Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 40

Kodi Kulapa Kwenikweni N’ciani?

Kodi Kulapa Kwenikweni N’ciani?

‘Ine ndinabwela kudzaitana . . . ocimwa kuti alape.’—LUKA 5:32.

NYIMBO 36 Titeteze Mitima Yathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

TIYENI tikambilane za mafumu aŵili a m’nthawi yamakedzana. Wina anali kulamulila mu ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10, ndipo wina anali kulamulila mu ufumu wa Yuda wa mafuko aŵili. Olo kuti anakhalako pa nthawi zosiyana, iwo anali ofanana pa zinthu zambili. Mafumu aŵili amenewa anapandukila Yehova, ndipo anapangitsa anthu a Mulungu kucimwa. Onse anali kulambila mafano, komanso anali kupha anthu. Ngakhale n’conco, amuna aŵiliwa anacita zinthu mosiyana. Mmodzi anapitiliza kucita zinthu zoipa mpaka imfa yake, koma wina analapa macimo ake ndipo anakhululukidwa. Kodi iwo anali ndani?

1-2. Kodi mafumu aŵili anali kusiyana motani? Nanga tikambilane mafunso ati?

2 Maina awo anali Ahabu, mfumu ya Isiraeli, komanso Manase, mfumu ya Yuda. Kusiyana kacitidwe ka zinthu ka amunawa, kutiphunzitsa zambili pankhani yofunika ngako ya kulapa. (Mac. 17:30; Aroma 3:23) Kodi kulapa n’kutani? Nanga tingaonetse bwanji kuti ndife olapa? Tiyenela kudziŵa mayankho pa mafunso aya, cifukwa timafuna Yehova atikhululukile tikacimwa. Kuti tipeze mayankho pa mafunsowa, tikambilane mbili ya mafumu aŵiliwa na kuona zimene tingaphunzilepo pa zitsanzo zawo. Tikambilanenso zimene Yesu anaphunzitsa pankhani ya kulapa.

ZIMENE TIPHUNZILAPO PA NKHANI YA MFUMU AHABU

3. Kodi Ahabu anali mfumu yotani?

3 Ahabu anali mfumu ya nambala 7 ya ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10. Iye anakwatila Yezebeli, mwana wa mfumu ya ku Sidoni, mzinda wocita bwino m’zacuma. Popeza Ahabu anakwatila Yezebeli, Aisiraeli ambili anakhala na mwayi wocita bwino m’zacuma. Koma ukwati umenewo unapangitsanso mtundu wa Isiraeli kucimwila-cimwila Yehova. Yezebeli anali kulambila Baala, ndipo analimbikitsa Ahabu kucilikiza cipembedzo conyansa cimeneco, cimene cinaphatikizapo uhule pakacisi komanso kupeleka ana nsembe. Pamene Yezebeli anali mfumukazi, aneneli onse a Yehova miyoyo yawo inali pa ciwopsezo, moti ambili mwa iwo anaphedwa na Yezebeli. (1 Maf. 18:13) Ngakhale Ahabu amene, “anacita zoipa kwambili pamaso pa Yehova kuposa onse amene anakhalapo iye asanakhale.” (1 Maf. 16:30) Yehova anali kudziŵa bwino zimene Ahabu na Yezebeli anali kucita. Mwacifundo cake, iye anatuma mneneli Eliya kukacenjeza anthu kuti asiye njila zawo zoipa zinthu zisanafike poipa. N’zacisoni kuti Ahabu na Yezebeli sanamvele.

4. Kodi Ahabu anali kudzalandila cilango cotani? Ndipo zimenezi zinam’khudza motani?

4 Koma Yehova sanapitilize kuwalezela mtima. Anatuma Eliya kuti akauze Ahabu na Yezebeli mmene iye adzawalangila. Anati onse a m’banja lawo adzaphedwa. Mawu a Eliya amenewo anam’khudza kwambili Ahabu. Zodabwitsa n’zakuti munthu wonyada ameneyu ‘anadzicepetsa.’—1 Maf. 21:19-29.

Poonetsa kuti sanalape mocokela pansi pamtima, Mfumu Ahabu anaponya mneneli wa Mulungu m’ndende (Onani ndime 5-6) *

5-6. N’ciani cionetsa kuti Ahabu sanalape kwenikweni?

5 Ngakhale kuti Ahabu anadzicepetsa pa nthawiyo, zimene anacita pambuyo pake zinaonetsa kuti sanalape kwenikweni. Iye sanathetse kulambila Baala mu ufumu wake. Komanso sanalimbikitse anthu kulambila Yehova. Palinso zina zimene Ahabu anacita zoonetsa kuti iye sanalape.

6 Patapita nthawi, Ahabu anapempha Yehosafati Mfumu yabwino ya Ayuda kuti akawathandize kukamenyana na Asiriya. Koma Yehosafati anati coyamba iwo afunsile kwa mneneli wa Yehova asanapite ku nkhondo. Poyamba, Ahabu anakana kucita zimenezo. Iye anati: “Pali munthu mmodzi amene tingathe kufunsila kwa Yehova kudzela mwa iye, koma ineyo ndimadana naye kwambili, cifukwa salosela zabwino zokhudza ine, koma zoipa.” Koma pambuyo pake, iwo anapitabe kukafunsila kwa mneneli Mikaya. Ahabu anakamba zoona, mneneliyo analoseladi zoipa zokhudza Ahabu! M’malo molapa na kupempha Yehova kuti amukhululukile, Ahabu anaponya mneneliyo m’ndende. (1 Maf. 22:7-9, 23, 27) Olo kuti mfumu yoipayi inaponya mneneli wa Yehova m’ndende, iyo sinalepheletse ulosiwo kukwanilitsika. Pankhondo yotsatila, Ahabu anaphedwa.—1 Maf. 22:34-38.

7. Ahabu atafa, kodi Yehova anakamba zotani zokhudza iye?

7 Ahabu atafa, Yehova anaonetsa mmene anali kuonela munthuyu. Pamene Mfumu yabwino Yehosafati inacoka ku nkhondo, Yehova anatuma mneneli Yehu kuti akaidzudzule cifukwa cogwilizana na Ahabu. Mneneli wa Yehova ameneyu anati: “Kodi cithandizo ciyenela kupelekedwa kwa oipa, ndipo kodi muyenela kukonda anthu odana ndi Yehova?” (2 Mbiri 19:1, 2) Ganizilani izi: Ngati Ahabu anali atalapadi na mtima wonse, mneneliyo sakanamuchula kukhala munthu woipa wodana na Yehova. N’zoonekelatu kuti ngakhale kuti Ahabu anamva kuipa na zocita zake, iye sanalape mocokela pansi pa mtima.

8. Kunena za Ahabu, kodi tiphunzilapo ciani pa nkhani ya kulapa?

8 Tiphunzilapo ciani pa nkhani ya Ahabu? Poyamba, Ahabu anadzicepetsa pamene anamva uthenga wa Eliya wokamba za cilango cimene banja lake lidzalandila. Ici cinali ciyambi cabwino. Koma zimene anacita pambuyo pake zinaonetsa kuti iye sanalape mocokela pansi pamtima. Conco, kulapa kwenikweni si kungomvela cisoni pa zimene unacita. Tiyeni tikambilane citsanzo ca munthu wina cotithandiza kumvetsa kulapa kwenikweni.

ZIMENE TIPHUNZILAPO PA CITSANZO CA MFUMU MANASE

9. Kodi Manase anali mfumu yotani?

9 Patapita zaka pafupi-fupi 200, Manase anakhala mfumu ya Ayuda. Iye anacita macimo aakulu kuposa Ahabu. Baibo imati: “Iye anacita zinthu zambili zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.” (2 Mbiri 33:1-9) Manase anamanga maguwa ansembe a milungu yacikunja. Anafika ngakhale poika cifanizilo cosema mkati mwenimweni mwa kacisi woyela wa Yehova, kukhala ngati cinali fano la mulungu wamkazi wa mphamvu zobeleketsa. Iye anali kucita zamatsenga, kuwombeza, komanso zanyanga. Manase “anakhetsanso magazi osalakwa oculuka zedi,” kuphatikizapo ‘kutentha ana ake amuna pamoto,’ powapeleka nsembe kwa milungu yonyenga.—2 Maf. 21:6, 7, 10, 11, 16.

10. Kodi Yehova anam’patsa cilango cotani Manase? Nanga mfumuyo inacita ciani?

10 Mofanana na Ahabu, Manase mouma khosi, sanalabadile macenjezo a Yehova amene anapeleka kupitila mwa aneneli ake. Potsilizila pake, “Yehova anawabweletsela akulu-akulu a asilikali a mfumu ya Asuri. Iwo anagwila Manase akubisala m’dzenje. Atatelo anam’manga ndi zomangila ziŵili zamkuwa n’kupita naye ku Babulo.” Ali m’ndende ku dziko lacilendo, Manase ayenela kuti anaganizilapo mozama pa zimene anacita. Iye “anadzicepetsa kwambili pamaso pa Mulungu wa makolo ake.” Kuwonjezela apo, anapitiliza kucondelela Yehova Mulungu wake kuti amukhululukile. Munthu woipayu anasintha. Anayamba kuona Yehova kuti ni “Mulungu wake,” ndipo anali kupemphela kwa iye nthawi zonse.—2 Mbiri 33:10-13.

Poonetsa kuti analapa mocokela pansi pamtima, Mfumu Manase anatsutsa kulambila konama (Onani ndime 11) *

11. Malinga n’kunena kwa 2 Mbiri 33:15, 16, kodi Manase anaonetsa bwanji kuti analapa mocokela pansi pamtima?

11 M’kupita kwa nthawi, Yehova anayankha mapemphelo a Manase. Mapemphelo ake anaonetsa kuti iye anasinthadi, ndipo Yehova anaona zimenezo. Conco, iye anamubwezanso pa ufumu. Manase anacita zonse zotheka poonetsa kuti analapadi. Anacita zimene Ahabu analephela kucita. Manase anasintha khalidwe lake, anatsutsa kulambila konama, ndipo analimbikitsa anthu kulambila Yehova. (Ŵelengani 2 Mbiri 33:15, 16.) Koma kuti acite zimenezi, anafunika kukhala na cikhulupililo komanso wolimba mtima cifukwa kwa zaka zambili, anali citsanzo coipa ku banja lake, anzake, komanso kwa anthu ena. Ku ukalamba wake, iye anayesa kukonza zina zimene analakwitsa. N’kutheka kuti iye anakhala citsanzo cabwino kwa mdzukulu wake Yosiya, amene anadzakhala mfumu yabwino.—2 Maf. 22:1, 2.

12. Pa citsanzo ca Manase, kodi tiphunzilapo ciani pa nkhani ya kulapa?

12 Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Manase? Iye anadzicepetsa, koma sanalekele pamenepo. Anapempha Mulungu kuti am’citile cifundo, ndipo anasintha khalidwe lake. Iye anayesetsa kukonza zimene analakwitsa, komanso anacita zonse zotheka kuti alambile Yehova na kuthandiza ena kucita cimodzimodzi. Citsanzo ca Manase n’cothandiza ngakhale kwa aja amene anacita macimo aakulu. Cipeleka umboni wamphamvu wakuti Yehova Mulungu ni ‘wabwino ndipo ni wokonzeka kukhululuka.’ (Sal. 86:5) Yehova amakhululukila anthu amene alapadi zenizeni.

13. Fotokozani citsanzo cotithandiza kumvetsa zimene tiphunzilapo pa nkhani ya kulapa.

13 Manase sanangodzimvela cisoni pa macimo ake, koma anacitapo kanthu. Apa pali phunzilo lofunika ngako pa nkhani ya kulapa kwenikweni. Ganizilani izi: Tiyelekeze kuti mwapita ku shopu kukagula keke. M’malo mokupatsani keke, wogulitsayo akukupatsani mazila. Kodi mungakhutile? Kutalitali! Kapena kodi mungakhutile iye atakufotokozelani kuti mazila ndiwo ofunika kwambili popanga keke? Ayinso. Mofananamo, Yehova naye amafuna kuti munthu wocimwa alape. Ndipo zimakhala bwino kwambili ngati wocimwayo amvela cisoni pa chimo lake. Kumvela cisoni kumeneko ni mbali yofunika ngako pa kulapa, koma zimenezo si zokwanila. N’cianinso cina cofunikila? Tiyeni tione m’fanizo logwila mtima limene Yesu anakamba.

MMENE TINGADZIŴILE NGATI MUNTHU WALAPADI ZENIZENI

Nzelu zitamubwelela, mwana woloŵelela anayenda ulendo wautali kubwelela ku nyumba (Onani ndime 14-15) *

14. M’fanizo la Yesu, kodi mwana woloŵelela anaonetsa bwanji cizindikilo cakuti wayamba kulapa?

14 Yesu anafotokoza fanizo logwila mtima la mwana woloŵelela, lopezeka pa Luka 15:11-32. Mwanayo anapandukila atate ake na kucoka pa nyumba, ndipo anapita “kudziko lina lakutali.” Kumeneko, iye anayamba makhalidwe oipa. Koma pamene zinthu zinayamba kumuthina, anazindikila kuti anapanga cisankho colakwika. Anazindikilanso kuti ku nyumba kwa atate ake anali kukhala umoyo wabwino kwambili. Yesu anati mwanayo “nzelu zitam’bwelela,” anaganiza zobwelela ku nyumba na kukapempha cikhululukilo kwa atate ake. Mwanayo anacita bwino ngako kuzindikila kuti anapanga cisankho coipa. Koma kodi kuzindikilako kunali kokwanila? Ayi! Anayenela kucitapo kanthu.

15. Kodi mwana wa m’fanizo la Yesu anacitapo ciani poonetsa analapadi mocokela pansi pamtima?

15 Mwana woloŵelela anaonetsa kuti analapadi mocokela pansi pamtima pa zimene anacita. Anayenda ulendo wautali kubwelela ku nyumba. Atafika, anauza atate ake kuti: “Ndacimwila kumwamba komanso ndacimwila inu. Sindilinso woyenela kuchedwa mwana wanu.” (Luka 15:21) Kulapa kwa mwanayo mocokela pansi pamtima, kunaonetsa kuti anali kufuna kukonza ubale wake na Yehova. Anazindikilanso kuti zocita zake zinakhumudwitsa atate ake. Iye anali wokonzeka kucita zonse zotheka kuti akhalenso pa ubale wabwino na atate ake. Analinso wokonzeka kuseŵenzela atate ake monga mmodzi wa aganyu. (Luka 15:19) Fanizoli si nthano cabe yogwila mtima. Koma lingathandize akulu mu mpingo kudziŵa ngati m’bale kapena mlongo amene anacita chimo lalikulu walapadi zenizeni.

16. N’cifukwa ciani si copepuka kwa akulu kudziŵa ngati munthu amene anacita chimo analapadi zenizeni?

16 Si copepuka kwa akulu kudziŵa ngati munthu amene anacita chimo lalikulu, analapadi mocokela pansi pamtima. Cifukwa ciani? Cifukwa akulu sangakwanitse kudziŵa za mu mtima mwa munthu. Conco, iwo amadalila zimene aona na maso kuti adziŵe ngati m’bale kapena mlongo ni wolapadi. Nthawi zina, munthu angacite chimo lalikulu cakuti akulu mwina sangakhale okhutila ngati iye walapadi zenizeni.

17. (a) Ni citsanzo citi coonetsa kuti kungodzimvela cisoni si kokwanila kuti munthu aonetse kulapa kwenikweni? (b) Malinga na 2 Akorinto 7:11, kodi munthu ayenela kucita ciani kuti aonetse kuti ni wolapadi?

17 Ganizilani citsanzo ici. M’bale wakhala akucita cigololo kwa zaka zambili. M’malo mopempha thandizo, iye akubisa chimolo kwa mkazi wake, mabwenzi ake, na akulu. Pothela pake, zikuulika. Ndiyeno akulu akumufikila na umboni wakuti iye anacita cigololo. Iye akuvomela kuti anacitadi cigololo, ndipo akucita kuonekelatu kuti ni wacisoni pa zimene anacita. Koma kodi izi n’zokwanila? Ayi. Akulu amene akusamalila mlanduwo sangakhutile na cisoni cimene munthuyo waonetsa. Munthuyo sanacite chimo limeneli kamodzi kokha, koma wakhala akucita zoipa zimenezi kwa zaka zambili. Wolakwayo sanaulule yekha chimo lake, koma anam’tulukila. Conco, akulu adzafuna kuona umboni woonetsa kuti wocimwayo anasintha zenizeni kaganizidwe kake, mmene amaonela zinthu, na khalidwe lake. (Ŵelengani 2 Akorinto 7:11.) Pangafunike nthawi yokwanila kuti munthuyo apange masinthidwe ofunikila. Kuthekela kwakukulu n’kwakuti adzacotsedwa mu mpingo.—1 Akor. 5:11-13; 6:9, 10.

18. Kodi munthu wocotsedwa angaonetse bwanji kuti analapa zenizeni? Nanga pangakhale zotulukapo zotani?

18 Kuti munthu wocotsedwa aonetse kuti walapa zenizeni, ayenela kupezeka ku misonkhano nthawi zonse, komanso kucita zimene akulu anamulangiza kuti azipemphela nthawi zonse na kuŵelenga Baibo. Ayenelanso kucita khama kuti apewe zinthu zimene zinam’tsogolela ku chimolo. Ngati wayesetsa kukonza ubale wake na Yehova, iye ayenela kutsimikiza kuti Yehova adzamukhululukila, ndipo akulu adzamubwezeletsa mu mpingo. Posamalila nkhani ya munthu aliyense, akulu amapenda nkhaniyo malinga na zolowetsedwamo zake. Mwakutelo, amapewa kuweluza mlandu mopanda cilungamo.

19. Kodi kulapa kwenikweni kumaphatikizapo ciani? (Ezekieli 33:14-16)

19 Monga mmene taphunzilila, kulapa kwa zoona sikumangolekezela pa kudzimvela cisoni pa chimo lalikulu limene tinacita. Koma kumafuna kuti munthu asinthe kaganizidwe kake, mmene aonela zinthu, na kucita zinthu zoonetsa kuti iye walapadi. Izi ziphatikizapo kuleka khalidwe lake loipa, na kutembenuka n’kuyambanso kuyenda m’njila ya Yehova. (Ŵelengani Ezekieli 33:14-16.) Wocimwayo ayenela kudziŵa kuti colinga cake cacikulu ni kukonza ubale wake na Yehova.

THANDIZANI OCIMWA KUTI ALAPE

20-21. Kodi tingamuthandize bwanji munthu amene wagwela m’chimo lalikulu?

20 Yesu anaonetsa colinga cake cacikulu pa utumiki wake mwa kukamba kuti: ‘Ine ndinabwela kudzaitana . . . ocimwa kuti alape.’ (Luka 5:32) Ifenso tiyenela kukhala na colinga cimeneco. Ngati mnzathu wapamtima wacita chimo lalikulu, kodi tiyenela kucita ciani?

21 Tingapweteketse mnzathu ngati tiyesa kubisa chimo lake. Kucita izi n’kosathandiza cifukwa Yehova amaona. (Miy. 5:21, 22; 28:13) Muuzeni mnzanuyo kuti akulu afuna kum’thandiza. Ngati iye wakana kukaonana na akulu, inu pitani mukaŵauze akulu za chimolo. Makatelo, mudzaonetsa kuti mufuna kumuthandizadi mnzanuyo, cifukwa ubale wake na Yehova uli pa ciopsezo.

22. Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

22 Koma bwanji ngati munthu wakhala akucita macimo aakulu kwa nthawi yaitali, cakuti akulu apanga cigamulo comucotsa mu mpingo? Kodi izi zingatanthauze kuti amuweluza mopanda cifundo? M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene Yehova amapelekela cilango mwacifundo kwa anthu olakwa, komanso mmene tingatengele citsanzo cake.

NYIMBO 103 Abusa ni Mphatso za Amuna

^ ndime 5 Kulapa kwenikweni sikungovomeleza cabe mwa kunena kuti n’nacimwa, koma kumafuna kucitapo kanthu. Nkhani ino, idzatithandiza kumvetsa kuti kulapa kwenikweni n’ciani. Tikambilane citsanzo ca Mfumu Ahabu, Mfumu Manase, komanso ca mwana woloŵelela wa m’fanizo la Yesu. Tikambilanenso zimene akulu ayenela kuona kuti adziŵe ngati m’bale kapena mlongo amene anacita chimo lalikulu ni wolapadi.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mfumu Ahabu mwaukali akulamula asilikali ake kuponya m’ndende Mikaya mneneli wa Yehova.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mfumu Manase akuuza anchito ake kuti awononge zifanizilo zimene iye anaika m’kacisi.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mwana woloŵelela amene watopa na ulendo wautali, akumva bwino kuona nyumba yawo ali capatali.