Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 36

Muziyamikila Mphamvu za Acinyamata

Muziyamikila Mphamvu za Acinyamata

“Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo.”—MIY. 20:29.

NYIMBO 88 N’dziŵitseni Njila Zanu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Pamene tipita tikalamba, kodi tingadziikile colinga cotani?

PAMENE tipita tikalamba, tingayambe kuona kuti Yehova sangatiseŵenzetse poyelekezela na mmene zinalili tikali acinyamata. N’zoona kuti mphamvu n’zocepekela, koma tingagwilitsile nchito nzelu na cidziŵitso cimene tili naco, pothandiza acinyamata kufikapo mwauzimu kuti asamalile maudindo ena. Mkulu wina amene watumikila kwa zaka zambili anati, “N’tayamba kuona kuti nikulephela kucita zambili cifukwa ca ukalamba, n’nakondwela kuona kuti pali abale acinyamata oyenelela amene angasenze maudindo amenewo.”

2. Tikambilana ciani m’nkhani ino?

2 M’nkhani yapita, tinakambilana mmene acicepele angapindulile akamaceza na okalamba. M’nkhani ino, tiona mmene makhalidwe monga kudzicepetsa, kuyamikila, komanso kuolowa manja, kungathandizile okalamba kuseŵenzela pamodzi na acinyamata, kumene kumapindulitsa mpingo wonse.

KHALANI ODZICEPETSA

3. Malinga na Afilipi 2:3, 4, kodi kudzicepetsa n’kutani? Nanga kungam’thandize bwanji Mkhristu?

3 Okalamba ayenela kukhala odzicepetsa pothandiza acinyamata. Munthu wodzicepetsa amaona ena kukhala omuposa. (Ŵelengani Afilipi 2:3, 4.) Okalamba odzicepetsa amadziŵa kuti pali njila zambili za mogwilila nchito, zimene zimagwilizana na Malemba. Paja amati pali njila zambili zophela khoswe. Conco, okalamba sayembekezela kuti aliyense azicita zinthu mmene iwo anali kucitila kale. (Mlal. 7:10) Olo kuti ali na cidziŵitso cokulilapo cimene angagaŵileko acinyamata, iwo amadziŵa kuti “zocitika za padzikoli zikusintha,” komanso kuti angafunike kuphunzila njila zatsopano za mocitila zinthu.—1 Akor. 7:31.

Mowolowa manja, acikulile amagaŵilako ena cidziŵitso cimene ali naco (Onani ndime 4-5) *

4. Kodi oyang’anila madela, amaonetsa motani mzimu umene Alevi anali nawo?

4 Okalamba odzicepetsa amadziŵa kuti malinga na msinkhu wawo, sangakwanitse kucita zambili mmene anali kucitila kale. Mwacitsanzo, ganizilani za oyang’anila madela. Akafika zaka 70, amapemphedwa kukacita utumiki wina. Koma izi zimakhala zovuta, cifukwa amakonda kwambili kutumikila abale awo. Nchito ya m’dela, imakhala utumiki umene amaukonda ngako, ndipo amakhalabe na mtima wofuna kupitiliza utumikiwo. Komabe, iwo amadziŵa kuti cingakhale bwino kuti abale acinyamata agwile nchito imeneyi. Akatelo, amaonetsa mzimu umene Alevi anali nawo m’nthawi ya Aisiraeli. Aleviwo akafika zaka 50, anali kutula pansi udindo wawo wotumikila pa cihema. Utumiki umene Alevi acikulilewo anali kucita si ndiwo anali maziko a cimwemwe cawo. Iwo anali kucita utumiki uliwonse umene apatsidwa mokangalika, komanso kucita zimene angathe pophunzitsa acinyamata nchito. (Num. 8:25, 26) Mofananamo, abale amene kale anali oyang’anila madela, olo kuti lomba sacezela mipingo, iwo ni dalitso ku mipingo kumene alili.

5. Mwaphunzila ciani pa citsanzo ca m’bale Dan na mkazi wake Katie?

5 Ganizilani citsanzo ca m’bale Dan, amene anali wadela kwa zaka 23. Atakwanitsa zaka 70, iye na mkazi wake Katie, anawasintha utumiki kuti akhale apainiya apadela. Kodi akupindula bwanji na utumiki wawo watsopano? M’bale Dan anakamba kuti tsopano amakhala na zocita zambili kuposa kale. Iye ali na maudindo mu mpingo, amathandiza abale kuti ayenelele kukhala atumiki othandiza, komanso kuphunzitsa ena mocitila ulaliki wapoyela, ndiponso kulalikila kundende. Inu okalamba, kaya muli mu utumiki wanthawi zonse kapena ayi, mungacite zambili pothandiza ena. Motani? Muyenela kuzoloŵela mikhalidwe yatsopano, kudziikila zolinga zatsopano, na kusumika maganizo anu pa zimene mungakwanitse kucita, osati pa zimene simungakwanitse.

6. N’cifukwa ciani n’kwanzelu kukhala wodzicepetsa? Fotokozani citsanzo.

6 Munthu wodzicepetsa amazindikilanso na kuvomeleza zimene sakwanitsa kucita. (Miy. 11:2) Cifukwa cokhala wodzicepetsa, iye sayembekezela kucita zimene sangakwanitse. Izi zimam’thandiza kukhala wacimwemwe komanso wokangalika. Munthu wodzicepetsa tingamuyelekezele na dalaivala amene akuyendetsa motoka pa makata. Dalaivala amabwezako magiya kuti apitilize kuyenda mpaka atafika ku msondo. N’zoona kuti adzayendetsa motokayo pang’ono-pang’ono, koma adzapitilizabe ulendo wake. Mofananamo, munthu wodzicepetsa amadziŵa nthawi yoyenela “kubweza magiya,” n’colinga cakuti apitilize kutumikila Yehova na kuthandiza ena.—Afil. 4:5.

7. Kodi Barizilai anaonetsa bwanji kuti anali wodzicepetsa?

7 Ganizilani citsanzo ca Barizilai. Iye anali na zaka 80 pamene Mfumu Davide anam’pempha kuti akakhale naye ku nyumba ya mfumu. Cifukwa ca kudzicepetsa, Barizilai anakana pempho la mfumu limeneli. Podziŵa zimene sangakwanitse kucita cifukwa ca ukalamba, Barizilai anapempha kuti wacinyamata Chimamu apite m’malo mwa iye. (2 Sam. 19:35-37) Mofanana na Barizilai, okalamba amakondwela kupatsa mwayi acinyamata wakuti atumikile.

Mfumu Davide anagwilizana na cisankho ca Yehova cakuti mwana wake ndiye adzamanga kacisi (Onani ndime 8)

8. Kodi Mfumu Davide anaonetsa bwanji kudzicepetsa pamene anali kufuna kumanga kacisi?

8 Mfumu Davide nayenso anapeleka citsanzo cabwino ngako pa kudzicepetsa. Iye anali kufunitsitsa na mtima wake wonse kumanga nyumba ya Yehova. Koma Yehova atauza Davide kuti adzamange nyumbayo ni wacinyamata Solomo, Davide anagwilizana na cisankho ca Yehova, ndipo anacilikiza nchitoyo na mtima wonse. (1 Mbiri 17:4; 22:5) Davide sanaganize kuti ndiye anali woyenelela kumanga nyumbayo poona kuti Solomo anali “wamng’ono ndi wosakhwima.” (1 Mbiri 29:1) Iye anadziŵa kuti, kuti nchito yomangayo itheke, zinadalila pa dalitso la Yehova osati pa msinkhu kapena cidziŵitso ca otsogolela. Mofanana na Davide, okalamba masiku ano amakhalabe okangalika olo kuti utumiki wawo wasintha. Ndipo amadziŵa kuti Yehova adzadalitsa acinyamata amene amagwila nchito imene iwo anali kucita.

9. Kodi ciwalo cina ca Komiti ya Nthambi cinaonetsa bwanji kudzicepetsa?

9 Citsanzo camakono pa kudzicepetsa, ni m’bale Shigeo. Mu 1976, ali na zaka 30, iye anaikidwa kukhala ciwalo ca Komiti ya Nthambi. Mu 2004, anakhala mgwilizanitsi wa Komiti ya Nthambi. Patapita nthawi, iye anazindikila kuti sakuthanso kusamalila bwino udindo wake cifukwa ca msinkhu wake. Mwapemphelo iye anaganizila mapindu amene angakhalepo ngati m’bale wacinyamata wasenza udindo umenewo. Ngakhale kuti m’bale Shigeo salinso mgwilizanitsi, iye akali kutumikila mogwilizana na abale ena m’Komiti ya Nthambi. Monga taonela pa citsanzo ca Barizilai, Mfumu Davide, komanso m’bale Shigeo, munthu wodzicepetsa sasumika maganizo ake pa zimene acinyamata sakwanitsa kucita, koma pa mphamvu zawo. Iye sawaona kukhala opikisana nawo, koma monga anchito anzake.—Miy. 20:29.

KHALANI OYAMIKILA

10. Kodi okalamba ayenela kuwaona motani acinyamata mu mpingo?

10 Okalamba amaona acinyamata kukhala mphatso yocokela kwa Yehova. Pamene mphamvu zawo zicepela-cepela, iwo amayamikila kuti pali acinyamata amphamvu amene mofunitsitsa amasamalila maudindo mu mpingo.

11. Kodi Rute 4:13-16, ionetsa bwanji madalitso amene amakhalapo ngati okalamba alandila thandizo kwa acinyamata?

11 Citsanzo cabwino ngako ca m’Baibo ca wokalamba amene anayamikila thandizo la wacitsikana, ni Naomi. Poyamba, Naomi anauza Rute mpongozi wake wamasiye kubwelela kwawo. Komabe, Rute ataumilila kupita naye Naomi ku Betelehemu, Naomi anayamikila cicilikizo ca Rute ca mtima wonse. (Rute 1:7, 8, 18) Linali dalitso cotani nanga kwa akazi onse aŵiliwa! (Ŵelengani Rute 4:13-16.) Kudzicepetsa kudzathandiza okalamba kutengela citsanzo ca Naomi.

12. Kodi mtumwi Paulo anaonetsa bwanji ciyamikilo cake?

12 Mtumwi Paulo anayamikila thandizo limene anali kulandila. Mwacitsanzo, iye anayamikila Akhristu a ku Filipi kaamba ka mphatso imene anam’tumizila. (Afil. 4:16) Anayamikilanso thandizo la Timoteyo. (Afil. 2:19-22) Paulo anathokoza Mulungu pamene abale ake anabwela kudzam’limbikitsa paulendo wake wopita ku Roma monga mkaidi. (Mac. 28:15) Iye anali munthu wamphamvu, ndipo anali kuyenda mitunda itali-itali kukalikila, komanso kukalimbikitsa mipingo. Ngakhale n’conco, sanali wonyada moti n’kukana thandizo la abale na alongo ake.

13. Kodi okalamba angaonetse bwanji kuti amayamikila acinyamata?

13 Imwe okalamba, mungaonetse kuti mumayamikila acinyamata mu mpingo m’njila zambili. Akafuna kukuthandiza pa mayendedwe, kugula zinthu, kapena pa zosoŵa zina zakuthupi, conde landilani thandizo lawo. Muziona thandizo limenelo monga njila imene Yehova akukuonetselani cikondi. Mukatelo, mudzakhala pa ubwenzi wolimba na ŵanthu amene amakuthandizani. Cina, muzionetsa cidwi mabwenzi anu acinyamata amene akukula mwauzimu, ndipo auzeni kuti mumakondwela kuwaona akuyesetsa kucita zambili pothandiza mpingo. Komanso, muziwasimbilako zocitika mu umoyo wanu. Mukatelo, mudzaonetsa “kuti ndinu oyamikila” kwa Yehova kaamba ka acinyamata amene waakokela mu mpingo wake.—Akol. 3:15; Yoh. 6:44; 1 Ates. 5:18.

KHALANI OWOLOWA MANJA

14. Kodi Mfumu Davide anaonetsa bwanji kuwolowa manja?

14 Khalidwe lina lofunika kwambili limene okalamba angatengele kwa Mfumu Davide, ni kuwolowa manja. Iye anapeleka zinthu zambili pa cuma cake kuti zithandizile pa nchito yomanga kacisi. (1 Mbiri 22:11-16; 29:3, 4) Anacita izi ngakhale kuti kacisiyo anali kudzadziŵika na dzina la mwana wake Solomo. Ngati tilibenso mphamvu zakuti tigwile nawo nchito zamamangidwe, tingacilikizebe nchitoyo mwa kupanga zopeleka mmene tingathele. Cina, tingathandize acinyamata kupindula na maluso amene taphunzila kwa zaka zambili.

15. Ni mphatso ziti zamtengo wapatali zimene mtumwi Paulo anagaŵila Timoteyo?

15 Pa nkhani ya kuwolowa manja, ganizilaninso citsanzo ca mtumwi Paulo. Iye anapempha Timoteyo kuti azigwila naye nchito ya umishonale. Ndipo na mtima wonse, iye anaphunzitsa wacinyamatayu njila zolalikila na kuphunzitsa. (Mac. 16:1-3) Zimene Timoteyo anaphunzila kwa Paulo, zinam’thandiza kuti azilalikila mogwila mtima. (1 Akor. 4:17) Nayenso Timoteyo anaseŵenzetsa zimene anaphunzila kwa Paulo kuphunzitsa ena.

16. N’cifukwa ciani m’bale Shigeo amaphunzitsako ena?

16 Okalamba saopa kuti angalandidwe udindo akaphunzitsa acinyamata nchito zimene iwo anali kucita mu mpingo. Mwacitsanzo, kwa zaka zambili, m’bale Shigeo amene tam’chula kumayambililo, anali kuphunzitsa abale acinyamata m’Komiti ya Nthambi. Anacita izi pofuna kupititsa patsogolo nchito ya Ufumu m’dziko limene akutumikila. Zotulukapo n’zakuti iye atatula pansi udindo wa ugwilizanitsi, m’bale wophunzitsidwa bwino anamuloŵa m’malo. M’bale Shigeo watumikila m’Komiti ya Nthambi kwa zaka zoposa 45, ndipo amathandizabe abale acinyamata m’komiti imeneyi. Anthu otelo ni dalitso kwa anthu a Mulungu.

17. Mogwilizana na Luka 6:38, kodi okalamba angapatse ena ciani?

17 Inu abale na alongo okalamba, mwadzionela mwekha kuti kutumikila Yehova mokhulupilika, ndiye umoyo wabwino koposa. Mwacitsanzo canu, mwaonetsadi kuti kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo n’kopindulitsa kwambili. Pa umoyo wanu wonse, mwaona mmene gulu linali kucitila zinthu kale, ndipo mwaonanso kufunika kozoloŵela njila zatsopano zocitila zinthu. Inu okalamba amene munabatizika posacedwa, mungauzeko ena cimwemwe cimene mwapeza cifukwa codziŵa Yehova pa msinkhu wanu umenewo. Acinyamata adzayamikila ngako kumva zocitika za pa umoyo wanu, komanso zimene mwaphunzila. Ngati ‘mukhala opatsa’ kocokela mu nkhokwe yanu ya cidziŵitso, Yehova adzakudalitsani mowilikiza.—Ŵelengani Luka 6:38.

18. Pamakhala mapindu otani ngati okalamba na acinyamata aseŵenzela pamodzi?

18 Inu okalamba okondedwa, mukamayandikana kwambili na acinyamata, mudzakwanitsa kuthandizana. (Aroma 1:12) Aliyense ali na cina cake cofunika cimene mnzake alibe. Okalamba ali na nzelu, komanso cidziŵitso cimene akhala naco m’kupita kwa nthawi. Koma acinyamata ali na mphamvu. Okalamba na acinyamata akamaseŵenzela pamodzi monga mabwenzi, amapeleka citamando kwa Atate wathu wacikondi wakumwamba, ndipo onse amakhala dalitso mu mpingo.

NYIMBO 90 Tilimbikitsane Wina na Mnzake

^ ndime 5 M’mipingo yathu, tili na anyamata na atsikana ambili amene amayesetsa kucilikiza gulu la Yehova. Okalamba mu mpingo, mosasamala kanthu za cikhalidwe cawo, angathandize acinyamata kuseŵenzetsa mphamvu zawo mokwanila potumikila Yehova.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Pamene woyang’anila dela wakwanitsa zaka 70, iye na mkazi wake apatsidwa utumiki watsopano. Cidziŵitso cimene akhala naco cikuwathandiza kuphunzitsa ena mu mpingo umene akutumikila.