Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 44

Kodi Cikondi Cosasintha ca Yehova N’ciani?

Kodi Cikondi Cosasintha ca Yehova N’ciani?

“Kukoma mtima kosatha [cikondi cosasintha ca Yehova] kudzakhalapobe mpaka kalekale.”—SAL. 136:1.

NYIMBO 108 Cikondi Cokhulupilika ca Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Yehova amatilimbikitsa kucita ciani?

YEHOVA amakondwela kuonetsa cikondi cosasintha. (Hos. 6:6) Iye amalimbikitsa atumiki ake kuti naonso azionetsana khalidwe limeneli. Koma coyamba, tiyenela kudziŵa kuti cikondi cosasintha n’ciani.

2. Kodi cikondi cosasintha n’ciani?

2 Kodi cikondi cosasintha n’ciani? Malinga na mbali yakuti “Matanthauzo a Mawu Ena” mu Baibo la Dziko Latsopano la Cizungu, mawuwa amatanthauza “kukonda munthu mokhulupilika, modzipeleka, na kumamatila kwa iye zivute zitani. Nthawi zambili, amagwilitsidwa nchito pokamba za cikondi cimene Mulungu amaonetsa anthu, komanso cimene anthu amaonetsana pakati pawo.” Yehova n’citsanzo cabwino koposa pa kuonetsa cikondi cosasintha. M’nkhani ino, tikambilane mmene iye amaonetsela anthu cikondi cosasintha. Ndipo m’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene atumiki a Mulungu angaonetselane cikondi cosasintha cimeneci, potengela citsanzo ca Yehova.

YEHOVA NI WODZAZA NA CIKONDI COSASINTHA

3. Kodi Yehova anadzidziŵikitsa motani kwa Mose?

3 Pasanapite nthawi yaitali Aisiraeli atacoka ku Iguputo, Yehova anadzidziŵikitsa kwa Mose mwa kuchula dzina lake na makhalidwe ake. Iye anati: “Yehova, Yehova, Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha [“cikondi cosasintha,” NW-E] ndi coonadi. Wosungila mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukila zolakwa ndi macimo.” (Eks. 34:6, 7) Pokamba mawu amenewa oonetsa makhalidwe ake, Yehova anauza Mose mbali yapadela yokhudza cikondi cake cosasintha. Ni mbali iti imeneyo?

4-5. (a) Kodi Yehova anadzifotokoza motani? (b) Tikambilane mafunso ati?

4 Yehova podzifotokoza, sanangonena kuti ali na cikondi cosasintha [kapena kuti “kukoma mtima kosatha”], koma anati ni “wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.” Kafotokozedwe kameneka kamapezekanso nthawi zisanu m’Baibo. (Num. 14:18; Sal. 86:15; 103:8; Yow. 2:13; Yona 4:2) Pa nthawi zonsezi, mawu amenewa amakamba za Yehova yekha basi osati anthu. Kodi izi si zocititsa cidwi kuti Yehova amaligogomeza kwambili khalidwe lake limeneli? Mosakayikila, cikondi cosasintha n’cofunika ngako kwa iye. * Ndiye cifukwa cake, Mfumu Davide anati: “Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha [cikondi cosasintha] kuli kumwamba . . . Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali! Ndipo ana a anthu amabisala mu mthunzi wa mapiko anu.” (Sal. 36:5, 7) Mofanana na Davide, kodi timayamikila kwambili cikondi cosasintha ca Mulungu?

5 Kuti timvetsetse zimene cikondi cosasintha cimatanthauza, tiyeni tikambilane mafunso aŵili aya: Kodi Yehova amaonetsa ndani cikondi cosasintha? Nanga tingapindule motani na nchito za Yehova zoonetsa cikondi cosasintha?

KODI YEHOVA AMAONETSA NDANI CIKONDI COSASINTHA?

6. Ndani amene Yehova amawaonetsa cikondi cosasintha?

6 Kodi Yehova amaonetsa ndani cikondi cosasintha? Baibo imakamba kuti tingakonde zinthu zambili monga “ulimi,” “vinyo na mafuta,” “cidzudzulo,” “cidziŵitso,” “nzelu”—kungochulako zocepa cabe. (2 Mbiri 26:10; Miy. 12:1; 21:17; 29:3) Komabe, cikondi cosasintha sitingacionetse ku zinthu, koma kwa anthu okha basi. Yehova saonetsa cikondi cosasintha kwa aliyense, koma amacionetsa kwa anthu amene ali naye pa ubale wolimba. Mulungu wathu ni wokhulupilika kwa mabwenzi ake. Iye ali nawo na colinga cabwino, ndipo sadzaleka kuwakonda.

Yehova amapeleka zinthu zabwino kwa anthu onse, kuphatikizapo aja amene samutumikila (Onani ndime 7) *

7. Kodi Yehova anaonetsa motani kuti amakonda anthu onse?

7 Yehova anaonetsa cikondi kwa anthu onse. Yesu anauza Nikodemo kuti: “Mulungu anakonda kwambili dziko [kutanthauza mtundu wa anthu] mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yoh. 3:1, 16; Mat. 5:44, 45.

Malinga na zimene Mfumu Davide komanso mneneli Danieli anakamba, Yehova amaonetsa cikondi cosasintha kwa anthu amene amam’dziŵa, kumuopa, kum’konda na kusunga malamulo ake (Onani ndime 8-9)

8-9. (a) N’cifukwa ciani Yehova amaonetsa atumiki ake cikondi cosasintha? (b) Nanga tikambilane ciani tsopano?

8 Monga takambila, Yehova amaonetsa cikondi cosasintha kwa okhawo amene ali pa ubale wabwino na iye—atumiki ake. Mfundo imeneyi ni yoona, tikaona zimene Mfumu Davide komanso mneneli Danieli anakamba. Mwacitsanzo, Davide anati: “Pitilizani kusonyeza kukoma mtima kwanu kosatha [cikondi cosasintha] kwa anthu okudziŵani.” “Yehova adzapitiliza kusonyeza kukoma mtima kwake kosatha [cikondi cosasintha] mpaka kalekale, kwa anthu amene amamuopa.” Ndipo Danieli anakamba kuti: “Inu Yehova Mulungu woona, anthu amene amakukondani ndi kusunga malamulo anu mumawasonyeza kukoma mtima kosatha.” (Sal. 36:10; 103:17; Dan. 9:4) Malinga na mawu ouzilidwa amenewa, Yehova amaonetsa cikondi cosasintha kwa atumiki ake cifukwa amam’dziŵa, amamuopa, amam’konda, komanso amasunga malamulo ake. Zoonadi, Yehova amasungila alambili ake oona cikondi cosasintha.

9 Tisanayambe kutumikila Yehova, iye anationetsa cikondi cimene amaonetsa anthu onse. (Sal. 104:14) Koma popeza tsopano ndife alambili ake, timapindulanso na cikondi cake cosasintha. Iye amatsimikizila atumiki ake kuti: “Kukoma mtima kwanga kosatha [cikondi cosasintha] sikudzacotsedwa kwa iwe.” (Yes. 54:10) Ndithudi, monga zinalili kwa Davide, “Yehova adzapatula wokhulupilika wake.” (Sal. 4:3) Kodi tiyenela kucita ciani tikaona mmene Yehova amationetsela cikondi m’njila yapadela imeneyi? Wamasalimo anati: “Wanzelu ndani? Iye aona zimenezi, ndi kucita cidwi ndi nchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha [cikondi cosasintha].” (Sal. 107:43) Tili na mfundo imeneyi m’maganizo, tiyeni tikambilane njila zitatu mmene atumiki a Yehova amapindulila na nchito zake zoonetsa cikondi cake cosasintha.

KUPINDULA NA NCHITO ZA YEHOVA ZA CIKONDI CAKE COSASINTHA

Yehova amapeleka madalitso owonjezela kwa anthu amene amam’lambila (Onani ndime 10-16) *

10. Timapindula motani tikadziŵa kuti cikondi cosasintha ca Mulungu cidzakhalapo mpaka muyaya? (Salimo 31:7)

10 Cikondi cosasintha ca Mulungu cidzakhalapobe mpaka muyaya. Cikondi cosasintha cimeneci [kukoma mtima kosatha], cimachulidwa maulendo 26 pa Salimo 136. Pa vesi yoyamba timaŵelenga kuti: “Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino; kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.” (Sal. 136:1) Pa vesi 2 mpaka 26, anabweleza mawu akuti, “kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.” Tikaŵelenga Salimo limeneli, timacita cidwi na njila zosiyana-siyana za mmene Yehova amationetsela cikondi cake cosasintha nthawi zonse. Mawu obwelezedwa akuti “kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale,” amatitsimikiza kuti cikondi ca Mulungu pa anthu ake sicisintha-sintha. N’zolimbikitsa cotani nanga kudziŵa kuti Yehova saleka msanga kukonda atumiki ake! M’malo mwake, iye amadziphatika kwa atumiki ake, na kumamatila kwa iwo makamaka pa nthawi zovuta. Mmene timapindulila: Kudziŵa kuti Yehova amatimamatila kumatipatsa cimwemwe, komanso mphamvu zofunikila kuti tipilile mavuto athu, na kupitiliza kuyenda pa njila yopita ku moyo.—Ŵelengani Salimo 31:7.

11. Malinga n’kunena kwa Salimo 86:5, n’ciani cimasonkhezela Yehova kukhululuka?

11 Cikondi cosasintha ca Mulungu cimamusonkhezela kukhululuka. Yehova akaona kuti munthu wocimwa walapa na kusiyila njila yake yoipa, cikondi cake cosasintha cimamusonkhezela kukhululukila munthuyo. Ponena za Yehova, wamasalimo Davide anati: “Sanaticitile mogwilizana ndi macimo athu, kapena kutipatsa cilango cogwilizana ndi zolakwa zathu.” (Sal. 103:8-11) Davide anali kudziŵa bwino lomwe mmene cimamvekela kukhala na cikumbumtima cokuimba mlandu. Koma anadziŵanso kuti Yehova ni “wokonzeka kukhululuka.” N’ciani cimasonkhezela Yehova kukhululuka? Yankho tilipeza pa Salimo 86:5. (Ŵelengani.) Inde, malinga na zimene Davide anakamba m’pemphelo, Yehova amakhululuka cifukwa amaonetsa cikondi cake cosasintha kwa onse oitana pa iye.

12-13. N’ciani cingatithandize tikalefuka cifukwa codziimba mlandu pa zolakwa zimene tinacita m’mbuyomu?

12 Tikacimwa, m’poyenela komanso n’cinthu cabwino kumvela cisoni pa zimene tinacita. Kumva cisoniko kungatilimbikitse kulapa, na kutenga masitepe ofunikila kuti tikonze zimene tinalakwitsa. Komabe, atumiki ena a Yehova amakhalabe na maganizo odziimba mlandu cifukwa ca zolakwa zimene anacita m’mbuyomu. Kudziimba mlandu koteloko, kungawapangitse kuganiza kuti Yehova sanawakhululukile, ngakhale kuti iwo analapadi mocokela pansi pa mtima. Ngati muli na maganizo amenewo, kudziŵa kuti Mulungu amaonetsa atumiki ake cikondi cosasintha, kudzakuthandizani kuwathetsa.

13 Mmene timapindulila: Ngakhale kuti timalakwitsa, tingatumikile Yehova mwacimwemwe tili na cikumbumtima coyela. Izi n’zotheka cifukwa “magazi a Yesu Mwana wake akutiyeletsa ku ucimo wonse.” (1 Yoh. 1:7) Mukalefuka cifukwa cocita chimo, muzikumbukila kuti Yehova ni wokonzeka, inde ni wofunitsitsa kukhululukila munthu amene walapadi. Davide anaonetsa kugwilizana kumene kulipo pakati pa cikondi cosasintha na kukhululuka. Iye anati: “Monga mmene kumwamba kulili pamwamba kwambili kuposa dziko lapansi, kukoma mtima kwake kosatha nakonso ndi kwapamwamba kwa onse omuopa. Monga mmene kum’maŵa kwatalikilana ndi kumadzulo, momwemonso, watiikila kutali zolakwa zathu.” (Sal. 103:11, 12) Kukamba zoona, Yehova “amakhululuka ndi mtima wonse.”—Yes. 55:7.

14. Kodi Davide anafotokoza motani mmene cikondi cosasintha ca Yehova cimatitetezela?

14 Cikondi cosasintha ca Mulungu cimatiteteza mwauzimu. Popemphela kwa Yehova, Davide anati: “Ndinu malo anga obisalamo, mudzanditeteza ku masautso. Mudzacititsa kuti cisangalalo cindizungulile pamene mukundipulumutsa. . . . “Wokhulupilila Yehova amazungulilidwa ndi kukoma mtima kosatha.” (Sal. 32:7, 10) M’nthawi za m’Baibo, anthu mumzinda anali kukhala motetezeka cifukwa ca zipupa zimene zinali kuzungulila mzindawo. Mofananamo, nchito za Yehova zoonetsa cikondi cosasintha cimatizungulila, na kupeleka citetezo cauzimu ku zinthu zimene zingawononge umphumphu wathu. Cina, khalidwe limeneli la Yehova limamusonkhezela kutikokela kwa iye.—Yer. 31:3.

15. Pali kugwilizana kotani pakati pa cikondi cosasintha ca Yehova na malo othaŵilako acitetezo?

15 Davide anaseŵenzetsa mawu ena ofanizila, pofotokoza mmene Mulungu amatetezela anthu ake. Iye anati: “Mulungu ndiye malo anga okwezeka ndiponso acitetezo, Mulungu wandisonyeza kukoma mtima kosatha [cikondi cosasintha].” Anakambanso kuti: “Iye amandisonyeza kukoma mtima kwake kosatha ndipo ndiye malo anga acitetezo, malo anga okwezeka ndi Wopeleka cipulumutso, cishango canga ndi malo anga othaŵilako.” (Sal. 59:17; 144:2) N’cifukwa ciani Davide anayelekezela cikondi cosasintha ca Yehova na malo othaŵilako acitetezo? Kulikonse kumene tingakhale m’dzikoli, malinga ngati ndife atumiki ake, Yehova adzapitiliza kupeleka citetezo cofunikila, kuti titeteze ubale wathu wamtengo wapatali na iye. Citsimikizo cimeneci cipezekanso pa Salimo 91. Wolemba Salimo limeneli anati: “Ndidzauza Yehova kuti: ‘Inu ndinu pothaŵilapo panga ndi malo anga acitetezo.’” (Sal. 91:1-3, 9, 14) Mose nayenso anaseŵenzetsa mawu ofanizila ofanana na amenewa. (Sal. 90:1) Kuwonjezela apo, kumapeto kwa moyo wake, Mose anakamba mfundo yolimbikitsa yakuti: “Mulungu wakale lomwe ndiwo malo ako obisalamo, ndipo iwe uli m’manja amene adzakhalapo mpaka kalekale.” (Deut. 33:27) Kodi mawu akuti “uli m’manja amene adzakhalapo mpaka kalekale,” atiuza ciani ponena za Yehova?

16. Kodi ndife odalitsika m’njila ziŵili ziti? (Salimo 136:23)

16 Yehova akakhala Pothaŵilapo pathu, timamva kukhala otetezeka. Ngakhale n’telo, nthawi zina tingalefuke cakuti tingayambe kuona kuti sitilinso otetezeka. Pa nthawi zotelo, kodi Yehova adzacitanji kwa ife? (Ŵelengani Salimo 136:23.) Iye mwacikondi adzatinyamula na manja ake, na kutithandiza kuti tisakhalenso olefuka. (Sal. 28:9; 94:18) Mmene timapindulila: Kudziŵa kuti Mulungu adzaticilikiza, kumatithandiza kukumbukila kuti ndife odalitsika m’njila ziŵili izi: Yoyamba, tili na malo othaŵilapo acitetezo, mosasamala kanthu za kumene tikhala. Yaciŵili, Atate wathu wacikondi wakumwamba amasamala kwambili za ife.

MULUNGU SADZALEKA KUTIONETSA CIKONDI COSASINTHA

17. Cifukwa ca cikondi cosasintha ca Mulungu, kodi tiyenela kukhala na cidalilo cotani? (Salimo 33:18-22)

17 Monga taonela, tikakumana na mayeso, tingakhale na cidalilo cakuti Yehova adzaticilikiza mwa kutipatsa thandizo lofunikila kuti tisunge umphumphu wathu. (2 Akor. 4:7-9) Mneneli Yeremiya anati: “Cifukwa ca kukoma mtima kosatha Yehova, ife sitinafafanizidwe, ndipo cifundo cake sicidzatha.” (Maliro 3:22) Tili na cidalilo cakuti Yehova adzapitiliza kutionetsa cikondi cosasintha, cifukwa wamasalimo anatitsimikizila kuti: “Diso la Yehova lili pa anthu amene amamuopa, amene amayembekezela kukoma mtima kwake kosatha.”—Ŵelengani Salimo 33:18-22.

18-19. (a) Kodi tiyenela kukumbukila ciani? (b) Nanga tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

18 Kodi tiyenela kukumbukila ciani? Tisanayambe kutumikila Yehova, iye anationetsa cikondi cimene amaonetsa anthu onse. Koma popeza tsopano ndife alambili ake, timapindulanso na cikondi cake cosasintha. Mosonkhezeledwa na khalidwe limeneli, Yehova amatifungatila na manja ake kuti atiteteze. Iye adzakhala nafe pafupi nthawi zonse, na kukwanilitsa colinga cake ponena za ife. Ndipo amafuna kuti tikhale mabwenzi ake mpaka muyaya. (Sal. 46:1, 2, 7) Conco, kaya tikumane na mayeso otani, Yehova adzatipatsa mphamvu zofunikila kuti tisunge umphumphu wathu.

19 Taona mmene Yehova amaonetsela cikondi cosasintha kwa atumiki ake. Ndipo iye amafuna kuti tizionetsana khalidwe limeneli. Kodi tingacite motani zimenezi? Nkhani yotsatila idzayankha funso lofunika kwambili limeneli.

NYIMBO 136 Yehova “Akufupe Mokwanila”

^ ndime 5 Kodi cikondi cosasintha n’ciani? Kodi Yehova amaonetsa ndani cikondi cosasintha cimeneci? Nanga awo amene amaonetsedwa cikondi cotelo amapindula motani? Tidzakambilana mayankho pa mafunso amenewa, m’nkhani ziŵili zoyambilila zimene zifotokoza khalidwe lofunika kwambili limeneli.

^ ndime 4 Mfundo yakuti Mulungu ni wodzaza na cikondi cosasintha, imachulidwanso pa Malemba ena.—Onani Nehemiya 13:22; Salimo 69:13; 106:7; komanso Maliro 3:32.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yehova amaonetsa cikondi anthu onse, kuphatikizapo atumiki ake. Tumapikica tuli pa cithunzici tuonetsa njila zimene Yehova waonetsela cikondi kwa anthu onse. Njila yaikulu imene watiolnetsela cikondi, ni dipo imene anapeleka kuti tipindule.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Anthu amene amakhala atumiki a Yehova na kuika cikhulupililo cawo mu dipo, iye amawasamalila mwapadela. Mulungu amaonetsa cikondi kwa anthu onse, koma atumiki ake amawaonetsanso cikondi cake cosasintha. Zitsanzo zake zikuonekela pa cithunzi.