Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 38

Yandikilani Banja Lanu Lauzimu

Yandikilani Banja Lanu Lauzimu

“Ine ndikukwela kwa Atate wanga ndi Atate wanu.”—YOH. 20:17.

NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi anthu okhulupilika angakhale pa ubale wotani na Yehova?

BANJA la alambili a Yehova liphatikizapo Yesu, amene ni “woyamba kubadwa wa cilengedwe conse,” na angelo miyanda-miyanda. (Akol. 1:15; Sal. 103:20) Ali padziko lapansi, Yesu anaonetsa kuti n’zotheka anthu okhulupilika kuchula Yehova kuti Atate wawo. Pokamba na ophunzila ake, iye anachula Yehova kuti “Atate wanga ndi Atate wanu.” (Yoh. 20:17) Tikadzipatulila na kubatizika, timakhala m’banja la abale na alongo.—Maliko 10:29, 30.

2. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

2 Ena cimawavuta kuona Yehova kuti ni Tate wacikondi. Ndipo enanso cimawavuta kuonetsa cikondi abale na alongo awo. M’nkhani ino, tione mmene Yesu amatithandizila kuona Yehova kuti ni Tate wacikondi amene tingayandikane naye kwambili. Tionenso mmene tingatengele citsanzo ca Yehova poonetsa cikondi abale na alongo athu.

YEHOVA AFUNA KUTI IMWE MUMUYANDIKILE

3. Kodi pemphelo lacitsanzo limatiyandikilitsa bwanji kwa Yehova?

3 Yehova ni Tate wacikondi. Yesu amafuna kuti tiziona Yehova mmene iye amamuonela—inde monga kholo lacikondi lofikilika, osati lokhwimitsa zinthu. Izi zionekela bwino tikaona mmene Yesu anaphunzitsila ophunzila ake mopemphelela. M’pemphelo lake lacitsanzo, iye anayamba na mawu akuti: “Atate wathu.” (Mat. 6:9) Yesu akanafuna sembe anatiuza kuchula Yehova kuti “Wamphamvuyonse,” “Mlengi,” kapena “Mfumu yamuyaya,” amene ni maina audindo oyenelela a m’Malemba. (Gen. 49:25; Yes. 40:28; 1 Tim. 1:17) Komabe, Yesu anatiuza kuchula Yehova kuti “Atate.”

4. Tidziŵa bwanji kuti Yehova amafuna kuti timuyandikile?

4 Kodi cimakuvutani kuona Yehova kuti ni Tate wacikondi? Ni mmene zilili kwa ena a ife. Cimakhaladi covuta makamaka ngati atate athu akuthupi anali kuticitila nkhanza. Koma n’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova amamvetsa mmene timvelela. Iye amafuna kukhala nafe pafupi. Ndiye cifukwa cake Baibo imatilimbikitsa kuti: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yak. 4:8) Yehova amatikonda, ndipo amatiuza kuti adzakhala Atate wathu wabwino koposa.

5. Malinga na Luka 10:22, kodi Yesu amatithandiza bwanji kuyandikila Yehova?

5 Yesu angatithandize kuyandikila Yehova. Iye amam’dziŵa bwino Yehova, ndipo anatengela ndendende makhalidwe a Atate wake cakuti anati: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Pokhala woyamba kubadwa, Yesu amatiphunzitsa mmene tingalemekezele Atate wathu na kuwamvela, mmene tingapewele kuwakhumudwitsa, komanso zimene tingacite kuti atiyanje. Koma umoyo wa Yesu padziko lapansi maka-maka, unaonetsa kuti Yehova ni wacikondi komanso wokoma mtima. (Ŵelengani Luka 10:22.) Tiyeni tikambilaneko zitsanzo.

Pokhala Tate wacikondi, Yehova analimbikitsa Mwana wake kupitila mwa mngelo (Onani ndime 6) *

6. Fotokozani zitsanzo zoonetsa mmene Yehova anamvetsela kwa Yesu.

6 Yehova amamvetsela kwa ana ake. Mwacitsanzo, iye anamvetsela mapemphelo ambili amene Mwana wake woyamba kubadwa anapeleka ali padziko lapansi. (Luka 5:16) Iye anamvetsela pamene Yesu anali kupemphela popanga zisankho zazikulu, monga posankha atumwi ake 12. (Luka 6:12, 13) Yehova anamvetselanso Yesu pamene anali kupemphela ali wopsinjika maganizo. Atatsala pang’ono kupelekedwa, Yesu anapemphela mocokela pansi pamtima kwa Atate wake za mayeso ovuta amene anali kudzakumana nawo. Yehova sanangomvetsela pemphelo la Yesu limenelo, koma anatumanso mngelo kuti akalimbikitse Mwana wake wokondeka.—Luka 22:41-44.

7. Kodi tiyenela kumvela bwanji podziŵa kuti Yehova amamvetsela mapemphelo athu?

7 Masiku ano, Yehova amapitilizabe kumvetsela mapemphelo a atumiki ake, ndipo amawayankha panthawi yoyenela, komanso m’njila yabwino koposa. (Sal. 116:1, 2) Onani mmene Yehova anayankhila mapemphelo a mlongo wina ku India. Iye anali na vuto la kupsinjika maganizo kwa nthawi yaitali, ndipo anali kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pamtima za vutolo. Iye anati: “Pulogilamu ya Broadcasting® ya May 2019, inanilimbikitsa ngako cifukwa inali kukamba za mmene tingagonjetsele nkhawa zathu. Ndipo izi n’zimene n’nali kufunikila pa nthawiyo. Linali yankho la pemphelo langa.”

8. Kodi Yehova anaonetsa motani cikondi kwa Yesu?

8 Yehova amatikonda ndipo amasamala za ife, monga mmene anali kukondela Yesu na kumusamalila pocita utumiki wake wovuta ali padziko lapansi. (Yoh. 5:20) Iye anapatsa Yesu zonse zofunikila, zauzimu komanso zakuthupi. Ndipo Yehova sanalephele kuonetsa Mwana wake kuti amam’konda na kukondwela naye. (Mat. 3:16, 17) Yesu sanadzione kuti ali yekha, cifukwa nthawi zonse anali kudziŵa kuti Atate wake wakumwamba anali naye.—Yoh. 8:16.

9. Tidziŵa bwanji kuti Yehova amatikonda?

9 Mofanana na Yesu, tonsefe taona mmene Yehova amatikondela m’njila zambili. Ganizilani cabe: Yehova anatikokela kwa iye, ndipo anatipatsa banja lauzimu lacikondi komanso logwilizana, kuti tizikhala okondwela na kulimbikitsidwa tikapsinjika maganizo. (Yoh. 6:44) Yehova amatipatsa cakudya cauzimu ca pa nthawi yake kuti tikhalebe olimba m’cikhulupililo. Ndipo amatithandizanso kupeza zofunikila zakuthupi tsiku na tsiku. (Mat. 6:31, 32) Tikaganizila za cikondi ca Yehova pa ife, cikondi cathu pa iye cimakulilako.

TIZIONETSA CIKONDI BANJA LATHU LAUZIMU MMENE YEHOVA AMACITILA

10. Tiphunzilapo ciani tikaona mmene Yehova amakondela abale na alongo athu?

10 Yehova amakonda abale na alongo athu. Koma ife nthawi zina cingativute kuonetsa cikondi abale na alongo athu auzimu. Ndi iko komwe, tinakulila kosiyana. Ndipo tonsefe tingacite zinthu zokhumudwitsa ena. Ngakhale n’telo, tingakwanitse kucita zinthu zimene zingalimbikitse cikondi m’banja lathu lauzimu. Motani? Mwa kutengela Atate wathu poonetsa cikondi abale na alongo athu. (Aef. 5:1, 2; 1 Yoh. 4:19) Tiyeni tione zimene tingaphunzile pa citsanzo ca Yehova.

11. Kodi Yesu anaonetsa bwanji “cifundo cacikulu” potengela Yehova?

11 Yehova amaonetsa “cifundo cacikulu.” (Luka 1:78) Munthu wacifundo amakhudzika akaona anthu ena akuvutika, ndipo amayesetsa kupeza njila zowathandizila na kuwatonthoza. Pocita zinthu na ŵanthu, Yesu anaonetsa kuti Yehova amasamala za iwo. (Yoh. 5:19) Tsiku lina ataona khamu la anthu, Yesu “anawamvela cisoni cifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Yesu sanangowamvela cifundo, koma anacitapo kanthu. Anacilitsa odwala na kuthandiza awo amene anali kugwila “nchito yolemetsa ndi olemedwa.”—Mat. 11:28-30; 14:14.

Tengelani Yehova mwa kukhala acifundo komanso owolowa manja kwa abale na alongo anu (Onani ndime 12-14) *

12. Tingawaonetse motani cifundo abale na alongo athu?

12 Kuti tikwanitse kuonetsa cifundo abale na alongo athu, coyamba tiyenela kudziŵa mavuto amene akukumana nawo. Mwacitsanzo, mlongo angakhale kuti adwala matenda aakulu. Iye mwina sakambapo za matenda ake, koma n’kutheka kuti angayamikile thandizo limene angapatsidwe. Kodi iye amakwanitsa bwanji kupezela banja lake zosoŵa zakuthupi? Kodi tingamuthandize kuphika cakudya kapena kuyeletsa m’nyumba? M’bale angakhale kuti nchito inatha. Kodi mungamupatseko mphatso ya ndalama mosaonetsela kuti yacokela kwa imwe, kuti ithandizile pa zosoŵa zake mpaka atapeza nchito ina?

13-14. Tingakhale bwanji owolowa manja mofanana na Yehova?

13 Yehova ni woolowa manja. (Mat. 5:45) Conco, tisacite kuyembekezela kuti abale na alongo athu acite kutipempha thandizo m’pamene tiwaonetse cifundo. Mofanana na Yehova, tingawathandize iwo asanatipemphe n’komwe. Iye amatiwalitsila dzuŵa tsiku lililonse popanda kum’pempha. Kuthuma kwa dzuŵa kumapindulitsa aliyense, osati cabe anthu oyamikila. Kodi simungavomeleze kuti Yehova amationetsa cikondi mwa kutipatsa zofunikila? Timam’konda ngako Yehova cifukwa ni wokoma mtima komanso wopatsa!

14 Potengela citsanzo ca Atate wathu wakumwamba, abale na alongo ambili ni opatsa. Mwacitsanzo, mu 2013, cimphepo camkuntho cochedwa Haiyan cinasakaza kwambili ku Philippines. Nyumba na katundu wa abale na alongo anawonongeka. Koma banja lathu lauzimu linapita kumeneko mwamsanga kuti likawathandize. Ambili anapeleka ndalama, ndipo enanso anadzipeleka pa nchito yaikulu yomanga. Izi zinathandiza kuti akonze kapena kumanganso nyumba pafupi-fupi 750 caka cisanakwane. Pa nthawi ya mlili wa COVID-19, abale na alongo anagwila nchito molimbika pothandiza Akhristu anzawo. Ngati timathandiza banja lathu lauzimu mwamsanga, timaonetsa kuti timakonda abale na alongo athu.

15-16. Malinga na Luka 6:36, tingaonetse bwanji kuti tikutengela Atate wathu wakumwamba?

15 Yehova ni wacifundo komanso wokhululuka. (Ŵelengani Luka 6:36.) Tsiku lililonse Atate wathu wakumwamba amationetsa cifundo. (Sal. 103:10-14) Otsatila a Yesu anali opanda ungwilo. Olo n’telo, iye anawacitila cifundo na kuwakhululukila. Mofunitsitsa anapeleka moyo wake kuti macimo athu akhululukidwe. (1 Yoh. 2:1, 2) Yehova na Yesu ni acifundo komanso okhululuka, ndipo izi zimatipangitsa kuwayandikila, si conco kodi?

16 Timalimbitsa cikondi m’banja lathu lauzimu ngati ‘tikhululukilana na mtima wonse.’ (Aef. 4:32) Komabe, nthawi zina kukhululukila ena kumakhala kovuta, conco tiyenela kuyesetsa ndithu. Mlongo wina anaona kuti nkhani ya mutu wakuti, “Muzikhululukilana ndi Mtima Wonse” ya mu Nsanja ya Olonda inamuthandiza ngako. * Iye anati: “Kuŵelenga nkhaniyi, kwanithandiza kukhala na kapenyedwe koyenela pa nkhani yokhululukila. Inafotokoza kuti kukhala wofunitsitsa kukhululukila ena sikutanthauza kuti mukuvomeleza zoipa zimene acita, kapena kuona kuti zimene acitazo n’zosapweteka kwambili. Koma kumatanthauza kusasunga cakukhosi na kukhalabe na mtendele wa mumtima.” Tikamakhululukila abale na alongo athu na mtima wonse, timaonetsa kuti timawakonda, ndipo timatengela Atate wathu Yehova.

MUZIYAMIKILA MALO ANU M’BANJA LAUZIMU

Acicepele na acikulile amaonetsa kuti amakonda abale na alongo awo (Onani ndime 17) *

17. Malinga na Mateyu 5:16, kodi tingaonetse bwanji kuti timalemekeza Atate wathu wakumwamba?

17 Ni mwayi wapadela kukhala m’banja lokondana la padziko lonse. Tifuna kuti anthu ambili agwilizane nafe pa kulambila Mulungu wathu. Pa cifukwa cimeneci, tiyenela kukhala osamala kuti tisabweletse citonzo pa anthu a Yehova, kapena kwa Atate wathu wakumwamba. Tiziyesetsa kukhala na khalidwe limene lingakope anthu kuti amvetsele uthenga wabwino.—Ŵelengani Mateyu 5:16.

18. N’ciani cingatithandize kulalikila molimba mtima?

18 Nthawi zina, anthu ena angatitonze kapena kutizunza cabe cifukwa timamvela Atate wathu wakumwamba. Koma bwanji ngati timacita mantha kuuzako ena za cikhulupililo cathu? Tingakhale otsimikiza kuti Yehova na Mwana wake adzatithandiza. Yesu anauza ophunzila ake kuti sayenela kuda nkhawa na zimene adzakamba. Cifukwa ciani? Cifukwa Yesu anakamba kuti: “Mudzapatsidwa nthawi yomweyo zoti mulankhule, pakuti wolankhula simudzakhala inu panokha, koma mzimu wa Atate wanu udzalankhula kudzela mwa inu.”—Mat. 10:19, 20.

19. Fotokozani citsanzo ca m’bale amene analalikila molimba mtima.

19 Ganizilani citsanzo ca m’bale Robert. Kumbuyoku pamene anali na cidziŵitso cocepa ca m’Baibo, iye anapita kukaonekela pamaso pa khoti la asilikali ku South Africa. Iye molimba mtima anauza akhoti kuti safuna kuloŵa usilikali cifukwa cokonda abale ake acikhristu. Anacita zimenezi kaamba koyamikila malo ake m’banja lathu lauzimu. Woweluza anamufunsa kuti: “Abale ako ndani?” M’bale Robert sanayembekezele funso limeneli. Koma nthawi yomweyo, iye anakumbukila lemba la tsiku la pa tsikulo. Linali Mateyu 12:50 limene limati: “Aliyense wocita cifunilo ca Atate wanga wakumwamba, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga, ndi mayi anga.” Olo kuti m’bale Robert anali wophunzila Baibo watsopano, mzimu wa Yehova unam’thandiza kuyankha funso limenelo, na mafunso ena amene anamufunsa. Yehova anakondwela ngako na m’bale Robert! Ndipo iye amakondwelanso akaona kuti timam’dalila kuti tilalikile molimba mtima m’mikhalidwe yovuta.

20. Kodi tiyenela kupitiliza kucita ciani? (Yohane 17:11, 15)

20 Tiyeni tipitilize kuyamikila mwayi wathu wokhala m’banja lauzimu la anthu okondana. Tili na Tate wabwino koposa, komanso abale na alongo ambili amene amatikonda. Conco, tiyenela kukhala oyamikila nthawi zonse. Satana komanso omutsatila ake oipa amafuna kutipangitsa kukayikila ngati Atate wathu wakumwamba amatikonda, ndipo amafunanso kusokoneza mgwilizano wathu. Ndiye cifukwa cake, Yesu anapemphela kuti Atate wathu atiyang’anile n’colinga cakuti banja lathu likhalebe logwilizana. (Ŵelengani Yohane 17:11, 15.) Yehova akuyankha pemphelo limenelo. Mofanana na Yesu, tisamakayikile kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda na kuticilikiza. Tiyeni tipitilize kuyandikila kwambili banja lathu lauzimu.

NYIMBO 99 Abale Miyanda Miyanda

^ ndime 5 Ni mwayi waukulu cotani nanga kukhala m’banja la abale na alongo okondana. Tonsefe tiyenela kulimbitsa cikondi cimeneco pakati pathu. Tingacite bwanji zimenezi? Tingatelo mwa kutengela citsanzo ca mmene Yehova amationetsela cikondi, komanso kutengela citsanzo ca Yesu, ndiponso ca abale na alongo athu.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yehova anatuma mngelo kuti akalimbikitse Yesu m’munda wa Getsemane.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pa nthawi ya mlili wa COVID-19, ambili anagaŵilako abale awo cakudya.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mayi akuthandiza mwana wake kulemba kalata yacilimbikitso yopita kwa m’bale ku ndende.