Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 47

Kodi Cikhulupililo Canu Cidzakhala Colimba Motani?

Kodi Cikhulupililo Canu Cidzakhala Colimba Motani?

“Mitima yanu isavutike. Khulupililani Mulungu.” —YOH. 14:1.

NYIMBO 119 Tikhale na Cikhulupililo

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi tingadzifunse funso lotani?

KODI nthawi zina mumada nkhawa mukaganizila zimene zidzacitika kutsogolo—monga kuwonongedwa kwa cipembedzo conyenga, kuukila kwa Gogi wa Magogi, na nkhondo ya Aramagedo? Kodi munadzifunsapo kuti, ‘Nthawiyo ikadzafika, kodi nidzakwanitsa kupilila zinthu zocititsa mantha zimenezo, na kukhalabe wokhulupilika?’ Ngati n’conco, kukambilana mawu a Yesu, amene ni lemba la mutu wa nkhani ino, kudzakuthandizani kwambili. Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Mitima yanu isavutike. Khulupililani Mulungu.” (Yoh. 14:1) Cikhulupililo colimba cidzatithandiza kuyang’ana kutsogolo mwacidalilo.

2. Kodi tingalimbitse bwanji cikhulupililo cathu? Nanga tikambilane ciani m’nkhani ino?

2 Tingalimbitse cikhulupililo cathu kuti tikakwanitse kupilila mayeso kutsogolo, tikaganizila zimene timacita cikhulupililo cathu cikayesedwa pali pano. Kucita zimenezi kudzatithandiza kuona mbali zofunika kugwililapo nchito, kuti tilimbitse cikhulupililo cathu. Tikapilila mayeso alionse, cikhulupililo cathu cimalimbilako. Izi zidzatithandiza kukapililanso mayeso a kutsogolo. M’nkhani ino, tikambilane mikhalidwe yovuta inayi imene ophunzila a Yesu anakumana nawo. Mikhalidwe imeneyo inafuna kuti iwo akhale na cikhulupililo colimba. Kenaka, tikambilane mmene tingapilile mikhalidwe yofananayo masiku ano, komanso mmene tingakonzekelele za kutsogolo.

TIFUNIKA KUKHULUPILILA KUTI MULUNGU ADZATISAMALILA KUTHUPI

Tingakumane na mavuto azacuma, koma cikhulupililo cathu cidzatithandiza kusumika maganizo pa zinthu za Ufumu (Onani ndime 3-6)

3. Malinga n’kunena kwa Mateyu 6:30, 33, kodi Yesu anamveketsa mfundo yotani yokhudza cikhulupililo?

3 Mwacibadwa, mutu wa banja amafuna kupezela mkazi wake na ŵana zakudya zokwanila, zovala, komanso nyumba. Koma kupeza zinthu zimenezi kungakhale kovuta. Nthawi zina, Akhristu anzathu amacotsedwa nchito, ndipo ngakhale atayesetsa kufuna-funa ina samaipeza. Ena amasiya nchito imene ni yosayenela kwa Akhristu. Pa zocitika zonsezi, tifunika kukhala na cikhulupililo colimba cakuti Yehova adzaonetsetsa kuti watipatsa zofunikila za banja lathu. Yesu anafotokoza zimenezi momveka bwino kwa ophunzila ake pa ulaliki wa pa Phili. (Ŵelengani Mateyu 6:30, 33.) Tikakhala na cidalilo cakuti Yehova sadzatisiya konse, tidzasumika maganizo athu pa zinthu za Ufumu. Tikaona mmene Yehova amatisamalila kuthupi, tidzamuyandikila kwambili, ndipo cikhulupililo cathu cidzalimba.

4-5. N’ciani cinathandiza banja lina kuthana na nkhawa yokhudza zosoŵa zawo zakuthupi?

4 Onani mmene Yehova anathandizila banja lina ku Venezuela, limene linali kudela nkhawa zosoŵa zakuthupi. Banja la m’bale Castro, linali kupeza zofunika zakuthupi mwa kugwila nchito pa famu yawo-yawo. Koma zigaŵenga za mfuti zinawalanda zinthu zawo, na kuwathamangitsa pa famupo. M’bale Castro, tate wa banjali anati: “Tsopano umoyo wathu umadalila pa zimene timalima pa kamalo kocepa kamene tinapempha kwa munthu wina. Tsiku lililonse, nimapempha Yehova kuti atipatse zofunikila pa tsikulo.” Umoyo wa banjali ni wovutikila, koma cifukwa cokhulupilila kuti Atate wathu wacikondi adzawasamalila tsiku lililonse, banja la m’bale Castro limasonkhana na kulalikila nthawi zonse. Iwo amaika zinthu za Ufumu patsogolo, ndipo Yehova amawapatsa zofunikila.

5 Pa nthawi yovuta imeneyo, m’bale Castro na mkazi wake Yurai, anaona mmene Yehova anawasamalila. Nthawi zina, Yehova anaseŵenzetsa Akhristu anzawo kuti awathandize mwakuthupi, kapena kuthandiza m’bale Castro kupeza nchito. Nthawi zinanso, Yehova anawasamalila kupitila m’makonzedwe opeleka thandizo ocokela ku ofesi ya nthambi. Iye sanawasiye ngakhale pang’ono. Cotulukapo cake n’cakuti, onse m’banjali cikhulupililo cawo calimba. Pambuyo pofotokoza mwacindunji mmene Yehova waathandizila, mwana wawo wamkulu wamkazi, dzina lake Yoselin, anati: “N’zolimbikitsa kwambili kuona dzanja la Yehova. Nimamuona kuti ni bwenzi langa limene ningadalile kwa moyo wonse.” Iye anatinso: “Mayeso amene takumana nawo monga banja, atikonzekeletsa mayeso aakulu m’tsogolo.”

6. Mungalimbitse bwanji cikhulupililo canu mukakumana na mavuto azacuma?

6 Kodi mukumana na mavuto azacuma? Ngati n’telo, iyi ni nthawi yovuta kwa imwe. Komabe, mungaseŵenzetse nthawi yovutayo kuti mulimbitse cikhulupililo canu. Pemphelani kwa Yehova, na kuŵelenga mawu a Yesu apa Mateyu 6:25-34, komanso kuwasinkhasinkha. Ganizilani zitsanzo zamakono zoonetsa kuti Yehova amasamalila awo amene amakhala otangwanika na zinthu zauzimu. (1 Akor. 15:58) Kucita izi kudzalimbitsa cidalilo canu cakuti Atate wanu wakumwamba adzakusamalilani, monga anacitila kwa ena omwe anali m’mikhalidwe yofanana na yanu. Iye amadziŵa zimene mufunikila, ndipo amadziŵanso mmene adzakuthandizilani. Mukamaona Yehova akukuthandizani, cikhulupililo canu cidzalimbilako, ndipo mudzatha kupilila mayeso aakulu m’tsogolo.—Hab. 3:17, 18.

TIFUNIKA CIKHULUPILILO KUTI TIPILILE “MPHEPO YAMPHAMVU”

Cikhulupililo colimba cingatithandize kupilila mphepo iliyonse yamkuntho, kaya ikhale yeniyeni kapena yophiphilitsa (Onani ndime 7-11)

7. Malinga na Mateyu 8:23-26, kodi “mphepo yamphamvu” inayesa bwanji cikhulupililo ca ophunzila?

7 Pamene Yesu na ophunzila ake anakumana na cimphepo panyanja, iye anaseŵenzetsa cocitikaci powathandiza kuona mbali zimene anafunikila kukhala na cikhulupililo colimba. (Ŵelengani Mateyu 8:23-26.) Yesu anali gone pamene cimphepo cinali kuwomba, na kupangitsa madzi kuloŵa m’bwato. Ophunzila ake atacita mantha, anamuutsa na kum’pempha kuti awapulumutse. Mokoma mtima, iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciani mukucita mantha conci, anthu acikhulupililo cocepa inu?” Ophunzila a mantha amenewo anayenela kukumbukila kuti Yehova akanateteza Yesu na anthu amene anali naye ku zoopsa zimenezo. Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Cikhulupililo colimba cingatithandize kupilila “mphepo [iliyonse] yamphamvu,” kaya ikhale yeniyeni kapena yophiphilitsa.

8-9. Kodi cikhulupililo ca mlongo Anel cinayesedwa motani? Nanga n’ciani cinam’thandiza?

8 Onani mmene cikhulupililo ca mlongo Anel wa ku Puerto Rico, amene ni mbeta, cinalimbila pambuyo popilila mayeso aakulu. Mayeso amenewo inali “mphepo yamphamvu” yeniyeni. Mu 2017, cikhulupililo ca mlongo Anel cinayesedwa, pamene cimphepo camkuntho cochedwa Hurricane Maria cinawononga nyumba yake. Cifukwa ca cimphepoco, nchito yake inatha. Iye anati: “Pa nthawi zovutazo, n’nali na nkhawa, koma n’naphunzila kudalila Yehova mwa kupemphela kwa iye, ndipo sin’nalole nkhawazo kunilefula.”

9 Mlongo Anel, wachula cimene cinam’thandiza kupilila mayeso—kumvela. Iye anati: “Kutsatila malangizo a gulu kunanithandiza kukhala wosatekeseka. Yehova ananithandiza kwambili kupitila mwa abale na alongo. Iwo ananilimbikitsa mwauzimu, na kunipatsa zofunikila zakuthupi.” Iye anawonjezela kuti: “Yehova ananipatsa zoculuka kuposa zimene n’nam’pempha, ndipo cikhulupililo canga cinalimba kwambili.”

10. Kodi mungacite ciani mukakumana na mavuto ali monga “mphepo yamphamvu”?

10 Kodi mukukumana na “mphepo yamphamvu” mu umoyo wanu? Mwina mukuvutika cifukwa ca ngozi yacilengedwe, kapena mphepo yophiphilitsa, monga matenda aakulu amene akulefulani kwambili moti n’kusoŵa mtengo wogwila. Nthawi zina, mungakhale na nkhawa, koma musalole kuti nkhawazo zikutayitseni cikhulupililo canu mwa Yehova. Muyandikileni mwa kupemphela mocokela pansi pa mtima. Limbitsani cikhulupililo canu mwa kusinkhasinkha mmene Yehova anakuthandizilani m’mbuyomu. (Sal. 77:11, 12) Mukatelo, mudzakhala na cidalilo cakuti iye sadzakusiyani pali pano, ngakhalenso m’tsogolo.

11. N’cifukwa ciani tiyenela kuyesetsa kumvela awo amene amatitsogolela?

11 N’ciani cina cingakuthandizeni kupilila mayeso? Monga anakambila mlongo Anel, ni kumvela. Muzidalila anthu amene Yehova komanso Yesu amawadalila. Nthawi zina, awo amene amatsogolela angapeleke malangizo amene tingaone kuti ni osathandiza. Komabe, Yehova amadalitsa anthu omvela. Timadziŵa zimenezi kupitila m’Mawu ake, komanso pa zitsanzo za atumiki okhulupilika, zoonetsa kuti kumvela kumapulumutsa moyo. (Eks. 14:1-4; 2 Mbiri 20:17) Muzisinkhasinkha zitsanzo zotelo. Mukatelo, mudzakhala ofunitsitsa kugwilizana na makonzedwe a gulu pali pano, ngakhalenso kutsogolo. (Aheb. 13:17) Ndipo simudzaopa cimphepo camkuntho cimene cikubwela posacedwa.—Miy. 3:25.

TIFUNIKA CIKHULUPILILO KUTI TIPILILE ZOPANDA CILUNGAMO

Tikapitiliza kupemphela, cikhulupililo cathu cidzalimba (Onani ndime 12)

12. Malinga n’kunena kwa Luka 18:1-8, kodi pali kugwilizana kotani pakati pa cikhulupililo na kupilila zopanda cilungamo?

12 Yesu anadziŵa kuti zopanda cilungamo zidzayesa cikhulupililo ca ophunzila ake. Kuti awathandize kupilila, iye anawauza fanizo lopezeka m’buku la Luka. Yesu anasimba nkhani ya mkazi wamasiye amene sanaleke kupempha kuti woweluza wopanda cilungamo am’citile cilungamo. Mkaziyo anali na cidalilo cakuti akalimbikila kupempha, adzayankhidwa. Potsilizila pake, woweluza anamvetsela pempho lake. Kodi tiphunzilapo ciani? Yehova si wopanda cilungamo. Ndiye cifukwa cake Yesu anati: “Ndithu, ngakhale kuti Mulungu amalezela mtima osankhidwa ake, kodi sadzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa iwo, amene amafuulila kwa iye usana ndi usiku?” (Ŵelengani Luka 18:1-8.) Kenako, Yesu anakambanso kuti: “Mwana wa munthu akadzafika, kodi adzapezadi cikhulupililo [cotelo] padziko lapansi?” Tikacitilidwa zopanda cilungamo, tiyenela kuonetsa kuti tili na cikhulupililo colimba cofanana na ca mkazi wamasiye, mwa kukhala oleza mtima komanso kupilila. Cikhulupililo cotelo, cidzatithandiza kukhala na cidalilo cakuti posacedwa Yehova adzacitapo kanthu. Cina, tiyenela kukhulupilila mphamvu ya pemphelo. Nthawi zina, mapemphelo athu angakhale na zotulukapo zimene sitinali kuyembekezela.

13. Kodi pemphelo linathandiza bwanji banja lina limene linacitilidwa zopanda cilungamo?

13 Ganizilani cocitika ca mlongo Vero, wa ku Democratic Republic of Congo. Iye, mwamuna wake amene si Mboni, komanso mwana wawo wamkazi wa zaka 15, anafunika kuthaŵa pamene mudzi wawo unaukilidwa na gulu la asilikali. Ali pa ulendo wothaŵa, iwo anafika pa lodibuloko. Asilikali anawaimitsa, na kuwaopseza kuti adzawapha. Mlongo Vero atayamba kulila, mwana wake anayamba kum’tonthoza mwa kupemphela mokweza na kuchula dzina la Yehova mobweleza-bweleza. Atatsiliza kupemphela, mkulu wa asilikaliyo anafunsa mtsikanayo kuti, “Iwe, ndani anakuphunzitsa kupemphela?” Mtsikanayo anayankha kuti, “Ni amayi, potengela citsanzo ca pa Mateyu 6:9-13.” Mkulu wa asilikaliyo anati, “Mwanawe, pita mu mtendele na makolo ako, ndipo Yehova Mulungu wako akuteteze.”

14. N’ciani cingaike cikhulupililo cathu pa mayeso? Nanga n’ciani cingatithandize kupilila?

14 Zocitika ngati zimenezi zitiphunzitsa kuti sitiyenela kupeputsa mphamvu ya pemphelo. Koma bwanji ngati mapemphelo anu sakuyankhidwa mwamsanga? Mofanana na mkazi wamasiye wa m’fanizo la Yesu uja, pitilizani kupemphela muli na cidalilo cakuti Mulungu wathu sadzakusiyani, komanso kuti m’kupita kwa nthawi adzayankha pemphelo lanu. Musaleke kucondelela mzimu woyela wa Yehova. (Afil. 4:13) Kumbukilani kuti posacedwa, Yehova adzakudalitsani mowilikiza cakuti mudzaiŵala mavuto onse amene munali kukumana nawo. Mukamapilila mayeso mokhulupilika mothandizidwa na Yehova, mudzatha kupililanso mayeso a kutsogolo.—1 Pet. 1:6, 7.

TIFUNIKA CIKHULUPILILO KUTI TIGONJETSE ZOVUTA

15. Malinga na Mateyu 17:19, 20, kodi ophunzila a Yesu anakumana na zovuta zotani?

15 Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kuti cikhulupililo cidzawathandiza kugonjetsa zovuta. (Ŵelengani Mateyu 17:19, 20.) Pa nthawi ina, iwo analephela kutulutsa ciŵanda, ngakhale kuti anali atakwanitsa kucita zimenezo m’mbuyomo. Kodi vuto linali ciani? Yesu anawauza kuti anafunika kuwaonjezela cikhulupililo. Anawauza kuti ngati ali na cikhulupililo cokwanila, iwo akanakwanitsa kusuntha zovuta zokhala ngati mapili. Masiku ano, nafenso timakumana na mavuto ooneka ngati n’zosatheka kuwapilila.

Tingakhale na cisoni cacikulu, koma cikhulupililo cidzatithandiza kukhalabe otangwanika mu utumiki wa Yehova (Onani ndime 16)

16. Kodi cikhulupililo cinam’thandiza bwanji mlongo Geydi kupilila cisoni cacikulu pa imfa ya mwamuna wake?

16 Ganizilani citsanzo ca mlongo Geydi wa ku Guatemala. Mwamuna wake Edi, anaphedwa pamene iwo anali kubwelela ku nyumba kucokela ku misonkhano. Kodi cikhulupililo ca mlongo Geydi, cinam’thandiza motani kupilila cisoni cake cacikulu? Iye anati: “Pemphelo linanithandiza kutulila Yehova nkhawa zanga. Izi zinanipangitsa kumvelako bwino. Naona cisamalilo ca Yehova kupitila m’banja lathu, komanso mabwenzi anga mu mpingo. Kukhala otangwanika mu utumiki wa Yehova kwanithandiza kucepetsa cisoni canga. Kwanithandizanso kuti nisamadele nkhawa kwambili za tsiku lotsatila. Pa zimene zinanicitikilazi, naphunzila kuti kaya nidzakumane na mayeso otani m’tsogolo, nidzakwanitsa kuwapilila mothandizidwa na Yehova, Yesu, komanso gulu la Mulungu.”

17. Tingacite ciani tikakumana na zovuta zokhala ngati mapili?

17 Kodi muli na cisoni cifukwa cofeledwa munthu amene mumam’konda? Muzipatula nthawi kuti mulimbitse cikhulupililo canu cakuti akufa adzauka, mwa kuŵelenga nkhani za m’Baibo zokamba za anthu amene anaukitsidwa. Kodi muli na cisoni cifukwa wa m’banja mwanu anacotsedwa mu mpingo? Ŵelengani na kufufuza kuti mutsimikize zakuti cilango ca Yehova n’copindulitsa nthawi zonse. Kaya mukumane na vuto lotani, seŵenzetsani mpata umenewo kuti mulimbitse cikhulupililo canu. Khuthulani za mu mtima mwanu kwa Yehova. Musamadzipatule, koma gwilizanani kwambili na abale na alongo anu. (Miy. 18:1) Muzicita zinthu zimene zingakuthandizeni kupilila, olo kuti mungamalile pamene mukucita zimenezo. (Sal. 126:5, 6) Musaleke kupezeka ku misonkhano, kulalikila, na kuŵelenga Baibo. Cina, sumikani maganizo anu pa madalitso amene Yehova wakusungilani. Mukamaona mmene Yehova akukuthandizilani, cikhulupililo canu mwa iye cidzalimbila-limbilako.

“TIWONJEZELENI CIKHULUPILILO”

18. Ngati cikhulupililo canu cayamba kufooka, kodi mungacite ciani?

18 Ngati cikhulupililo canu cafooka cifukwa ca mayeso amene munakumanapo nawo m’mbuyomu, kapena amene mukukumana nawo pali pano, musalefuke. Onani umenewu kukhala mwayi wolimbitsa cikhulupililo canu. Mofanana na ophunzila a Yesu, inunso muzipemphela kuti: “Tiwonjezeleni cikhulupililo.” (Luka 17:5) Cina, sinkhasinkhani pa zitsanzo zimene takambilana m’nkhani ino. Mofanana na m’bale Castro komanso Yurai, muzikumbukila mmene Yehova anali kukuthandizilani nthawi zonse. Mofanananso na mwana wa mlongo Vero komanso Anel, muzipemphela mosalekeza kwa Yehova, maka-maka mukakumana na vuto lalikulu. Ndipo monga Geydi, dziŵani kuti Yehova angakuthandizeni kupitila mwa a m’banja mwanu, kapena anzanu. Mukalola Yehova kuti akuthandizeni kupilila mayeso pali pano, mudzakulitsa cidalilo canu cakuti adzakuthandizani kupilila mayeso alionse amene mungakumane nawo kutsogolo.

19. Kodi Yesu anali na cidalilo cotani? Nanga mungakhale otsimikiza za ciani?

19 Yesu anaunikila mbali zimene ophunzila ake anali kufunikila cikhulupililo, koma sanakayikile kuti mwa thandizo la Yehova iwo adzakwanitsa kupilila mayeso a m’tsogolo. (Yoh. 14:1; 16:33) Iye anali na cidalilo cakuti khamu lalikulu lidzapulumuka cisautso cacikulu cimene cikubwela, cifukwa ca cikhulupililo cawo colimba. (Chiv. 7:9, 14) Kodi inu mudzakhala mmodzi wa opulumuka? Mwa cisomo ca Yehova, mudzapulumuka ngati pali pano muyesetsa kugwilitsila nchito mpata uliwonse kuti mulimbitse cikhulupililo canu.—Aheb. 10:39.

NYIMBO 118 “Tiwonjezeleni Cikhulupililo”

^ ndime 5 Timayembekezela mwacidwi mapeto a dongosolo lino la zinthu. Koma nthawi zina, tingakayikile ngati cikhulupililo cathu cidzakhala colimba, kuti tikakwanitse kupilila pa nthawi yovutayo. M’nkhani ino, tikambilane zitsanzo za ena, komanso zimene tiphunzilapo zotithandiza kutilimbitsa cikhulupililo cathu.