Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Kodi lamulo la pa Levitiko 19:16, lakuti “usacite kanthu kalikonse kuti uphetse mnzako” litanthauza ciani? Nanga tiphunzilapo ciani?

Yehova anauza Aisiraeli kuti ayenela kukhala oyela. Kuti akhale oyela, iye anawauza kuti: “Usamayendeyende pakati pa anthu amtundu wako n’kumacita misece. Usacite kanthu kalikonse kuti uphetse mnzako. Ine ndine Yehova.”—Lev. 9:2, 16.

Mawu akuti “usacite kanthu kalikonse,” ndiwo amamasulila bwino mawu oyambilila a Ciheberi. Koma kodi mawuwa atanthauza ciani? Pokamba za buku la Levitiko, buku lina la Ciyuda linati: “Mbali ya vesili ni . . . yovuta kuimvetsetsa, cifukwa n’covuta kudziŵa lingalilo lenileni la mawu aciheberi, amene kwenikweni [pa vesili] atanthauza ‘kusaima pafupi.’”

Akatswili ena a Baibo amagwilizanitsa mawuwa na vesi 15, imene imati: “Musamaweluze mopanda cilungamo. Musamakondele munthu wosauka, ndiponso musamakondele munthu wolemela. Mnzako uzimuweluza mwacilungamo.” (Lev. 19:15) Conco, lamulo la pa vesi 16, lakuti usacite kanthu kalikonse kwa mnzako, lingatanthauze kuti anthu a Mulungu sanafunike kupweteka anzawo poweluza mlandu kukhoti, pocita malonda, kapena pa nkhani za banja. Komanso, sanafunike kucita zinthu mwacinyengo kuti iwo apeze phindu. N’zoona kuti tiyenela kupewa kucita zimenezi. Koma pali njila yosavuta yomvetsa bwino mawu apa vesi 16.

Pa mawu oyambilila pa vesi imeneyi, Mulungu analamula anthu ake kuti asamayendeyende n’kufalitsa misece. Kumbukilani kuti misece imasiyana na mijedo, ngakhale kuti mijedo nayonso ingayambitse mavuto. (Miy. 10:19; Mlal. 10:12-14; 1 Tim. 5:11-15; Yak. 3:6) Kambili, misece imakhala bodza limene wina mwadala angakambe pofuna kuipitsa mbili ya munthu wina. Iye angapeleke umboni wabodza ponena za munthu wina, ngakhale kuti kucita zimenezi kungaike moyo wa munthuyo pa ciwopsezo. Kumbukilani kuti anthu olankhula misece anam’kambila zoipa Naboti, zimene zinapangitsa kuti iye aweluzidwe mopanda cilungamo mwa kuponyedwa miyala. (1 Maf. 21:8-13) Inde, munthu wamisece angacite kanthu kalikonse pofuna kuwonongetsa moyo wa mnzake, monga mmene mbali yaciŵili pa Levitiko 19:16 imakambila.

Kuwonjezela apo, bodza lamkunkhuniza lingaonetse kukula kwa cidani cimene munthu ali naco pa mnzake. Pa 1 Yohane 3:15 timaŵelenga kuti: “Aliyense amene amadana ndi m’bale wake ndi wopha munthu, ndipo mukudziŵa kuti aliyense wopha munthu sadzalandila moyo wosatha.” N’zocititsa cidwi kuti Mulungu pambuyo pokamba mawu apa vesi 16, anawonjezela kuti: “Usadane ndi m’bale wako mumtima mwako.”—Lev. 19:17.

Conco, lamulo locititsa cidwi la pa Levitiko 19:16, limapeleka uphungu wamphamvu kwa Akhristu. Tiyenela kukaniza maganizo alionse oipa, komanso kupewa kukambila mnzathu misece. Mwacidule tinganene kuti, ngati ‘ticita kanthu kalikonse’ kwa mnzathu mwa kum’kambila misece cifukwa comuzonda kapena com’citila kaduka, ndiye kuti tikumuda munthuyo. Akhristu ayenela kupewelatu khalidwe loipali.—Mat. 12:36, 37.