Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini a chaka chino a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi lemba la Yakobo 5:11, limatitsimikizira bwanji kuti Yehova ndi “wachikondi chachikulu” ndi “wachifundo”?

Timadziwa kuti Yehova, mwachifundo chake amatikhululukira zinthu zomwe timalakwitsa. Lemba la Yakobo 5:11, limatitsimikizira kuti chifukwa amatikonda, iye ndi wofunitsitsa kutithandiza. Tingachite bwino kumamutsanzira.​—w21.01, tsamba 21.

N’chifukwa chiyani Yehova anakonza zoti ena azikhala ndi udindo wotsogolera?

Iye anachita zimenezi chifukwa choti amatikonda. Ndipo izi zimathandiza kuti m’banja la lake, zinthu zizichitika mwamtendere komanso mwadongosolo. Aliyense m’banja akamachita zinthu mogwirizana ndi zimene Yehova anakonzazi, sizivuta kudziwa amene ayenera kusankha zochita komanso amene angatsogolere pochita zimene asankhazo.​—w21.02, tsamba 3.

N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kusamala kwambiri akamagwiritsa ntchito mapulogalamu otumizira ndi kulandirira mauthenga?

Ngati munthu wasankha kugwiritsa ntchito mapulogalamu amenewa, ayenera kusankha anthu abwino ocheza nawo. Komatu kuchita zimenezi ndi kovuta makamaka tikamatumizirana mauthenga m’magulu okhala ndi anthu ambiri. (1 Tim. 5:13) Pangakhalenso ngozi yaikulu ngati titamafalitsa nkhani zopanda umboni komanso kugwiritsa ntchito ma adiresi a gulu pochita zamalonda.​—w21.03, tsamba 31.

Kodi Mulungu analola kuti Yesu avutike komanso kufa pa zifukwa zina ziti?

Chifukwa choyamba n’choti kupachikidwa kwake pamtengo kunathandiza kuti Ayuda amasulidwe ku temberero linalake. (Agal. 3:10, 13) Chachiwiri, Yehova ankamukonzekeretsa kuti adzakwaniritse udindo wake monga Mkulu wa Ansembe. Ndipo chachitatu, kukhulupirika kwake mpaka imfa kunatsimikizira kuti anthu angakhalebe okhulupirika kwa Yehova ngakhale atakumana ndi mayesero aakulu. (Yobu 1:9-11)​—w21.04, tsamba 16-17.

Kodi muyenera kuchita chiyani ngati simukupeza anthu panyumba mukamalalikira?

Muzisintha nthawi n’kumapita pa nthawi imene amapezeka panyumba. Mungayesenso kusintha malo olalikira. Ndiponso muziyesa kugwiritsa ntchito njira ina yolalikirira monga kulembera makalata.​—w21.05, tsamba 15-16.

Kodi mtumwi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Mwa chilamulo, ine ndinafa ku chilamulo”? (Agal. 2:19)

Chilamulo cha Mose chinasonyeza bwino kuti anthu si angwiro ndipo chinatsogolera Aisiraeli kwa Khristu. (Agal. 3:19, 24) Zimenezi zinachititsa kuti Paulo avomereze komanso kukhulupirira Khristu. Apa iye ‘anafa ku chilamulo’ moti Chilamulo chinalibenso mphamvu pa iyeyo.​—w21.06, tsamba 31.

Kodi Yehova amatipatsa bwanji chitsanzo pa nkhani ya kupirira?

Yehova wakhala akupirira kunyozedwa kwa dzina lake, kutsutsidwa kwa Ulamuliro wake, kusamvera kwa ana ake ena, mabodza amene Mdyerekezi amanena, kuvutika kwa atumiki ake, kusowana ndi anzake amene anamwalira, kuponderezedwa kwa anthu komanso kuwonongedwa kwa zinthu zimene analenga.​—w21.07, tsamba 9-12.

Kodi Yosefe anatipatsa chitsanzo chotani pa nkhani ya kuleza mtima?

Iye anapirira zinthu zopanda chilungamo zimene abale ake anamuchitira. Zimenezi zinachititsa kuti aimbidwe mlandu wabodza ndipo anakakhala m’ndende kwa zaka zambiri ku Iguputo.​—w21.08, tsamba 12.

Kodi lemba la Hagai 2:6-9, 20-22 linaneneratu za kugwedeza kophiphiritsira kuti?

Mitundu ya anthu sifuna kumvetsera uthenga wa Ufumu komabe anthu ambiri akuphunzira choonadi. Posachedwapa anthu agwedezedwa komaliza pamene azidzawonongedwa.​—w21.09, tsamba 15-19.

N’chifukwa chiyani sitiyenera kufooka pa ntchito yathu yolalikira?

Yehova amaona khama lathu ndipo amasangalala. Tikapanda kutopa kapena kufooka, tidzapeza moyo wosatha.​—w21.10, tsamba 25-26.

Kodi mfundo za mu Levitiko 19 zingatithandize bwanji kutsatira malangizo akuti: “Inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse”? (1 Pet. 1:15)

Zikuoneka kuti mawu a pavesili anatengedwa pa Levitiko 19:2. Chaputala19 chimafotokoza zitsanzo zambiri za mmene tingagwiritsire ntchito malangizo a pa 1 Petulo 1:15, tsiku lililonse pa moyo wathu.​—w21.12, tsamba 3-4.