Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 8

Kodi Uphungu Wanu ‘Umasangalatsa Mtima’?

Kodi Uphungu Wanu ‘Umasangalatsa Mtima’?

“Mafuta ndi zofukiza zonunkhila n’zimene zimasangalatsa mtima, cimodzimodzinso kukoma kwa mnzako cifukwa ca malangizo ake ocokela pansi pa mtima, kumasangalatsa mtima.”—MIY. 27:9.

NYIMBO 102 “Thandizani Ofooka”

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi m’bale wina anaphunzila ciani pa nkhani yopeleka uphungu?

 ZAKA zambili kumbuyoku, akulu aŵili anafikila mlongo amene sanali kupezeka ku misonkhano kwakanthawi. Mkulu amene anatsogolela makambilanowo, anaŵelenga naye malemba oonetsa kufunika kopezeka ku misonkhano. Mkuluyo anaona kuti ulendo wa ubusa umenewo wayenda bwino. Koma pamene iye na mkulu mnzake anali kucoka, mlongoyo anati: “Abale inu, kungoti simudziŵa mavuto amene nipitamo!” Abalewo anapatsa uphungu mlongoyo popanda kumufunsa mavuto amene anali kukumana nawo. Cotulukapo cake n’cakuti, mlongoyo anaona kuti uphunguwo sunali wothandiza.

2 Pokumbukila zinacitika, mkulu amene anatsogolela makambilanowo anati: “Pa nthawiyo, n’naona kuti mlongoyo alibe ulemu. Koma n’taganizilapo, n’naona kuti n’nafulumila kuŵelenga naye malemba coyamba, m’malo momufunsa mafunso monga akuti, ‘Kodi zinthu zili motani pa umoyo wanu?’ ‘Kodi pali mbali imene tingathandizilepo?’” Mkuluyo anatengapo phunzilo lofunika pa zimene zinacitikazo. Tsopano iye ni m’busa wacifundo komanso wolimbikitsa.

3. Ndani mu mpingo ayenela kupeleka uphungu?

 3 Pokhala abusa, akulu ali na udindo wopeleka uphungu pakafunika kutelo. Komabe, nthawi zina ofalitsa ena mu mpingo nawonso angapeleke uphungu. Mwacitsanzo, m’bale kapena mlongo angapatse mnzake uphungu wocokela m’Baibo. (Sal. 141:5; Miy. 25:12) Kapena mlongo wacikulile “[angalangize] akazi acitsikana” pa nkhani monga zachulidwa pa Tito 2:3-5. Ndipo nawonso makolo, ayenela kulangiza ana awo kaŵili-kaŵili. Conco, olo kuti nkhani ino analembela maka-maka akulu a mpingo, tonsefe tingapindule na malangizo amenewa oonetsa mmene tingapelekele uphungu wothandiza komanso wolimbikitsa, umene ‘umasangalatsa mtima.’—Miy. 27:9.

4. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

4 M’nkhani ino, tikambilane mafunso anayi pa nkhani yopeleka uphungu: (1) Kodi uphungu uyenela kupelekedwa na colinga cotani? (2) Kodi m’pofunikiladi kupeleka uphungu? (3) Ndani ayenela kuupeleka uphunguwo?, komanso (4) Muyenela kucita ciani kuti mupeleke uphungu wothandiza?

KODI UPHUNGU UYENELA KUPELEKEDWA NA COLINGA COTANI?

5. Kodi kukhala na colinga cabwino kungathandize bwanji mkulu kupeleka uphungu mwacikondi? (1 Akorinto 13:4, 7)

5 Akulu amakonda abale na alongo awo. Nthawi zina, amaonetsa cikondi cimeneco mwa kuwongolela munthu amene akuloŵela njila yolakwika. (Agal. 6:1) Mkulu asanapeleke uphungu, coyamba ayenela kuganizila zimene mtumwi Paulo anakamba zokhudza cikondi. Iye anati: “Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima. . . . Cimakwilila zinthu zonse, cimakhulupilila zinthu zonse, cimayembekezela zinthu zonse, cimapilila zinthu zonse.” (Ŵelengani 1 Akorinto 13:4, 7.) Kusinkhasinkha mfundo ya palembali, kudzathandiza mkulu kupenda colinga cake copelekela uphungu, ndipo adzatha kupeleka uphunguwo mwacikondi. Ngati wolandila uphungu aona kuti mkuluyo amam’dela nkhawa, iye angalandile uphunguwo mosavuta.—Aroma 12:10.

6. Kodi mtumwi Paulo anapeleka citsanzo cabwino cotani?

6 Pokhala mkulu, mtumwi Paulo anapeleka citsanzo cabwino. Mwacitsanzo, pamene abale na alongo ku Tesalonika anafunikila uphungu, Paulo sanazengeleze kuupeleka. M’makalata ake, coyamba iye anawayamikila pa nchito zawo za cikhulupililo, za cikondi, komanso kupilila kwawo. Anaganizilanso mmene zinthu zinalili pa umoyo wawo, ndipo anawauza kuti iye anali kudziŵa mavuto anali kupitamo, komanso mazunzo amene iwo anali kupilila. (1 Ates. 1:3; 2 Ates. 1:4) Anafika ngakhale pouza abalewo kuti anali citsanzo kwa Akhristu ena. (1 Ates. 1:8, 9) Iwo anakondwela kwambili Paulo atawayamikila mwa njila imeneyi. Sitikayikila kuti Paulo anali kuwakonda ngako Akhristu amenewo. Ndiye cifukwa cake, iye anakwanitsa kuwapatsa uphungu wothandiza m’makalata ake aŵili amene analembela Atesalonika.—1 Ates. 4:1, 3-5, 11; 2 Ates. 3:11, 12.

7. N’cifukwa ciani ena angakhumudwe akapatsidwa uphungu?

7 N’ciani cingacitike ngati uphungu sitinaupeleke m’njila yabwino? Mkulu wina amene ni ciyambakale anati: “Ena amakhumudwa akapatsidwa uphungu, osati cifukwa cakuti uphunguwo ni wolakwika ayi, koma cifukwa cakuti sunapelekedwe mwacikondi.” Tiphunzilapo ciani pamenepa? Uphungu umakhala wosavuta kuulandila ukapelekedwa mwacikondi, osati cifukwa cokwiya.

KODI M’POFUNIKILADI KUPELEKA UPHUNGU?

8. Kodi mkulu ayenela kudzifunsa ciani ngati akuganizila zopatsa wina uphungu?

8 Akulu sayenela kuthamangila kupeleka uphungu. Asanapeleke uphungu, mkulu ayenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi niyeneladi kupeleka uphungu? Kodi ndine wotsimikiza kuti zimene munthuyu akucita n’zolakwika? Kodi iye waphwanya lamulo la m’Baibo? Kapena kodi wangocita zinthu mosiyana na mmene ine n’kanacitila?’ Akulu ayenela kupewa kukhala ‘opupuluma m’mawu awo.’ (Miy. 29:20) Mkulu akaona kuti si wotsimikiza ngati ayeneladi kupatsa wina uphungu, angakambilane na mkulu mnzake ngati zimene munthuyo wacita n’zosemphana na zimene Baibo imakamba.—2 Tim. 3:16, 17.

9. Tiphunzilapo ciani kwa Paulo zokhudza kupeleka uphungu pa nkhani ya mavalidwe na kudzikongoletsa? (1 Timoteyo 2:9, 10)

9 Ganizilani citsanzo ici. Tinene kuti mkulu akuona kuti Mkhristu mnzake, sanasankhe bwino pa nkhani ya mavalidwe na kudzikongoletsa. Mkuluyo angadzifunse kuti, ‘Kodi pali cifukwa ca m’Malemba copelekela uphungu?’ Posafuna kupeleka uphungu motengela mmene amaonela zinthu, iye angakambilane na mkulu mnzake, kapena wofalitsa wokhwima mwauzimu kuti akambepo maganizo ake. Iwo capamodzi, angapende malangizo a Paulo pa nkhani ya mavalidwe na kudzikongoletsa. (Ŵelengani 1 Timoteyo 2:9, 10.) Paulo anangofotokoza kuti Mkhristu ayenela kuvala moyenela, komanso mwaulemu. Iye sanacite kuchula mtundu wa zovala zimene Mkhristu ayenela kuvala kapena kusavala. Anadziŵa kuti abale na alongo ali na ufulu wovala ciliconse cimene asankha malinga ngati cigwilizana na mfundo za m’Malemba. Mwa ici, pofuna kuona ngati m’pofunikiladi kupeleka uphungu kapena ayi, akulu ayenela kupenda ngati munthuyo amavala na kudzikongoletsa moyenela komanso mwaulemu.

10. Kodi tizikumbukila ciani pa nkhani ya cisankho ca munthu mwini?

10 Ni bwino kukumbukila kuti Akhristu aŵili okhwima mwauzimu, angapange zisankho zosiyana zimene si zolakwika. Motelo, tiyenela kupewa kuikila Akhristu anzathu miyezo yathu ya cabwino na coipa.—Aroma 14:10.

NDANI AYENELA KUUPELEKA UPHUNGUWO?

11-12. Ngati uphungu ni wofunikila, ni mafunso ati amene mkulu ayenela kudzifunsa? Nanga n’cifukwa ciani?

11 Ngati n’zoonekelatu kuti uphungu uyenela kupelekedwa, funso n’lakuti, Ndani ali pamalo abwino oupeleka? Mkulu asanapeleke uphungu kwa mlongo wokwatiwa kapena mwana, coyamba angakambilane na mutu wa banjalo ngati angakonde kupeleka yekha uphunguwo. * Kapena mutu wa banjayo angapemphe kuti akhalepo pamene mkuluyo akupeleka uphungu. Ndipo monga taonela  m’ndime 3, nthawi zina, cimakhalanso bwino kuti mlongo wacikulile apeleke uphungu kwa mlongo wacitsikana.

12 Palinso mbali ina imene mkulu ayenela kukumbukila. Iye angadzifunse kuti, ‘Kodi ndine woyenelela kupeleka uphungu? Kapena kodi uphunguwo angaulandile mosavuta ngati ataupeleka ni munthu wina?’ Mwacitsanzo, munthu amene amavutika na maganizo odziona kukhala wosafunika angalandile uphungu mosavuta ngati wacokela kwa mkulu amene nayenso anakumanapo na vuto limenelo, kuposa uja amene sanakumanepo nalo. Mkulu amene anakumanapo na vutolo angamvetse mmene munthuyo akumvelela, ndipo zimene angakambe zingam’fike msanga pamtima wolandila uphunguwo. Mulimonsemo, akulu onse ali na udindo wolimbikitsa abale na alongo awo kupanga masinthidwe ofunikila mogwilizana na Malemba. Conco, uphungu ukafunikila, uyenela kupelekedwa ndithu.

MUYENELA KUCITA CIANI KUTI MUPELEKE UPHUNGU WOTHANDIZA?

N’cifukwa ciani akulu ayenela kukhala ‘ofulumila kumva’? (Onani ndime 13-14)

13-14. N’cifukwa ciani n’kofunika kuti akulu azimvetsela?

13 Khalani wokonzeka kumvetsela. Mkulu akamakonzekela zokapeleka uphungu, ayenela kudzifunsa kuti: ‘Nidziŵako zotani zokhudza mmene zinthu zilili kwa m’bale wangayo? Kodi zinthu zili bwanji pa umoyo wake? Kodi iye angakhale kuti akukumana na mavuto ine osadziŵa? N’ciani cimene pali pano akufunikila maka-maka?’

14 Mfundo ya pa Yakobo 1:19, imagwila nchito kwa awo amene amapeleka uphungu. Yakobo analemba kuti: “Munthu aliyense akhale wofulumila kumva, wodekha polankhula, wosafulumila kukwiya.” Mwina mkulu angaganize kuti akudziŵa mikhalidwe yonse ya munthu amene akufuna kupatsa uphungu, koma kodi iye adziŵadi zonse? Miyambo 18:13 imatikumbutsa kuti: “Munthu aliyense woyankhila nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amacita manyazi.” Conco, ni bwino kufunsa mwiniwake kuti afotokoze zoona zake. Izi ziphatikizapo kumvetsela coyamba musanalankhule. Kumbukilani zimene anaphunzilapo mkulu amene tachula kuciyambi kwa nkhani ino. Iye anazindikila kuti m’malo mongofikila kufotokoza zimene anakonzekela, coyamba akanayenela kufunsa mlongoyo mafunso monga akuti: “Kodi zinthu zili motani pa umoyo wanu?” “Kodi pali mbali imene tingathandizilepo?” Akulu akamamvetsela coyamba kwa abale na alongo awo kuti adziŵe zimene akupitamo, adzipeleka thandizo lofunikila komanso cilimbikitso.

15. Kodi akulu angaiseŵenzetse bwanji mfundo ya pa Miyambo 27:23?

15 Zidziŵeni bwino nkhosa. Monga takambila kumayambililo, kupeleka uphungu wothandiza sikungoŵelenga cabe malemba angapo kapena kupelekapo malingalilo ayi. Abale na alongo athu ayenela kuona kuti timawadela nkhawa, timawamvetsetsa, komanso tifuna kuwathandiza. (Ŵelengani Miyambo 27:23.) Akulu ayenela kuyesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba na abale na alongo awo.

N’ciani cingathandize akulu kuti kupeleka uphungu kusamawavute? (Onani ndime 16)

16. N’ciani cingathandize akulu kupeleka uphungu wogwila mtima?

16 Akulu ayenela kupewa kupangitsa abale na alongo kuganiza kuti nthawi yokhayo imene amakambilana nawo, ni powapatsa uphungu pamene alakwitsa cina cake. M’malo mwake, iwo ayenela kumaceza nawo nthawi zonse abale na alongo, na kuonetsa kuti amasamala za iwo akakumana na mavuto. Mkulu wina amene ni ciyambakale anati: “Mukacita zimenezo, mudzakhala nawo pa ubwenzi wolimba. Ndiyeno mukaona kuti m’pofunikila kuwapatsa uphungu, cidzakhala cosavuta kwa imwe kucita zimenezo.” Ndipo amene akupatsidwa uphunguwo, sadzavutika kuulandila.

N’cifukwa ciani mkulu ayenela kukhala woleza mtima komanso wacifundo akamapeleka uphungu? (Onani ndime 17)

17. Ni liti maka-maka pamene mkulu ayenela kukhala woleza mtima komanso wacifundo?

17 Khalani woleza mtima komanso wacifundo. Kuleza mtima ndiponso cifundo, n’zofunika kwambili maka-maka ngati wina poyamba akukana uphungu wozikika m’Baibo. Mkulu sayenela kukwiya kapena kukhumudwa ngati amene wapatsa uphungu sanaugwilitsile nchito. Pokamba za Yesu Baibo inati: “Bango lophwanyika sadzalisansantha ndipo nyale yofuka sadzaizimitsa.” (Mat. 12:20) Popemphela payekha, mkulu angapemphe Yehova kuti athandize wopatsidwa uphungu kumvetsa cifukwa cake wapatsidwa uphunguwo, komanso kuti auseŵenzetse. Munthu amene wapatsidwa uphunguwo angafunikile nthawi kuti asinkhesinkhe zimene anauzidwa. Ngati mkulu apeleka uphungu modekha komanso mokoma mtima, cidzakhala cosavuta munthu kuulandila. Ndipo nthawi zonse uphungu uyenela kucokela m’Mawu a Mulungu.

18. (a) Tikamapeleka uphungu, kodi tiyenela kukumbukila ciani? (b) Malinga na cithunzi komanso bokosi, kodi makolo akukambilana ciani?

18 Phunzilamponi kanthu pa zolakwa zanu. Cifukwa ndife opanda ungwilo, n’zosatheka kuseŵenzetsa malangizo a m’nkhani ino ndendende. (Yak. 3:2) Tidzalakwitsabe mbali zina, ndipo zikakhala conco, tiyenela kuphunzilapo kanthu. Abale na alongo athu akaona kuti timawakonda, cidzakhala cosavuta kwa iwo kutikhululukila tikawakhumudwitsa m’mawu kapena m’zocita zathu.—Onani bokosi lakuti “ Mawu kwa Makolo.”

KODI TAPHUNZILA CIANI?

19. Kodi tingausangalatse bwanji mtima wa abale na alongo athu?

19 Monga taonela, si copepuka kupeleka uphungu wothandiza. Ife komanso aja amene tikuwapatsa uphungu tonse ndife opanda ungwilo. Muzikumbukila mfundo zimene takambilana m’nkhani ino. Muzionetsetsa kuti uphungu wapelekedwa na colinga cabwino. Cina, onetsetsani ngati m’pofunikiladi kupeleka uphunguwo, komanso kuti ndinu munthu woyenelela kuupeleka. Musanapeleke uphungu, m’funseni mafunso na kumvetsela mwachelu kuti mudziŵe mavuto amene munthuyo akukumana nawo. Yesani kuona zinthu mmene iye amazionela. Khalani wodekha, ndipo limbitsani ubwenzi na abale na alongo anu. Kumbukilani colinga cathu: Tifuna kuti uphungu wathu ukhale wothandiza, komanso ‘wosangalatsa mtima.’—Miy. 27:9.

NYIMBO 103 Abusa—ni Mphatso za Amuna

^ ndime 5 Nthawi zina, si copepuka kupatsa wina uphungu. Koma ngati pangafunike kutelo, kodi tingapeleke bwanji uphungu m’njila yabwino komanso yolimbikitsa? Nkhani ino, idzathandiza maka-maka akulu kuona mmene angapelekele uphungu m’njila imene ingathandize munthu kuulandila mosavuta.

^ ndime 11 Onani nkhani yakuti, “Kumvetsa Tanthauzo la Umutu Mumpingo” mu Nsanja ya Mlonda ya February 2021.