Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 42

Gwilani Coonadi Mwamphamvu Komanso Motsimikiza

Gwilani Coonadi Mwamphamvu Komanso Motsimikiza

“Tsimikizilani zinthu zonse. Gwilani mwamphamvu cimene cili cabwino.”—1 ATES. 5:21.

NYIMBO 142 Tigwilitsitse Ciyembekezo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciani anthu ambili ni osokonezeka maganizo?

PALI zipembedzo zambili zacikhristu zimene zimati zimalambila Mulungu m’njila yovomelezeka. N’cifukwa cake, anthu ambili ni osokonezeka maganizo, ndipo amafunsa funso lakuti, “Kodi cipembedzo coona ni citi, kodi zonse zimakondweletsa Mulungu?” Kodi timakhulupililadi mu mtima mwathu kuti ife a Mboni za Yehova timaphunzitsa coonadi, komanso kuti timalambila Yehova m’njila imene iye amavomeleza? Ngati n’conco, kodi pali umboni wa zimenezi? Tiyeni tione umboni wake.

2. Malinga na 1 Atesalonika 1:5, n’cifukwa ciani mtumwi Paulo anali kukhulupilila kuti anali na coonadi?

2 Mtumwi Paulo anali kukhulupilila kuti anali na coonadi. (Ŵelengani 1 Atesalonika 1:5.) Koma sanakhulupilile zimenezi cabe cifukwa cokondwela na coonadi. Paulo anali kuphunzila mawu a Mulungu mwakhama. Anali kukhulupilila kuti “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu.” (2 Tim. 3:16) Kodi anaphunzila zotani? Paulo anapeza umboni wosatsutsika m’Malemba wakuti Yesu anali Mesiya wolonjezedwa, umboni umene atsogoleli acipembedzo aciyuda anaukana. Atsogoleli amenewo anali kunena kuti amaphunzitsa coonadi ponena za Mulungu, koma anali kumukana mwa zocita zawo. (Tito 1:16) Mosiyana na iwo, Paulo sanasankhe zinthu zimene ayenela kukhulupilila m’Mawu a Mulungu. Iye anali wokonzeka kuphunzitsa na kucita “cifunilo conse ca Mulungu.”—Mac. 20:27.

3. Kodi tiyenela kudziŵa mayankho onse pa mafunso athu, kuti titsimikize kuti tili na coonadi? (Onaninso bokosi lakuti, “ Nchito za Yehova Komanso Maganizo Ake N’zoculuka Kwambili Moti Sitingathe Kuzifotokoza.”)

3 Ena amaganiza kuti cipembedzo coona ciyenela kuyankha mafunso onse, ngakhale aja amene mayankho ake sapezeka m’Baibo. Koma kodi zimenezi n’zotheka? Ganizilani citsanzo ca Paulo. Iye analimbikitsa Akhristu anzake ‘kutsimikizila zinthu zonse,’ koma anavomeleza kuti pali zambili zimene sanali kudziŵa. (1 Ates. 5:21) Iye anakamba kuti: “Tikudziŵa mopeleŵela, pakuti pa nthawi ino sitikuona bwino-bwino cifukwa tikugwilitsa nchito galasi losaoneka bwino-bwino.” (1 Akor. 13:9, 12) Paulo sanali kudziŵa zonse. N’cimodzi-modzi na ife. Koma iye anali kudziŵa zambili zokhudza Yehova. Zimene anali kudziŵazo, zinali zokwanila kuti atsimikize kuti analidi na coonadi.

4. Tingalimbitse bwanji cikhulupililo cathu cakuti tili na coonadi? Nanga tikambilane ciani za Akhristu oona?

4 Imodzi mwa njila zimene tingalimbitsile cikhulupililo cathu cakuti tili na coonadi, ni kuona ngati zimene Mboni za Yehova zimacita masiku ano, zigwilizana na dongosolo la kulambila limene Yesu anakhazikitsa. M’nkhani ino, tidzaona kuti Akhristu oona (1) salambila mafano, (2) amalemekeza dzina la Mulungu, (3) amakonda coonadi, komanso (4) amakondana mocokela pansi pamtima.

SITILAMBILA MAFANO

5. Tiphunzila ciani kwa Yesu za kulambila Mulungu m’njila yovomelezeka? Nanga tingatsatile bwanji zimene iye anaphunzitsa?

5 Cifukwa cokonda kwambili Mulungu, Yesu anali kulambila Yehova yekha basi, ali kumwamba komanso atabwela padziko lapansi. (Luka 4:8) Anauzanso ophunzila ake kuti azilambila Yehova yekha. Yesu komanso ophunzila ake, sanali kugwilitsila nchito zifanizilo polambila. Popeza Mulungu ni mzimu, palibe cimene munthu angapange cimene cingafanane naye m’maonekedwe. (Yes. 46:5) Nanga bwanji za kupanga zifanizilo za anthu amene amati ni oyela mtima, na kuyamba kupemphela ku zifanizilo zimenezo? Lamulo laciŵili pa Malamulo Khumi, Yehova anati: “Usadzipangile fano kapena cifanizilo ca cinthu ciliconse cakumwamba, kapena ca padziko lapansi . . . Usaziŵelamile kapena kuzitumikila.” (Eks. 20:4, 5) Anthu ofuna kukondweletsa Mulungu, amadziŵa kuti iye safuna kuti tizilambila mafano.

6. Kodi Mboni za Yehova zimatsatila kulambila kotani?

6 Olemba mbili yakale anati Akhristu oyambilila anali kulambila Mulungu yekha basi. Mwacitsanzo, buku lakuti History of the Christian Church inati, Akhristu oyambilila anali “kudana kwambili” na kuseŵenzetsa zifanizilo polambila. Masiku ano, Mboni za Yehova zimatsatila mmene Akhristu a m’zaka za zana loyamba anali kulambilila. Sitipemphela ku zifanizilo za “anthu oyela mtima,” angelo, ngakhale kwa Yesu amene. Cina, siticitila saliyuti mbendela, kapena kucita ciliconse coonetsa kuti tikulambila dziko lathu. Olo munthu atikakamize bwanji, timamvelabe mawu a Yesu akuti: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kumulambila.”—Mat. 4:10.

7. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa Mboni za Yehova na zipembedzo zina?

7 Masiku ano, anthu ambili amakonda kumvetsela kwa atsogoleli acipembedzo ochuka. Iwo amakopeka na atsogoleliwo, moti amacita ngati n’kuwalambila. Ambili amakhamukila ku machalichi awo, kugula mabuku awo, na kupeleka ndalama zambili kwa iwo. Ndipo ena amakhulupilila zonse zimene atsogoleli amenewo amakamba. Ngati anthuwo amacita zimenezi kwa atsogoleli acipembedzo, ndiye kuti ngati angaone Yesu angacite zoposa pamenepa. Koma mosiyana na zipembedzo zina, alambili oona a Yehova alibe ochedwa atsogoleli pakati pawo. Ngakhale kuti timalemekeza amene amatitsogolela, timatsatila kwambili mawu a Yesu akuti: “Nonsenu ndinu abale.” (Mat. 23:8-10) Sititsatila munthu, kaya akhale mtsogoleli wacipembedzo kapena wandale. Siticilikiza zolinga zawo, ndipo sititengela mbali iliyonse mu za dziko. Pa mbali zimenezi, timasiyana kwambili na zipembedzo zimene zimati n’zacikhristu.—Yoh. 18:36.

TIMALEMEKEZA DZINA LA MULUNGU

Akhristu oona amakondwela kuuzako ena za Yehova (Onani ndime 8-10) *

8. Tidziŵa bwanji kuti Yehova amafuna kuti dzina lake lilemekezedwe, komanso kuti anthu onse alidziŵe?

8 Panthawi ina, Yesu anapemphela kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” Yehova anayankha pemphelo limeneli na mawu amphamvu ocokela kumwamba, na kulonjeza kuti adzalilemekezadi dzina lake. (Yoh. 12:28) Yesu analemekeza dzina la Atate wake pa utumiki wake wonse. (Yoh. 17:26) Conco, Akhristu oona amaona kuti ni mwayi waukulu kugwilitsila nchito dzina la Mulungu, na kulidziŵikitsa kwa ena.

9. Kodi Akhristu oyambilila anaonetsa bwanji kuti anali kulilemekeza dzina la Mulungu?

9 M’zaka za zana loyamba, mpingo wacikhristu utangokhazikitsidwa kumene, Yehova “anaceukila anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa iwo atengemo anthu odziŵika ndi dzina lake.” (Mac. 15:14) Akhristu oyambilila amenewo, anali kunyadila kuchula dzina la Mulungu na kulidziŵikitsa kwa ena. Atumwi komanso ophunzila analiseŵenzetsa kwambili polalikila, ndiponso polemba mabuku a m’Baibo. * Iwo anaonetsadi kuti anali anthu odziŵika na dzina la Mulungu.—Mac. 2:14, 21.

10. N’ciani cionetsa kuti Mboni za Yehova ni anthu ocilikiza dzina la Mulungu?

10 Kodi Mboni za Yehova zilidi anthu ocilikiza dzina la Mulungu? Coyamba, taonani zimene atsogoleli acipembedzo ambili acita. Iwo acita zonse zotheka kuti aphimbe coonadi cakuti Mulungu ali na dzina lake-lake. Iwo alicotsa m’ma Baibo awo, ndipo afika ngakhale poletsa anthu kuti asamalichule m’machalichi mwawo. * Kodi alipo amene angatsutse mfundo yakuti a Mboni za Yehova ndiwo okha amalemekeza dzina lakuti Yehova mofunikila? Timadziŵikitsa dzina la Mulungu kwambili kuposa cipembedzo cina ciliconse. Ndipo timayesetsa kucita zinthu mogwilizana na dzina lathu lakuti, Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12) Tafalitsa makope a Baibulo la Dziko Latsopano oposa 240 miliyoni. M’Baibo imeneyi tinabwezeletsa dzina la Mulungu m’malo amene omasulila ma Baibo analicotsa. Ndipo timatulutsa zofalitsa zozikidwa pa Baibo zokhala na dzina la Mulungu m’zinenelo zoposa 1,000.

TIMAKONDA COONADI

11. Kodi Akhristu oyambilila anaonetsa bwanji kuti amakonda coonadi?

11 Yesu anali kukonda coonadi conena za Mulungu komanso colinga cake. Iye anali kukhala mogwilizana na coonadi, komanso kuuzako ena coonadi cimeneco. (Yoh. 18:37) Nawonso otsatila a Yesu anali kukonda kwambili coonadi. (Yoh. 4:23, 24) N’cifukwa cake, mtumwi Petulo anati Cikhristu ni “njila ya coonadi.” (2 Pet. 2:2) Cifukwa cokonda kwambili coonadi, Akhristu oyambilila anapewa zikhulupililo zacipembedzo, miyambo, komanso maganizo a anthu osemphana na coonadi. (Akol. 2:8) Mofananamo, masiku ano Akhristu oona amayesetsa “kuyenda m’coonadi,” ndipo amazika cikhulupililo cawo na umoyo wawo pa Mawu a Yehova.—3 Yoh. 3, 4.

12. Cimacitika n’ciani Bungwe Lolamulila likaona kuti pakufunika kusintha kamvedwe kathu? Nanga n’cifukwa ciani limacita zimenezo?

12 Anthu a Mulungu masiku ano, saona kuti amadziŵa zonse za m’Baibo. Nthawi zina, iwo alakwitsapo mbali zina za ciphunzitso ca m’Baibo kapena m’kayendetsedwe ka zinthu m’gulu. Izi siziyenela kutidabwitsa. Baibo imaonetsa kuti cidziŵitso colondola cimawonjezeleka m’kupita kwa nthawi. (Akol. 1:9, 10) Yehova amavumbula coonadi mwapang’ono-pang’ono, ndipo tiyenela kuyembekezela moleza mtima kufikila kuwala kwa coonadi kutaunikilidwa bwino-bwino. (Miy. 4:18) Bungwe Lolamulila likaona kuti kamvedwe kathu kafunika kusinthadwa pa mfundo ina yake ya coonadi, silizengeleza kupanga masinthidwe ofunikila. Machalichi ambili amasintha ziphunzitso zawo kuti akondweletse anthu awo, kapena kuti dziko liwakonde. Koma gulu la Yehova posintha kamvedwe kawo ka coonadi, colinga cathu cimakhala kuti timuyandikile kwambili Mulungu wathu, komanso kuti tim’lambile m’njila imene Yesu anakhazikitsa. (Yak. 4:4) Timapanga masinthidwe amenewa cifukwa comvetsa bwino Malemba, osati cifukwa cotengela umoyo wamakono, kapena zimene anthu ambili amafuna. Kunena zoona, ife coonadi timacikonda ngako!—1 Ates. 2:3, 4.

TIMAKONDANA MOCOKELA PANSI PA MTIMA

13. Ni khalidwe lalikulu liti limene Akhristu oona amaonetsa? Nanga Mboni za Yehova zimaonetsa motani khalidwe limeneli?

13 Akhristu oyambilila anali kudziŵika na makhalidwe awo abwino. Koma khalidwe lalikulu pa onse linali cikondi. Yesu anati: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:34, 35) Masiku ano, Mboni za Yehova padziko lonse zimakondana kwambili na kugwilizana. Mosiyana na zipembedzo zina, ubale wathu wacikondi suyang’ana dziko, mtundu, cikhalidwe, maphunzilo, na zina zotelo. Timaona umboni wa cikondi ceniceni pa misonkhano yathu ya mpingo, yadela, komanso yacigawo. Izi zimatithandiza kukhulupilila kwambili kuti timalambila Yehova m’njila imene iye amavomeleza.

14. Mogwilizana na Akolose 3:12-14, kodi tingaonetse bwanji kuti timakondana kwambili?

14 Malemba amatilimbikitsa kuti ‘tizikondana kwambili.’ (1 Pet. 4:8) Ndipo timaonetsa kuti timakondana ngati tikhululukilana, na kulolelana pa zophophonya zathu. Timafunanso kukhala opatsa komanso oceleza kwa onse mu mpingo, ngakhale kwa aja amene anatilakwila. (Ŵelengani Akolose 3:12-14.) Cikondi coteloco ndiye cizindikilo cacikulu cotidziŵila kuti ndife Akhristu oona.

“CIKHULUPILILO CIMODZI”

15. Kodi timatsatila dongosolo la kulambila la Akhristu oyambilila m’njila zinanso ziti?

15 Timatsatila dongosolo la kulambila la Akhristu oyambilila m’njila zinanso. Mwacitsanzo, m’gulu lathu tili na oyang’anila madela, akulu, komanso atumiki othandiza, potengela Akhristu a m’zaka za zana loyamba. (Afil. 1:1; Tito 1:5) Cina, timatengela citsanzo ca Akhristu amenewo pa nkhani yokhudza kugonana, ukwati, kupatulika kwa magazi, komanso kuteteza mpingo kwa anthu ocita zoipa osalapa.—Mac. 15:28, 29; 1 Akor. 5:11-13; 6:9, 10; Aheb. 13:4.

16. Tiphunzilapo ciani pa mawu a pa Aefeso 4:4-6?

16 Yesu anati anthu ambili azikamba kuti ni ophunzila ake, koma si onse adzakhala oona. (Mat. 7:21-23) Baibo inakambilatu kuti m’masiku otsiliza, anthu adzakhala “ooneka ngati odzipeleka kwa Mulungu.” (2 Tim. 3:1, 5) Komabe, imatiuzanso momveka bwino kuti pali “cikhulupililo cimodzi” covomelezeka kwa Mulungu.—Ŵelengani Aefeso 4:4-6.

17. Kodi ndani masiku ano amatsatila Yesu ndipo ali na cikhulupililo cimodzi coona?

17 Kodi ndani ali na cikhulupililo cimodzi coona masiku ano? Taona kale umboni wake. Taona dongosolo la kulambila limene Yesu anakhazikitsa, ndiponso mmene Akhristu a m’zaka za zana loyamba anatsatilila zimenezo. Conco, yankho ni lakuti, ni Mboni za Yehova. Ha, ni mwayi waukulu cotani nanga kukhala pakati pa anthu a Yehova, komanso kudziŵa coonadi conena za Yehova na colinga cake! Motelo, tiyeni tigwilebe coonadi mwamphamvu komanso motsimikiza.

YIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu

^ ndime 5 M’nkhani ino, tikambilane dongosolo la kulambila koona limene Yesu anakhazikitsa, komanso mmene Akhristu oyambilila anatsatilila dongosolo limenelo. Tionenso mmene Mboni za Yehova nazonso zimatsatilila kulambila koona kumeneko masiku ano.

^ ndime 9 Onani bokosi lakuti, “Kodi Akhristu Oyambilila Ankachula Dzina la Mulungu?” mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2010, tsa. 6.

^ ndime 10 Mwacitsanzo, mu 2008, Papa Benedict wa nambala 16, analamula kuti dzina la Mulungu “siliyenela kugwilitsidwa nchito kapena kuchulidwa” pa misonkhano ya Akatolika, poimba nyimbo, kapena popemphela.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Gulu la Yehova latulutsa Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenelo zoposa 200 lokhala na dzina la Mulungu, kuti anthu aziiŵelenga m’cinenelo cawo.