Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

N’nali Kufuna-funa Umoyo Waphindu

N’nali Kufuna-funa Umoyo Waphindu

PAMENE n’nali pakati panyanja ya Mediterranean, n’nadabwa kuona kuti madzi ambili anali kuloŵa m’boti yanga yakale imene n’nali kuyendetsa. Kenako, cimphepo camphamvu cinayamba kuwomba. N’nacita mantha, ndipo kwa nthawi yoyamba n’napemphela kwa Mulungu. Kodi n’napezeka bwanji mu mkhalidwe wovuta umenewu? Lekani nifotokoze mmene zinayambila.

Pamene n’nali na zaka 7, ine na banja lathu tinali kukhala ku Brazil

N’nabadwa mu 1948 ku Netherlands. Caka cotsatila, banja lathu linasamukila ku São Paulo, Brazil. Makolo anga anali akhama pa nkhani yopita ku chalichi, ndipo tikatsiliza kudya cakudya camadzulo, tinali kuŵelenga Baibo monga banja. Mu 1959, tinasamukanso kupita ku America, ndipo tinali kukhala mu mzinda wa Massachusetts.

Atate anali kugwila nchito molimbika kuti asamalile banja lathu la ana 8. Iwo anagwilapo nchito yoyenda-yenda kumagulitsa zinthu, yokonza misewu, komanso pa kampani ya ndeke. Tonse m’banja tinakondwela iwo ataloŵa nchito pa kampani ya ndeke, cifukwa tinadziŵa kuti tsopano tizipita nawo pa maulendo ambili.

Nili pa sukulu, n’nali kudzifunsa kuti, ‘Kodi nizigwila nchito yanji n’kadzakula?’ Anzanga ena anasankha kupita ku yunivesiti, ndipo ena anangena usilikali. Koma ine, nchito ya usilikali sinaikondepo cifukwa n’nali kudana na mikangano, ngakhale nkhondo. Conco, n’nasankha kuyenda ku yunivesiti n’colinga cakuti nisaloŵe usilikali. Ndipo pansi pa mtima, colinga canga cinali kufuna kuthandiza anthu, cifukwa n’naona kuti kucita zimenezi kungapangitse umoyo wanga kukhala waphindu.

UMOYO WA KU YUNIVESITI

Kwa zaka zambili, n’nali kufuna-funa umoyo waphindu

Ku yunivesiti, n’nakondwela kwambili kuphunzila za cikhalidwe ca anthu, cifukwa n’nali wofunitsitsa kudziŵa mmene moyo unayambila. Anatiphunzitsa za cisanduliko, ndipo aziphunzitsi anali kutiuza kuti tizikhulupilila zimenezo. Koma zina zimene anali kuphunzitsa sizinanifike pa mtima, ndipo anafuna kuti nizikhulupilila zimenezo popanda umboni wake.

Ku yunivesiti kumeneko, sanatiphunzitsepo mfundo za makhalidwe abwino. M’malo mwake, anali kungotiphunzitsa mmene tingakhozele bwino maphunzilo athu. Nikapezeka ku maphwando na anzanga, komanso kuseŵenzetsa amkolabongo, n’nali kukhala wacimwemwe. Koma cimwemweco cinali ca kanthawi kocepa. N’nali kudzifunsa kuti, ‘Kodi umenewu ndiwodi umoyo waphindu?’

Pambuyo pake, n’nasamukila mu mzinda wa Boston, ndipo kumeneko n’nabwelelanso ku yunivesiti. Kuti nizipeza ndalama yolipila ku sukulu, n’nali kugwilako kanchito tikatsekela sukulu. Ku nchitoko, n’nakumana na wa Mboni za Yehova kwa nthawi yoyamba. Mnzanga wa ku nchito ameneyo ananiuza za ulosi wa m’buku la Danieli caputa 4 wokamba za “nthawi zokwanila 7,” ndipo anafotokoza kuti tikukhala m’nthawi yamapeto. (Dan. 4:13-17) Mwamsanga n’nazindikila kuti nikapitiliza kukambilana naye nkhani za m’Baibo, n’dzafunika kusintha umoyo wanga. Conco, n’nacita zonse zotheka kuti nisamaceze naye.

Ku yunivesiti, n’nacita maphunzilo amene anali kudzanithandiza kukagwila nchito yongodzipeleka ku South America. N’naona kuti kuthandiza ena mwa kuwacitila zabwino, n’kumene kungapangitse umoyo wanga kukhala waphindu. Koma n’nali kukaikilabe ngati kucita zimenezo ndiwo unalidi umoyo waphindu. Poona kuti n’nangodzigwilitsa mwala, n’naleka maphunzilo a pa yunivesiti pambuyo pa miyezi 6.

N’NAPITILIZA KUFUNA-FUNA UMOYO WAPHINDU KU MAIKO AKUTALI

Mu May 1970, n’nasamukila ku mzinda wa Amsterdam, ku Netherlands. Kumeneko, n’nayamba kuseŵenza pa kampani ya ndeke kumene atate anali kuseŵenza. Cifukwa ca nchitoyi, n’nali kuyenda ku maiko a ku Africa, Americas, Europe, komanso Asia. Posakhalitsa, n’nazindikila kuti dziko lililonse limene n’napitako, anthu anali kukumana na mavuto aakulu, ndipo palibe akanawathetsa mavutowo. Ngakhale n’telo, n’nali kufunabe kucita cina cake cofunika kwambili. Conco, n’naganiza zobwelela ku America kukayambanso maphunzilo pa yunivesiti imodzi-modziyo mu mzinda wa Boston.

Koma nili pa yunivesiti pomwepo, n’naona kuti sinikupeza mayankho pa mafunso anga okhudza moyo. Pothedwa nzelu, n’nafunsila malangizo kwa mphunzitsi wanga. N’nadabwa iye ataniuza kuti: “N’cifukwa ciani ufuna kupitiliza maphunzilo? Bwanji osaleka cabe?” N’natsatila zimene anakamba, ndipo n’nasiyilatu maphunzilo a ku yunivesiti.

Poona kuti umoyo wanga ukali wopanda tanthauzo, n’naganiza zogwilizana na gulu lina limene sinali kutsatila malamulo. Gululi linali kuoneka monga limalimbikitsa mtendele na cikondi. Ine na anzanga tinasamuka ku America, n’kupita ku mzinda wa Acapulco, ku Mexico. Kumeneko, tinali kukhala pamodzi na kagulu ka anyamata amene sanali kutsatila mfundo za makhalidwe abwino. Posakhalitsa, n’nazindikila kuti umoyo umenewo unali wopanda tanthauzo, ndipo sunatipatse cimwemwe cokhalitsa. M’malo mwake, n’naona kuti anthuwo anali osaona mtima, komanso osakhulupilika.

N’NAPITILIZA KUFUNA-FUNA KWANGA PA BOTI

Ine na mnzanga, tinali kufuna-funa cisumbu cokongola

Pa nthawi imeneyo, n’nayamba kuganizila zimene n’nali kufuna kucita nili mwana. N’nali kufuna kumayenda na boti, osati monga wongokwelamo cabe, koma woyendetsa. Izi zikanatheka kokha ngati n’nali na boti yanga-yanga. Popeza ine na mnzanga Tom tinali na zolinga zofanana, tinaganiza zopitilila pamodzi kukayendela maiko padziko lonse. N’nali kufuna kupeza cisumbu cokongola coti nizikhalapo kuti nisamauzidwe zocita na munthu wina aliyense.

Ine na Tom tinapita ku Arenys de Marnear, pafupi na mzinda wa Barcelona, ku Spain. Kumeneko, tinagula boti ya mamita 9.4 yochedwa Llygra. Tinayamba kuikonza bwino botiyo n’colinga cakuti tiziyenda nayo pa madzi mosavuta. Popeza kuti sitinali ofulumila kwambili kupita kumene tinali kufuna, tinacotsa injini ya botiyo, ndipo pa molopo tinali kusungilapo madzi akumwa owonjezela. Kuti tikwanitse kuyendetsa boti yathu pa madoko aang’ono, tinali kuseŵenzetsa nkhafi ziŵili zofika mamita 5. Pothela pake, tinauyamba ulendo wa panyanja ya Indian Ocean kupita ku Seychelles. Colinga cathu cinali kupita ku magombe a kumadzulo kwa Africa, komanso ku Cape of Good Hope, ku South Africa. Tinali kuseŵenzetsa nyenyezi, mapu, mabuku, na zipangizo zina kuti tisasocele. N’nacita cidwi kuona kuti tikudziŵa bwino kumene tinali kupita.

Posakhalitsa, tinaona kuti boti yathu yakale ya matabwa sikanatha kuyenda panyanja yamcele. Botiyo inali kuloŵetsa madzi pafupi-fupi malita 22 pa ola limodzi. Monga nakambila kuciyambi, n’nacita mantha, ndipo n’napemphela kwa Mulungu kwa nthawi yoyamba. N’namulonjeza kuti ngati ningapulumuke, nidzayesetsa kuti nimudziŵe. Cimphepoco cinaleka, ndipo n’nasungabe lonjezo langa.

Nayamba kuŵelenga Baibo pamene tinali panyanja. Zinali zokondweletsa kwambili kukhala m’boti pakati panyanja ya Mediterranean, n’kumaona nsomba za mitundu yosiyana-siyana. Usiku, n’nali kucita cidwi na nyenyezi zambili zimene n’nali kuona. Izi zinanipangitsa kutsimikiza kuti kuli Mulungu amene amasamala za anthu.

Pambuyo pa milungu ingapo, tinafika ku gombe la Alicante, ku Spain. Kumeneko, tinagulitsa boti yathu kuti tigule ina yabwinopo. Cinali covuta kupeza munthu wogula boti yathu yakale, yopanda injini, komanso yoloŵetsa madzi. Komabe, imeneyi inali nthawi yabwino kwa ine yoŵelenga Baibo.

Pamene n’nali kuŵelenga Baibo kwambili, m’pamenenso n’nayamba kuiona kuti ni buku la malangizo othandiza kuti tikhale na umoyo wacimwemwe. N’nacita cidwi kuona kuti Baibo imafotokoza momveka bwino za kukhala na makhalidwe abwino. Ndipo sin’nali kumvetsa cifukwa cake anthu ambili amene amati ni Akhristu—kuphatikizapo ine—tinali kunyalanyaza zimene Baibo imakamba.

N’nayesetsa kutenga masitepe ofunikila kuti nisinthe khalidwe langa. Conco, n’naleka amkolabongo. N’naona kuti payenela kukhala anthu amene amatsatila mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino, ndipo n’nali kufuna kuti tsiku lina nikakumane nawo. Kwa nthawi yaciŵili, n’napemphela kwa Mulungu kuti anithandize kupeza anthuwo.

N’NAYAMBA KUFUNA-FUNA CIPEMBEDZO COONA

N’naona kuti zingakhale bwino kupita m’zipembedzo zonse n’colinga cakuti nipeze cipembedzo coona. Pamene n’nali kudutsa mu mzinda wa Alicante, n’naona zimango za machalichi ambili. Cifukwa cakuti machalichi ambili anali na zifanizilo, cinali cosavuta kwa ine kudziŵa kuti zinali zipembedzo zabodza.

Tsiku lina pa Sondo masana, n’nali khale m’mbali mwa phili moyang’anana ndi doko. N’nali kuŵelenga Yakobo 2:1-5, imene imaonetsa kuti n’kulakwa kukondela anthu acuma. Pamene n’nali kubwelela kunali boti, naona malo ena amene anali kuoneka kuti ni olambililapo, ndipo pamwamba pa khomo loloŵela panali polemba kuti: “Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.”

Mu mtima n’nati, ‘Lekani niŵayese anthu amenewa, tione mmene anilandilile.’ Conco, n’naloŵa mu Nyumba ya Ufumu imeneyo copanda nsapato, nili na ndevu zazitali, komanso n’tavala jini yong’ambika-ng’ambika. Akalinde ananitenga n’kuniuza kuti nikhale pamodzi na mzimayi wina wokalamba amene ananithandiza kupeza malemba amene mkambi anali kuchula. Pambuyo pa misonkhano, n’nadabwa kwambili kuona kukoma mtima kwa anthu onse amene anali kubwela kudzanipatsa moni. Munthu wina ananiitanila kunyumba kwake kuti tikakambilane zokhudza Baibo. Koma cifukwa n’nali nisanatsilize kuŵelenga Baibo n’namuuza kuti, “Nidzakudziŵitsani nikakakonzeka.” Koma n’nayamba kupezeka ku misonkhano yonse.

Pambuyo pa milungu ingapo, n’napita ku nyumba kwa munthu uja, ndipo iye anayankha mafunso anga okhudza Baibo. Patapita mlungu umodzi, ananipatsa cola codzala na zovala zabwino. Iye ananiuza kuti mwini wa zovalazo ali kundende cifukwa cotsatila lamulo la m’Baibo lakuti tizikondana, komanso kuti tisamamenye nkhondo. (Yes. 2:4; Yoh. 13:34, 35) Apa tsopano, n’nakhala wotsimikiza kuti napeza cimene n’nali kufuna-funa—anthu otsatila zimene Baibo imakamba ponena za makhalidwe abwino. Colinga canga lomba sicinali kusakila cisumbu cokongola, koma kuphunzila Baibo mozama. Conco, n’nabwelela ku Netherlands.

KUFUNA-FUNA NCHITO

Zinanitengela masiku anayi kuti nikafike mu mzinda wa Groningen, ku Netherlands. N’tafika, n’nayamba kufuna-funa nchito kuti nizipeza zofunikila pa umoyo. N’tafunsila nchito pa shopu ina ya za ukalipentala, ananipatsa pepala limene panali funso lina lofuna kudziŵa cipembedzo canga. N’nalemba kuti, “Mboni ya Yehova.” Mwini wa shopuyo ataŵelenga, n’naona kuti nkhope yake yasintha. Iye anati, “N’dzakutumila foni.” Koma iye sanatume.

N’napitanso pa shopu ina ya za ukalipentala, na kufunsa mwini wa shopuyo ngati anali kufuna wanchito. Iye ananiuza kuti nipeleke mapepala a ku sukulu, komanso kalata ya kunchito yanga yakale. N’namufotokozela kuti n’nagwilako nchito yokonza boti yamatabwa. N’nadabwa iye ataniuza kuti, “Ungayambe kuseŵenza masana ano, koma pokhapo ukatsatila lamulo ili: Sinifuna munthu wobweletsa msokonezo pa shopu yanga cifukwa ndine wa Mboni za Yehova, ndipo nimatsatila mfundo za m’Baibo.” N’nadabwa kwambili, ndipo n’namuyankha kuti, “Inenso ndine Mboni!” Mosakayikila, poona tsitsi langa lalitali komanso ndevu, iye anati, “N’dzayamba kukuphunzitsa Baibo.” Mwacimwemwe n’navomela. Apa tsopano n’namvetsa cifukwa cake mwini shopu woyambayo sananitumile foni. Yehova anali kuyankha mapemphelo anga. (Sal. 37:4) N’naseŵenza pa shopu ya m’baleyo kwa caka cimodzi. Pa nthawi imeneyo, iye anali kuniphunzitsa Baibo. Pambuyo pake, n’nabatizika mu January 1974.

POTSILIZILA PAKE, N’NAUPEZA UMOYO WAPHINDU!

Patapita mwezi, n’nayamba utumiki watsopano—upainiya. Utumiki umenewu wanibweletsela cimwemwe cacikulu. Mwezi wotsatila, n’nasamukila ku Amsterdam kukacilikiza kagulu katsopano kokamba ci Spanish. Zinali zokondweletsa kutsogoza maphunzilo a Baibo m’ci Spanish komanso Cipwitikizi. Mu May 1975, n’naikidwa kukhala mpainiya wapadela.

Tsiku lina, mpainiya wina wapadela dzina lake Ineke, anabwela ku misonkhano yathu ya ci Spanish kudzadziŵikitsa wophunzila wake wa ku Bolivia. Ine na Ineke tinaganiza zakuti tidziŵane bwino mwa kulembelana makalata. Pamapeto pake, tonse tinaona kuti tili na zolinga zofanana. Mu 1976, tinakwatilana, ndipo tinapitiliza kutumikila monga apainiya apadela. Mu 1982, anatiitana ku sukulu ya Giliyadi, kalasi nambala 73. Tinadabwa komanso tinakondwela kwambili atatitumiza ku East Africa, kumene tinatumikila kwa zaka 5 mu mzinda wa Mombasa, ku Kenya. Mu 1987, anatituma ku Tanzania, pa nthawiyo n’kuti ciletso pa nchito yathu yolalikila citacotsedwa. Tinatumikila m’dzikolo kwa zaka 26, kenako tinabwelela ku Kenya.

Ine na mkazi wanga tapeza cimwemwe coculuka cifukwa cothandiza anthu kuphunzila Baibo ku East Africa

Kuthandiza anthu oyamikila kuphunzila coonadi ca m’Baibo, kwatithandiza kukhala na umoyo waphindu. Mwacitsanzo, wophunzila Baibo wanga woyamba ku Mombasa, n’nakumana naye pocita ulaliki wapoyela. N’tamupatsa magazini aŵili, iye ananifunsa kuti, “N’kakatsiliza kuŵelenga, niyenela kucita ciani?” Mlungu wotsatila, n’nayamba kuphunzila naye Baibo m’buku lakuti, Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha M’paradaiso pa Dziko Lapansi. Pa nthawiyi, n’kuti langotulutsidwa kumene m’Ciswahili. Patapita caka, iye anabatizika na kukhala mpainiya wanthawi zonse. Kucokela nthawiyo, iye na mkazi wake athandiza anthu pafupi-fupi 100 kudzipatulila na kubatizika.

Ine na mkazi wanga taona mmene Yehova amadalitsila anthu ake powapatsa umoyo waphindu

Pamene n’nadziŵa colinga ca moyo, n’namvela monga wamalonda woyenda-yenda amene anapeza ngale yamtengo wapatali, ndipo sanafune kuti itaike. (Mat. 13:45, 46) N’nali kufuna kuseŵenzetsa moyo wanga kuthandiza ena kukhala na umoyo waphindu. Ine na mkazi wanga wokondedwa, tadzionela tekha mmene Yehova amadalitsila anthu ake powapatsa umoyo waphindu.