NKHANI YOPHUNZIRA 37

“Ndidzagwedeza Mitundu Yonse ya Anthu”

“Ndidzagwedeza Mitundu Yonse ya Anthu”

“Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu zidzalowa m’nyumba imeneyi.”​HAG. 2:7.

NYIMBO NA. 24 Bwerani Kuphiri la Yehova

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi ndi kugwedeza kotani kumene kunanenedweratu kuti kudzachitika mu nthawi yathu?

“M’MAMINITSI ochepa, mashopu komanso nyumba zakale zinayamba kugwa.” “Aliyense ankachita mantha . . . Anthu ambiri amanena kuti kugwedezako kunachitika pafupifupi kwa 2 minitsi. Koma kwa ine ndinkangoona ngati kunachitika nthawi yaitali.” Zimenezi ndi zomwe ananena anthu ena omwe anapulumuka chovomerezi chomwe chinachitika ku Nepal mu 2015. Inunso zinthu zochititsa mantha ngati zimenezi zikanakuchitikirani, mwina simukanaiwala.

2 Koma panopa tikukhala pa nthawi imene pakuchitika kugwedeza kwina kumene sikukuchitika mumzinda kapena m’dziko limodzi. M’malomwake, kugwedeza kumeneku kukukhudza mitundu yonse ya anthu ndipo kwakhala kukuchitika kwa zaka zambiri. Mneneri Hagai ananeneratu za kugwedeza kumeneku. Iye analemba kuti: “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Posachedwapa ndigwedezanso kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndi mtunda.’”​—Hag. 2:6.

3. Kodi kugwedeza kumene Hagai anatchula n’kosiyana bwanji ndi kugwedeza kwa chivomerezi?

3 Kugwedeza kumene Hagai anakufotokoza n’kosiyana ndi kugwedeza kwa chivomerezi komwe kumangokhala kowononga. M’malomwake, kugwedeza uku kumakhala ndi zotsatirapo zabwino. Yehova amatiuza kuti: “Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu zidzalowa m’nyumba imeneyi. Ine ndidzadzaza nyumbayi ndi ulemerero.” (Hag. 2:7) Kodi ulosi umenewu unkatanthauza chiyani kwa anthu a mu nthawi ya Hagai? Nanga ukutanthauza chiyani kwa ife masiku ano? Tikambirana mayankho a mafunso amenewa komanso tiphunzira zimene tingachite kuti tizigwira nawo ntchito yogwedezayi masiku ano.

UTHENGA WOLIMBIKITSA MU NTHAWI YA HAGAI

4. N’chifukwa chiyani Yehova anatumiza mneneri Hagai kwa anthu ake?

4 Yehova anapatsa mneneri Hagai ntchito yofunika kwambiri yoti agwire. Taganizirani mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Hagai ayenera kuti anali m’gulu la anthu omwe anabwerera ku Yerusalemu mu 537 B.C.E., kuchokera ku ukapolo ku Babulo. Atangofika, mwamsanga atumiki okhulupirikawa anamanga maziko a nyumba ya Yehova, kapena kuti kachisi. (Ezara 3:8, 10) Koma pasanapite nthawi yaitali, iwo anakumana ndi mavuto omwe anawafooketsa ndipo anasiya kugwira ntchitoyi chifukwa chotsutsidwa. (Ezara 4:4; Hag. 1:1, 2) Choncho mu 520 B.C.E., Yehova anatumiza Hagai kukathandiza anthuwo kuti akhalenso ndi khama pa ntchito yomanga kachisi. *​—Ezara 6:14, 15.

5. N’chifukwa chiyani uthenga wa Hagai unali wolimbikitsa kwa anthu a Mulungu?

5 Cholinga cha uthenga wa Hagai chinali kulimbikitsa Ayuda kuti azikhulupirira kwambiri Yehova. Molimba mtima, mneneriyu analankhula mawu awa kwa Ayuda omwe anafookawo: “‘Limbani mtima anthu nonse a m’dzikoli ndipo gwirani ntchito,’ watero Yehova. ‘Pakuti ine ndili ndi inu,’ watero Yehova wa makamu.” (Hag. 2:4) Mawu akuti “Yehova wa makamu” ayenera kuti anawalimbikitsa kwambiri. Yehova ali ndi gulu lalikulu lankhondo la angelo, choncho Ayudawo ankafunika kumudalira kuti zinthu ziwayendere bwino.

6. Kodi zotsatirapo za kugwedeza komwe Hagai analosera zikanakhala zotani?

6 Yehova anatuma Hagai kuti auze Ayuda kuti iyeyo adzagwedeza mitundu yonse ya anthu. Uthenga umenewu unathandiza Ayuda omwe anafooka pa ntchito yomanga kachisi kudziwa kuti Yehova adzagwedeza ufumu wa Perisiya, womwe unali ulamuliro wamphamvu padziko lonse pa nthawiyo. Ndiye kodi zotsatirapo zake zikanakhala zotani? Choyamba, anthu a Mulungu akanamaliza kumanga kachisi. Kenako, anthu a mitundu ina akanagwirizana ndi Ayuda polambira Yehova m’kachisi amene anamangidwansoyo. Umenewutu uyenera kuti unali uthenga wolimbikitsa kwa anthu a Mulungu.​—Zek. 8:9.

NTCHITO YOGWEDEZA IMENE IKUCHITIKA PADZIKO LONSE MASIKU ANO

Kodi mukugwira nawo mokwanira ntchito yogwedeza mitundu yonse ya anthu yomwe ikuchitika masiku ano? (Onani ndime 7-8) *

7. Kodi ndi ntchito yogwedeza iti imene tikugwira nawo masiku ano? Fotokozani.

7 Kodi ulosi wa Hagai ukutanthauza chiyani kwa ife masiku ano? Kachiwirinso, Yehova akugwedeza mitundu yonse ya anthu ndipo ife tikuthandiza nawo pa ntchitoyi. Taganizirani mfundo iyi: Mu 1914, Yehova anaika Yesu Khristu kukhala Mfumu ya Ufumu wake wakumwamba. (Sal. 2:6) Kukhazikitsidwa kwa Ufumu umenewu sinali nkhani yosangalatsa kwa olamulira a m’dzikoli. Zimenezi zinkatanthauza kuti “nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu” ina, kapena kuti nthawi yomwe padzikoli panalibe wolamulira woimira Yehova, zinali zitakwanira kapenanso kuti zitafika kumapeto. (Luka 21:24) Pozindikira mfundo imeneyi, makamaka kuyambira mu 1919, anthu a Yehova akhala akulengeza kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ungathetse mavuto onse a anthu. Ntchito yolalikira ‘uthenga wabwino wa ufumuyi’ yagwedeza dziko lonse lapansi.​—Mat. 24:14.

8. Mogwirizana ndi Salimo 2:1-3, kodi anthu ambiri amatani akamva uthenga wa Ufumu?

8 Kodi anthu amatani akamva uthenga wa Ufumu? Ambiri amakana kumvetsera. (Werengani Salimo 2:1-3.) Mitundu ya anthu imakwiya ikamva uthengawu. Iwo amakana Wolamulira amene Yehova wamusankha. Saona uthenga wabwino wa Ufumu umene timalalikirawu ngati “uthenga wabwino.” Ndipotu maboma ena afika poletsa ntchito yathu yolalikira. Ngakhale kuti ambiri mwa olamulira adzikoli amanena kuti amatumikira Mulungu, safuna kutula pansi udindo wawo. Mofanana ndi zimene anachita olamulira mu nthawi ya Yesu, olamulira masiku ano amatsutsa Wodzozedwa wa Yehova polimbana ndi otsatira ake okhulupirika.​—Mac. 4:25-28.

9. Kodi Yehova amatani chifukwa cha zimene mitundu ya anthu imachita pokana uthenga wa Ufumu?

9 Kodi Yehova amatani chifukwa cha zimene mitundu ya anthu imachita pokana uthenga wa Ufumu? Lemba la Salimo 2:10-12 limayankha kuti: “Tsopano inu mafumu, sonyezani kuzindikira, lolani kuti maganizo anu akonzedwe, inu oweruza a dziko lapansi. Tumikirani Yehova mwamantha. Kondwerani ndipo nthunthumirani. Psompsonani mwanayo kuopera kuti Mulungu angakwiye, ndipo mungawonongeke ndi kuchotsedwa panjirayo. Pakuti mkwiyo wake umatha kuyaka mofulumira. Odala ndi onse amene akuthawira kwa iye.” Mokoma mtima, Yehova akuwapatsa otsutsawa mpata woti asankhe zochita. Akhoza kusintha maganizo n’kuvomereza Ufumu wa Yehova. Komabe, iwo angotsala ndi kanthawi kochepa kuti achite zimenezi. Panopa tili ‘m’masiku otsiriza’ a dziko loipali. (2 Tim. 3:1; Yes. 61:2) Kuposa kale lonse, panopa anthu akufunika kuchita changu kuti aphunzire mfundo zoona n’kusankha kutumikira Yehova.

ZOTSATIRAPO ZABWINO ZA NTCHITO YOGWEDEZA

10. Kodi pali zotsatirapo zabwino ziti pa ntchito yogwedeza yotchulidwa pa Hagai 2:7-9?

10 Ntchito yogwedeza yomwe Hagai analosera imakhalanso ndi zotsatira zabwino. Iye ananena kuti chifukwa cha ntchito yogwedezayi, “zinthu zamtengo wapatali [kapena kuti anthu oona mtima] zochokera ku mitundu yonse ya anthu” zidzalowa m’nyumba imeneyi kudzalambira Yehova. * (Werengani Hagai 2:7-9.) Yesaya komanso Mika, ananeneratunso kuti zofanana ndi zimenezi zidzachitika “m’masiku otsiriza.”​—Yes. 2:2-4; Mika 4:1, 2.

11. Kodi m’bale wina anachita chiyani atamva koyamba uthenga wa Ufumu?

11 Taganizirani mmene uthenga womwe ukugwedeza dziko lonse unakhudzira m’bale wina dzina lake Ken, yemwe akutumikira kulikulu lathu. Iye amakumbukira bwino zomwe zinachitika atamva uthenga wa Ufumu koyamba zaka 40 zapitazo. Ken anati: “Nditamva koyamba choonadi cha m’Mawu a Mulungu, ndinasangalala kudziwa kuti tikukhala m’masiku otsiriza a dziko loipali. Ndinaona kuti, kuti Mulungu azisangalala nane komanso kuti ndidzapeze moyo wosatha, ndiyenera kupeweratu kukhala kumbali ya dziko losadalirikali, n’kuima zolimba kumbali ya Yehova. Ndinapemphera kwa Yehova ndipo nthawi yomweyo ndinachita zimenezi. Ndinasiya kuchita zinthu za m’dzikoli ndipo ndinathawira ku Ufumu wa Mulungu womwe sungagwedezeke kuti ndipeze chitetezo.”

12. Kodi kachisi wauzimu wa Yehova wadzaza bwanji ndi ulemerero m’masiku otsiriza ano?

12 N’zosachita kufunsa kuti Yehova wakhala akudalitsa anthu ake. M’masiku otsirizawa, taona chiwerengero cha anthu omulambira chikuwonjezereka kwambiri. Mu 1914 tinalipo anthu masauzande ochepa. Koma panopa tilipo oposa 8 miliyoni ndipo anthu mamiliyoni ambiri amachita nafe Chikumbutso chaka chilichonse. Pachifukwa chimenechi, bwalo la padziko lapansi la kachisi wauzimu wa Yehova, lomwe ndi dongosolo lake lokhudza kulambira koona, ladzaza ndi “zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu.” Komanso dzina la Yehova limalemekezedwa chifukwa cha kusintha kumene anthu amenewa amachita povala umunthu watsopano.​—Aef. 4:22-24.

13. Kodi ndi maulosi ena ati omwe akwaniritsidwa chifukwa choti anthu ambiri ayamba kulambira Yehova? (Onani chithunzi chapachikuto)

13 Zimene zikuchitikazi zakhala zikukwaniritsanso maulosi ena, mwachitsanzo ulosi wa pa Yesaya chaputala 60. Vesi 22 muchaputalachi limati: “Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.” Popeza anthu ambiri akuyamba kulambira Yehova, pakuchitikanso zinthu zina zochititsa chidwi. “Zinthu zamtengo wapatali,” kapena kuti anthu amenewa, amabwera m’gulumu ndi maluso osiyanasiyana komanso amakhala ofunitsitsa kugwira nawo ntchito yolalikira “uthenga wabwino wa Ufumu.” Zotsatira zake, monga mmene Yesaya ananenera, n’zakuti anthu a Yehova akuyamwa “mkaka wa mitundu ya anthu.” (Yes. 60:5, 16) Mothandizidwa ndi amuna komanso akazi amenewa, tikulalikira uthenga wabwino m’mayiko okwana 240 komanso tikusindikiza mabuku athu m’zinenero zoposa 1,000.

NTHAWI YOYENERA KUSANKHA ZOCHITA

Anthu a Mulungu padziko lonse amasangalala kuuza ena zokhudza Ufumu wa Mulungu (Onani ndime 13)

14. Kodi anthu ayenera kusankha kuchita chiyani panopa?

14 M’masiku amapeto ano, ntchito yogwedeza mitundu ya anthu ikuwachititsa kuti asankhe zochita. Kodi iwo asankha kukhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu, kapena azidalira maboma a anthu? Imeneyi ndi nkhani imene aliyense ayenera kusankha. Ngakhale kuti anthu a Yehova amamvera malamulo a boma lam’dziko limene akukhala, iwo salowerera ngakhale pang’ono ndale za m’dzikoli. (Aroma 13:1-7) Amadziwa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto onse a anthu. Ufumu umenewu suli mbali ya dzikoli.​—Yoh. 18:36, 37.

15. Kodi buku la Chivumbulutso likusonyeza bwanji kuti kukhulupirika kwa atumiki a Mulungu kudzayesedwa?

15 Buku la Chivumbulutso limafotokoza kuti m’masiku otsiriza kukhulupirika kwa anthu a Mulungu kudzayesedwa. Pa nthawi imeneyo, atumiki a Mulungu azidzatsutsidwa komanso kuzunzidwa kwambiri. Maboma a m’dzikoli azidzatiuza kuti tisiye kulambira Mulungu ndipo azidzazunza aliyense amene adzakane kukhala kumbali yawo. (Chiv. 13:12, 15) Iwo ‘azidzakakamiza anthu onse, olemekezeka ndi onyozeka, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti apatsidwe chizindikiro padzanja lawo lamanja kapena pamphumi pawo.’ (Chiv. 13:16) Kale akapolo ankadindidwa chizindikiro chowazindikiritsa kuti ali ndi mbuye wawo. Mofanana ndi zimenezi, masiku anonso anthu azidzayembekezera kuti aliyense akhale ndi chizindikiro chophiphiritsa padzanja kapena pamphumi. Zochita komanso maganizo awo zidzasonyeza kuti ali kumbali ya maboma a m’dzikoli.

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala okhulupirika kwambiri kwa Yehova panopa?

16 Kodi ifeyo tidzalola kulandira chizindikiro chophiphiritsachi n’kukhala kumbali ya maboma a m’dzikoli? Amene adzakane kulandira chizindikirocho adzakumana ndi mavuto aakulu komanso zinthu zoopsa. Buku la Chivumbulutso limapitiriza kunena kuti: “Aliyense asathe kugula kapena kugulitsa, kupatulapo ngati ali ndi chizindikirocho.” (Chiv. 13:17) Koma anthu a Mulungu amadziwa zimene iye adzachite ndi anthu omwe adzakhale ndi chizindikiro chotchulidwa pa Chivumbulutso 14:9, 10. Ndiye m’malo mokhala ndi chizindikiro chimenecho, iwo adzalemba padzanja lawo kuti: “Wa Yehova.” (Yes. 44:5) Inoyo ndi nthawi yoti tiziyesetsa kukhala okhulupirika kwambiri kwa Yehova. Tikamachita zimenezi, iye adzasangalala kutitchula kuti ndife anthu ake.

KUGWEDEZA KOMALIZA

17. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani pa nkhani ya kuleza mtima kwa Yehova?

17 Yehova wakhala akuleza mtima kwambiri m’masiku otsiriza ano. Iye safuna kuti aliyense adzawonongedwe. (2 Pet. 3:9) Yehova wapereka mwayi kwa anthu onse woti alape n’kusankha kumutumikira. Komabe, kuleza mtima kwake kuli ndi malire. Anthu amene amakana mwayi umenewu adzaona zimene Farao wa mu nthawi ya Mose anakumana nazo. Yehova anauza Farao kuti: “Pofika pano ndikanatambasula kale dzanja langa ndi kukupha ndi mliri, iweyo ndi anthu ako, kukufafanizani padziko lapansi. Koma ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.” (Eks. 9:15, 16) Pamapeto pake, mitundu yonse ya anthu idzadziwa kuti Yehova yekha ndiye Mulungu woona. (Ezek. 38:23) Kodi zimenezi zidzachitika bwanji?

18. (a) Kodi ndi kugwedeza kwina kuti komwe kukutchulidwa pa Hagai 2:6, 20-22? (b) Kodi timadziwa bwanji kuti mawu a Hagai adzakwaniritsidwa m’tsogolo?

18 Patapita zaka zambiri kuchokera mu nthawi ya Hagai, mtumwi Paulo anauziridwa kulemba mawu omwe anasonyeza kuti mawu a pa Hagai 2:6, 20-22, adzakwaniritsidwa m’tsogolo. (Werengani.) Iye analemba kuti: “Tsopano walonjeza kuti: ‘Ndidzagwedezanso kumwamba, osati dziko lapansi lokhali.’ Tsopano, mawu akuti ‘ndidzagwedezanso,’ akusonyeza kuti zinthu zimene adzazigwedezezo zidzachotsedwa. Zimenezi ndi zinthu zimene zinapangidwa ndi winawake, ndipo adzazichotsa kuti zimene sizikugwedezeka zitsale.” (Aheb. 12:26, 27) Mosiyana ndi kugwedeza kwa pa Hagai 2:7, kugwedeza uku kudzachititsa kuwonongedwa kwa anthu onse okhala ngati Farao, omwe amakana kuti Yehova ndi woyenera kulamulira.

19. Kodi n’chiyani chomwe sichidzagwedezeka nanga tikudziwa bwanji zimenezi?

19 Kodi n’chiyani chomwe sichidzagwedezeka kapena kuchotsedwa? Paulo anapitiriza kuti: “Poona kuti tidzalandira ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tipitirize kulandira kukoma mtima kwakukulu, kuti kudzera m’kukoma mtima kwakukulu kumeneko, tichitire Mulungu utumiki wopatulika m’njira yovomerezeka, ndipo tiuchite moopa Mulungu komanso mwaulemu waukulu.” (Aheb. 12:28) Pambuyo pa kugwedeza komalizaku Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzakhale wosagwedezeka ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.​—Sal. 110:5, 6; Dan. 2:44.

20. Kodi anthu ayenera kusankha zochita pa nkhani iti, nanga tingawathandize bwanji?

20 Panopa nthawi yatha. Anthu ayenera kusankha kuti, kodi apitiriza kuchita zinthu zimene dzikoli limalimbikitsa zomwe ndi zotsogolera kuchiwonongeko kapena asankha kumachita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna zomwe zingachititse kuti adzapeze moyo wosatha? (Aheb. 12:25) Tikamagwira ntchito yolalikira, timathandiza anthu kuti asankhe zochita pa nkhani yofunika kwambiriyi. Tiyeni tizithandiza anthu ambiri omwe ali ngati zinthu zamtengo wapatali kuti akhale kumbali ya Ufumu wa Mulungu. Tiyeninso tizikumbukira mawu a Ambuye wathu Yesu akuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”​—Mat. 24:14.

NYIMBO NA. 40 Kodi Ndife a Ndani?

^ ndime 5 Nkhaniyi ikufotokoza kamvedwe katsopano ka lemba la Hagai 2:7. Tiphunzira zimene tingachite kuti tizigwira nawo ntchito yosangalatsa imene ikugwedeza mitundu yonse ya anthu. Tionanso kuti anthu ena amamvetsera uthenga wabwino chifukwa cha ntchito yogwedezayi pomwe ena amadana nayo.

^ ndime 4 Timadziwa kuti Hagai anakwaniritsa ntchito imene Yehova anamutuma chifukwa kachisi anamalizidwa pofika mu 515 B.C.E.

^ ndime 10 Zimenezi zikusintha zimene tinkakhulupirira m’mbuyomu. Poyamba tinkanena kuti anthu oona mtima sayamba kutumikira Yehova chifukwa cha ntchito yogwedeza mitundu yonse ya anthu. Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2006.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Hagai analimbikitsa anthu a Mulungu kuchita khama pa ntchito yomanganso kachisi ndipo masiku anonso anthu a Mulungu amachita khama kulengeza uthenga wabwino. Banja likugwira nawo ntchito imene ikugwedeza dziko lonse yonena za kugwedeza komaliza kumene kukubwera.