Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 38

Muzikonda Kwambiri Yehova Komanso Abale ndi Alongo Anu

Muzikonda Kwambiri Yehova Komanso Abale ndi Alongo Anu

“Ine ndikukwera kwa Atate wanga ndi Atate wanu.”​—YOH. 20:17.

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi anthu okhulupirika akhoza kukhala pa ubwenzi wotani ndi Yehova?

 M’BANJA la Yehova muli Yesu, yemwe ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse,” komanso angelo ambirimbiri. (Akol. 1:15; Sal. 103:20) Ali padzikoli, Yesu anasonyeza kuti anthu okhulupirika akhoza kumaona Yehova ngati Atate wawo. Ponena za Yehova pamene ankalankhula ndi ophunzira ake, iye ananena kuti “Atate wanga ndi Atate wanu.” (Yoh. 20:17) Ndipo tikadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa, timakhala m’banja la abale ndi alongo omwe amakondana.​—Maliko 10:29, 30.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Anthu ena zimawavuta kuti aziona Yehova monga Atate wawo wachikondi. Enanso sadziwa mmene angasonyezere chikondi kwa abale ndi alongo awo. Munkhaniyi tiona mmene Yesu amatithandizira kuti tiziona Yehova monga Atate wathu wachikondi, yemwe tingakhale naye pa ubwenzi wolimba. Tionanso mmene tingatsanzirire Yehova tikamachita zinthu ndi abale ndi alongo athu.

YEHOVA AKUFUNA KUTI MUKHALE NAYE PA UBWENZI

3. Kodi pemphero lachitsanzo limatithandiza bwanji kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

3 Yehova ndi Atate wachikondi. Yesu amafuna kuti tiziona Yehova ngati mmene iye amamuonera. Iye amamuona monga kholo lachikondi komanso lokoma mtima lomwe tikhoza kulankhula nalo nthawi iliyonse, osati ngati munthu waudindo wouma mtima amene amangouza ena zochita. Umboni wa zimenezi ndi zimene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake pa nkhani ya pemphero. Iye anayamba pemphero lachitsanzo ndi mawu akuti: “Atate wathu.” (Mat. 6:9) Yesu akanatha kunena kuti tizitchula Yehova kuti “Wamphamvuyonse,” “Mlengi” kapena “Mfumu yamuyaya.” Ndipotu amenewa ndi mayina audindo oyenera opezeka m’Malemba. (Gen. 49:25; Yes. 40:28; 1 Tim. 1:17) M’malomwake Yesu anatiuza kuti tizitchula Yehova kuti “Atate.”

4. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi?

4 Kodi zimakuvutani kuti muziona Yehova ngati Atate wachikondi? Ena zimawavuta. Mwina chifukwa cha mmene tinaleredwera zingativute kumvetsa kuti pali makolo achikondi. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amamvetsa mmene timamvera. Iye amafuna kukhala nafe pa ubwenzi. N’chifukwa chake Mawu ake amatilimbikitsa kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yak. 4:8) Yehova amatikonda ndipo amatiuza kuti adzakhala Atate wathu wabwino kwambiri.

5. Mogwirizana ndi Luka 10:22, kodi Yesu angatithandize bwanji kukhala pa ubwenzi ndi Yehova?

5 Yesu angatithandize kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova. Iye amamudziwa bwino Yehova ndipo amatsanzira kwambiri makhalidwe ake moti ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Mofanana ndi mwana wamkulu m’banja, Yesu amatiphunzitsa zimene tingachite kuti tizilemekeza komanso kumvera Atate wathu, kupewa kuwakhumudwitsa komanso kuti azisangalala nafe. Zimene Yesu anachita ali padzikoli, zimatithandizanso kwambiri kumvetsa kuti Yehova ndi wokoma mtima komanso wachikondi. (Werengani Luka 10:22.) Tiyeni tiganizire zitsanzo zingapo.

Monga Atate wachikondi, Yehova analimbikitsa Mwana wake pomutumizira mngelo (Onani ndime 6 *

6. Perekani zitsanzo zosonyeza zimene Yehova anachita pomvetsera Yesu.

6 Yehova amamvetsera ana ake akamapemphera kwa iye. Tiyeni tione zimene anachita pomvetsera Mwana wake woyamba kubadwa. Mosakayikira Yehova ankamva mapemphero ambirimbiri amene Mwana wake ankapereka pamene anali padziko lapansi. (Luka 5:16) Iye anamva Yesu akupempherera nkhani zofunika kwambiri, mwachitsanzo pamene ankasankha atumwi ake 12. (Luka 6:12, 13) Anamvanso Yesu akupemphera pa nthawi imene anali ndi nkhawa kwambiri. Atatsala pang’ono kuperekedwa, Yesu anapemphera mochokera pansi pamtima kwa Atate wake pa nkhani yokhudza mayesero aakulu amene ankayembekezera kukumana nawo. Sikuti Yehova anangomvetsera pemphero la Yesu, koma anatumizanso mngelo kuti akalimbikitse Mwana wake wokondedwayu.​—Luka 22:41-44.

7. Kodi mumamva bwanji kuona kuti Yehova amamvetsera mapemphero a anthu ake?

7 Masiku anonso Yehova akupitiriza kumvetsera mapemphero a atumiki ake, ndipo amawayankha pa nthawi yoyenera komanso m’njira yabwino kwambiri. (Sal. 116:1, 2) Mlongo wina wa ku India anaona mmene Yehova anayankhira mapemphero ake. Iye ankavutika kwambiri ndi nkhawa ndipo anapemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima za vuto lakelo. Mlongoyu analemba kuti: “Pulogalamu ya May 2019 ya JW Broadcasting® yomwe inkafotokoza zomwe tingachite tikakhala ndi nkhawa, inali ya pa nthawi yake kwa ine. Pulogalamuyi inali yankho la mapemphero anga.”

8. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti amakonda Yesu?

8 Yehova amatikonda komanso kutisamalira ngati mmene anachitira ndi Yesu pa nthawi yonse imene ankachita utumiki wake padzikoli, womwe unali wovuta kwambiri. (Yoh. 5:20) Iye anathandiza Yesu kuti akhalebe ndi chikhulupiriro cholimba, kumulimbikitsa pamene anali ndi nkhawa komanso anaonetsetsa kuti ali ndi zofunika pa moyo. Yehova ankauzanso Mwana wakeyu kuti amamukonda ndipo ankasangalala naye. (Mat. 3:16, 17) Popeza ankadziwa kuti Atate wake wachikondi sangamusiye, Yesu sankadziona kuti ali yekhayekha.​—Yoh. 8:16.

9. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amatikonda?

9 Mofanana ndi Yesu, tonsefe takhala tikuona kuti Yehova akutisonyeza chikondi m’njira zosiyanasiyana. Tangoganizani, Yehova watilola kuti tikhale mabwenzi ake komanso watipatsa abale ndi alongo ambiri omwe amatithandiza kukhala osangalala komanso kutilimbikitsa tikakumana ndi mavuto. (Yoh. 6:44) Yehova amatipatsanso zonse zofunikira kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Iye amatithandizanso kuti tizipeza zinthu zimene timafunikira pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. (Mat. 6:31, 32) Tikamaganizira chikondi chimene Yehova amatisonyeza, ifenso timayamba kumukonda kwambiri.

MUZIONA ABALE NDI ALONGO ANU MMENE YEHOVA AMAWAONERA

10. Kodi tikuphunzira chiyani pa mmene Yehova amachitira zinthu ndi abale ndi alongo athu?

10 Yehova amakonda abale ndi alongo athu. Koma mwina nthawi zina ifeyo zingamativute kuti tiziwakonda. Mwina izi zingachitike chifukwa chosiyana zikhalidwe komanso kochokera. Ndiponso tonsefe tingachite zinthu zina zimene zingakwiyitse kapena kukhumudwitsa anthu ena. Komabe tonsefe tingachite zinthu zomwe zingathandize kuti abale ndi alongo azikondana. Tingatero potsanzira Atate wathu n’kumakonda abale ndi alongo. (Aef. 5:1, 2; 1 Yoh. 4:19) Tiyeni tione zimene tikuphunzirapo pa chitsanzo cha Yehova.

11. Kodi Yesu anasonyeza bwanji “chifundo chachikulu” cha Yehova?

11 Yehova ndi ‘wachifundo chachikulu.’ (Luka 1:78) Munthu wachifundo amakhudzika akaona ena akuvutika ndipo amafunafuna njira yoti awathandizire komanso kuwalimbikitsa. Mmene Yesu ankachitira zinthu ndi anthu, zinkasonyeza mmene Yehova amawakondera. (Yoh. 5:19) Pa nthawi ina Yesu ataona khamu la anthu, “anawamvera chisoni, chifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Kuwonjezera powachitira chifundo, Yesu anachitanso zinthu zina powathandiza. Iye anachiritsa odwala komanso kuthandiza anthu “ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa.”​—Mat. 11:28-30; 14:14.

Muzitsanzira Yehova pokhala achifundo komanso owolowa manja kwa abale ndi alongo anu (Onani ndime 12-14) *

12. Kodi tingasonyeze bwanji chifundo kwa abale ndi alongo athu?

12 Tiyenera kuganizira kaye mavuto amene abale ndi alongo athu akukumana nawo kuti tikwanitse kuwachitira chifundo. Mwachitsanzo, mlongo wina akhoza kukhala akuvutika ndi matenda aakulu. Mwina sangamalankhulelankhule za vuto lakelo koma angayamikire kwambiri ngati ena atamuthandiza. Kuti tidziwe mmene tingamuthandizire tingachite bwino kudzifunsa kuti: Kodi akukwanitsa kugwira ntchito zosamalira banja lake? Kodi tingamuthandize kuphika chakudya kapena kukonza m’nyumba? Kapenanso m’bale wina ntchito yamuthera. Kodi tingamupatse mphatso ya ndalama, mwinanso osamuuza kuti yachokera kwa ife, n’cholinga chofuna kumuthandiza mpaka atapezanso ntchito ina?

13-14. Kodi tingatani kuti tikhale owolowa manja ngati Yehova?

13 Yehova ndi wowolowa manja. (Mat. 5:45) Mofanana ndi Yehova tizithandiza ena ngakhale asanatipemphe. Tisamachite kudikira kuti abale ndi alongo athu atipemphe kaye kuti tiwasonyeze chifundo. Yehova amatiwalitsira dzuwa lake tsiku lililonse ndipo sitimachita kumupempha. Komanso kutentha kwa dzuwalo kumathandiza aliyense, osati anthu amene amayamikira okha. Kodi simukuvomereza kuti Yehova amasonyeza kuti amatikonda potipatsa zimene timafunikira? Timakonda kwambiri Yehova chifukwa ndi wokoma mtima komanso wowolowa manja.

14 Potsanzira Atate wathu wakumwamba, abale ndi alongo athu ambiri amasonyeza kuwolowa manja. Mwachitsanzo mu 2013, chimphepo champhamvu kwambiri chotchedwa Haiyan chinawononga kwambiri zinthu ku Philippines. Nyumba komanso katundu wambiri wa abale ndi alongo anawonongeka. Koma banja lawo la padziko lonse linawathandiza mwamsanga. Ambiri anapereka ndalama zawo kapena kugwira nawo ntchito zomanga, moti nyumba pafupifupi 750 zinakonzedwa kapena kumangidwanso pasanathe chaka. Pa nthawi ya mliri wa COVID-19, abale ndi alongo anachita khama pothandizana. Tikamafulumira kuthandizana timasonyeza kuti timakondana.

15-16. Kodi Lemba la Luka 6:36, limatiuza kuti tizichita chiyani potsanzira Atate wathu wakumwamba?

15 Yehova ndi wachifundo komanso wokhululuka. (Werengani Luka 6:36.) Tsiku lililonse Atate wathu wakumwamba amatisonyeza kuti ndi wachifundo. (Sal. 103:10-14) Otsatira a Yesu sanali anthu angwiro komabe iye ankawasonyeza chifundo komanso kuwakhululukira. Iye anali wofunitsitsa ngakhale kupereka moyo wake n’cholinga choti machimo athu akhululukidwe. (1 Yoh. 2:1, 2) Mtima wokhululukira ena komanso chifundo cha Yehova ndi Yesu zimatipangitsa kuti tikhale nawo pa ubwenzi.

16 Timayamba kukondana kwambiri ndi abale athu ‘tikamakhululukirana ndi mtima wonse.’ (Aef. 4:32) N’zoona kuti nthawi zina kukhululukira ena kungakhale kovuta kwambiri koma tiyenera kuyesetsa kuti tizikhululuka. Mlongo wina anaona kuti nkhani ya mu Nsanja ya Olonda, yamutu wakuti, “Muzikhululukirana ndi Mtima Wonse” inamuthandiza kwambiri. * Iye analemba kuti: “Nkhaniyi yandithandiza kumvetsa mmene kukhululukira ena kumandithandizira. Inafotokoza kuti kukhululukira ena sikutanthauza kuti ukuona kuti zimene akuchitirazo ndi zabwino kapena ndi zazing’ono. M’malomwake kumatanthauza kusasunga zifukwa n’kupitiriza kukhala ndi mtendere wa mumtima.” Tikamakhululukira abale ndi alongo athu ndi mtima wonse timasonyeza kuti timawakonda komanso timatsanzira Atate wathu Yehova.

MUZIYAMIKIRA MWAYI WOKHALA M’BANJA LA YEHOVA

Ana ndi akulu omwe amasonyeza kuti amakonda abale ndi alongo awo (Onani ndime 17) *

17. Mogwirizana ndi Mateyu 5:16, kodi tingatani kuti tizilemekeza Atate wathu wakumwamba?

17 Timayamikira kwambiri kukhala m’banja la padziko lonse lomwe anthu ake amakondana. Timafunitsitsa kuthandiza anthu ambiri mmene tingathere kuti nawonso ayambe kulambira Mulungu wathu. Poganizira mfundo imeneyi, tiyenera kukhala osamala kuti tisamachite chilichonse chomwe chingachititse kuti anthu aziganiza zoipa zokhudza anthu a Yehova kapena Atate wathu wakumwamba. Nthawi zonse tiziyesetsa kuchita zinthu zimene zingathandize anthu kuti azichita chidwi ndi uthenga wabwino.​—Werengani Mateyu 5:16.

18. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizilalikira molimba mtima?

18 Nthawi zina anthu ena akhoza kumatinyoza kapena kutizunza chifukwa timamvera Atate wathu wakumwamba. Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani ngati timaopa kuuza ena zimene timakhulupirira? Tizidalira Yehova komanso Mwana wake kuti atithandiza. Yesu anauza ophunzira ake kuti sankayenera kuda nkhawa za mmene akalankhulire kapena zimene akanene. Chifukwa chiyani? Iye anafotokoza kuti, “Mudzapatsidwa nthawi yomweyo zoti mulankhule.” Anapitirizanso kuti, “Pakuti wolankhula simudzakhala inu panokha, koma mzimu wa Atate wanu udzalankhula kudzera mwa inu.”​—Mat. 10:19, 20.

19. Perekani chitsanzo cha m’bale wina yemwe analalikira molimba mtima.

19 Taganizirani zimene zinachitikira Robert. Pa nthawi ina atangoyamba kumene kuphunzira Baibulo anaitanidwa kukhothi lina la asilikali ku South Africa. Pa nthawiyi sankadziwa zambiri zokhudza Baibulo. Iye anafotokoza molimba mtima kwa woweruza kuti sankafuna kulowa usilikali chifukwa amakonda abale ake. Robert ankayamikira kukhala m’banja la Yehova. Woweruzayo anamufunsa kuti: “Abale akowo ndi ndani?” Iye sankayembekezera funsoli koma mwamsanga anakumbukira lemba la tsiku limenelo. Linali lemba la Mateyu 12:50, lomwe limati: “Aliyense wochita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga ndi mayi anga.” Ngakhale kuti Robert anali atangoyamba kumene kuphunzira Baibulo, mzimu wa Yehova unamuthandiza kuti ayankhe funsoli komanso mafunso ena omwe sankawayembekezera. Yehova ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi zimene iye anachita. Yehova amasangalalanso tikamamudalira n’kumalalikira molimba mtima ngakhale pa nthawi zovuta.

20. Kodi tiyenera kukhala otsimikiza mtima kuchita chiyani? (Yohane 17:11, 15)

20 Tiyeni tipitirize kuyamikira mwayi wathu wokhala m’banja lauzimu lomwe anthu ake ndi okondana. Tili ndi Atate wabwino kwambiri komanso abale ndi alongo athu ochuluka omwe amatikonda. Nthawi zonse tiyenera kumayamikira kwambiri chifukwa cha zimenezi. Satana ndi otsatira ake oipa amayesetsa kutichititsa kuti tizikayikira chikondi cha Atate wathu wakumwamba ndiponso amafuna kusokoneza mgwirizano womwe tili nawo. Komabe Yesu anapempha Atate wathu kuti azitiyang’anira n’cholinga choti banja lathu likhale logwirizana. (Werengani Yohane 17:11, 15.) Yehova amayankha pemphero limeneli. Mofanana ndi Yesu tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda komanso kutithandiza. Tiyeni titsimikize mtima kuti tipitirizabe kugwirizana ndi anthu a m’banja lathu lauzimu.

NYIMBO NA. 99 Khamu la Abale

^ ndime 5 Timasangalala chifukwa cha mwayi womwe tili nawo wokhala m’banja la abale ndi alongo omwe amakondana. Tonsefe timafunitsitsa kulimbitsa kwambiri mgwirizano umene ulipo pakati pathu. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingatero tikamatsanzira chikondi cha Atate wathu komanso potsanzira Yesu ndi abale ndi alongo athu.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Yehova anatumiza mngelo kuti akalimbikitse Yesu m’munda wa Getsemane.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Pa nthawi ya mliri wa COVID-19, abale ambiri anagwira nawo ntchito yokonza komanso kugawa zakudya

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mayi akuthandiza mwana wake kulemba kalata yolimbikitsa m’bale yemwe ali m’ndende.