Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 49

Zimene Timaphunzila m’Buku la Levitiko pa Nkhani Yocita Zinthu na Ŵena

Zimene Timaphunzila m’Buku la Levitiko pa Nkhani Yocita Zinthu na Ŵena

“Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.”—LEV. 19:18.

NYIMBO 109 Tizikondana ndi Mtima Wonse

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi tinaphunzila ciani m’nkhani yapita? Nanga tiphunzile ciani m’nkhani ino?

 M’NKHANI yapita, tinaphunzila malangizo othandiza apa Levitiko caputala 19. Mwacitsanzo, mu vesi 3, Yehova anauza Aisiraeli kuti azilemekeza makolo awo. Tinaona mmene tingaseŵenzetsele malangizo amenewa posamalila makolo athu kuthupi, kuuzimu, komanso kuwalimbikitsa. Mu vesi imodzi-modziyo, anthu a Mulungu analamulidwa kuti azisunga Sabata. Tinaphunzila kuti ngakhale sitisunga Sabata masiku ano, tingatsatile mfundo yake mwa kupatula nthawi yocita zinthu zauzimu. Tikatelo, tidzaonetsa kuti tikuyesetsa kukhala oyela, mmene Levitiko 19:2 komanso 1 Petulo 1:15 imakambila.

2 M’nkhani ino, tipitiliza kukambilana Levitiko caputala 19. Kodi caputala cimeneci cimatiphunzitsa ciani pa nkhani yoganizila anthu olemala, kukhala oona mtima pocita malonda, komanso kuonetsa cikondi kwa anzathu? Timafuna kukhala oyela mmene Mulungu alili woyela. Conco, tiyeni tione zimene tingaphunzile m’caputula cimeneci.

KUKOMELA MTIMA ANTHU OLEMALA

Kodi Levitiko 19:14, imatilimbikitsa kucita nawo zinthu motani anthu ogontha kapena akhungu? (Onani ndime 3-5) *

3-4. Malinga n’kunena kwa Levitiko 19:14, kodi anthu ogontha komanso akhungu anayenela kucitilidwa zinthu motani?

3 Ŵelengani Levitiko 19:14. Yehova anafuna kuti anthu ake azikomela mtima olemala. Mwacitsanzo, anauza Aisiraeli kuti sayenela kutembelela munthu wogontha. Kutembelelako kunaphatikizapo kuopseza munthu kapena kum’kambila zoipa. Kucita izi kunali kum’lakwila kwambili munthu wogonthayo! Popeza sanali kumva zoipa zimene anali kum’kambila, iye sakanatha kudziteteza.

4 Cinanso, mu vesi 14 timaphunzila kuti kunali kosayenela atumiki a Mulungu ‘kuikila munthu wakhungu cinthu copunthwitsa.’ Ponena za anthu olemala, buku lina linati: “Kalelo ku Middle East, [olemala] anali kuwacitila nkhanza komanso zopanda cilungamo.” Mwina munthu wosaganizila ena anali kuika copunthwitsa kutsogolo kwa munthu wosaona cifukwa comuzonda, kapena kumupanga kukhala coseketsa. Uku kunali kupanda cifundo! Kupitila mu lamulo limeneli, Yehova anathandiza anthu ake kuona kuti ayenela kucitila cifundo anthu olemala.

5. Kodi tingawaonetse bwanji cifundo anthu olemala?

5 Yesu anali kucitila cifundo anthu olemala. Kumbukilani uthenga umene iye anatumiza kwa Yohane M’batizi. Anati: “Akhungu akuona, olumala akuyenda, akhate akuyeletsedwa, ogontha akumva, [ndipo] akufa akuukitsidwa.” Poona zozizwitsa za Yesu, ‘anthu onse anatamanda Mulungu.’ (Luka 7:20-22; 18:43) Akhristu amatengela citsanzo ca Yesu mwa kucitila cifundo anthu olemala. Conco, timakhala okoma mtima, oganizila ena, komanso oleza mtima kwa anthu otelo. N’zoona kuti Yehova sanatipatse mphamvu yocita zozizwitsa. Koma tili na mwayi wouzako anthu ali na khungu lakuthupi kapena lauzimu uthenga wabwino wokamba za paradaiso, mmene anthu adzakhala na thanzi labwino kuthupi komanso kuuzimu. (Luka 4:18) Uthenga wabwino umenewu wathandiza anthu ambili kutamanda Mulungu.

KHALANI OONA MTIMA POCITA MALONDA

6. Kodi zimene zili pa Levitiko caputala 19, zimatithandiza bwanji kumvetsa bwino Malamulo Khumi?

6 Mavesi ena mu Levitiko caputala 19, amaunika momveka bwino zimene zinakambidwa m’Malamulo Khumi. Mwacitsanzo, lamulo la nambala 8 limangokamba kuti: “Usabe.” (Eks. 20:15) Mwina munthu angaganize kuti malinga ngati sanatengepo cinthu ciliconse cimene si cake, ndiye kuti akumvela lamulo limeneli. Komabe, iye angamabe m’njila zina.

7. Kodi wamalonda angaphwanye motani lamulo la nambala 8 lokamba za kuba?

7 Munthu wamalonda anganyadile poona kuti sanatengepo cinthu cisali cake. Koma bwanji pocita malonda ake? Pa Levitiko 19:35, 36, Yehova anati: “Musamacite cinyengo poyeza utali wa cinthu, kulemela kwa cinthu kapena poyeza zinthu zamadzi. Muzikhala ndi masikelo olondola, miyala yolondola yoyezela kulemela kwa zinthu, muyezo wolondola wa efa ndi muyezo wolondola wa hini.” Conco, wamalonda amene amaseŵenzetsa sikelo yacinyengo n’colinga conamiza makasitomala ake, amakhala akuwabela. Mavesi enanso mu Levitiko caputala 19, afotokoza mfundo imeneyi momveka bwino.

Malinga na Levitiko 19:11-13, kodi Mkhristu ayenela kudzifunsa funso lotani pa malonda ake? (Onani ndime 8-10) *

8. Kodi Levitiko 19:11-13, inawathandiza bwanji Ayuda kuseŵenzetsa mfundo ya m’lamulo la nambala 8? Nanga ife tingapindule bwanji?

8 Ŵelengani Levitiko 19:11-13. Mawu oyamba pa Levitiko 19:11 amati: “Musabe.” Ndipo vesi 13, imaonetsa kuti kucita malonda mosaona mtima ni kuba. Imati: “Usabele mnzako mwacinyengo.” Conco, ngati munthu amacita malonda mwacinyengo, ndiye kuti akuba. Ngakhale kuti lamulo la nambala 8 linaletsa kuba, mfundo za m’buku la Levitiko zinali kuthandiza Ayuda kukhala oona mtima m’zinthu zonse. Nafenso tingapindule tikaganizila mmene Yehova amaonela kuba komanso kusaona mtima. Tingadzifunse kuti: ‘Malinga na Levitiko 19:11-13, kodi pali mbali zimene niyenela kuwongolela, maka-maka pa nkhani yocita malonda kapena kagwilidwe ka nchito?’

9. Kodi lamulo la pa Levitiko 19:13 linali kuthandiza bwanji aganyu?

9 Pa nkhani ya kuona mtima, palinso mbali ina imene Mkhristu amene amalemba anthu nchito ayenela kukumbukila. Levitiko 19:13 imati: “Malipilo a munthu waganyu asagone m’nyumba mwako kufikila m’maŵa.” Mu Isiraeli, munthu wogwila nchito yaganyu m’munda anali kupatsidwa malipilo ake pakutha kwa tsiku. Kusamulipila wanchito wotelo, kukanapangitsa kuti asoŵe ndalama zosamalila banja lake pa tsikulo. Yehova anati: “Iye ndi wovutika. [Ndipo] akuyembekezela malipilo akewo mwacidwi.”—Deut. 24:14, 15; Mat. 20:8.

10. Kodi titengapo phunzilo lotani pa Levitiko 19:13?

10 Masiku ano, anchito ambili amalandila malipilo awo kamodzi kapena kaŵili pa mwezi, osati tsiku lililonse. Komabe, mfundo ya pa Levitiko 19:13 ikali kugwilabe nchito. Mabwana ena amadyela masuku pa mutu anchito awo mwa kuwalandilitsa ndalama yocepa yosayendelana na nchito imene amagwila. Iwo amadziŵa kuti anchito awo kulibe kumene angapite, koma azigwilabe nchitoyo ngakhale alandile malipilo ocepa. M’mawu ena tingati, mabwana otelo ‘akugoneka malipilo a anchito awo.’ Mkhristu amene amalemba anthu nchito ayenela kukumbukila mfundo imeneyi. Tiyeni tionenso cina cimene tingaphunzile pa Levitiko caputala 19.

TIZIKONDA ANZATHU MMENE TIMADZIKONDELA TOKHA

11-12. Kodi Yesu anali kugogomeza mfundo yotani pogwila mawu Levitiko 19:17, 18?

11 Mulungu samangofuna kuti tizipewa kucita zinthu zopweteka ena. Timaona zimenezi pa Levitiko 19:17, 18. (Ŵelengani.) Onani lamulo lomveka bwino ili lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” Kucita zimenezi n’kofunika kwambili kwa Mkhristu amene afuna kukondweletsa Mulungu.

12 Onani mmene Yesu anagogomezela kufunika kwa lamulo la pa Levitiko 19:18. Mfarisi wina anafunsa Yesu kuti: “Kodi lamulo lalikulu kwambili m’Cilamulo ndi liti?” Yesu anamuyankha kuti “lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba,” ni kukonda Yehova Mulungu na mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, komanso maganizo athu onse. Ndiyeno Yesu anagwila mawu Levitiko 19:18, imene imati: “Laciŵili lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’” (Mat. 22:35-40) Pali njila zambili zoonetsela cikondi kwa anzathu, ndipo zina mwa izo zimachulidwa pa Levitiko caputala 19.

13. Kodi nkhani ya m’Baibo ya Yosefe, imaonetsa motani mfundo imene inadzalembedwa pa Levitiko 19:18?

13 Njila ina imene tingaonetsele cikondi kwa anzathu, ni kuseŵenzetsa langizo la pa Levitiko 19:18 lakuti: ‘Usabwezele coipa kapena kusunga cakukhosi.’ Ambili a ife timadziŵako anthu amene anasungila cakukhosi mnzawo wa kunchito, kusukulu, wacibale, kapena wa m’banja mwawo, mwina kwa zaka. Kumbukilani kuti abale ake 10 a Yosefe anamusungila cakukhosi. Ndipo izi zinawafikitsa pa kum’citila coipa. (Gen. 37:2-8, 25-28) Koma Yosefe anacita zinthu mosiyana na iwo. Ataikidwa pa udindo, sanabwezele coipa kwa abale ake, koma anawacitila cifundo. Iye sanasunge cakukhosi. M’malo mwake, anacita zinthu mogwilizana na lamulo limene linadzalembedwa pa Levitiko 19:18.—Gen. 50:19-21.

14. N’ciani cionetsa kuti mfundo za m’lamulo la pa Levitiko 19:18, zikali kugwilabe nchito masiku ano?

14 Citsanzo ca Yosefe ca kukhululuka m’malo mosunga cakukhosi kapena kubwezela, n’cothandiza kwambili kwa Akhristu amene afuna kukondweletsa Mulungu. N’cogwilizana na zimene Yesu anakamba m’pemphelo lake lacitsanzo, pamene anati tizikhululukila amene atilakwila. (Mat. 6:9, 12) Mofananamo, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Okondedwa, musabwezele coipa.” (Aroma 12:19) Anawalimbikitsanso kuti: “Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake.” (Akol. 3:13) Mfundo za Yehova sizisintha. Mfundo za m’lamulo la pa Levitiko 19:18, zikali kugwilabe nchito masiku ano.

Monga mmene timapewela kumangonyaula pa cilonda, tiyenelanso kupewa kumangoganizila zimene wina anatilakwila. Tizikhululuka na kuiŵalako (Onani ndime 15) *

15. N’citsanzo citi cingatithandize kuona kufunika kokhululuka na kuiŵalako?

15 Ganizilani citsanzo ici. Kukhumudwa tingakuyelekezele na cilonda. Zilonda zina zimakhala zazing’ono, koma zina zimakhala zazikulu. Mwacitsanzo, tikamadula ndiwo zamasamba, mwina tingadziceke ku cala. Timamva ululu kwambili, koma ululu umenewo umatha ndipo timacila. Pakapita masiku, mwina sitingakumbukile pomwe tinadziceka. Mofananamo, zolakwa zina zimakhala zazing’ono. Mwacitsanzo, mnzathu angatikhumudwitse m’mawu kapena m’zocita, ndipo tingam’khululukile mosavuta. Koma ngati tili na cilonda cacikulu, dokotala angafunike kusoka cilondaco na kumangapo. Ngati timangokhalila kunyaula pa cilondapo, tingangopangitsa kuti cisapole. Munthu angacite zofanana na zimenezi wina akamukhumudwitsa kwambili. Nthawi zonse iye angamaganizile mmene wina anam’khumudwitsila. Telo anthu amene amasunga cakukhosi amadzipweteka okha. Conco, ni bwino kutsatila malangizo apa Levitiko 19:18.

16. Mogwilizana na Levitiko 19:33, 34, kodi alendo ku Isiraeli anayenela kucitilidwa zinthu motani? Nanga ife tiphunzilapo ciani?

16 Pamene Yehova anauza Aisiraeli kuti ayenela kukonda anzawo, sanatanthauze kuti azikonda cabe anthu a mtundu wawo okha. Iye anawauzanso kuti azikonda alendo okhala pakati pawo. Malangizo omveka bwino amenewa apezeka pa Levitiko 19:33, 34. (Ŵelengani.) Mlendo anayenela kuonedwa “ngati mbadwa,” ndipo Aisiraeli anayenela ‘kum’konda’ mmene anali kudzikondela okha. Mwacitsanzo, Aisiraeli anayenela kulola alendo komanso osauka kupindula na makonzedwe a kukunkha. (Lev. 19:9, 10) Mfundo yokamba za kukonda alendo igwilanso nchito kwa Akhristu masiku ano. (Luka 10:30-37) Motani? Pali anthu mamiliyoni amene anasamukila ku maiko ena, ndipo mwina ena a iwo amakhala kufupi na kwanu. N’kofunika kwambili kucita nawo zinthu mwaulemu anthu amenewo.

NCHITO YOFUNIKA NGAKO IMENE SINACHULIDWE PA LEVITIKO 19

17-18. (a) Kodi pa Levitiko 19:2 komanso pa 1 Petulo 1:15, pamatilimbikitsa kucita ciani? (b) Nanga ni nchito yofunika iti imene mtumwi Petulo anatilimbikitsa kugwila?

17 Pa Levitiko 19:2 komanso pa 1 Petulo 1:15, pamalimbikitsa anthu a Mulungu kukhala oyela. Mavesi enanso mu Levitiko caputala 19, angatithandize kuona zimene tingacite kuti Yehova atiyanje. Takambilanako mavesi amene amafotokoza zinthu zina zimene tiyenela kucita, komanso zimene tiyenela kupewa. * Malemba Acigiliki Acikristu amaonetsa kufunika kotsatila zimenezo. Komabe, mtumwi Petulo anakambanso cinthu cina.

18 Tingakhale kuti timacita zinthu zonse zauzimu, komanso kucitila ena zabwino. Koma Petulo anatilimbikitsa kucita cinthu cina cofunika kwambili. Iye asanatilimbikitse kukhala oyela m’makhalidwe athu onse, anati: “Konzekeletsani maganizo anu kuti mugwile nchito mwamphamvu.” (1 Pet. 1:13, 15) Kodi nchito imeneyi ni iti? Petulo anati abale a Khristu odzozedwa anali ‘kudzalengeza makhalidwe abwino kwambili’ a uyo amene anawaitana. (1 Pet. 2:9) Akhristu onse lelo lino, ali na mwayi wogwila nchito yofunika kwambili imeneyi, imene imathandiza anthu kwambili. Monga anthu oyela, ulidi mwayi wapadela kutengako mbali mokangalika pa nchito yolalikila na kuphunzitsa. (Maliko 13:10) Tikamacita zonse zotheka kutsatila mfundo za pa Levitiko caputala 19, timaonetsa kuti timakonda Mulungu komanso anzathu. Timaonetsanso kuti timafuna ‘kukhala oyela’ m’makhalidwe athu onse.

NYIMBO 111 Zifukwa Zokhalila Acimwemwe

^ Akhristu sali pansi pa Cilamulo ca Mose. Komabe, cilamuloco cimachula zinthu zambili zimene tiyenela kucita komanso kupewa. Kudziŵa zinthuzo kudzatithandiza kukonda anthu, na kukondweletsa Mulungu. Nkhani ino, ifotokoza mmene tingapindulile na maphunzilo amene titengamo m’buku la Levitiko caputala 19.

^ M’nkhani ino komanso yapita, sitinakambilane mavesi okamba za kukondela, kukambila ena misece, kudya magazi, kucita zamizimu, kuwomboza, komanso zaciwelewele.—Lev. 19:15, 16, 26-29, 31.—Onani “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” m’magazini ino.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mboni ikuthandiza m’bale wogontha kukambilana na dokotala.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale amene ali na kampani ya zopentapenta, akulandilitsa wanchito malipilo ake.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo angaiŵaleko mosavuta za kacilonda kakang’ono. Kodi sizingatheke kucitanso cimodzi-modzi na cilonda cacikulu?