NKHANI YOPHUNZIRA 6

Kodi Mumakhulupirira Kuti Yehova Amachita Zinthu M’njira Yoyenera?

Kodi Mumakhulupirira Kuti Yehova Amachita Zinthu M’njira Yoyenera?

“Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene sachita chosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.”​—DEUT. 32:4.

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. (a) N’chifukwa chiyani masiku ano anthu ambiri zimawavuta kukhulupirira anthu amene ali ndi udindo? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

 MASIKU ano anthu ambiri zimawavuta kukhulupirira amene ali ndi udindo. Iwo amaona kuti maboma komanso malamulo amateteza anthu olemera komanso audindo, koma sachitira chilungamo anthu osauka. Baibulo limanena molondola kuti: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlal. 8:9) Kuwonjezera pamenepo, atsogoleri ena achipembedzo amachita zinthu zoipa. Zimenezi zachititsa kuti anthu ena asamakhulupirire Mulungu. Choncho tikamaphunzira Baibulo ndi munthu, timafunika kumuthandiza kuti ayambe kukhulupirira Yehova komanso anthu amene iye wawasankha kuti azitsogolera gulu lake.

2 Komabe si ophunzira Baibulo okha amene amafunika kuphunzira kuti azikhulupirira Yehova ndi gulu lake. Ngakhale ife amene takhala tikutumikira Yehova kwa zaka zambiri, timafunika tisamakayikire kuti nthawi zonse Yehova amachita zinthu m’njira yoyenera. Nthawi zina pangachitike zinthu zina zomwe zingachititse kuti tiyambe kukayikira Yehova. Munkhaniyi tikambirana mbali zitatu pamene chikhulupiriro chathu chingayesedwe: (1) tikamawerenga nkhani zina za m’Baibulo, (2) tikalandira malangizo kuchokera kugulu la Yehova ndiponso (3) tikadzakumana ndi mavuto m’tsogolo.

MUZIKHULUPIRIRA YEHOVA MUKAMAWERENGA BAIBULO

3. Kodi nkhani zina za m’Baibulo zingatichititse bwanji kukayikira mmene Yehova amachitira zinthu?

 3 Tikamawerenga Mawu a Mulungu mwina tingamadabwe tikaganizira mmene Yehova anachitira zinthu ndi anthu ena komanso chifukwa chake anasankha kuchita zinazake. Mwachitsanzo, m’buku la Numeri timawerenga kuti Yehova anaweruza kuti Mwisiraeli wina aphedwe chifukwa chotola nkhuni pa tsiku la Sabata. M’buku la 2 Samueli, timawerenga kuti patapita zaka zambiri Yehova anakhululukira Mfumu Davide atachita tchimo lachigololo komanso kupha munthu. (Num. 15:32, 35; 2 Sam. 12:9, 13) Ndiye mwina tingadabwe kuti: ‘N’chifukwa chiyani Yehova anakhululukira Davide yemwe anapha munthu komanso kuchita chigololo koma n’kuweruza kuti munthu amene anachita tchimo looneka ngati laling’ono aphedwe?’ Kuti tiyankhe funsoli, tingafunike kuganizira zinthu zitatu zimene tiyenera kukumbukira tikamawerenga Baibulo.

4. Kodi pa Genesis 18:20, 21 komanso Deuteronomo 10:17, amatithandiza bwanji kuti tisamakayikire mmene Yehova amachitira zinthu?

4 Nthawi zina Baibulo silifotokoza mfundo zonse zokhudza nkhani inayake. Mwachitsanzo, timadziwa kuti Davide analapa mochokera pansi pa mtima pa zimene anachita. (Sal. 51:2-4) Koma bwanji za munthu yemwe anaphwanya lamulo la Sabata uja? Kodi anadzimvera chisoni chifukwa cha zimene anachita? Kodi analepherapo kumvera malamulo ena a Yehova m’mbuyomo? Kodi ananyalanyaza kapena kukana kumvera machenjezo omwe anapatsidwapo? Baibulo silinena. Komabe chomwe tikudziwa n’chakuti Yehova “sachita chosalungama.” (Deut. 32:4) Iye amachita zinthu poganizira mbali zonse za nkhaniyo, osati pongotengera zimene ena anena, tsankho kapenanso zinthu zina zomwe nthawi zambiri zimachititsa kuti anthu asamaweruze mwachilungamo. (Werengani Genesis 18:20, 21; Deuteronomo 10:17.) Tikamaphunzira kwambiri za Yehova komanso mfundo zake, m’pamenenso timayamba kumukhulupirira kwambiri pa nkhani ya mmene amachitira zinthu. Ngakhale pamene tikuwerenga nkhani inayake ya m’Baibulo ndipo tili ndi mafunso amene sitinapeze mayankho ake, timadziwa kuti Mulungu wathu “ndi wolungama m’njira zake zonse.”​—Sal. 145:17.

5. Popeza si ife angwiro, kodi zimenezi zingakhudze bwanji mmene timaonera zinthu zina? (Onaninso bokosi lakuti, “ Sitiona Zinthu Moyenera Chifukwa Si Ife Angwiro.”)

5 Tingalephere kuweruza moyenera chifukwa choti si ife angwiro. Mulungu anatilenga m’chifaniziro chake, choncho timafunitsitsa kuona anthu akuchitiridwa zinthu mwachilungamo. (Gen. 1:26) Koma chifukwa choti si ife angwiro, sitingamaone moyenera nkhani zina ngakhale pamene tikuganiza kuti tikudziwa mfundo zonse zokhudza nkhanizo. Mwachitsanzo, taganizirani mmene Yona anakhumudwira chifukwa choti Yehova anasonyeza chifundo anthu a ku Nineve. (Yona 3:10–4:1) Ndiye taganiziranso zimene zinachitika chifukwa choti Yehova anawasonyeza chifundo. Anthu okwanira 120,000 a ku Nineve omwe analapa anapulumutsidwa. Pamapeto pake, Yona ndi amene ankafunika kuthandizidwa kuti asinthe maganizo, osati Yehova.

6. N’chifukwa chiyani Yehova safunikira kutifotokozera chilichonse chimene wasankha?

6 Sikuti Yehova amachita kufunikira kufotokozera anthu chifukwa chake wasankhira zinazake. N’zoona kuti m’mbuyomu nthawi zina Yehova ankalola atumiki ake kufotokoza maganizo awo pa zimene iye wachita kapena zimene akufuna kuchita. (Gen. 18:25; Yona 4:2, 3) Ndipo pa nthawi zingapo anafotokoza chifukwa chake anachita zinazake. (Yona 4:10, 11) Komabe sikuti Yehova amafunikira kutifotokozera chilichonse. Monga Mlengi wathu, sachita kufunika chilolezo chathu kuti achite zinazake.​—Yes. 40:13, 14; 55:9.

MUZIKHULUPIRIRA YEHOVA MUKAPATSIDWA MALANGIZO

7. Kodi tingakumane ndi vuto lotani, nanga n’chifukwa chiyani?

7 Timakhulupirira ndi mtima wonse kuti zimene Yehova amachita nthawi zonse zimakhala zoyenera. Komabe mwina tingamavutike kukhulupirira anthu amene iye akuwagwiritsa ntchito. Tingamakayikire ngati anthu amene ali ndi udindo m’gulu la Yehova akuchita zinthu mogwirizana ndi malangizo a Yehovayo kapena maganizo awo. N’kutheka kuti anthu enanso akale ankaganiza choncho. Taganizirani zitsanzo zomwe zatchulidwa  mundime 3. Mwina wachibale wa munthu yemwe anaphwanya lamulo la Sabata ankakayikira ngati Mose anafunsa kaye Yehova asanaweruze kuti munthuyo aphedwe. Ndipo mnzake wa Uriya Mhiti, yemwe mkazi wake anachita chigololo ndi Davide akanaona kuti Davide anagwiritsa ntchito udindo wake monga mfumu pothawa chilango chomwe ankayenera kupatsidwa. Mfundo yosatsutsika ndi yakuti sitinganene kuti timakhulupirira Yehova pamene sitikhulupirira anthu omwe iye amawakhulupirira ndipo amawagwiritsa ntchito.

8. Kodi pali kufanana kotani pakati pa zimene zafotokozedwa pa Machitidwe 16:4, 5, ndi mmene zinthu zimachitikira mumpingo masiku ano?

8 Masiku ano Yehova amatsogolera mbali yapadziko lapansi ya gulu lake pogwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Mofanana ndi bungwe lolamulira la munthawi ya atumwi, kapoloyu amatsogolera anthu a Mulungu padziko lonse ndipo amapereka malangizo kwa akulu. (Werengani Machitidwe 16:4, 5.) Akulu nawonso amagwiritsa ntchito malangizowo m’mipingo. Timasonyeza kuti timakhulupirira mmene Yehova amachitira zinthu potsatira malangizo ochokera kugulu lake komanso kwa akulu.

9. Kodi ndi pa nthawi iti pamene zingativute kutsatira zimene akulu asankha, nanga n’chifukwa chiyani?

9 Nthawi zina zingativute kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene akulu asankha. Mwachitsanzo, m’zaka zaposachedwapa mipingo ndi madera ambiri zakonzedwanso. Nthawi zina, akulu amapempha ofalitsa ena kuti asamukire kumipingo ina n’cholinga choti mipando m’Nyumba ya Ufumu izigwiritsidwa ntchito mokwanira. Ngati atatipempha kusamukira mumpingo wina, mwina tingaone kuti n’zovuta kusiyana ndi anzathu komanso achibale. Kodi akulu amauzidwa mwanjira inayake ndi Mulungu kuti asamutsire ofalitsa mumpingo winawake? Ayi. Choncho izi zingachititse kuti zizitivuta kuti titsatire malangizo omwe tapatsidwa. Koma Yehova amakhulupirira kuti akulu asankha bwino pa nkhani zimenezi ndipo ifenso tiyenera kuwakhulupirira. *

10. Malinga ndi Aheberi 13:17, n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi akulu?

10 N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene akulu asankha, ngakhale kuti zimene asankhazo si zimene tikanakonda? Chifukwa tikamachita zimenezi, timathandiza kuti anthu a Mulungu apitirize kukhala ogwirizana. (Aef. 4:2, 3) Zinthu zimayenda bwino mumpingo, anthu onse akamatsatira modzichepetsa zimene bungwe la akulu lasankha. (Werengani Aheberi 13:17.) Koma chofunika kwambiri n’chakuti timamusonyeza Yehova kuti timamukhulupirira tikamachita zinthu mogwirizana ndi anthu omwe wawapatsa udindo wotisamalira.​—Mac. 20:28.

11. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri malangizo amene akulu amatipatsa?

11 Kukumbukira kuti akulu amayamba apempha Yehova kuti awapatse mzimu woyera akamakambirana nkhani zokhudza mpingo kungatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri malangizo omwe amatipatsa. Amaganiziranso mosamala mfundo zosiyanasiyana za m’Baibulo zimene zikugwirizana ndi nkhaniyo komanso malangizo amene gulu la Yehova limapereka. Iwo amafunitsitsa kusangalatsa Yehova komanso kusamalira anthu ake m’njira yabwino kwambiri. Amuna okhulupirikawa amadziwa kuti adzayankha kwa Mulungu pa zimene amachita pa udindo wawo. (1 Pet. 5:2, 3) Taganizirani mfundo iyi: M’dziko limene anthu ake ndi ogawikana chifukwa chosiyana mtundu, chipembedzo komanso nkhani zandale, anthu a Yehova amakhala ogwirizana polambira Mulungu woona yekha. Zimenezi zimatheka chifukwa choti Yehova amathandiza gulu lake.

12. Kodi akulu amayenera kuganizira mfundo ziti kuti adziwe ngati munthu ndi wolapa?

12 Yehova anapatsa akulu udindo waukulu woonetsetsa kuti mpingo ukhale woyera. Ngati Mkhristu wachita tchimo lalikulu, Yehova amayembekezera kuti akulu aone ngati munthuyo akufunika kupitiriza kukhala mumpingo. Mwa zina, iwo amafunika kufufuza kuti adziwe ngati munthuyo akudzimveradi chisoni chifukwa cha tchimo lakelo. Munthu angamanene kuti walapa, koma kodi akudanadi ndi zimene anachita? Kodi watsimikiza kuti sadzabwerezanso tchimolo? Ngati anachita tchimolo chifukwa chogwirizana ndi anthu oipa, kodi iye ndi wofunitsitsa kusiya kugwirizana nawo? Akulu amapempherera nkhaniyo, kufufuza mfundo za m’Malemba komanso kuona mmene munthuyo akuganizira. Akatero amaona ngati wochimwayo angapitirize kukhala mumpingo. Nthawi zina wochimwayo amafunika kuchotsedwa.​—1 Akor. 5:11-13.

13. Kodi tikhoza kuyamba kuganiza zinthu ziti mnzathu kapena wachibale wathu akachotsedwa?

13 Kodi chikhulupiriro chathu mwa akulu chingayesedwe bwanji? Ngati munthu yemwe wachotsedwa si mnzathu kapena wachibale wathu, mwina sizingativute kuvomereza zimene akulu asankha. Koma bwanji ngati yemwe wachotsedwayo ndi mnzathu wapamtima? Mwina tingamaone kuti akulu sanaganizire mfundo zonse za nkhaniyo kapena tingamakayikire ngati aweruza mogwirizana ndi zimene Yehova akufuna. Ndiye n’chiyani chingatithandize kuti tiziona moyenera zimene akulu asankha?

14. Kodi n’chiyani chingatithandize ngati akulu asankha kuti mnzathu kapena wachibale wathu achotsedwe?

14 Tiyenera kukumbukira kuti Yehova ndi amene anakonza zoti munthu wosalapa azichotsedwa mumpingo ndipo zimenezi zimapindulitsa mpingo komanso kuthandiza munthu wochimwayo. Ngati munthu wosalapayo atapitiriza kukhala mumpingo, angalimbikitse anthu ena kuti azichita zoipa. (Agal. 5:9) Kuwonjezera pamenepo, iye sangazindikire kukula kwa tchimo lake ndipo sangaone kufunika koti asinthe mmene amaganizira komanso zochita zake n’cholinga choti akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova. (Mlal. 8:11) Tingakhale otsimikiza kuti akulu akafuna kusankha ngati munthu akufunika kuchotsedwa, saona udindo wawo mopepuka. Iwo amadziwa kuti mofanana ndi oweruza a m’nthawi ya Isiraeli, ‘sakuweruzira munthu koma akuweruzira Yehova.’​—2 Mbiri 19:6, 7.

MMENE KUKHULUPIRIRA YEHOVA PANOPA KUMATITHANDIZIRA KUKONZEKERA ZA M’TSOGOLO

Kodi n’chiyani chidzatithandize kukhulupirira komanso kumvera malangizo omwe tidzapatsidwe pa chisautso chachikulu? (Onani ndime 15)

15. N’chifukwa chiyani panopa tiyenera kumakhulupirira malangizo ochokera kwa Yehova kuposa kale?

15 Pamene mapeto a dzikoli akuyandikira, tikufunika kukhulupirira kwambiri mmene Yehova amachitira zinthu kuposa kale. Chifukwa chiyani? Chifukwa pa chisautso chachikulu mwina tingadzapatsidwe malangizo ooneka achilendo, osathandiza kapenanso osamveka bwino. N’zoona kuti Yehova sadzalankhula nafe mwachindunji. N’zodziwikiratu kuti adzatipatsa malangizo kudzera mwa abale audindo. Imeneyi sidzakhala nthawi yomakayikira malangizo omwe tapatsidwa n’kumanena kuti, ‘Kodi malangizo amenewa akuchokeradi kwa Yehova, kapena abalewa akuchita zongoganiza okha?’ Kodi inuyo mudzachita bwanji zinthu pa nthawi yofunikayi? Mungadziwe zimene mudzachite pa nthawiyo, mukaganizira zomwe mumachita mukalandira malangizo ochokera kugulu la Yehova panopa. Ngati mumakhulupirira malangizo omwe timapatsidwa masiku ano, n’kumawatsatira mofunitsitsa, n’zosakayikitsa kuti mudzachitanso zomwezo pa chisautso chachikulu.​—Luka 16:10.

16. Kodi kukhulupirira kwathu Yehova kungadzayesedwe bwanji pamene azidzaweruza anthu m’tsogolomu?

16 Mfundo ina imene tiyenera kuiganizira ndi yokhudza chiweruzo chimene Yehova adzapereke pamapeto pa dziko loipali. Panopa timayembekezera kuti anthu omwe satumikira Yehova, kuphatikizapo achibale athu omwe si a Mboni, angasinthe n’kuyamba kumutumikira mapeto asanafike. Koma pa Aramagedo, Yehova kudzera mwa Yesu, ndi amene adzasankhe zimene ziwachitikire. (Mat. 25:31-33; 2 Ates. 1:7-9) Si ife amene tidzasankhe kuti Yehova awachitire chifundo kapena ayi. (Mat. 25:34, 41, 46) Kodi tidzakhulupirira kuti Yehova waweruza moyenera kapena tidzakhumudwa? Kunena zoona, tiyenera kumakhulupirira Yehova panopa kuti tidzathe kumukhulupiriranso kwambiri m’tsogolo.

17. Kodi tidzapindula bwanji chifukwa cha chiweruzo chimene Yehova adzapereke akamadzawononga dzikoli?

17 Tangoganizani mmene tidzamvere m’dziko latsopano kuona zotsatira za chiweruzo cha Yehova. Sipadzakhalanso chipembedzo chonyenga, amalonda adyera komanso maboma andale omwe akhala akupondereza anthu n’kubweretsa mavuto ochuluka kwa zaka zambiri. Matenda, ukalamba komanso imfa ya anthu amene timawakonda sizidzakhalanso mbali ya moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Satana ndi ziwanda adzamangidwa kwa zaka 1,000. Zoipa zomwe zinabwera chifukwa cha kusamvera kwawo zidzatha. (Chiv. 20:2, 3) Tidzasangalala kwambiri poona kuti tinakhulupirira mmene Yehova amachitira zinthu.

18. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Aisiraeli chopezeka pa Numeri 11:4-6 ndi 21:5?

18 Kodi m’dziko latsopano tingadzayesedwenso pa nkhani yokhulupirira mmene Yehova amachitira zinthu? Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika Aisiraeli atangomasulidwa kumene ku ukapolo ku Iguputo. Ena anayamba kudandaula chifukwa choti sankadyanso zakudya zabwino zimene ankadya ku Iguputo ndipo sankayamikira mana amene Yehova anawapatsa. (Werengani Numeri 11:4-6; 21:5.) Kodi ifenso tingadzakhale ndi maganizo ngati amenewa pambuyo pa chisautso chachikulu? Sitikudziwa kuchuluka kwa ntchito yomwe idzakhalepo yoti tichotse zinthu zomwe zawonongedwa n’kuyamba kukonza dzikoli pang’onopang’ono kuti likhale Paradaiso. N’zodziwikiratu kuti tidzakhala ndi ntchito yambiri komanso mavuto ena chakumayambiriro. Kodi tidzadandaula ndi zimene Yehova adzatipatse pa nthawi imeneyo? Mfundo yosatsutsika ndi yakuti: Tikamayamikira zimene Yehova akutipatsa panopa, n’zosakayikitsa kuti tidzayamikiranso zimene adzatipatse pa nthawiyo.

19. Kodi ndi mfundo zikuluzikulu ziti zomwe taphunzira munkhaniyi?

19 Nthawi zonse Yehova amachita zinthu m’njira yoyenera. Sitiyenera kukayikira zimenezi. Tizikhulupiriranso anthu amene Yehova amawadalira kuti atsatira malangizo ake. Tisamaiwale mawu amene Yehova analankhula kudzera mwa mneneri Yesaya kuti: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.”​—Yes. 30:15.

NYIMBO NA. 98 Malemba Anauziridwa ndi Mulungu

^ ndime 5 Nkhaniyi itithandiza kuona chifukwa chake tiyenera kumakhulupirira kwambiri Yehova ndi anthu amene amatsogolera gulu lake padzikoli. Tionanso mmene kuchita zimenezi kungatithandizire panopa komanso kutikonzekeretsa pa mavuto omwe tidzakumane nawo m’tsogolo.

^ ndime 9 Nthawi zina pangakhale zifukwa zomveka zomwe zingachititse munthu kapena banja kukhalabe mumpingo womwe ali. Onani “Bokosi la Mafunso” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2002.