Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 51

Pitilizani ‘Kumumvela’

Pitilizani ‘Kumumvela’

“Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwela naye, muzimumvela.”—MAT. 17:5.

NYIMBO 54 “Njila ni Iyi”

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. (a) Kodi atumwi atatu a Yesu analamulidwa kucita ciani? Nanga iwo analabadila motani? (b) Tikambilane ciani m’nkhani ino?

 PAMBUYO pa Pasika wa mu 32 C.E., atumwiwa—Petulo, Yakobo, na Yohane, anaona masomphenya ocititsa cidwi. Ali pa phili lalitali, mwina pa nsonga ya phili la Herimoni, Yesu anasandulika pamaso pawo. “Nkhope yake inawala ngati dzuŵa. Malaya ake akunja anawala kwambili.” (Mat. 17:1-4) Kumapeto kwa masomphenya amenewo, atumwiwo anamvela Mulungu akukamba kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwela naye, muzimumvela.” (Mat. 17:5) Zocita za atumwi atatuwo mu umoyo wawo zinaonetsadi kuti anamvela Yesu. Tiyenela kutengela citsanzo cawo.

2 M’nkhani yapita, tinaphunzila kuti kumvela mawu a Yesu kumafuna kuleka kucita zinthu zina. M’nkhani ino, tikambilane zinthu ziŵili zimene Yesu anati tizicita.

“LOŴANI PACIPATA COPAPATIZA”

3. Malinga n’kunena kwa Mateyu 7:13, 14, kodi tiyenela kucita ciani?

3 Ŵelengani Mateyu 7:13, 14. Onani kuti Yesu anachula zipata ziŵili zosiyana zotsogolela ku misewu iŵili yosiyana—msewu “wotakasuka,” komanso msewu “wopanikiza.” Palibe msewu wacitatu. Tifunika kusankha tokha msewu umene tidzayendamo. Ici ndiye cisankho cofunika kopambana cimene tiyenela kupanga, cifukwa moyo wosatha umadalila cisankho cimeneci.

4. Kodi msewu “wotakasuka” mungaufotokoze motani?

4 Tizikumbukila kuti misewu iŵili imeneyi imasiyana. Msewu “wotakasuka” ni wodziŵika cifukwa ni wosavuta kuyendamo. N’zacisoni kuti anthu oculuka asankha kuyendabe mu msewu umenewu potsatila unyinji umene ukuyendamo. Iwo sadziŵa kuti Satana Mdyelekezi, ndiye akupangitsa anthu kuyenda mu msewu umenewu wopita ku ciwonongeko.—1 Akor. 6:9, 10; 1 Yoh. 5:19.

5. Kodi ena anacita ciani kuti apeze msewu “wopanikiza” na kuyamba kuyendamo?

5 Mosiyana na msewu “wotakasuka,” msewu winawo ni “wopanikiza,” ndipo Yesu anati ni anthu oŵelengeka amene akuupeza. Cifukwa ciani? Pa vesi yotsatila, n’zocititsa cidwi kuti Yesu anacenjeza otsatila ake za aneneli onyenga. (Mat. 7:15) Ofufuza apeza kuti pali zipembedzo zofika masauzande, ndipo zambili mwa izo zimati zimaphunzitsa coonadi. Cifukwa cakuti zipembedzo n’zambili, anthu oculuka alibe cidwi cofuna-funa msewu wotsogolela ku moyo. Koma msewu umenewo mungaupeze. Yesu anati: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzila anga. Mudzadziŵa coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.” (Yoh. 8:31, 32) Tikuyamikilani kuti simunatsatile unyinji, koma munacita kucifuna-funa coonadi. Munayamba kuphunzila Mawu a Mulungu mozama kuti mudziŵe zimene iye amafuna kwa ife, ndipo munatsatila ziphunzitso za Yesu. Kuwonjezela apo, munaphunzila kuti Yehova amafuna tizikana ziphunzitso za cipembedzo conyenga, komanso kuleka kukondwelela maholide amene ciyambi cake n’cacikunja. Munaphunzilanso kuti kucita zimene Yehova amafuna, komanso kumasuka ku miyambo yosagwilizana na zimene iye amafuna, kungakhale kovuta. (Mat. 10:34-36) Kupanga masinthidwe amenewa kuyenela kuti kunali kovuta kwa imwe. Komabe, munayesetsa kusintha cifukwa cokonda Atate wanu wakumwamba, ndipo munali kufuna kum’kondweletsa. Iye ni wokondwela ngako pa zimene munacita!—Miy. 27:11.

MMENE TINGAPITILIZILE KUYENDA PA MSEWU WOPANIKIZA

Malangizo a Mulungu na miyezo yake, amatithandiza kusapatuka pa msewu “wopanikiza” (Onani ndime 6-8) *

6. Malinga na Salimo 119:9, 10, 45, 133, n’ciani cingatithandize kuyendabe pa msewu wopanikiza?

6 Tikangoyamba kuyenda pa msewu wopanikiza, n’ciani cingatithandize kukhalabe pa msewu umenewo? Ganizilani citsanzo ici. Zitsulo zochinga zimene amaika m’mphepete mwa msewu wa m’mbali mwa phili zimateteza oyendetsa mamotoka. Colinga ca zochinga zimenezo ni kuteteza oyendetsa mamotoka kuti asapite kwambili ku mbali kwa msewu kuopela kuti angagwele kuphompho. Kodi alipo woyendetsa motoka amene angadandaule kuti zochingazo zikumuphela ufulu? Ayi. Mofananamo, miyezo ya Yehova ya m’Baibo ili ngati zochingazo. Miyezo yake imeneyo imatithandiza kusacoka pa msewu wopanikizawu.—Ŵelengani Salimo 119:9, 10, 45, 133.

7. Kodi acicepele ayenela kuuona motani msewu wopanikiza?

7 Imwe acicepele, kodi nthawi zina mumaona kuti miyezo ya Yehova ni yopanikiza kwambili? Satana amafuna kuti muziona conco. Iye amafuna kuti muziona kuti amene akuyenda pa msewu wotakasuka, ndiwo amasangalala na umoyo. Angaseŵenzetse zocita za anzanu ku sukulu, kapena zimene mumaona pa Intaneti, kuti akupangitseni kuona kuti mukumanidwa zabwino. Satana amafuna muziona kuti miyezo ya Yehova imakuphelani ufulu wosangalala na moyo. * Koma kumbukilani kuti: Satana safuna kuti anthu amene akuyenda pa njila yake adziŵe kumene njilayo ikuwatsogolela. Koma Yehova, wakuonetsani bwino-bwino zimene wasungila awo amene amayendabe pa njila yopita ku moyo.—Sal. 37:29; Yes. 35:5, 6; 65:21-23.

8. Kodi acicepele angaphunzile ciani pa citsanzo ca Olaf?

8 Onani zimene mungaphunzile pa citsanzo ca m’bale wacinyamata dzina lake Olaf. * Anzake a m’kalasi anali kumuyengelela kuti azicita nawo makhalidwe oipa. Iye atawafotokozela kuti Mboni za Yehova zimatsatila mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibo, m’pamenenso atsikana ena m’kalasi mwake anapitiliza kum’nyengelela kuti azigona nawo. Koma Olaf sanasunthike pa kucita zoyenela. Iye anakumananso na mayeso ena. Iye anati: “Aphunzitsi anga anali kuniuza kuti niyenela kukacita maphunzilo apamwamba kuti anthu azinilemekeza. Ananiuza kuti ngati sinidzacita maphunzilowo, sinidzakhala na umoyo wabwino.” N’ciani cinathandiza Olaf kukaniza mayeso otelo? Iye anati: “N’nayamba kuceza kwambili na abale na alongo mu mpingo. Iwo anakhala ngati banja langa. Cina, n’nayamba kuŵelenga kwambili Baibo. Pamene n’nali kuiŵelenga kwambili, m’pamanenso n’nakhala wotsimikiza kuti cinali coonadi. Cotulukapo cake n’cakuti n’nakhala wofunitsitsa kutumikila Yehova.”

9. Kodi awo amene akufuna kupitiliza kuyenda pa msewu wopanikiza ayenela kucita ciani?

9 Satana amafuna kukupatutsani pa msewu wopita ku moyo. Iye amafuna kuti mugwilizane na ŵanthu ambili amene akuyenda pa msewu wotakasuka umene “ukupita kuciwonongeko.” (Mat. 7:13) Komabe, tingayendebe pa msewu wopanikiza, kokha ngati tipitiliza kumvela Yesu, na kuona kuti msewu umenewo ni citetezo. Lomba, tiyeni tikambilane cinthu cinanso cimene Yesu anati tizicita.

KHAZIKITSANI MTENDELE NA M’BALE WANU

10. Malinga na Mateyu 5:23, 24, kodi Yesu anati tiyenela kucita ciani?

10 Ŵelengani Mateyu 5:23, 24. Yesu anafotokoza cocitika cimene cinali cofunika kwambili kwa Ayuda amene anali kumumvetsela. Yelekezani kuti mukuona munthu wina pakacisi amene akufuna kupeleka nsembe ya nyama kwa wansembe. Ngati nthawi yomweyo munthuyo wakumbukila kuti ali na cifukwa na m’bale wake, anayenela kusiya nyama yake na “kupita.” Cifukwa ciani? N’ciani cinali cofunika kwambili kwa Yehova kuposa kupeleka nsembe? Yesu anakamba momveka bwino kuti: “Pita ukayanjane ndi m’bale wako coyamba.”

Kodi mudzatengela citsanzo ca Yakobo, amene modzicepetsa anakhazikitsa mtendele na m’bale wake? (Onani ndime 11-12) *

11. Fotokozani zimene Yakobo anacita kuti akhazikitse mtendele na Esau.

11 Titengapo maphunzilo ofunika kwambili pa nkhani yokhazikitsa mtendele tikaganizila citsanzo ca Yakobo. Patapita zaka 20 cisamukileni kwawo, Mulungu kupitila mwa mngelo anaumuuza kuti abwelele. (Gen. 31:11, 13, 38) Koma panali vuto. Mkulu wake Esau, anali kufuna kumupha. (Gen. 27:41) Yakobo “anacita mantha ndi kuda nkhawa kwambili,” kuti mwina mkulu wake akali kumsungila cidani. (Gen. 32:7) Kodi Yakobo anacita ciani kuti akhazikitse mtendele na m’bale wake? Coyamba, iye anapemphelela nkhaniyo kwa Yehova. Kenako, anatumiza mphatso kwa Esau. (Gen. 32:9-15) Potsilizila pake, iwo ataonana patapita zaka zambili, Yakobo anaonetsa ulemu kwa Esau. Iye anaŵelamila Esau, osati kamodzi kapena kaŵili kokha, koma maulendo 7! Mwa kucita zinthu modzicepetsa komanso mwaulemu, Yakobo anakhazikitsa mtendele na m’bale wake.—Gen. 33:3, 4.

12. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Yakobo?

12 Pali zimene tiphunzilapo kwa Yakobo tikaona zimene iye anacita pokonzekela kukaonana na m’bale wake Esau, na mmene anafikila kwa iye. Modzicepetsa, Yakobo anapempha thandizo kwa Yehova. Ndiyeno, iye anacita zinthu mogwilizana na pemphelo lake mwa kucita zofunikila kuti ayanjanenso na m’bale wake. Atakumana, Yakobo sanayambe kukangana na Esau zakuti anali wolakwa ndani. Colinga cake cinali kukhazikitsa mtendele basi. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yakobo?

MMENE TINGAKHALILE PA MTENDELE NA ENA

13-14. Kodi tiyenela kucita ciani tikakhumudwitsa Mkhristu mnzathu?

13 Ife amene tikuyenda pa msewu wopita ku moyo, tiyenela kulimbikitsa mtendele pakati pathu. (Aroma 12:18) Kodi tiyenela kucita ciani tikazindikila kuti takhumudwitsa Mkhristu mnzathu? Mofanana na Yakobo, tizipemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima. Tingamupemphe kuti atithandize kukhazikitsa mtendele na m’bale wathu.

14 Tiyenelanso kudzisanthula tokha. Tingadzifunse mafunso monga akuti: ‘Kodi nimavomeleza mwamsanga kulakwa kwanga, kupepesa, komanso kukhazikitsa mtendele? Kodi Yehova na Yesu adzamva bwanji ngati niyesetsa kukhazikitsa mtendele na m’bale kapena mlongo wanga?’ Mayankho pa mafunso amenewa angatilimbikitse kumvela Yesu, na kupita kwa abale athu kukakhazikitsa mtendele. Tikatelo, ndiye kuti tikutsatila citsanzo ca Yakobo.

15. Kodi kuseŵenzetsa mfundo ya pa Aefeso 4:2, 3, kungatithandize bwanji kukhazikitsa mtendele na m’bale wathu?

15 Ganizilani zikanacitika Yakobo akanaonetsa khalidwe la kunyada pokumana na m’bale wake. Zinthu sizikanayenda bwino. Tikapita kwa m’bale wathu kukathetsa kusamvana, tiyenela kudzicepetsa. (Ŵelengani Aefeso 4:2, 3.) Miyambo 18:19 imati: “M’bale amene walakwilidwa amaposa mzinda wolimba, ndipo pali mikangano imene imakhala ngati mtengo wotsekela pacipata ca nsanja yokhalamo.” Inde, kupepesa kudzatithandiza kukhalanso pa mtendele na munthuyo.

16. Kodi tiyenela kusamala za ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

16 Cina, tiyenelanso kusamala na zimene tidzakamba kwa m’bale wathu, komanso mmene tingazikambile. Tikakonzeka, tingapite kwa munthu amene tinamulakwilayo, n’colinga cakuti tikathetse kupweteka mu mtima mwake. Poyamba, mwina angakambe mawu otipweteka. Cingakhale capafupi kukwiya kapena kuyesa kudzilungamitsa. Koma kodi kucita zimenezi kungatithandize kukhazikitsa mtendele? Kutalitali! Tizikumbukila kuti kukhazikitsa mtendele, ndiye kofunika kwambili kuposa kufuna kudziŵa kuti wolakwa ndani.—1 Akor. 6:7.

17. Kodi muphunzilapo ciani pa citsanzo ca m’bale Gilbert?

17 M’bale wina, dzina lake Gilbert, anayesetsa kukhala munthu wobweletsa mtendele. Iye anati: “Panali vuto laliku pakati pa ine na mwana wanga. Kwa zaka zoposa ziŵili, n’nayesetsa kukambilana naye moona mtima komanso mwamtendele, n’colinga cakuti tiyambenso kugwilizana.” Kodi m’baleyu anacitanso ciani? Iye anati: “Nikalibe kukambilana naye, n’nali kupemphela na kukonzekeletsa maganizo anga ku mawu opweteka amene angakambe. N’nafunika kukhala wokonzeka kukhululuka. N’naphunzila kuti siniyenela kudzilungamitsa, komanso kuti colinga canga cizikhala kukhazikitsa mtendele.” Kodi panakhala zotulukapo zotani? M’bale Gilbert anati: “Tsopano, nili na mtendele wa maganizo cifukwa tonse m’banja mwathu tili pa ubale wabwino.”

18-19. Tikakhumudwitsa munthu, kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

18 Ndiye, kodi muyenela kuyesetsa kucita ciani mukazindikila kuti mwakhumudwitsa Mkhristu mnzanu? Tsatilani malangizo a Yesu mwa kukhazikitsa mtendele. Muuzeni Yehova nkhaniyo m’pemphelo, kenako dalilani mzimu wake woyela kuti ukuthandizeni kukhala munthu wobweletsa mtendele. Mukatelo, mudzakhala acimwemwe, ndipo mudzaonetsanso kuti mukumvela Yesu.—Mat. 5:9.

19 Tiyamikila kwambili kuti Yehova amatipatsa malangizo acikondi kupitila mwa Yesu Khristu, amene ni “mutu wa mpingo.” (Aef. 5:23) Lekani kuti tipitilize ‘kumumvela [Yesu],’ monga anacitila atumwi atatu aja—Petulo, Yakobo, na Yohane. (Mat. 17:5) Monga taonela, tingacite zimenezo mwa kukhazikitsa mtendele tikakhumudwitsa Mkhristu mnzathu. Tikatelo, komanso tikapitiliza kuyenda pa msewu wopanikiza wopita ku moyo, tidzalandila madalitso ambili pali pano, komanso cimwemwe cosatha m’tsogolo.

NYIMBO 130 Khalani Wokhululuka

^ Yesu anatilimbikitsa kuloŵa pa cipata copapatiza cotsogolela ku njila yopita ku moyo. Iye anatilamulanso kukhazikitsa mtendele na Akhristu anzathu. Kodi tingakumane na zovuta ziti poseŵenzetsa malangizo amenewa? Nanga tingazigonjetse bwanji?

^ Onani funso 6 yakuti, “Ningakane Bwanji Kutunthiwa na Anzanga?” m’bulosha yakuti, Mayankho pa Mafunso 10 Amene Acicepele Amafunsa. Onaninso vidiyo ya zithunzi zodrowing’a yakuti, Musagonje Anzanu Pokunyengelelani, pa jw.org.

^ Maina ena asinthidwa.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Kuti tisacoke pa msewu “wopanikiza”wotetezedwa na malangizo a Mulungu, tiyenela kupewa zinthu zoipa monga zamalisece, mayanjano oipa, komanso mayeselo akuti tiike patsogolo maphunzilo apamwamba.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Kuti akhazikitse mtendele, Yakobo anaŵelamila m’bale wake Esau mobweleza-bweleza.