Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 50

Mvelani Mawu a M’busa Wabwino

Mvelani Mawu a M’busa Wabwino

“Zidzamva mawu anga.”—YOH. 10:16.

NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciani Yesu anayelekezela otsatila ake na nkhosa?

 YESU anayelekezela ubale wake ndi otsatila ake, na mgwilizano umene umakhalapo pakati pa m’busa na nkhosa zake. (Yoh. 10:14) Mpake kuyelekezela mwa njila imeneyo, cifukwa nkhosa zimadziŵa m’busa wawo, komanso kumvetsela mawu ake. Munthu wina wa paulendo anadzionela yekha zimenezi. Iye anati: “Tinali kufuna kujambula nkhosa. Conco, tinayamba kuziitana kuti zibwele pafupi nafe. Koma nkhosazo sizinabwele pafupi cifukwa sizinali kudziŵa mawu athu. Kenako, panafika m’busa wacicepele. Iye ataziitana, nkhosazo zinayamba kumutsatila.”

2-3. (a) Kodi otsatila a Yesu amaonetsa bwanji kuti amamvela mawu ake? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino komanso yotsatila?

2 Cocitika ca munthu wa paulendoyo citikumbutsa mawu a Yesu onena za nkhosa zake, kutanthauza ophunzila ake. Iye anati: “Zidzamva mawu anga.” (Yoh. 10:16) Popeza Yesu ali kumwamba, kodi tingamvele bwanji mawu ake? Njila yaikulu imene timaonetsela kuti timamvela mawu a Mbuye wathu, ni kucita zimene iye anatiphunzitsa.—Mat. 7:24, 25.

3 M’nkhani ino komanso yotsatila, tidzakambilana zina mwa zimene Yesu anaphunzitsa. Monga tionele, Yesu anatiphunzitsa zimene tiyenela kuleka kucita, komanso zimene tiyenela kucita. Coyambilila, tikambilane zinthu ziŵili zimene m’busa wabwinoyo anatilamula kuti tisamacite.

“SIYANI KUVUTIKA MUMTIMA”

4. Malinga n’kunena kwa Luka 12:29, n’ciani cingapangitse munthu “kuvutika mumtima”?

4 Ŵelengani Luka 12:29. Yesu analangiza otsatila ake kuti ‘asiye kuvutika mumtima,’ cifukwa cosoŵa zofunikila zakuthupi. Timadziŵa kuti nthawi zonse malangizo a Yesu ni abwino, komanso othandiza. Timafuna kuyaseŵenzetsa, koma nthawi zina cimakhala covuta kucita zimenezi. Cifukwa ciani?

5. N’cifukwa ciani ena amadela nkhawa zosoŵa zawo zakuthupi?

 5 Ena amadela nkhawa zofunikila zakuthupi monga cakudya, zovala, komanso nyumba, cifukwa angamakhale m’dziko limene muli mavuto azacuma. Conco, cingakhale covuta kwa iwo kupeza ndalama zokwanila zosamalila banja lawo. Kapena wosamalila banjalo angamwalile, n’kusiya banja lonse pamavuto popanda wolisamalila. Cina, ena nchito ingathe cifukwa ca mlili wa COVID-19. (Mlal. 9:11) Ngati takumanako na mavuto amenewa kapena ena alionse, kodi tingatsatile bwanji mawu a Yesu akuti lekani kudela nkhawa?

M’malo momila m’nkhawa ya zinthu zakuthupi mophiphilitsa, limbitsani cidalilo canu mwa Yehova (Onani ndime 6-8) *

6. Fotokozani zinacitika kwa mtumwi Petulo pa nthawi ina.

6 Pa nthawi ina, mtumwi Petulo na atumwi ena anali m’boti panyanja ya Galileya. Mphepo yamkhuntho itayamba kuwomba, iwo anaona Yesu akuyenda pamadzi. Petulo anati: “Ambuye, ngati ndinudi, ndiuzeni ndiyende pamadzipa ndibwele kuli inuko.” Yesu atamuuza kuti ‘bwela,’ Petulo anatsika m’botimo “n’kuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu.” Onani zimene zinacitika. Iye “ataona mphepo yamkuntho, anacita mantha, ndipo atayamba kumila anafuula kuti: ‘Ambuye, ndipulumutseni!’” Yesu anatambasula dzanja lake na kumupulumutsa. Petulo akanapitiliza kuyang’ana Yesu, akanakwanitsa kuyenda pamadzi amphamvu amenewo. Koma cifukwa coyang’ana cimphepoco, iye anacita mantha ndipo anakayikila. Kenako, anayamba kumila.—Mat. 14:24-31.

7. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Petulo?

7 Tingapindule na citsanzo ca Petulo. Iye atatsika m’boti na kuyenda pamadzi, sanadziŵe kuti zinthu zina zidzamuceutsa n’kuyamba kumila. Anali kufuna kupitiliza kuyenda pamadzipo mpaka atafika kwa Mbuye wake. Koma analephela kulunjikitsa maganizo ake pa colinga cakeco. N’zoona kuti sitingayende pamadzi, koma timakumana na mavuto oika cikhulupililo cathu pamayeso. Tikalephela kusumika maganizo athu pa Yehova na malonjezo ake, tidzayamba kumila mwauzimu. Kaya tikumane na mphepo yophiphilitsa yotani, tiyenela kupitiliza kusumika maganizo athu pa Yehova, komanso thandizo lake. Tingacite bwanji zimenezi?

8. N’ciani cingatithandize kusadela nkhawa kwambili zosoŵa zathu zakuthupi?

8 M’malo modela nkhawa za mavuto athu, tiyenela kudalila Yehova. Kumbukilani kuti Atate wathu wacikondi Yehova, analonjeza kuti adzatisamalila pa zakuthupi tikaika zauzimu patsogolo. (Mat. 6:32, 33) Iye nthawi zonse amakwanilitsa lonjezo lake limeneli. (Deut. 8:4, 15, 16; Sal. 37:25) Ngati Yehova amasamalila mbalame na maluŵa, palibe cifukwa codela nkhawa za cakudya kapena zovala. (Mat. 6:26-30; Afil. 4:6, 7) Monga mmene cikondi cimasonkhezela makolo kupezela ana awo zofunikila zakuthupi, nayenso Atate wathu wakumwamba cikondi cimam’sonkhezela kusamalila anthu ake mwakuthupi. Ndithudi, sitikayika olo pang’ono kuti Yehova adzatisamalila.

9. Tiphunzilapo ciani pa zimene zinacitikila banja lina?

9 Onani citsanzo ici coonetsa kuti Yehova amatisamalila pa zakuthupi. M’bale na mkazi wake amene akucita upainiya, anayendetsa motoka yawo yakale kwa ola limodzi kukatenga alongo ku msasa wa othaŵa kwawo, n’kupita nawo ku misonkhano. M’baleyo anati: “Pambuyo pa misonkhano, tinaitanila alongowo ku cakudya ku nyumba kwathu. Koma kenako, tinazindikila kuti tinalibe cakudya cowapatsa.” Kodi cinacitika n’ciani? M’baleyo anapitiliza kuti: “Titafika ku nyumba, tinapeza zola ziŵili za zakudya pakhomo. Sitinadziŵe amene anazibweletsa. Yehova anatisamalila.” Patapita nthawi, motoka ya banjali inawonongeka. Inali kuwathandiza pocita ulaliki, koma analibe ndalama zoikonzetsela. Pamene motokayo anaipeleka ku galaji kuti akaikonze, munthu wina anabwela na kufunsa kuti: “Ni motoka ya ndani iyi?” M’baleyo anayankha kuti ni yake, komanso kuti ifunika kukonzedwa. Munthuyo anati: “Musavutike, mkazi wanga afuna motoka ya mtundu umenewu. Kodi munganigulitse zingati?” M’baleyo anagulutsa motokayo, ndipo ndalama zake anapita kukagulila motoka ina yatsopano. Iye anati: “Siningathe kufotokoza za cimwemwe cimene tinali naco pa tsikulo. Tinadziŵa kuti izi sizinacitike mwangozi, koma Yehova ndiye anatithandiza.”

10. N’cifukwa ciani Salimo 37:5, imatilimbikitsa kusadela nkhawa zofunikila zakuthupi?

10 Tikamamvela m’busa wabwino na kusadelanso nkhawa kwambili zinthu zakuthupi, tingakhale na cidalilo cakuti Yehova adzatisamalila. (Ŵelengani Salimo 37:5; 1 Pet. 5:7) Ganizilani za mikhalidwe yovuta imene tachula  m’ndime 5. Pofika pano, zingakhale kuti Yehova akuseŵenzetsa mutu wa banja, kapena abwana a kunchito kuti atithandize pa zosoŵa zathu. Ngati mutu wa banja sakuthanso kucita zimenezi, kapena ngati tacotsedwa nchito, Yehova adzatisamalila m’njila zina, ndipo sitikaiyikila zimenezi. Tiyeni tsopano tikambilane cina cimene m’busa wabwino amatilangiza kuleka.

“LEKANI KUWELUZA ENA”

Kuona zabwino mwa ena kungatithandize kuleka kuwaweluza (Onani ndime 11, 14-16) *

11. Malinga na Mateyu 7:1, 2, kodi Yesu anati tileke kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani kuleka kungakhale kovuta?

11 Ŵelengani Mateyu 7:1, 2. Yesu anadziŵa kuti anthu opanda ungwilo amakonda kuweluza ena. N’cifukwa cake iye anati: “Lekani kuweluza ena.” Tingayesetse kupewa kuweluza Akhristu anzathu, koma timalephela cifukwa tonse ndife opanda ungwilo. Tikaona kuti nthawi zina timaweluza ena, kodi tiyenela kucita ciani? Timvele Yesu, ndipo tiyesetse kuleka kuweluza ena.

12-13. Kodi kusinkhasinkha mmene Yehova anali kuonela Mfumu Davide kungatithandize bwanji kuleka kuweluza ena?

12 Tingapindule kwambili tikaganizila citsanzo ca Yehova. Iye amayang’ana zabwino mwa anthu. Timadziŵa izi tikaona mmene anacitila zinthu na Mfumu Davide, munthu amene anacita macimo aakulu. Mwacitsanzo, iye anacita cigololo na Batiseba, ndipo anafika ngakhale pa kuphetsa mwamuna wake. (2 Sam. 11:2-4, 14, 15, 24) Cotulukapo cake, zimene Davide anacita sizinavutitse iye yekha cabe, koma zinavutitsanso banja lake, kuphatikizapo akazi ake ena. (2 Sam. 12:10, 11) Pa nthawi ina, Davide analephela kudalila Yehova na mtima wonse pamene analamula atumiki ake kuti aŵelenge khamu la Aisiraeli popanda cilolezo. Mwina anacita izi cifukwa ca kunyada, komanso poona kuculuka kwa asilikali ake. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Aisiraeli pafupifupi 70,000 anafa na mlili!—2 Sam. 24:1-4, 10-15.

13 Mukanakhala kuti munaliko ku Isiraeli nthawi imeneyo, mukanamuona bwanji Davide? Kodi mukanamuweluza kuti sayenela cifundo ca Yehova? Umu si mmene Yehova anamuonela. Iye anayang’ana kwambili pa mbili ya Davide ya kukhulupilika, komanso kulapa kwake mocokela pansi pa mtima. Pa cifukwa cimeneci, Yehova anam’khululukila Davide pa macimo ake aakuluwo. Iye anali kudziŵa kuti Davide anali kum’konda kwambili, ndipo anali kufuna kucita zoyenela. Kodi simuyamikila kuti Yehova amaona zabwino mwa ife?—1 Maf. 9:4; 1 Mbiri 29:10, 17.

14. N’ciani cingathandize Akhristu kuleka kuweluza ena?

14 Cifukwa Yehova satiyembekezela kucita zinthu mwangwilo, nafenso tisamayembekezele ena kucita zinthu mwangwilo. Tiziona zabwino mwa iwo. N’cosavuta kuona zophophonya za ena, komanso kuwaweluza. Komabe, munthu wauzimu amaona zophophonya zimenezo, koma n’kupitilizabe kukhala bwino na ena. Maonekedwe a mwala wa dayamondi saoneka okongola mwalawo asanaudule na kuuyeletsa kuti unyezimile. Koma munthu wozindikila amadziŵa kuti mwalawo akauyeletsa udzakhala wokongola komanso wa mtengo wapatali. Monga Yehova komanso Yesu, ifenso tiyenela kuyang’ana zabwino mwa ena m’malo moyang’ana kwambili pa zophophonya zawo.

15. Kodi kuganizila mmene zinthu zilili pa umoyo wa anthu kungatithandize bwanji kupewa kuwaweluza?

15 Kuwonjezela pa kuyang’ana zabwino mwa ena, n’ciani cina cingatithandize kuti tipewe kuwaweluza? Ni kuganizila mmene umoyo wawo ulili. Onani citsanzo ici. Tsiku lina Yesu ali pakacisi, anaona mkazi wamasiye wosauka akuponya tumakobili tuŵili twatung’ono moponyamo zopeleka. Iye sanafunse kuti: “N’cifukwa ciani mkaziyu sanaponye zambili?” M’malo mosumika maganizo pa zimene mkazi wamasiye anapeleka, Yesu anaganizila colinga ca mkaziyo komanso mmene zinthu zinalili pa umoyo wake. Ndipo anamuyamikila pa zimene anatha kucita.—Luka 21:1-4.

16. Kodi muphunzilapo ciani pa citsanzo ca mlongo Veronica?

16 Cocitika ca mlongo Veronica, citionetsa cifukwa cake n’kofunika kuganizila mmene zinthu zilili pa umoyo wa anthu ena. Mu mpingo umene iye analili munali mlongo wina amene anali kulela yekha mwana. Mlongo Veronica anati: “N’nali kuona kuti iye na mwana wake sanali okangalika mu mpingo. Kaamba ka izi, n’nakhala na maganizo olakwika. Koma tsiku lina, n’nalalikila pamodzi na mlongoyo. Iye ananiuza mavuto amene anali kupitamo posamalila mwana wake wodwala matenda a maganizo. Anali kucita zonse zotheka kuti asamalile zosoŵa zawo zakuthupi komanso zauzimu. Nthawi zina cifukwa ca kudwalila kwa mwana wake, anali kusonkhana ku mpingo wina.” Mlongo Veronica anakambanso kuti: “Sin’nadziŵe kuti mlongoyo anali kupita m’mavuto aakulu conco. Tsopano nimamukonda kwambili mlongoyo, na kumuyamikila pa zimene amatha kucita potumikila Yehova.”

17. Kodi Yakobo 2:8, imatilangiza kucita ciani? Nanga tingacite bwanji zimenezo?

17 Kodi tingacite ciani tikazindikila kuti taweluza Mkhristu mnzathu? Tizikumbukila kuti tiyenela kukonda abale athu. (Ŵelengani Yakobo 2:8.) Tiyenelanso kucondelela Yehova kuti atithandize kuleka kuweluza ena. Tingacite zinthu mogwilizana na mapemphelo athu, mwa kupatula nthawi yoceza na munthu amene tinali kumuweluza. Izi zingatithandize kumudziŵa bwino. Tingam’pemphe kuti tikaseŵenze naye mu ulaliki, kapena kukadya naye cakudya kwathu. Tikafika pomudziŵa bwino m’bale wathu, tidzayamba kuona zabwino mwa iye potengela citsanzo ca Yehova na Yesu. Tikatelo, tidzaonetsa kuti tikumvela lamulo la m’busa wathu wabwino lakuti tileke kuweluza ena.

18. Tingaonetse bwanji kuti timamvela mawu a m’busa wabwino?

18 Monga mmene nkhosa zimamvela mawu a m’busa wawo, nawonso otsatila a Yesu amamvela mawu ake. Tikamayesetsa kuleka kudela nkhawa zosoŵa zathu zakuthupi, komanso kuleka kuweluza ena, Yehova na Yesu adzadalitsa khama lathu. Kaya ndife a “kagulu ka nkhosa” kapena a “nkhosa zina,” tiyeni tipitilize kumvela mawu a m’busa wabwino. (Luka 12:32; Yoh. 10:11, 14, 16) M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zinthu ziŵili zimene Yesu anauza otsatila ake kuti azicita.

NYIMBO 101 Tisunge Umodzi Wathu

^ Pamene Yesu anakamba kuti nkhosa zake zidzamva mawu ake, anatanthauza kuti ophunzila ake adzamvela ziphunzitso zake, na kuziseŵenzetsa pa umoyo wawo. M’nkhani ino, tikambilane ziphunzitso ziŵili za Yesu zofunika kwambili, zimene ni kuleka kudela nkhawa zinthu zakuthupi, komanso kuleka kuweluza ena. Tikambilanenso mmene tingaseŵenzetsele malangizo a Yesu amenewa.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale wacotsedwa nchito, alibe ndalama zosamalila banja lake, ndipo ayenela kupeza nyumba. Ngati sangasamale, mavutowo angam’pangitse kuleka kuika kulambila Mulungu patsogolo.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale wafika mocedwa ku misonkhano. Koma akuonetsa makhalidwe abwino pamene akucita ulaliki wamwayi, akuthandiza wokalamba, komanso akuyeletsa pa Nyumba ya Ufumu.