Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndinapeza Chinthu Chabwino Kwambiri Kuposa Kukhala Dokotala

Ndinapeza Chinthu Chabwino Kwambiri Kuposa Kukhala Dokotala

“ZIMENE mukundiuzazo ndi zomwe ndakhala ndikuzilakalaka kuyambira ndili mwana.” Mwansangala ndinauza mawu amenewa banja lina lomwe linabwera kuchipatala changa mu 1971. Pa nthawiyi ndinali nditangokhala kumene dokotala ndipo ndinatsegula chipatala changa choyamba. Kodi anthu awiri omwe anabwera kuchipatala changawa anali ndani? Nanga zomwe ndinkalakalakazo zinali chiyani? Tadikirani ndikufotokozereni kaye mmene zimene tinakambirana pa tsikuli zinandithandizira kusintha zinthu zomwe ndinkaona kuti ndi zofunika kwambiri, komanso chifukwa chake ndimakhulupirira kuti zinthu zomwe ndinkalakalaka ndili mwana zija zichitika posachedwapa.

Ndinabadwa mu 1941, mumzinda wa Paris ku France m’banja lina lomwe silinali lolemera. Ndinkakonda kwambiri sukulu. Ndiye tangoganizani mmene ndinakhumudwira pamene ndili ndi zaka 10 ndinapezeka ndi TB moti ndinkafunika kusiya kupita kusukulu. Madokotala ananena kuti ndinkafunika ndizigona chifukwa choti mapapo anga anali ofooka. Choncho kwa miyezi ingapo ndinkawerenga dikishonale komanso kumvetsera mapulogalamu apawailesi amaphunziro ochititsidwa ndi yunivesite ya Paris. Pamapeto pake dokotala wanga atanena kuti ndachira, ndipo ndingabwererenso kusukulu, ndinasangalala kwambiri. Ndiye ndinadziuza kuti, ‘Madokotalawa amagwira ntchito yaikulu.’ Kuyambira pamenepo, ndinkafunitsitsa kudzagwira ntchito yochiritsa anthu. Bambo anga akandifunsa kuti ndikufuna kudzachita chiyani ndikadzakula, nthawi zonse ndinkawayankha kuti, “Ndikufuna kudzakhala dokotala.” Umu ndi mmene ndinayambira kukonda ntchito ya udokotala.

SAYANSI INANDITHANDIZA KUTI NDIYAMBE KUKONDA MULUNGU

Banja lathu linali la Katolika. Koma sindinkadziwa zambiri zokhudza Mulungu ndipo ndinali ndi mafunso ambiri omwe ndinalibe mayankho ake. Nditayamba kuphunzira za udokotala kuyunivesite, ndi pamene ndinatsimikizira kuti zamoyo zinachita kulengedwa.

Ndikukumbukira pomwe kwa nthawi yoyamba ndinaona maselo a zomera pa chipangizo choonera tinthu ting’onoting’ono. Ndinachita chidwi ndi mmene tizigawo tamaselo tinkachitira kunja kukamatentha kapena kuzizira. Ndinaonanso kuti timadzi tamuselo timachepa m’madzi a mchere ndipo timakula m’madzi opanda mchere. Zimenezi komanso zinthu zina zomwe zimachitika m’maselo zimathandiza kuti tizilombo ting’onoting’ono tizitha kukhala m’malo osiyanasiyana. Nditaona kuti selo lililonse limachita zinthu mogometsa kwambiri, ndinayamba kukhulupirira kuti moyo sunangokhalapo mwangozi.

M’chaka chachiwiri cha maphunziro anga a udokotala, ndinaona umboni woonjezera woti Mulungu alipo. Pamene tinkaphunzira zokhudza thupi la munthu, tinaona mmene dzanja lathu limathandizira kuti tizitha kupinda kapena kuwongola zala zathu, mmene minofu inalumikizidwira ku mafupa, komanso mmene zonse zimagwirira ntchito limodzi. Zimenezi ndi zogometsa kwambiri. Mwachitsanzo, tinaphunzira kuti pali mtsempha wina umalumikiza mnofu wa dzanja lathu kufupa lachiwiri la chala chathu. Mtsempha umenewu umagawanika pawiri zomwe zimachititsa kuti mtsempha womwe ukupita kunsonga kwa chala chathu udutse pansi pake. Mitsempha imeneyi imagwirana kwambiri ndi mafupa a zala. Zikanakhala kuti zala zathu sizinapangidwe mwanjira imeneyi, mitsemphayi ikanakhala yokungika komanso si bwenzi ikupindika zomwe zikanachititsa kuti zala zathu zisamagwire bwino ntchito. Apa ndinaoneratu kuti thupi la munthu linapangidwa ndi winawake wanzeru kwambiri.

Ndinachitanso chidwi kwambiri ndi Mlengi pamene ndinkaphunzira zokhudza kubadwa kwa mwana. Ndinaphunzira kuti mwana akakhala m’mimba mwa mayi ake, safunikira kupuma chifukwa chakuti amalandira mpweya wa okosijeni kuchokera kwa mayi akewo. Choncho timatumba ting’onoting’ono ta mpweya tomwe timakhala m’mapapo, timakhala kuti tilibe mpweya. Nthawi yoti abadwe ikamayandikira, timadzi tinatake timakuta mkati mwa kathumba kalikonse. Ndiyeno mwana akabadwa, asanapume kwa nthawi yoyamba, pamachitika zinthu zina zochititsa chidwi. Bowo lomwe limakhala pamtima wa mwanayo limatsekeka zomwe zimachititsa kuti magazi ayambe kufika kumapapo. Pa nthawi yofunikayi, timadzi tija timachititsa kuti timatumba ta mpweya timasuke ndipo mudzaze mpweya. Nthawi yomweyo mwanayo amayamba kutha kupuma payekha.

Ndinkafunitsitsa kudziwa yemwe analenga zinthu zodabwitsazi, choncho ndinayamba kuwerenga Baibulo moikirapo mtima. Ndinachita chidwi ndi malamulo okhudza ukhondo omwe Mulungu anapereka kwa Aisiraeli zaka zoposa 3,000 zapitazo. Iye anawalamula kuti azikwirira zoipa, azisamba pafupipafupi komanso azipatula munthu aliyense yemwe akusonyeza zizindikiro za matenda opatsirana. (Lev. 13:50; 15:11; Deut. 23:13) Baibulo linanena zinthu zimenezi, komatu asayansi angotulukira mmene matenda amafalikira m’zaka 150 zapitazi. Ndinazindikiranso kuti malamulo okhudza kugonana omwe ali m’buku la Levitiko ankathandiza kuti Aisiraeli onse akhale a thanzi. (Lev. 12:1-6; 15:16-24) Ndinaona kuti Mlengi anapatsa Aisiraeli malamulowa n’cholinga choti zinthu ziziwayendera bwino ndipo ankadalitsa anthu omwe ankatsatira malamulo akewo. Ndinatsimikiza kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu yemwe pa nthawiyi sindinkadziwa dzina lake.

MMENE NDINAPEZERA MKAZI WANGA KOMANSO KUDZIWA YEHOVA

Ine ndi Lydie pa tsiku la ukwati wathu, pa 3 April 1965

Pamene ndinkachita maphunziro anga a udokotala kuyunivesite, ndinakumana ndi mtsikana wina dzina lake Lydie yemwe ndinagwa naye m’chikondi. Tinakwatirana mu 1965 nditatsala pang’ono kumaliza maphunziro anga. Pofika mu 1971, ine ndi Lydie tinali kale tili ndi ana atatu pa ana 6 omwe tinabereka. Lydie wakhala akundithandiza kwambiri pa ntchito yanga ya udokotala komanso m’banja lathu.

Ndinagwira ntchito pachipatala china kwa zaka zitatu ndisanakhale ndi chipatala changa. Patangopita kanthawi kochepa, banja lina lomwe ndalitchula kumayambiriro lija linabwera kuti ndidzalithandize. Pamene ndinkati ndizilembera mwamunayo mankhwala, mkazi wake ananena kuti: “Adokotala! Chonde m’mankhwalawo musakhale magazi.” Modabwa ndinafunsa kuti: “Zoona? Chifukwa chiyani?” Iye anayankha kuti: “Ndife a Mboni za Yehova.” Ndinali ndisanamvepo zokhudza a Mboni za Yehova kapenanso zimene amakhulupirira pa nkhani ya magazi. Mkaziyo anatenga Baibulo lake n’kundionetsa mfundo za m’Malemba zomwe zimawachititsa kuti azikana magazi. (Mac. 15:28, 29) Kenako iye ndi mwamuna wake anapitiriza kundisonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite monga kuthetsa mavuto, matenda komanso imfa. (Chiv. 21:3, 4) Mosangalala ndinanena kuti: “Zimene mukundiuzazi ndi zimene ndakhala ndikulakalaka kuyambira ndili mwana. Ndinasankha kukhala dokotala kuti ndizithandiza anthu amene akuvutika.” Ndinasangalala kwambiri moti tinakambirana kwa ola limodzi ndi hafu. Pamene banjali linkachoka, mumtima mwanga sindinkaonanso kuti ndine Mkatolika ndipo ndinaphunzira kuti Mlengi amene ankandichititsa chidwi uja ali ndi dzina ndipo dzina lake ndi Yehova.

Ndinakumana katatu ndi banja la a Mboni lija kuchipatala kwanga ndipo pa nthawi iliyonse yomwe takumana, tinkakambirana koposa ola limodzi. Ndinawaitanira kunyumba kwanga kuti tikhale ndi nthawi yokwanira yokambirana mfundo za m’Baibulo. Ngakhale kuti Lydie anavomera kumakhala nawo tikamaphunzira Baibulo, sankavomereza kuti mfundo zina zomwe tinkaphunzitsidwa ku Katolika sizinali zoona. Choncho ndinaitana wansembe kuti abwere kunyumba kwathu. Tinakambirana mpaka usiku pogwiritsa ntchito Baibulo kuti tione ngati zimene tchalitchichi chimaphunzitsa zili zoona. Zimene tinakambirana tsiku limeneli zinamutsimikizira Lydie kuti a Mboni za Yehova amaphunzitsa choonadi. Kuchokera pa nthawi imeneyo, tinayamba kukonda kwambiri Yehova moti mpaka tonse tinabatizidwa mu 1974.

NDINAYAMBA KUIKA YEHOVA PAMALO OYAMBA

Zimene ndinaphunzira zokhudza cholinga cha Mulungu, zinakhudza kwambiri zinthu zomwe ndinkaona kuti ndi zofunika. Ine ndi Lydie tinayamba kuona kuti kutumikira Yehova ndiye kofunika kwambiri pa moyo wathu. Tinkafunitsitsa kuti tizilera ana athu mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Tinawaphunzitsa kuti azikonda Mulungu komanso anthu, ndipo zimenezi zinachititsa kuti tizigwirizana kwambiri m’banja lathu.​—Mat. 22:37-39.

Nthawi zambiri ine ndi Lydie timaseka tikamakumbukira mmene ana athu ankaonera kuti ndife ogwirizana. Iwo ankadziwa kuti malangizo a Yesu onena kuti “mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi,” ndi amene tinkatsatira m’banja lathu. (Mat. 5:37) Mwachitsanzo, mwana wathu wina wamkazi ali ndi zaka 17, Lydie sanamulole kuti apite kokacheza ndi anzake. Mnzake wina pagululo anauza mwana wathuyo kuti, “Ngati mayi ako akukuletsa, kapemphe kwa bambo ako.” Koma mwana wathuyo anayankha kuti: “Sizingathandize zimenezo. Nthawi zonse amachita zinthu mogwirizana.” Ana athu 6 ankaoneratu kuti timagwirizana potsatira mfundo za m’Baibulo. Timayamikira Yehova kuti anthu ambiri m’banja mwathu akumutumikira.

Ngakhale kuti zinthu zomwe ndinkaona kuti ndi zofunika zinasintha chifukwa chophunzira choonadi, ndinkafuna kugwiritsa ntchito luso langa la za udokotala pothandiza anthu a Mulungu. Choncho ndinadzipereka kuti ndizikathandiza zachipatala ku Beteli ya ku Paris, yomwe kenako anaisamutsira ku Louviers. Ndakhala ndikuchita utumiki woyendera pa Beteli kwa zaka pafupifupi 50. Pa nthawi imeneyi ndakhala ndi mwayi wopeza anzanga abwino m’banja la Beteli ndipo ena ali ndi zaka za m’ma 90. Tsiku lina ndinasangalala kwambiri nditakumana ndi m’bale wina wachinyamata, yemwe anali atangofika kumene kudzachita utumiki wa pa Beteli. Ndinali dokotala amene anathandiza mayi ake pamene iye ankabadwa zaka 20 m’mbuyomo.

NDAONA MMENE YEHOVA AMASAMALIRA ANTHU AKE

Kwa zaka zambiri, ndaona mmene Yehova amatsogolera komanso kutetezera anthu ake pogwiritsa ntchito gulu lake ndipo zimenezi zachititsa kuti ndizimukonda kwambiri. Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1980, Bungwe Lolamulira linakonza pulogalamu yothandiza madokotala ku United States kuti azimvetsa zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira pa nkhani ya magazi.

Kenako mu 1988, Bungwe Lolamulira linakhazikitsa dipatimenti yatsopano pa Beteli, yoyang’anira zachipatala. Poyamba, depatimentiyi inkayang’anira Makomiti Olankhulana ndi Achipatala omwe anakhazikitsidwa m’dziko la United States kuti azithandiza a Mboni kulandira thandizo loyenera. Makomitiwa anayamba kukhazikitsidwanso padziko lonse kuphatikizapo ku France. Ndimachita chidwi kuona mmene gulu la Yehova limathandizira mwachikondi abale ndi alongo omwe akudwala pa nthawi yomwe akufunikira thandizo.

ZIMENE NDINKAFUNA ZINACHITIKA

Timasangalala kugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu

Poyamba ndinkakonda kwambiri za udokotala. Koma kenako tinazindikira kuti chofunika kwambiri ndi kuthandiza anthu kuti akhale pa ubwenzi ndi Mulungu zomwe zili ngati kuwachiritsa mwauzimu. Nditapuma pa ntchito, tinayamba kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu kwa maola ambiri mwezi uliwonse ngati apainiya okhazikika. Panopa timachita zonse zomwe tingathe pa ntchito yopulumutsa moyo imeneyi.

Ine ndi Lydie mu 2021

Ndikupitirizabe kuchita zomwe ndingathe pothandiza anthu omwe akudwala. Komabe ndimadziwa kuti ngakhale dokotala yemwe ndi wodziwa kwambiri ntchito yake, sangakwanitse kuchiritsa matenda onse kapenanso kuthandiza anthu kuti asamafe. Choncho ndikuyembekezera mwachidwi nthawi imene kupweteka, kudwala komanso imfa sizidzakhalaponso. M’dziko latsopano lomwe likubwera, ndidzakhala ndi moyo mpaka kalekale zomwe zidzandithandize kuphunzira zokhudza zimene Mulungu analenga, kuphatikizapo thupi la munthu lomwe analipanga modabwitsa kwambiri. N’zoona kuti zina zomwe ndinkalakalaka ndili mwana zakwaniritsidwa koma ndikukhulupirira kuti zabwino zili m’tsogolo.