Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndinu Wogwira Naye Ntchito Wabwino?

Kodi Ndinu Wogwira Naye Ntchito Wabwino?

“INE ndinali pambali pake monga mmisiri waluso. . . . Ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.” (Miy. 8:30) Umu ndi mmene Baibulo limafotokozera zokhudza Mwana wa Mulungu pa nthawi imene anakhala akugwira ntchito ndi Atate ake zaka zambirimbiri asanabwere padzikoli. Tikuona kuti lembali likufotokozanso mmene Yesu ankamvera monga wogwira ntchito ndi Mulungu. Iye ‘ankasangalala’ pamaso pake.

Yesu anaphunzira kwa Atate wake makhalidwe amene anamuthandiza kuti akhale wogwira naye ntchito wabwino atabwera padzikoli. Kodi chitsanzo cha Yesu chingatithandize bwanji? Kuganizira chitsanzo chake, kungatithandize kupeza mfundo zitatu zomwe zingachititse kuti tikhale anthu abwino kugwira nawo ntchito. Mfundo zimenezi zidzatithandiza kuti tizigwirizana kwambiri ndi abale athu.

Poganizira chitsanzo cha Yehova ndi Yesu, tiyenera kukhala okonzeka kuuzako antchito anzathu zimene tikudziwa

MFUNDO 1: ‘MUZISONYEZANA ULEMU’

Munthu wogwira naye ntchito wabwino amakhala wodzichepetsa ndipo sachita zinthu modzionetsera koma amaona kuti anzake ndi ofunika kwambiri. Yesu anaphunzira khalidwe lodzichepetsali kwa a Atate ake. Ngakhale kuti Yehova yekha ndi amene amatchedwa Mlengi, iye anafuna kuti ena adziwe ntchito yofunika kwambiri imene Mwana wake anagwira. Timamvetsa mfundo imeneyi pa mawu amene Mulungu analankhula akuti: “Tiyeni tipange munthu m’chifaniziro chathu.” (Gen. 1:26) N’zachidziwikire kuti ndi mawu amenewa Yesu anaona kuti Yehova ndi wodzichepetsa kwambiri.​—Sal. 18:35.

Ali padziko lapansili, Yesu nayenso anali wodzichepetsa. Anthu akamutamanda chifukwa cha zimene wachita, iye ankapereka ulemerero kwa Mulungu. (Maliko 10:17, 18; Yoh. 7:15, 16) Yesu ankakhala mwamtendere ndi ophunzira ake ndipo ankawaona ngati anzake osati akapolo. (Yoh. 15:15) Iye anafika powasambitsa mapazi pofuna kuwaphunzitsa khalidwe la kudzichepetsa. (Yoh. 13:5, 12-14) Ifenso tingachite bwino kumalemekeza antchito anzathu n’kumaika patsogolo zofuna zawo m’malo mwa zofuna zathu. ‘Tikamasonyezana ulemu’ popanda kuganizira kuti ndi ndani amene atamandidwe, tingakwanitse kuchita zambiri.​—Aroma 12:10.

Munthu wodzichepetsa amazindikiranso kuti “aphungu akachuluka [zolingalira] zimakwaniritsidwa.” (Miy. 15:22) Choncho kaya timadziwa zinthu zochuluka bwanji kapena tili ndi luso lotani, tizikumbukira kuti palibe munthu amene amadziwa zonse. Ngakhale Yesu anavomereza kuti panali zinthu zina zomwe sankadziwa. (Mat. 24:36) Iye ankachitanso chidwi ndi zimene ophunzira ake omwe sanali angwiro ankadziwa komanso kuganiza. (Mat. 16:13-16) N’chifukwa chake antchito anzakewa ankamasuka naye. Mofanana ndi zimenezi, tikamadzichepetsa n’kumazindikira zinthu zomwe sitingakwanitse kuchita komanso kulola kuti ena apereke maganizo awo, tikhoza kumakhala nawo mwamtendere ndipo tonse pamodzi ‘tingakwaniritse’ zinthu zambiri.

N’zofunika kwambiri kuti akulu azitsanzira Yesu pa nkhaniyi akamagwira ntchito limodzi. Iwo ayenera kukumbukira kuti mzimu woyera ungachititse mkulu aliyense kulankhula zinthu zimene zingathandize bungwe lonse kusankha zochita mwanzeru. Ngati akulu amayesetsa kuchita zinthu mwamtendere pa zokambirana zawo, aliyense angakhale womasuka kuperekapo maganizo ake zomwe zingachititse kuti asankhe zinthu zimene zingathandize mpingo wonse.

MFUNDO 2: “ANTHU ONSE ADZIWE KUTI NDINU OLOLERA”

Wogwira naye ntchito wabwino ayenera kukhala wololera akamagwira ntchito ndi ena. Iye sayenera kukhala wokhwimitsa zinthu. N’zodziwikiratu kuti Yesu anali ndi mipata yambiri yoona Atate ake akusonyeza khalidwe la kulolera. Mwachitsanzo, Yehova anamutumiza kuti adzawombole anthu ku chilango cha imfa chimene anapatsidwa.​—Yoh. 3:16.

Yesu ankachita zinthu mololera ngati pakufunika kutero. Kumbukirani mmene anachitira zinthu ndi mayi wa ku Foinike ngakhale kuti anali atatumidwa kwa Aisiraeli. (Mat. 15:22-28) Iye ankasonyezanso khalidweli akamachita zinthu ndi ophunzira ake. Mnzake wapamtima Petulo atamukana pamaso pa anthu, Yesu anali wokonzeka kumukhululukira ndipo pambuyo pake anamupatsa maudindo akuluakulu. (Luka 22:32; Yoh. 21:17; Mac. 2:14; 8:14-17; 10:44, 45) Chitsanzo cha Yesu chikusonyeza kuti tiyenera kuthandiza ‘anthu onse kuti adziwe kuti ndife ololera.’​—Afil. 4:5.

Kukhala ololera kungatichititse kuti tizisintha zinthu n’kumagwira ntchito mogwirizana ndi anthu osiyanasiyana. Yesu ankachita bwino zinthu ndi anthu omwe ankamvetsera uthenga wake moti adani ake omwe ankamuchitira nsanje ankamunena kuti “bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa.” (Mat. 11:19) Mofanana ndi Yesu, kodi ifenso tikhoza kukwanitsa kuchita zinthu ndi anthu omwe amasiyana nafe pa zinthu zina? M’bale wina dzina lake Louis, yemwe wakhala akutumikira monga woyang’anira dera komanso pabeteli, wakhala akugwira ntchito ndi anthu osiyanasiyana. Iye anati: “Ndimayerekezera anthu osiyanasiyana omwe ndimagwira nawo ntchito ndi khoma la mpanda womangidwa ndi miyala. Ukamasuntha mwala uliwonse kuti ugwirizane ndi unzake ungamange mpanda woongoka. Choncho inenso ndimasintha zina ndi zina kuti ndithandizire kuti mpandawu ukhale woongoka.” Amenewatu ndi maganizo abwino.

Munthu wogwira naye ntchito wabwino sayesa kubisa mfundo zothandiza zimene akudziwa pongofuna kukhalabe ndi udindo

Kodi ndi pa nthawi iti pamene tingasonyeze mtima wololera mumpingo mwathu? Tingasonyeze mtima umenewu tikamachita zinthu ndi kagulu kathu ka utumiki. N’kutheka kuti tikhoza kuyenda mu utumiki ndi ofalitsa amene ali maudindo osiyana ndi athu pa nkhani yosamalira banja kapena omwe timasiyana nawo misinkhu. Ndiye kodi tingasinthe mmene tikuchitira zinthu n’cholinga choti iwo asangalale ndi utumiki?

MFUNDO 3: MUZIKHALA “OKONZEKA KUGAWIRA ENA”

Wogwira naye ntchito wabwino ayenera kukhala wokonzeka “kugawira ena” zimene akudziwa. (1 Tim. 6:18) Pamene ankagwira ntchito ndi Atate ake, Yesu ayenera kuti anaona kuti iwo sankamubisira zinthu. Pamene ‘ankakonza kumwamba,’ Yesu ‘anali pomwepo’ ndipo ankaphunzira kwa iwo. (Miy. 8:27) Patapita nthawi, Yesu anasangalala kuphunzitsa otsatira ake “zinthu zimene anamva” kwa Atate ake. (Yoh. 15:15) Poganizira chitsanzo chimenechi ifenso tiyenera kukhala okonzeka kugawira antchito anzathu zimene tikudziwa. Munthu wogwira naye ntchito wabwino sayesa kubisira ena zimene akudziwa pongofuna kukhalabe ndi udindo. Iye amasangalala kuuzako ena zinthu zabwino zimene waphunzira.

Tikhozanso kulankhula mawu olimbikitsa kwa antchito anzathu. Kodi sitimamva bwino munthu wina akaona khama lathu n’kutiyamikira mochokera pansi pamtima? Yesu ankapeza nthawi yowauza antchito anzake zinthu zabwino zimene waona mwa iwo. (Yerekezerani ndi Mateyu 25:19-23; Luka 10:17-20.) Anafika powauza kuti “adzachita ntchito zazikulu kuposa” iye. (Yoh. 14:12) Pa usiku wake womaliza iye anayamikira atumwi ake powauza kuti: “Inu mwakhalabe ndi ine m’mayesero anga.” (Luka 22:28) Tangoganizani mmene mawu amenewa anakhudzira mtima ophunzirawo komanso kuwalimbikitsa. Ifenso tikamayamikira antchito anzathu iwo adzakhala osangalala komanso adzachita zambiri.

MUNGATHE KUKHALA MUNTHU WABWINO KUGWIRA NAYE NTCHITO

M’bale wina dzina lake Kayode ananena kuti: “Sikuti wogwira naye ntchito wabwino amachita kufunika kukhala wabwino pa chilichonse. M’malo mwake iye amachititsa kuti onse omwe akugwira naye ntchito azisangalala komanso asamaone kuti ntchitoyo ndi yolemetsa.” Kodi ndi mmene inuyo mulili? Bwanji osafunsa Akhristu anzanu mmene amakuonerani pa nkhani imeneyi. Ngati amasangalala kugwira nanu ntchito monganso mmene ophunzira a Yesu ankasangalalira kugwira naye ntchito, munganene mofanana ndi mtumwi Paulo kuti: “Ndife antchito anzanu kuti mukhale ndi chimwemwe.”​—2 Akor. 1:24.