Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 48

“Muzikhala Oyela”

“Muzikhala Oyela”

“Khalani oyela m’makhalidwe anu onse.”—1 PET. 1:15.

NYIMBO 34 N’dzayenda mu Umphumphu Wanga

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi mtumwi Petulo anapeleka malangizo otani kwa Akhristu anzake? Nanga n’cifukwa ciani malangizo akewo angaoneke osatheka kuwatsatila?

 KAYA ciyembekezo cathu n’cakumwamba kapena padziko lapansi, tonsefe tingapindule na malangizo amene mtumwi Petulo anapatsa Akhristu oyambilila odzozedwa. Iye anati: “Khalani motsanzila Woyela amene anakuitanani. Inunso khalani oyela m’makhalidwe anu onse, cifukwa Malemba amati: ‘Mukhale oyela, cifukwa ine ndine woyela.’” (1 Pet. 1:15, 16) Mawu aya aonetsa kuti n’zotheka kutengela Yehova, amene ni citsanzo cabwino koposa pa nkhani ya ciyelo. Conco, tifunika kukhala oyela m’makhalidwe athu onse. Koma izi zingaoneke zosatheka cifukwa ndife opanda ungwilo. Ngakhale Petulo iye mwini analakwitsapo zinthu zina, koma citsanzo cake cionetsa kuti tingathe kukhala oyela.

2. Tikambilane mafunso ati m’nkhani ino?

2 M’nkhani ino, tikambilane mafunso aya: Kodi ciyelo n’ciani? Kodi Baibo imatiphunzitsa ciani za ciyelo ca Yehova? Kodi tingakhale bwanji oyela m’makhalidwe athu? Nanga ciyelo cathu cimakhudza bwanji ubale wathu na Yehova?

KODI CIYELO N’CIANI?

3. Kodi anthu ambili ali na maganizo otani pa nkhani ya ciyelo? Nanga n’kuti kumene tingapeze mfundo zolondola?

3 Anthu ambili amaganiza kuti munthu woyela, ni uja amene sasangalala konse, wovala zovala zacipembedzo, komanso nkhope yake yooneka yacifundo-cifundo. Koma zimenezi si zoona. Yehova, amene ni woyela, amafotokozedwa kuti ni “Mulungu wacimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Anthu amene amamulambila amachedwa “odala.” (Sal. 144:15) Yesu anadzudzula anthu ovala zovala zapadela, komanso odzionetsela kuti ni olungama pamaso pa anthu. (Mat. 6:1; Maliko 12:38) Pokhala Akhristu, timadziŵa zimene kukhala woyela kumatanthauza cifukwa ca zimene timaphunzila m’Baibo. Timadziŵanso kuti Mulungu wathu woyela komanso wacikondi, sangatiuze kucita zinthu zimene sitingakwanitse. Conco, Yehova akamatiuza kuti: “Muzikhala oyela,” timadziŵa kuti n’zotheka kucita zimenezo. Komabe, kuti tikhale oyela m’makhalidwe athu, coyamba tiyenela kudziŵa zimene ciyelo cimatanthauza.

4. Kodi mawu akuti “ciyelo” amatanthauza ciani?

4 Kodi ciyelo n’ciani? M’Baibo, mawu akuti “ciyelo” amatanthauza kukhala na makhalidwe oyela aumulungu kapena kukhala wopatulika. Mawuwa angatanthauzenso kudzipatulila kuti utumikile Mulungu. M’mawu ena tingati, timakhala oyela ngati tili na makhalidwe abwino, timalambila Yehova m’njila yovomelezeka, komanso ngati tili pa ubale wabwino na Mulungu. Timacita cidwi kwambili tikaona kuti Yehova, amene ni woyela koposa, amafuna kuti tikhalebe mabwenzi ake, olo kuti ndife opanda ungwilo.

“WOYELA, WOYELA, WOYELA NDIYE YEHOVA”

5. Tingaphunzile ciani za Yehova kwa angelo okhulupilika?

5 Yehova ni woyela m’njila zake zonse. Timadziŵa zimenezi tikaona zimene aserafi, amene ni angelo okhala pafupi na mpando wacifumu wa Mulungu anakamba. Ena a iwo analengeza kuti: “Woyela, woyela, woyela ndiye Yehova wa makamu.” (Yes. 6:3) Komabe, kuti angelo akhale pa ubale wolimba na Mulungu, ayenela kukhala oyela, ndipo ni mmene alili. Ndiye cifukwa cake, malo amene angelo a Yehova anaimapo padziko lapansi popeleka uthenga anali kukhala oyela. Izi n’zimene zinacitika pamene Mose anali pa citsamba caminga coyaka moto.—Eks. 3:2-5; Yos. 5:15.

Mawu akuti “Ciyelo n’ca Yehova” anawagoba pa kacitsulo kagolide panduwila ya mkulu wa ansembe (Onani ndime 6-7)

6-7. (a) Malinga na Ekisodo 15:1, 11, kodi Mose anagogomeza motani ciyelo ca Mulungu? (b) N’ciani cinakumbutsa Aisiraeli kuti Mulungu ni woyela? (Onani cithunzi pacikuto.)

6 Pambuyo pakuti Mose watsogolela Aisiraeli kuoloka Nyanja Yofiila, iye anagogomeza kwa iwo kuti Yehova Mulungu, ni woyela. (Ŵelengani Ekisodo 15:1, 11.) Aiguputo amene anali kulambila milungu yonyenga sanali oyela. Zinalinso cimodzimodzi na anthu olambila milungu ya Akanani. Kulambila kwawo kunaphatikizapo kupeleka ana nsembe, na khalidwe lonyansa la ciwelewele. (Lev. 18:3, 4, 21-24; Deut. 18:9, 10) Mosiyana na zimenezi, Yehova sanalole alambili ake kucita ciliconse codetsa. Iye ni gwelo la ciyelo. Izi zinaonekela bwino pa mawu amene analembedwa pa kacitsulo kagolide pa nduwila ya mkulu wa ansembe. Pa kacitsuloko panali polemba kuti, “Ciyelo n’ca Yehova.”—Eks. 28:36-38.

7 Uthenga wolembedwa pa kacitsuloko, unatsimikizila aliyense kuti Yehova alidi woyela. Nanga bwanji za Mwisiraeli amene sakanakwanitsa kuona kacitsuloko, cifukwa analibe mwayi woyandikila mkulu wa ansembe? Kodi akanauphonya uthenga wofunika umenewo? Ayi! Mwisiraeli aliyense anamvela uthengawo pamene Cilamulo cinali kuŵelengedwa kwa amuna, akazi, na ŵana. (Deut. 31:9-12) Mukanakhalako panthawiyo, mukanamvela mawu aya akuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu. . . . Muzikhala oyela, cifukwa ine ndine woyela.” “Mukhale oyela kwa ine, cifukwa ine Yehova ndine woyela.”—Lev. 11:44, 45; 20:7, 26.

8. Tiphunzilapo ciani pa Levitiko 19:2, komanso pa 1 Petulo 1:14-16?

8 Tiyeni tikambilane mawu apa Levitiko 19:2, amene anaŵelengedwa kwa Aisiraeli. Yehova anauza Mose kuti: “Uza khamu lonse la ana a Isiraeli kuti, ‘Mukhale oyela, cifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyela.’” Petulo ayenela kuti anagwila mawu vesi limeneli polimbikitsa Akhristu kuti ‘akhale oyela.’ (Ŵelengani 1 Petulo 1:14-16.) N’zoona kuti ife sitili pansi pa Cilamulo ca Mose. Ngakhale n’conco, malinga na Levitiko 19:2 zimene Petulo analemba zimatsimikizila kuti Yehova ni woyela, komanso kuti amene amam’konda ayenela kuyesetsa kukhala oyela. Mfundo imeneyi ni yoona, kaya ciyembekezo cathu n’cakumwamba kapena padziko lapansi.—1 Pet. 1:4; 2 Pet. 3:13.

“KHALANI OYELA M’MAKHALIDWE ANU ONSE”

9. Kodi tidzapindula bwanji na malangizo apa Levitiko caputala 19?

9 Popeza timafuna kukondweletsa Mulungu wathu woyela, timafunitsitsa kudziŵa mmene tingakhalile oyela. Yehova amatipatsa malangizo othandiza mmene tingakhalile oyela. Malangizowo timawapeza m’buku la Levitiko caputala 19. Katswili wina wa Ciheberi dzina lake Marcus Kalisch anati: “Caputala cimeneci mwina ndico cofunika kwambili, ndiponso cothandiza kwambili m’buku la Levitiko komanso pa mabuku asanu oyambilila a m’Baibo.” Tiyeni tioneko mavesi ena a caputala cimeneci, amene maphunzilo ake amatithandiza kukhala oyela pa umoyo wathu wa tsiku na tsiku. Pamene tikutelo, tikumbukile kuti Levitiko caputala 19 ciyamba na langizo lakuti, “Mukhale oyela.”

Kodi lamulo lokamba za kulemekeza makolo la pa Levitiko 19:3, liyenela kulimbikitsa Akhristu kucita ciani? (Onani ndime 10-12) *

10-11. Kodi Levitiko 19:3 imati tiyenela kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani kucita zimenezo n’kofunika?

10 Atauza Aisiraeli kuti azikhala oyela, Yehova anaonjezela kuti: “Aliyense wa inu aziopa mayi ndi bambo ake . . . Ine ndine Yehova Mulungu wanu.”—Lev. 19:2, 3.

11 N’zoonekelatu kuti tiyenela kumvela lamulo la Yehova lakuti tizilemekeza makolo athu. Kumbukilani zimene mwamuna wina anafunsa Yesu kuti: “N’ciani cabwino cimene ndiyenela kucita kuti ndikapeze moyo wosatha?” Poyankha, Yesu anauza munthuyo kuti anayenela kulemekeza atate ake na amayi ake. (Mat. 19:16-19) Yesu anadzudzula ngakhale Afarisi na alembi cifukwa cosalemekeza makolo awo. Iwo ‘anasandutsa mawu a Mulungu kukhala opanda pake.’ (Mat. 15:3-6) “Mawu a Mulungu” aphatikizapo lamulo lacisanu pa Malamulo Khumi, ndiponso zimene timaŵelenga pa Levitiko 19:3. (Eks. 20:12) Dziŵaninso kuti lamulo la pa Levitiko 19:3, lakuti tizilemekeza atate na amayi athu, libwela pambuyo pa langizo lakuti, “Mukhale oyela, cifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyela.”

12. Malinga na lamulo la pa Levitiko 19:3, kodi tiyenela kudzifunsa funso liti?

12 Mogwilizana na lamulo la Yehova lakuti tizilemekeza makolo athu, tingadzifunse kuti, ‘Kodi ine nimacita motani pa mbali imeneyi?’ Ngati muona kuti simunacite zambili polemekeza makolo anu m’mbuyomu, mungafunike kuwongolela mbali zina. Simungasinthe zakumbuyo, koma mungacite zotheka pali pano kuti mucite zambili pothandiza makolo anu. Mwina mungakonze zakuti muzikhala na nthawi yambili yoceza nawo. Kapena kupeleka thandizo lokwanila kuthupi, kuuzimu, komanso kuwalimbikitsa. Mukatelo, ndiye kuti mwacita mogwilizana na Levitiko 19:3.

13. (a) Ni lamulo lina liti limene timapeza pa Levitiko 19:3? (b) Nanga tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu ca pa Luka 4:16-18?

13 Levitiko 19:3, imatiphunzitsa cina cake pa nkhani yokhala oyela. Limakamba za kusunga Sabata. Ife Akhristu sitili pansi pa Cilamulo. N’cifukwa cake sitisunga Sabata mlungu uliwonse. Ngakhale n’telo, tingaphunzile zambili poona mmene Aisiraeli anali kusungila Sabata, ndiponso mmene anali kupindulila akacita zimenezo. Sabata inali nthawi yopumula ku nchito za kuthupi, kuti munthu asumike maganizo ake pa zauzimu. * Ndiye cifukwa cake, pa tsikuli Yesu anali kupita ku sunagoge m’tauni ya kwawo kukaŵelenga Mawu a Mulungu. (Eks. 31:12-15; ŵelengani Luka 4:16-18.) Lamulo la Mulungu la pa Levitiko 19:3 la ‘kusunga masabata,’ liyenela kutipangitsa kupatula nthawi ku zocita zathu za tsiku na tsiku, kuti tikhale na nthawi yoculuka yocita zauzimu. Kodi muona kuti muyenela kuwongolela pa mbali imeneyi? Nthawi zonse mukamapatula nthawi yocita zauzimu, mudzakhala pa ubale wolimba na Yehova, umene ni wofunika ngako kuti mukhale woyela.

LIMBITSANI UBALE WANU NA YEHOVA

14. Kodi Levitiko caputala 19 imatsindika mfundo iti ya coonadi?

14 Levitiko caputala 19, imatsindika mfundo ya coonadi imene ingatithandize kukhalabe oyela. Vesi 4 imatsiliza na mawu akuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu.” Mawuwa kapena ofanana nawo amapezeka nthawi 16 m’caputala cimeneci. Ndipo izi zimatikumbutsa lamulo loyamba lakuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu . . . Usakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine.” (Eks. 20:2, 3) Mkhristu amene afuna kukhala woyela, sayenela kuona cinthu ciliconse kapena munthu aliyense kukhala wofunika kwambili kuposa ubale wake na Mulungu. Ndipo cifukwa timadziŵika kuti Mboni za Yehova, timayesetsa kupewa kucita zinthu zimene zinganyozetse kapena kuipitsa dzina lake loyela.—Lev. 19:12; Yes. 57:15.

15. Kodi mavesi ena a m’buku la Levitiko caputala 19 okamba za kupeleka nsembe, ayenela kutilimbikitsa kucita ciani?

15 Aisiraeli anayenela kusunga malamulo poonetsa kuti Yehova ni Mulungu wawo. Levitiko 18:4 imati: “Muzisunga zigamulo zanga ndi kutsatila mfundo zanga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.” Caputala 19, cimachula zina mwa mfundozo. Mwacitsanzo, mavesi 5-8, 21, 22 amakamba za kupeleka nsembe za nyama. Nsembezo zinayenela kupelekedwa m’njila yakuti ‘zisaipitse cinthu copatulika ca Yehova.’ Kuŵelenga mavesi amenewa kuyenela kutilimbikitsa kukokondweletsa Yehova, komanso kupeleka nsembe zacitamando zovomelezeka, monga mmene Aheberi 13:15 imatilimbikitsila.

16. Ni mfundo iti yoonetsa kusiyana pakati pa anthu otumikila Mulungu na amene sam’tumikila?

16 Kuti tikhale oyela, tiyenela kukhala osiyana kothelatu na ŵanthu a m’dzikoli. Kucita izi kungakhale kovuta. Nthawi zina, anzathu a kusukulu, a kunchito, acibale athu amene si Mboni, komanso anthu ena angatikakamize kuti ticite nawo zinthu zimene zingaipitse kulambila kwathu. Zikakhala conco, tiyenela kupanga cisankho cofunika kwambili. N’ciani cingatithandize kupanga cisankho canzelu? Onani mfundo iyi yocititsa cidwi ya pa Levitiko 19:19, imene mbali yake imati: “Musamavale covala ca ulusi wa mitundu iŵili yosakaniza.” Lamulo limeneli linathandiza Aisiraeli kukhala osiyana na mitundu yowazungulila. Masiku ano, sitiletsa kuvala covala ca nsalu yosakaniza, monga nsalu yakotoni kusaniza na nsalu yawulu, nailoni kusakaniza na kilimpulini, yacitenje kusakaniza na polesta. Koma timapewa kukhala monga anthu amene zikhulupililo na miyambo yawo n’zosemphana na ziphunzitso za m’Baibo, olo kuti anthuwo ni anzathu a kusukulu, anzathu ocita nawo bizinesi, kapena acibale athu. N’zoona kuti timakonda acibale athu, komanso anthu anzathu. Komabe, tikabwela pa nkhani zofunika kwambili pa umoyo, timafuna kukhala osiyana nawo popeza ndife anthu a Yehova. Kucita zimenezi n’kofunika kwambili, cifukwa kukhala oyela kumafuna kuti tikhale opatulidwila Mulungu.—2 Akor. 6:14-16; 1 Pet. 4:3, 4.

Kodi Aisiraeli anatengapo phunzilo lotani pa Levitiko 19:23-25? Nanga imwe mwaphunzilapo ciani pa mavesi amenewa? (Onani ndime 17-18) *

17-18. Kodi pa Levitiko 19:23-25, tiphunzilapo mfundo yofunika yotani?

17 Mawu akuti “Ine ndine Yehova Mulungu wanu,” akanathandiza Aisiraeli kuika ubale wawo na Yehova patsogolo. Motani? Levitiko 19:23-25, imaonetsa njila imodzi imene akanacitila zimenezo. (Ŵelengani.) Ganizilani zimene mawuwa akanatanthauza kwa Aisiraeli pambuyo poloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Munthu akanabyala mtengo wa zipatso, iye sakanadya zipatso za mtengowo kwa zaka zitatu. M’caka ca cinayi, zipatsozo zinali kupatulidwa kuti akazigwilitsile nchito ku cihema ca Mulungu. Koma m’caka ca cisanu m’pamene mwini wake akanadya zipatsozo. Lamulo limeneli likanathandiza Aisiraeli kudziŵa kuti sayenela kuika zofuna zawo patsogolo. Anayenela kudalila Yehova monga Mpatsi wawo, na kuika kulambila kwake patsogolo. Iye akanaonetsetsa kuti anthu ake ali na zakudya zokwanila. Ndipo Mulungu anawalimbikitsa kupeleka mphatso moolowa manja pa cihema, cimene cinali malo olambililapo iye.

18 Lamulo la pa Levitiko 19:23-25, limatikumbutsa mawu a Yesu pa ulaliki wa pa Phili. Iye anati: “Lekani kudela nkhawa . . . kuti mudzadya ciani, kapena mudzamwa ciani.” Yesu anawonjezela kuti: “Atate wanu wakumwamba akudziŵa kuti inuyo mumafunikila zinthu zonsezi.” Mulungu adzatipatsa zosoŵa zathu, monga amacitila kwa mbalame. (Mat. 6:25, 26, 32) Timadalila Yehova cifukwa iye ni Mpatsi wathu. Ndipo mosadzionetsela timapeleka “mphatso za cifundo” pothandiza osoŵa. Cina, timapanga zopeleka kuti zicilikize zofunikila pa mpingo. Yehova amaona kuwolowa manja kotelo, ndipo adzatibwezela. (Mat. 6:2-4) Tikakhala oolowa manja, timaonetsa kuti tikuimvetsa mfundo ya pa Levitiko 19:23-25.

19. Kodi mwapindula bwanji pokambilana mavesi ena m’buku la Levitiko?

19 Takambilana mbali zocepa cabe m’buku la Levitiko caputala 19, ndipo taona mmene tingakhalile oyela mofanana na Mulungu wathu. Potengela citsanzo cake, timayesetsa ‘kukhala oyela m’makhalidwe athu onse.’ (1 Pet. 1:15) Anthu ambili amene satumikila Yehova amaona kuti tili na makhalidwe abwino. Ndipo makhalidwewo asonkhezela ena kulemekeza Mulungu. (1 Pet. 2:12) Koma pali zambili zimene tingaphunzile m’buku la Levitiko caputala 19. Nkhani yotsatila, idzafotokoza mavesi enanso m’caputala cimeneci, ndipo idzatithandiza kuona mbali zina mu umoyo wathu zimene tiyenela ‘kukhala oyela,’ monga anakambila Petulo.

NYIMBO 80 ‘Talaŵani, Muone Kuti Yehova ni Wabwino’

^ Yehova timam’konda kwambili, ndipo timafuna kum’kondweletsa. Iye ni woyela, ndipo amafuna kuti alambili ake akhale oyela. Kodi n’zotheka anthu opanda ungwilo kukhala oyela? Inde n’zotheka. Kuganizila mofatsa malangizo amene mtumwi Petulo anapatsa Akhristu anzake, komanso malamulo amene Yehova anapatsa Aisiraeli, kudzatithandiza kuona mmene tingakhalile oyela m’makhalidwe athu onse.

^ Kuti mudziŵe zambili zokhudza Sabata na zimene tiphunzilapo, onani nkhani yakuti, “‘Pali Nthawi’ Yogwila Nchito Komanso Yopumula,” mu Nsanja ya Mlonda ya December 2019.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mwana wamwamuna akuceza na makolo ake, ulendo wina wabwela na mkazi wake komanso mwana wake kudzawacezela, ndipo amayesetsa kukambilana nawo kaŵili-kaŵili pa foni.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlimi waciisiraeli akuyang’ana mtengo wa zipatso umene anabyala.