera zinthu zabwino kwa atumiki ake. Tionanso njira yapadera yosonyeza mmene Yehova amaperekera zinthu zabwino kwa atumiki ake amene amasankha kuchita zambiri pomutumikira.

^ ndime 7 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 14 Nkhani zimenezi, zomwe poyamba zinkafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda, panopa zikupezeka pa jw.org. Pitani pamene alemba kuti ZOKHUDZA IFEYO > ZOCHITIKA PA MOYO WA A MBONI ZA YEHOVA > KUKWANIRITSA ZOLINGA ZAUZIMU.