Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 43

Musaleke Kulimbikila!

Musaleke Kulimbikila!

“Tisaleke kucita zabwino.”—AGAL. 6:9.

NYIMBO 68 Fesani Mbewu za Ufumu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Ni mwayi waukulu uti umene tili nawo?

NI MWAYI waukulu cotani nanga kukhala Mboni za Yehova! Timachedwa na dzina la Mulungu, ndipo timacita mogwilizana na dzinalo mwa kulalikila na kupanga ophunzila. Timakondwela ngako tikathandiza munthu wa ‘maganizo abwino omuthandiza kukapeza moyo wosatha,’ kukhala wokhulupilila. (Mac. 13:48) Ndipo timamvela monga mmene Yesu anamvelela. Iye “anakondwela kwambili mwa mzimu woyela,” ophunzila ake atamuuza zocitika zokondweletsa za mu ulaliki.—Luka 10:1, 17, 21.

2. Tingaonetse motani kuti timaona nchito yolalikila kukhala yofunika kwambili?

2 Nchito yathu yolalikila sitiitenga mopepuka. Mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti: “Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umacita komanso zimene umaphunzitsa.” Anatinso: “Ukatelo udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvela.” (1 Tim. 4:16) Izi n’zoona cifukwa miyoyo ya anthu ili pa ciswe. Timasamala na zimene timacita cifukwa ndife nzika za Ufumu wa Mulungu. Motelo, nthawi zonse zocita zathu ziyenela kubweletsa citamando kwa Yehova, komanso kugwilizana na uthenga umene timalalikila. (Afil. 1:27) Timaonetsa kuti ‘timasamala na zimene timaphunzitsa,’ ngati tikonzekela bwino ulaliki, na kupempha thandizo kwa Yehova tisanayambe kulalikila.

3. Kodi ni anthu onse amene angamvetsele uthenga wa Ufumu? Fotokozani citsanzo.

3 Komabe, tingapeze kuti anthu ambili alibe cidwi na uthenga wa Ufumu, olo kuti tacita zonse zotheka kuti tiwalalikile. Ganizilani za m’bale Georg Lindal. Iye anali kulalikila yekha-yekha ku Iceland kucokela mu 1929 mpaka 1947. Anagaŵila zofalitsa zambili-mbili, koma palibe aliyense anaphunzila coonadi. Iye anati: “Ena anali kuoneka kuti akutsutsa uthenga wa m’Baibo, koma ambili analibe cidwi olo pang’ono.” Amishonale otsiliza maphunzilo a Giliyadi, anapita ku dzikoli kuti akapititse patsogolo nchito yolalikila. Iwo analalikila kwa zaka 9 asanapeze anthu acidwi amene anadzipatulila kwa Yehova na kubatizika. *

4. Kodi timamvela bwanji anthu akakana uthenga wathu?

4 Timakhwinyilila ngati anthu safuna kuphunzila Baibo. Tingamve monga mmene Paulo anamvelela. Iye anali na ‘cisoni cacikulu ndipo mtima unali kumupweteka nthawi zonse,’ cifukwa Ayuda ambili anakana kukhulupilila kuti Yesu ni Mesiya wolonjezedwa. (Aroma 9:1-3) Bwanji ngati mwayesetsa kuphunzila Baibo na munthu ndiponso kumupemphelela, koma iye sapita patsogolo, ndipo mwaganiza zoleka kuphunzila naye? Kapena bwanji ngati mukalibe kuthandizapo munthu mpaka kufika pobatizika? Kodi muyenela kudziimba mlandu, mwina kuganiza kuti Yehova sasangalala na utumiki wanu? M’nkhani ino, tiyankha mafunso aŵili aya: (1) N’ciani cimapangitsa ulaliki kukhala wopambana? (2) Kodi tiziyembekezela zotani tikamalalikila anthu?

N’CIANI CIMAPANGITSA ULALIKI KUKHALA WOPAMBANA?

5. Si nthawi zonse pamene utumiki wathu kwa Yehova umakhala na zotulukapo zabwino. Cifukwa ciani?

5 Ponena za munthu amene amacita cifunilo ca Mulungu, Baibo imati: “Zocita zake zonse zidzamuyendela bwino.” (Sal. 1:3) Komabe, izi sizitanthauza kuti zilizonse zimene tingacite kwa Yehova zidzayenda bwino mmene tifunila. Umoyo ni “wodzaza ndi masautso” cifukwa ca kupanda ungwilo kwathu, komanso kwa ena. (Yobu 14:1) Cina, anthu otsutsa angatiletse kulalikila mwaufulu. (1 Akor. 16:9; 1 Ates. 2:18) Kodi Yehova amayang’ana pa ciani pofuna kuona ngati ndife opambana pa nchito yolalikila? Tiyeni tione mfundo zina za m’Baibo zimene zitithandiza kuyankha funso limeneli.

Yehova amayamikila kuyesetsa kwathu, kaya tikulalikila mwacindunji, kupitila m’makalata, kapena pafoni (Onani ndime 6)

6. Kodi Yehova amayang’ana pa ciani pofuna kuona ngati ndife opambana pa nchito yolalikila?

6 Yehova amayang’ana kwambili pa kuyesetsa kwathu na kupilila kwathu. Iye amaona kuti nchito yathu yolalikila ikuyenda bwino, tikamaigwila mwakhama cifukwa com’konda, kaya anthu amvetsele kapena ayi. Paulo anati: “Mulungu si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu ndi cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake, mwa kutumikila oyela ndipo mukupitiliza kuwatumikila.” (Aheb. 6:10) Yehova amayamikila khama lathu na cikondi cathu, olo kuti sipangakhale zotulukapo zabwino pa nchito yathu yolalikila. Conco, mawu amene Paulo anauza Akorinto angakhale olimbikitsa kwa inu. Iye anati: “Zimene mukucita mu nchito ya Ambuye sizidzapita pacabe,” kaya padzakhala zotulukapo zabwino mmene imwe munali kufunila kapena ayi.—1 Akor. 15:58.

7. Tiphunzilapo ciani tikaona mmene mtumwi Paulo anaufotokozela utumiki wake?

7 Mtumwi Paulo anali mmishonale wokangalika kwambili. Iye anakhazikitsa mipingo m’mizinda yambili. Koma pamene ena anayamba kumutsutsa kuti sanali mphunzitsi wabwino, Paulo poyankha sanachule ciŵelengelo ca anthu amene iye anathandiza kukhala Akhristu. M’malo mwake, iye anati: “Nacita nchito zoculuka.” (2 Akor. 11:23, NW-E) Mofanana na Paulo, tizikumbukila kuti kuyesetsa kwathu na kupilila kwathu, n’zimene Yehova amayamikila koposa.

8. Kodi tizikumbukila mfundo yanji ponena za utumiki wathu?

8 Utumiki wathu umakondweletsa Yehova. Yesu atatuma ophunzila ake 70 kukalalikila uthenga wa Ufumu, iwo “anabwelela ali osangalala.” N’cifukwa ciani anali osangalala? Iwo anati: “Ngakhale ziwanda zinatigonjela pamene tinagwilitsa nchito dzina lanu.” Komabe, Yesu anawongolela maganizo awo mwa kuwauza kuti: “Musakondwele ndi zimenezi, kuti mizimu yakugonjelani, koma kondwelani cifukwa maina anu alembedwa kumwamba.” (Luka 10:17-20) Yesu anadziŵa kuti si nthawi zonse pamene iwo azikhala na zocitika zokondweletsa conco mu ulaliki. Ndi iko komwe, sitidziŵa kuti ni angati amene anamvetsela kwa ophunzilawo na kukhala Akhristu. Ophunzilawo anayenela kukondwela, osati cabe cifukwa ulaliki unawayendela bwino, koma cacikulu, cifukwa codziŵa kuti Yehova anayamikila khama lawo.

9. Malinga n’kunena kwa Agalatiya 6:7-9, kodi tidzapindula motani tikamapilila mu utumiki wathu?

9 Tikamapilila mu utumiki wathu, tidzapeza moyo wosatha. Tikamayesetsa kubyala mbewu za coonadi za Ufumu na kuzithilila, timakhalanso kuti ‘tikutsatila mzimu wa Mulungu,’ mwa kulola mzimuwo kugwila nchito pa ife. Ngati ‘sitilema’ kapena kulefuka, Yehova adzatipatsa moyo wosatha, kaya tathandiza wophunzila watsopano kudzipatulila kwa Mulungu kapena ayi.—Ŵelengani Agalatiya 6:7-9.

KODI TIZIYEMBEKEZELA ZOTANI TIKAMALALIKILA ANTHU?

10. N’cifukwa ciani anthu amalandila uthenga wathu mosiyana-siyana?

10 Kuti munthu alandile coonadi kapena kucikana, kwenikweni zimadalila mmene mtima wake ulili. Yesu anafotokoza mfundo ya coonadi imeneyi m’fanizo lake la wofesa mbewu. Munthuyo anafesa mbewu pa nthaka zosiyana-siyana, koma mbewu imene inagwela panthaka yabwino ndiyo inabala zipatso. (Luka 8:5-8) Yesu anati nthaka zosiyana-zosiyana, ziimila mitima ya anthu amene amalabadila “mawu a Mulungu” mosiyana-siyana. (Luka 8:11-15) Mofanana na wofesa mbewu wa m’fanizoli, sitingacititse mbewu ya coonadi kukula m’mitima ya anthu, cifukwa zimadalila mmene mitima yawo ilili. Ife nchito yathu ni kupitiliza kubyala mbewu zabwino za Ufumu. Monga mmene Paulo anakambila, “aliyense payekha adzalandila mphoto yake mogwilizana ndi nchito yake,” osati malinga na zotulukapo za nchitoyo.—1 Akor. 3:8.

Olo kuti Nowa analalikila mokhulupilika kwa zaka zambili, palibe anapulumuka kupatulapo iye na banja lake. Ngakhale n’telo, iye anakhalabe womvela kwa Mulungu! (Onani ndime 11)

11. N’cifukwa ciani Nowa anali “mlaliki wa cilungamo” wopambana? (Onani cithunzi pacikuto)

11 Atumiki a Yehova akale naonso anali kulalikila anthu amene sanali kufuna kumvetsela. Mwacitsanzo, Nowa anali “mlaliki wa cilungamo,” ndipo ayenela kuti analalikila kwa zaka zambili. (2 Pet. 2:5) Mosakaika konse, iye anali na cikhulupililo cakuti ena adzamvetsela uthenga wake. Koma Yehova sanamuuze zilizonse zoonetsa kuti anthu adzamvetsela kapena ayi. M’malo mwake, pouza Nowa kuti akhome cingalawa, Mulungu anati: “Udzaloŵe m’cingalawaco limodzi ndi ana ako, mkazi wako, ndi akazi a ana ako.” (Gen. 6:18) Poona kuti ni anthu ocepa cabe angakwane m’cingalawa cimene Mulungu anamuuza kukhoma, Nowa ayenela kuti anazindikila kuti si onse adzamvetsela. (Gen. 6:15) Ndipo monga tidziŵila, palibe ngakhale mmodzi m’dziko loipalo amene anamvetsela uthenga wa Nowa. (Gen. 7:7) Kodi Yehova anaona Nowa kukhala wolephela? Kutalitali! Mulungu anaona Nowa kukhala mlaliki wopambana, cifukwa anacita mokhulupilika zonse zimene Yehova anamuuza.—Gen. 6:22.

12. N’ciani cinathandiza mneneli Yeremiya kukhalabe wacimwemwe mu utumiki wake, olo kuti anthu analibe cidwi komanso anali kumutsutsa?

12 Nayenso mneneli Yeremiya analalikila anthu opanda cidwi komanso otsutsa kwa zaka zambili. Iye analefuka kwambili cifukwa ‘conyozedwa na kutonzedwa’ na anthu otsutsa, moti anaganiza zongoleka utumiki wake. (Yer. 20:8, 9) Koma Yeremiya sanafooke! N’ciani cinam’thandiza kuthetsa maganizo olefula, na kukhalanso wacimwemwe mu utumiki wake? Iye anasumika maganizo pa mfundo ziŵili izi zofunika. Yoyamba, uthenga wa Mulungu umene Yeremiya anauza anthu unali kukamba za “tsogolo labwino.” (Yer. 29:11) Yaciŵili, Yeremiya anali kudziŵika na dzina Mulungu. (Yer. 15:16) Mofananamo, ifenso timalalikila uthenga wopatsa ciyembekezo, komanso timadziŵika na dzina la Mulungu pokhala Mboni zake. Tikamasumika maganizo pa mfundo ziŵili zofunika zimenezi, tidzakhala acimwemwe kaya anthu amvetsele kapena ayi.

13. Tiphunzilapo ciani pa fanizo la Yesu la pa Maliko 4:26-29?

13 Kukula mwauzimu kumacitika pang’ono-pang’ono. Yesu anaphunzitsa mfundo ya coonadi imeneyi m’fanizo la wofesa mbewu amene amagona usiku. (Ŵelengani Maliko 4:26-29.) Iye atafesa mbewu zake, zinayamba kukula pang’ono-pang’ono, koma palibe cimene akanacita kuti afulumizitse kukula kwa mbewuzo. Inunso simungaone zotulukapo nthawi yomweyo panchito yanu yopanga ophunzila, cifukwa kukula mwauzimu kumacitika pang’ono-pang’ono. Monga mmene mlimi sangakakamizile mbewu zake kuti zikule mofulumila mmene iye afunila, nafenso sitingakakamize wophunzila Baibo wathu kupita patsogolo mwauzimu mmene ife tifunila. Conco, musalefuke kapena kutaya mtima ngati wophunzila Baibo wanu sakupita patsogolo mmene imwe mufunila. Mofanana na mlimi, kupanga ophunzila kumafuna kuleza mtima.—Yak. 5:7, 8.

14. N’citsanzo citi cimene cionetsa kuti pangatenge nthawi kuti anthu ayambe kumvetsela uthenga wathu?

14 M’madela ena, cimatenga zaka kuti munthu abatizike. Ganizilani za alongo aŵili a mimba imodzi, Gladys komanso Ruby Allen. Mu 1959, iwo anawatuma monga apainiya anthawi zonse mu mzinda wa Quebec ku Canada. * Anthu sanali kumvetsela uthenga wa Ufumu cifukwa coopa anthu a m’dela lawo, komanso atsogoleli acipembedzo ca Akatolika. Mlongo Gladys anati: “Kwa zaka ziŵili, tinali kulalikila nyumba na nyumba kwa maola 8 pa tsiku, koma palibe anali kutimvetsela. Anthu akasuzila pakhomo, n’kuona kuti ndife Mboni, anali kubwelela m’nyumba. Koma ife sitinaleke.” M’kupita kwa nthawi, mitima ya anthu inafewa, ndipo iwo anayamba kumvetsela uthenga wabwino. Tsopano muli mipingo itatu m’dela limenelo.—Yes. 60:22.

15. Kodi 1 Akorinto 3:6, 7, itiphunzitsa ciani pa nchito yopanga ophunzila?

15 Kupanga ophunzila kumafuna kuthandizana. Paja kuthandiza munthu kuti afike mpaka pobatizika n’kwa mpingo wonse. (Ŵelengani 1 Akorinto 3:6, 7.) Mwacitsanzo, wofalitsa angagaŵile munthu wacidwi thilakiti kapena magazini. Ndiyeno, wofalitsayo akuona kuti pulogilamu yake simulola kubwelelako kwa munthu wacidwiyo. Conco, akupempha wofalitsa wina kuti akapiteko. Wofalitsa winayo akuyambitsa phunzilo la Baibo. Kenaka, iye akuyamba kutengela ku phunzilolo abale na alongo osiyana-siyana, cakuti aliyense wa iwo akulimbikitsa wophunzila Baibo ameneyo. M’bale kapena mlongo aliyense amene akupezekapo pa phunzilolo, amathandiza kuthilila mbewu ya coonadi. Wophunzilayo akabatizika, wofesa komanso wokolola onse amakondwela, monga anakambila Yesu.—Yoh. 4:35-38.

16. Kodi mungapeze motani cimwemwe mu utumiki wanu, olo kuti muli na matenda kapena thanzi lofooka?

16 Bwanji ngati simukwanitsa kutengako mbali mokwanila pa nchito yolalikila na kupanga ophunzila, cifukwa ca matenda kapena thanzi lofooka? Mungakhalebe acimwemwe pa zimene mumakwanitsa kucita pa nchito yokolola. Ganizilani za Mfumu Davide. Pa nthawi ina, iye pamodzi na asilikali ake anapulumutsa mabanja awo na katundu wawo kwa Aamaleki. Koma asilikali ena 200 sanapite nawo ku nkhondo cifukwa anali olema kwambili. Conco, iwo anatsala kuti azilonda katundu. Atapambana nkhondoyo, Davide analamula kuti zinthu zimene anafunkha zigaŵidwe mofanana kwa aliyense. (1 Sam. 30:21-25) Izi n’zofanana na nchito yathu yopanga ophunzila ya padziko lonse. Conco, aliyense akacita zonse zotheka pa nchitoyi, tonse tidzakhala na cimwemwe cofanana pothandiza munthu kudziŵa Yehova, na kuyamba kuyenda pa njila ya ku moyo.

17. Tiziyamikila Yehova kaamba ka ciani?

17 Tiyamikila kwambili Yehova cifukwa ca mmene amaonela utumiki wathu. Adziŵa kuti sitingakakamize anthu kuti atimvetsele kapena kuyamba kum’lambila. Ngakhale n’conco, iye amaona kuyesetsa kwathu na zolinga zathu zabwino, ndipo amatidalitsa. Amatiphunzitsanso mmene tingapezele cimwemwe pa nchito yaikulu yokolola. (Yoh. 14:12) Conco, tingakhale otsimikiza kuti Yehova amakondwela nafe malinga ngati sitifooka.

NYIMBO 67 “Lalikila Mawu”

^ ndime 5 Timakondwela anthu akalandila uthenga wathu, koma timakwinyilila akakana uthengawo. Bwanji ngati munthu amene mumaphunzila naye Baibo sapita patsogolo? Kapena bwanji ngati mukalibe kuthandizapo munthu mpaka kufika pobatizika? Kodi muyenela kuganiza kuti mwalephela nchito yopanga ophunzila? M’nkhani ino, tiona mmene tingakhalile opambana komanso acimwemwe mu ulaliki, kaya anthu amvetsele kapena ayi.

^ ndime 14 Onani nkhani yakuti, “Sindingasinthe Kanthu!” yokamba za mbili ya mlongo Gladys Allen, mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 2002.