Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 34

‘Laŵani’ Ubwino wa Yehova—Motani?

‘Laŵani’ Ubwino wa Yehova—Motani?

“Talaŵani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino. Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawila kwa iye.”—SAL. 34:8.

NYIMBO 117 Ubwino

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Malinga na Salimo 34:8, kodi tingaudziŵe bwanji ubwino wa Yehova?

YELEKEZANI kuti munthu wina wakupatsani cakudya cimene simucidziŵa ndipo mukalibe kudyapo. Mungacizindikile cakudyaco mukaciyang’anitsitsa, kucinunkhiza, kapena kufunsako ena kuti akuuzenkoni zimene adziŵa pa cakudyaco. Koma kuti mudziŵe ngati cakudyaco mungacikonde, muyenela kucilaŵa inu mwini.

2 Timaphunzila za ubwino wa Yehova mwa kuŵelenga Baibo, zofalitsa zathu, na zimene timamva kwa ena akamakamba za madalitso amene alandila kwa Yehova. Koma tidzamvetsetsa ubwino wa Yehova, ngati tadzilaŵila tekha ubwino wake. (Ŵelengani Salimo 34:8.) Tiyeni tione mmene tingacitile zimenezi. Tiyelekeze kuti mufuna kuyamba utumiki wanthawi zonse. Koma kuti mukwanilitse colinga cimeneci, muyenela kusintha zinthu zina mu umoyo wanu. Mwina mobweleza-bweleza mwakhala mukuŵelenga lonjezo la Yesu lakuti ngati tiika Ufumu patsogolo, Yehova adzatipatsa zosoŵa zathu. Koma mukalibe kuonapo kukwanilitsika kwa lonjezo limeneli pa inu. (Mat. 6:33) Ngakhale n’telo, cifukwa cokhulupilila lonjezo la Yesu limeneli, mukucepetsako zogula-gula, kusinthako zinthu zina pa nchito yanu yakuthupi, na kusumika maganizo anu pa ulaliki. Mwa kucita izi, mudzadzionela nokha kuti Yehova amatipatsadi zimene timafunikila pa umoyo. ‘Timalaŵa’ ubwino wa Yehova patekha.

3. Malinga na Salimo 16:1, 2, ndani amapindula na ubwino wa Yehova?

3 Yehova “amakomela mtima aliyense,” ngakhale anthu amene sam’dziŵa. (Sal. 145:9; Mat. 5:45) Koma amene amalandila madalitso oculuka kwa Yehova, ni amene amam’konda na kum’tumikila na mtima wonse. (Ŵelengani Salimo 16:1 2.) Tiyeni tikambilane zina mwa zinthu zabwino zimene Yehova waticitila.

4. Kodi Yehova waonetsa bwanji ubwino wake kwa amene ayamba kumuyandikila?

4 Nthawi zonse tikamaseŵenzetsa zimene taphunzila kwa Yehova, timakhala na umoyo wabwino. Pamene tiphunzila za iye na kuyamba kum’konda, amatithandiza kuthetsa maganizo oipa na makhalidwe amene amadana nawo. (Akol. 1:21) Ndipo pamene tinadzipatulila kwa Yehova na kubatizika, iye anatipatsanso zinthu zina zabwino, monga cikumbumtima cabwino komanso kukhala pa ubale na iye.—1 Pet. 3:21.

5. Kodi ubwino Yehova umaonekela motani tikakhala mu ulaliki?

5 Timaonanso ubwino wa Yehova pamene titengako mbali m’nchito yolalikila. Kodi ndinu wamanyazi? Ambili mwa anthu a Yehova ni a manyazi. Mwina musanakhale mtumiki wa Yehova, simunaganizilepo zogogoda pakhomo la munthu amene simum’dziŵa n’komwe, na kumuuza uthenga umene ni wacilendo kwa iye. Koma lomba, ndiye zimene mumacita nthawi zonse. Ndipo koposa zonse, Yehova amakuthandizani kupeza cimwemwe pamene mugwila nchito yolalikila. Mwaonanso cicilikizo ca Yehova m’njila zina zambili. Iye amakuthandizani kukhala odekha mukakumana na munthu wotsutsa mu ulaliki. Amakuthandizaninso kukumbukila lemba loyenelela pamene munthu wina waonetsa cidwi. Cina, amakuthandizani kupitiliza kulalikila olo kuti gawo lanu n’louma.—Yer. 20:7-9.

6. Kodi zimene Yehova amatiphunzitsa zimaonetsa bwanji ubwino wake?

6 Yehova wationetsanso ubwino wake mwa kutiphunzitsa mogwilila nchito yolalikila. (Yoh. 6:45) Pa misonkhano ya mkati mwa mlungu, timamvetsela maulaliki acitsanzo ogwila mtima, ndipo timalimbikitsidwa kuseŵenzetsa malangizo ake mu ulaliki. Poyamba, tingadodome kuseŵenzetsa malangizo atsopano mu ulaliki. Koma tikawaseŵenzetsa tidzaona kuti ni othandiza kwambili m’gawo lathu. Pa misonkhano ya mpingo komanso ya cigawo, timalimbikitsidwanso kuseŵenzetsa njila zina zolalikila zimene sitinaziseŵenzetsepo. Kucita zimenezi kumafuna kudzimanako zinthu zina. Koma tikatelo, Yehova amatidalitsa. Tiyeni tione ena mwa madalitso amene tidzapeza ngati tiseŵenzetsa njila zatsopano zimenezo, popatsa Yehova zabwino koposa mosasamala kanthu za mikhalidwe yathu. Kenaka, tikambilane zimene tingacite kuti tiwonjezele utumiki wathu.

YEHOVA AMADALITSA ANTHU AMENE AMAM’KHULUPILILA

7. Ni madalitso otani amene tidzapeza tikamayesetsa kuwonjezela utumiki wathu?

7 Timamuyandikila kwambili Yehova. Ganizilani citsanzo ca mkulu wina dzina lake Samuel, * amene akutumikila ku Colombia pamodzi na mkazi wake. Banjali linali kusangalala kucita upainiya mu mpingo wawo, koma linafuna kuwonjezela utumiki wawo mwa kupita kukathandiza ku mpingo wosoŵa. Kuti akwanilitse colinga cimeneci, anafunika kudzimana zinthu zina. M’bale Samuel anati: “Tinaseŵenzetsa mfundo ya pa Mateyu 6:33, na kusiya kugula zinthu zosafunika kwenikweni. Koma cinativuta kwambili ni kusiya nyumba yathu. Inali nyumba yabwino ngako.” Banjali litasamukila ku mpingo watsopano, linaona kuti silinali kufunikila ndalama zambili. M’bale Samuel anati: “Tinaona mmene Yehova anali kutitsogolela, na mmene anali kuyankhila mapemphelo athu. Tinaonanso kuti Yehova amakondwela nafe, ndipo anationetsa cikondi m’njila zimene sitinayembekezele.” Kodi inunso n’zotheka kuwonjezela utumiki wanu? Ngati n’zotheka, mungakhale wotsimikiza kuti mudzamuyandikila kwambili Yehova, ndipo adzakusamalilani.—Sal. 18:25.

8. Kodi mwaphunzilapo ciani pa zimene m’bale Ivan na mkazi wake Viktoria anakamba?

8 Timapeza cimwemwe mu utumiki wathu. Onani zimene m’bale Ivan na mkazi wake Viktoria, amene ni apainiya ku Kyrgyzstan anakamba. Iwo anakhala na umoyo wosalila zambili, n’colinga cakuti adzipeleke pa utumiki uliwonse, kuphatikizapo nchito yamamangidwe. M’bale Ivan anati: “Tinali kugwila nchito molimbika pa utumiki uliwonse. Olo kuti tinali kukhala olema pambuyo poseŵenzetsa tsiku lonse, tinali kukhala na mtendele wa maganizo komanso okhutila, podziŵa kuti taseŵenzetsa mphamvu zathu pocilikiza nchito ya Ufumu. Cina, tinapeza cimwemwe cacikulu cifukwa copeza mabwenzi atsopano, komanso kukhala na zocitika zosangalatsa.”—Maliko 10:29, 30.

9. Kodi mlongo amene ali na zovuta pa umoyo wake, wacita ciani kuti awonjezele utumiki wake? Nanga pakhala zotulukapo zotani?

9 Timapeza cimwemwe potumikila Yehova ngakhale zinthu zitakhala zovuta. Mwacitsanzo, mlongo wamasiye wokalamba dzina lake Mirreh, amene akhala kumadzulo kwa Africa, anayamba upainiya atapuma pa nchito yake ya udokotala. Mlongo Mirreh ali na matenda amene amapangitsa kuti zikhale zovuta kwa iye kuyenda, ndipo amangokwanitsa ola limodzi cabe mu ulaliki wa nyumba na nyumba. Koma amakwanitsa kuthela nthawi yoculuka pa ulaliki wapoyela. Ndipo ali na maulendo ambili obwelelako na maphunzilo a Baibo, amene ena mwa iwo amakambilana nawo pafoni. N’ciani cimamulimbikitsa kucita zimenezi? Iye anati: “Nimam’konda kwambili Yehova na Khristu Yesu. Ndipo nimapemphela kwa Yehova nthawi zonse kuti anithandize kucita zimene ningakwanitse pom’tumikila.”—Mat. 22:36, 37.

10. Malinga na 1 Petulo 5:10, kodi amene amawonjezela utumiki wawo kwa Yehova, amalandila madalitso otani?

10 Timalandila maphunzilo owonjezeleka kwa Yehova. M’bale Kenny amene ni mpainiya ku Mauritius, anaona kuti mfundo imeneyi ni yoona. Ataphunzila coonadi, iye anasiya maphunzilo a pa yunivesiti, n’kubatizika, na kuyamba utumiki wanthawi zonse. Iye anati: “Nimayesetsa kukhala ngati mneneli Yesaya amene anati: ‘Ine ndilipo! Nditumizeni.’” (Yes. 6:8) M’bale Kenny wakhala akugwila nawo nchito yamamangidwe, komanso kuthandizila kumasulila zofalitsa zozikidwa pa Baibo m’cinenelo cake. Iye anati: “N’nalandila maphunzilo amene ananithandiza kukhala na maluso kuti nikwanitse kucita bwino utumiki wanga.” Sanangophunzila mogwilila nchito cabe, koma anaphunzilanso zinthu zina zambili. Anakambanso kuti: “N’nadziŵa zimene sin’kanakwanitsa kucita, komanso makhalidwe amene n’nafunika kukulitsa kuti nikhale mtumiki wabwino wa Yehova.” (Ŵelengani 1 Petulo 5:10.) Mwina inunso mukhoza kusinthako zina pa umoyo wanu kuti mulandile maphunzilo owonjezela kwa Yehova.

Banja likulalikila kudela limene kuli alengezi a Ufumu ocepa; mlongo wacitsikana akuthandizila pa nchito yomanga Nyumba ya Ufumu; banja lokalamba likucita ulaliki wa pafoni. Onse akupeza cimwemwe mu utumiki wawo (Onani ndime 11)

11. Kodi alongo ku South Korea anacita ciani kuti azilalikila? Nanga panakhala zotulukapo zotani? (Onani cithunzi pacikuto)

11 Ngakhale amene atumikila Yehova kwa nthawi yaitali, angalandilebe maphunzilo pamene ayesa njila zatsopano zocitila utumiki. Mwacitsanzo, panthawi ino ya mlili wa COVID-19, akulu mu mpingo wina ku South Korea analemba kuti: “Ofalitsa ena amene anali kuona kuti sangathe kucita zambili mu ulaliki cifukwa ca thanzi lawo, tsopano amacita zimenezi kupitila pa zipangizo zamakono. Alongo atatu a zaka za m’ma 80, anaphunzila moseŵenzetsela zipangizo zamakono, ndipo amazigwilitsila nchito polalikila pafupifupi tsiku lililonse.” (Sal. 92:14, 15) Kodi mungakonde kuwonjezela utumiki wanu kuti mulaŵe ubwino wa Yehova? Nazi zimene mungacite zokuthandizani kukwanilitsa colinga canu cimeneci.

ZIMENE MUNGACITE

12. Kodi Yehova amawalonjeza ciani anthu amene amam’dalila?

12 Phunzilani kudalila Yehova. Iye analonjeza kuti tikam’dalila na kum’patsa zimene tingathe, adzatikhuthulila madalitso oculuka. (Mal. 3:10) Mlongo wina dzina lake Fabiola wa ku Colombia, anaona mmene Yehova anakwanilitsila lonjezo limeneli pa iye. Anali kufuna kukhala mpainiya wa nthawi zonse atangobatizika. Komabe, iye ndiye anali kusamalila mwamuna wake na ana ake atatu. Conco, itafika nthawi yakuti apume pa nchito yake, anapempha Yehova mocokela pansi pa mtima kuti amuthandize. Anati: “Zimatenga nthawi kuti munthu alandile ndalama zake za penshoni, koma ine n’nalandila ndalamazo patangopita mwezi umodzi cabe. Zinali ngati cozizwitsa!” Pambuyo pa miyezi iŵili anayamba upainiya. Tsopano ali na zaka za m’ma 70, ndipo wakhala akucita upainiya kwa zaka zoposa 20. Pa zaka zonsezi, wathandiza anthu 8 kufika pa kubatizika. Mlongo Fabiola anati: “Olo kuti nimakhala wofooka nthawi zina, Yehova amanithandiza tsiku lililonse kuti nipitilize upainiya.”

Kodi Abulahamu, Sara, Yakobo, komanso ansembe amene anawoloka mtsinje wa Yorodano, anaonetsa bwanji kuti anadalila Yehova? (Onani ndime 13)

13-14. Ni zitsanzo ziti zimene zingatithandize kudalila Yehova na kuwonjezela utumiki wathu?

13 Phunzilani ku zitsanzo za anthu amene anadalila Yehova. M’Baibo, muli zitsanzo za anthu amene anatumikila Yehova modzipeleka kwambili. Zitsanzo zambili zionetsa kuti Yehova anali kudalitsa atumiki ake, pambuyo pocita zinthu zoonetsa kuti amam’khulupilila. Mwacitsanzo, Abulahamu anadalitsidwa pambuyo posiya nyumba yake, “ngakhale sanadziŵe kumene anali kupita.” (Aheb. 11:8) Yakobo analandila dalitso lapadela pambuyo pogwebana na mngelo. (Gen. 32:24-30) Pamene Aisiraeli anali pafupi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, iwo anawoloka mtsinje wa Yorodano pambuyo pakuti ansembe aponda m’madzi a mtsinjewo.—Yos. 3:14-16.

14 Mungapindulenso na zitsanzo za atumiki a Yehova amakono, amene anam’dalila na kuwonjezela utumiki wawo. Mwacitsanzo, m’bale wina dzina lake Payton na mkazi wake Diana, anali kukonda kuŵelenga nkhani za abale na alongo amene anawonjezela utumiki wawo zopezeka m’nkhani zakuti, “Anadzipeleka na Mtima Wonse.” * M’bale Payton anati: “Tikaŵelenga nkhani zawo, tinali kukhumbila ngati kuti tikupenyelela munthu amene akudya cakudya cokoma. Tikaŵelenga kwambili nkhanizo, m’pamenenso tinali kukhala na cikhumbo cofuna ‘kulaŵa kuti tione kuti Yehova ni wabwino.’” Potsilizila pake, m’bale Payton na mkazi wake anasamukila kumalo osoŵa. Kodi inu munaziŵelengapo nkhani zimenezi? Nanga kodi munapenyelelako vidiyo yakuti, Kulalikila M’dela Lakutali—Australia, komanso ya m’Cizungu yakuti, Witnessing in Isolated Territory—Ireland, yopezeka pa jw.org? Zonsezi zingakuthandizeni kuona njila za mmene mungawonjezele utumiki wanu.

15. Kodi mabwenzi abwino angatithandize motani?

15 Sankhani mabwenzi abwino. Timakhala ofunitsitsa kulaŵako cakudya cimene sitinadyepo ngati tiyanjana na ŵanthu amene amakonda cakudyaco. Mofananamo, ngati timayanjana na ŵanthu amene amaika Yehova patsogolo mu umoyo wawo, cidzakhala cosavuta kwa ife kupeza njila zowonjezela utumiki wathu kwa Mulungu. M’bale Kent na mkazi wake Veronica, anaona kuti mfundo imeneyi ni yoona. M’bale Kent anati: “Mabwenzi na abululu ŵathu anatilimbikitsa kuti tiyese kucitako mautumiki ena. Tinaona kuti kugwilizana na ŵanthu amene amafunafuna ufumu coyamba, kunatilimbikitsa kucitako utumiki wina watsopano. Lomba, m’bale Kent na mkazi wake Veronica ni apainiya apadela ku Serbia.

16. Malinga na fanizo la Yesu lopezeka pa Luka 12:16-21, n’cifukwa ciani tiyenela kudzimana?

16 Khalani odzimana kaamba ka Yehova. Sitiyenela kucita kudzimana zinthu zonse kuti tikondweletse Yehova. (Mlal. 5:19, 20) Komabe, ngati tizengeleza kucita zambili potumikila Mulungu cabe cifukwa cosafuna kudzimana zinthu zina, tingacite zinthu mofanana na munthu wa m’fanizo la Yesu amene anadziunjikila cuma cambili koma n’kunyalanyaza Mulungu. (Ŵelengani Luka 12:16-21.) M’bale Christian wa ku France anati: “Sin’nali kupatsa Yehova komanso banja langa nthawi yokwanila.” Iye na mkazi wake anaganiza zocita upainiya. Koma kuti akwanilitse colinga cawo, anayenela kusiya nchito zawo. Kuti azipeza zofunikila pa umoyo, iwo anayamba bizinesi yawo-yawo yoyeletsa, ndipo anaphunzila kukhala okhutila na ndalama zocepa zimene anali kupeza. Kodi kudzimana kwawo kunawapindulila bwanji? M’bale Christian anati: “Tsopano tikucita zambili mu utumiki wathu kuposa kale, ndipo ndife acimwemwe pokhala na maphunzilo a Baibo komanso maulendo obwelelako.”

17. N’ciani cingatilepheletse kuseŵenzetsa njila zatsopano mu ulaliki?

17 Khalani okonzeka kuseŵenzetsa njila zatsopano mu utumiki. (Mac. 17:16, 17; 20:20, 21) Mlongo Shirley, amene ni mpainiya ku America, anasintha njila yolalikila pa nthawi ino ya mlili wa kolona. Poyamba, anali kudodoma kuyamba ulaliki wa pafoni. Koma atalandila malangizo kwa wadela pocezela mpingo wawo, iye anayamba kulalikila pafoni nthawi zonse. Anati: “Poyamba n’nali kucita mantha, koma tsopano nimaukonda ulaliki wa pafoni. Timalalikila anthu ambili kuposa mmene tinali kucitila polalikila nyumba na nyumba.”

18. N’ciani cingatithandize ngati mavuto akutilepheletsa kuwonjezela utumiki wathu?

18 Dziikileni colinga na kucikwanilitsa. Tikakumana na mavuto, mwapemphelo timayesetsa kuseŵenzetsa luso lathu la kuzindikila kuti tidziŵe mmene tingathanile nawo mavutowo. (Miy. 3:21) Mlongo Sonia amene ni mpainiya m’kagulu ka anthu okamba ci Romany ku Europe, anati: “Nimakonda kulemba zolinga zanga pa pepala, na kuiika pa malo oonekela. Pa thebulo langa n’najambula njila ziŵili zopita kumalo osiyana. Pamene nifuna kupanga cisankho, nimayang’ana njila ziŵilizo kuti nione ngati cisankhoco cidzanithandiza kukwanilitsa colinga canga.” Mlongo Sonia amakhala na maganizo oyenela pa mavuto amene amakumana nawo. Iye anati: “Vuto lililonse linali ngati cipupa conichingiliza, kapena ngati ulalo wonithandiza kukwanilitsa zolinga zanga. Koma kwenikweni zinali kudalila pa kapenyedwe kanga ka zinthu.”

19. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila zinthu zabwino zimene Yehova amatipatsa?

19 Yehova amatidalitsa m’njila zambili. Tingaonetse kuti timayamikila madalitso amenewa ngati ticita zonse zotheka kuti tim’tamande. (Aheb. 13:15) Izi ziphatikizapo kupeza njila zatsopano zowonjezela utumiki wathu, ndipo izi zingatibweletsela madalitso owonjezeleka. Tsiku lililonse, tiyeni tizifunafuna njila kuti timulaŵe Yehova na kuona kuti ni wabwino. Tikatelo, tidzakhala ngati Yesu amene anati: “Cakudya canga ndico kucita cifunilo ca amene anandituma ndi kutsiliza nchito yake.”—Yoh. 4:34.

NYIMBO 80 ‘Talaŵani, Muone Kuti Yehova ni Wabwino’

^ ndime 5 Yehova ndiye gwelo la zabwino zonse. Iye amapatsa zabwino anthu onse, kuphatikizapo oipa. Koma maka-maka amakonda kucitila zabwino alambili ake okhulupilika. M’nkhani ino, tione mmene Yehova amaonetsela ubwino wake kwa atumiki ake. Tionenso mmene awo amene amawonjezela utumiki wawo amapindulila na ubwino wa Yehova.

^ ndime 7 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 14 Nkhanizi, zimene kale zinali kupezeka mu Nsanja ya Mlonda, tsopano zipezeka pa jw.org. Pitani ku Chichewa pa ZOKHUDZA IFEYO > ZOCITIKA > KUKWANILITSA ZOLINGA ZAUZIMU.