Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 10

Mukhoza ‘Kuvula Umunthu Wakale’

Mukhoza ‘Kuvula Umunthu Wakale’

“Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.”​—AKOL. 3:9.

NYIMBO NA. 29 Tizichita Zinthu Zogwirizana ndi Dzina Lathu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi moyo wanu unali wotani musanayambe kuphunzira Baibulo?

 KODI zinthu zinali bwanji pa moyo wanu musanayambe kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova? Ambirife sitingakonde n’komwe kuti tiziganizira zimenezo. N’kutheka kuti mfundo za m’dzikoli zokhudza chabwino ndi choipa ndi zimene zinaumba umunthu wathu komanso mmene tinkaonera zinthu. Ngati ndi choncho, ndiye kuti ‘tinalibe chiyembekezo ndipo tinalibe Mulungu m’dzikoli.’ (Aef. 2:12) Koma titaphunzira Baibulo tinasintha moyo wathu.

2. Kodi munazindikira chiyani mutayamba kuphunzira Baibulo?

2 Mutayamba kuphunzira Baibulo munazindikira kuti muli ndi Atate wanu wakumwamba yemwe amakukondani kwambiri. Munazindikiranso kuti, kuti muzisangalatsa Yehova komanso kukhala m’banja lake la anthu amene amamulambira, muyenera kusintha moyo wanu, mmene mumaganizira komanso mmene mumaonera zinthu. Munkafunika kuphunzira kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake zapamwamba.​—Aef. 5:3-5.

3. Mogwirizana ndi Akolose 3:9, 10, kodi Yehova amafuna kuti tichite chiyani, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Yehova ndi Mlengi komanso Atate wathu wakumwamba. Choncho ali ndi ufulu wosankha mmene anthu a m’banja lake ayenera kumachitira zinthu. Ndipo iye amafuna kuti tisanabatizidwe, tiyesetse ‘kuvula umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.’ * (Werengani Akolose 3:9, 10.) Nkhaniyi ithandiza anthu amene akufuna kubatizidwa kupeza mayankho a mafunso atatu awa: (1) Kodi “umunthu wakale” n’chiyani? (2) N’chifukwa chiyani Yehova amatilimbikitsa kuti tiuvule? (3) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Kwa amene tinabatizidwa kale, nkhaniyi itithandiza kuti tisayambirenso kukhala ndi makhalidwe amene tinali nawo tisanavule umunthu wakale.

KODI “UMUNTHU WAKALE” N’CHIYANI?

4. Kodi munthu amene amalamuliridwa ndi “umunthu wakale” amachita zotani?

4 Munthu amene amalamuliridwa ndi “umunthu wakale” nthawi zambiri amaganiza komanso kuchita zinthu zoipa. Angakhale wodzikonda, wosachedwa kukwiya, wosayamika komanso wonyada. Angamasangalale kuonera zolaula, mafilimu achiwawa kapenanso osonyeza makhalidwe ena oipa. Mosakayikira munthuyo angakhale ndi makhalidwe ena abwino ndipo angamadziimbe mlandu chifukwa cha zinthu zoipa zimene walankhula kapena kuchita. Koma iye angakhale kuti alibe cholinga choti asinthe kaganizidwe komanso makhalidwe ake.​—Agal. 5:19-21; 2 Tim. 3:2-5.

Maganizo ndi makhalidwe oipa satilamuliranso tikavula “umunthu wakale” (Onani ndime 5) *

5. Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo oyenera ati pa nkhani yovula umunthu wakale? (Machitidwe 3:19)

5 Tonsefe si angwiro, choncho palibe amene angachotseretu maganizo oipa komanso zimene mtima wathu umalakalaka. Nthawi zina tingalankhule kapena kuchita zinthu zimene tinganong’oneze nazo bondo. (Yer. 17:9; Yak. 3:2) Koma tikavula umunthu wakale, sitilamuliridwanso ndi maganizo komanso makhalidwe oipa. Timasinthiratu n’kukhala munthu watsopano.​—Yes. 55:7; werengani Machitidwe 3:19.

6. N’chifukwa chiyani Yehova amatilimbikitsa kuti tisiye maganizo ndi makhalidwe oipa omwe amagwirizana ndi umunthu wakale?

6 Yehova amatilimbikitsa kuti tisiye maganizo komanso makhalidwe oipa amene tinazolowera chifukwa choti amatikonda kwambiri ndipo amafuna kuti tizisangalala ndi moyo. (Yes. 48:17, 18) Iye amadziwa kuti anthu amene amangotsatira zinthu zoipa zomwe amalakalaka amadzivulaza okha komanso anthu ena. Zimam’pweteka kutiona tikuchita zinthu zimene zingativulaze komanso zimene zingavulaze anthu ena.

7. Mogwirizana ndi Aroma 12:1, 2, kodi timayenera kusankha kuchita chiyani?

7 Poyamba mwina anzathu kapena achibale angamatinyoze chifukwa choyesetsa kusintha makhalidwe athu. (1 Pet. 4:3, 4) Iwo angamatiuze kuti tili ndi ufulu wochita chilichonse chimene tikufuna komanso kuti sitiyenera kulola aliyense kutiuza zochita. Koma amene amakana mfundo za Yehova zokhudza chabwino ndi choipa sikuti amakhaladi pa ufulu. M’malomwake, iwo amakhala kuti akulola dziko lolamulidwa ndi Satanali liziwaumba. (Werengani Aroma 12:1, 2.) Tonsefe tiyenera kusankha kuti kaya tipitirizabe kukhala ndi umunthu wathu wakale, womwe umatsogoleredwa ndi uchimo ndi dziko la Satanali, kapena kulola kuti Yehova atisinthe n’kukhala munthu wabwino kwambiri panopa.​—Yes. 64:8.

KODI TINGATANI KUTI ‘TIVULE’ UMUNTHU WAKALE?

8. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizipewa maganizo komanso makhalidwe olakwika?

8 Yehova amadziwa kuti pamafunika nthawi komanso khama kuti tizipewa maganizo ndi makhalidwe oipa. (Sal. 103:13, 14) Komabe pogwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu wake ndi gulu lake, Yehova amatipatsa nzeru, mphamvu komanso kutithandiza kuti tisinthe. N’zosakayikitsa kuti inunso wakuthandizani kale. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zina zimene zingakuthandizeni kuti mupitirizebe kuvula umunthu wakale kuti muyenerere kubatizidwa.

9. Kodi Mawu a Mulungu angakuthandizeni kuchita chiyani?

9 Muzigwiritsa ntchito Baibulo podzifufuza. Mawu a Mulungu ali ngati galasi. Angakuthandizeni kuti mudziwe mmene mumaganizira, mmene mumalankhulira komanso mmene mumachitira zinthu. (Yak. 1:22-25) Munthu amene amakuphunzitsani Baibulo komanso Akhristu ena olimba mwauzimu angakupatseni malangizo. Mwachitsanzo, iwo angagwiritse ntchito Malemba pokuthandizani kudziwa zimene mumachita bwino komanso zofooka zanu. Angakuthandizeni kudziwa mmene mungapezere mfundo za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kuti musiye makhalidwe oipa. Ndipo nthawi zonse Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani. Iye amadziwa bwino mmene angakuthandizireni chifukwa amadziwa zimene zili mumtima mwanu. (Miy. 14:10; 15:11) Choncho muzikhala ndi chizolowezi chopemphera kwa iye komanso kuphunzira Mawu ake tsiku lililonse.

10. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Elie?

10 Musamakayikire kuti mfundo za Yehova ndi zabwino kwambiri. Tikhoza kupindula ndi zonse zimene Yehova amatiuza kuti tizichita. Anthu amene amatsatira mfundo zake amalemekezedwa, amakhala ndi moyo watanthauzo komanso amapeza chimwemwe chenicheni. (Sal. 19:7-11) Koma anthu amene amanyalanyaza mfundo za Yehova amakumana ndi mavuto amene amabwera chifukwa chochita ntchito zathupi. Taonani zimene munthu wina dzina lake Elie ananena pa nkhani yokana kutsatira mfundo za Yehova. Iye analeredwa ndi makolo okonda Yehova. Koma pamene ankakula ankacheza ndi anthu oipa. Kenako anayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kuchita chiwerewere komanso kuba. Elie anaona kuti anayamba kumakhala wokwiya kwambiri komanso kuchita chiwawa. Iye anati: “Ndinganene kuti ndinkachita zonse zimene ndinaphunzitsidwa kuti Mkhristu sayenera kuchita.” Komabe Elie sanaiwale zimene anaphunzitsidwa ali mwana. Kenako anayambiranso kuphunzira Baibulo. Anachita khama kuti asiye makhalidwe oipa ndipo anabatizidwa m’chaka cha 2000. Kodi kutsatira mfundo za Yehova kunamuthandiza bwanji? Ellie anati: “Panopa ndili ndi mtendere wamumtima komanso chikumbumtima chabwino.” * Monga mmene chitsanzochi chikusonyezera, anthu amene amakana mfundo za Yehova amadzivulaza okha. Ngakhale zili choncho, Yehova ndi wofunitsitsa kuwathandiza kuti asinthe.

11. Kodi Yehova amadana ndi zinthu ziti?

11 Phunzirani kudana ndi zimene Yehova amadana nazo. (Sal. 97:10) Baibulo limasonyeza kuti Yehova amadana ndi ‘maso odzikweza, lilime lonama ndi manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.’ (Miy. 6:16, 17) Komanso “munthu wokhetsa magazi ndi wachinyengo, Yehova amaipidwa naye.” (Sal. 5:6) Yehova amadana kwambiri ndi anthu a makhalidwe amenewa moti anawononga anthu onse oipa munthawi ya Nowa chifukwa anadzaza dzikoli ndi zinthu zachiwawa. (Gen. 6:13) Taganizirani chitsanzo china ichi: Kudzera mwa mneneri Malaki, Yehova ananena kuti amadana ndi anthu amene mwachinyengo amasiya akazi awo omwe ndi osalakwa. Iye savomereza kulambira kwa anthu otere, ndipo adzawaimba mlandu chifukwa cha makhalidwe awo.​—Mal. 2:13-16; Aheb. 13:4.

Tiyenera kunyansidwa ndi kuchita zimene Yehova amanena kuti n’zoipa ngati mmene timachitira ndi chakudya chowola (Onani ndime 11-12)

12. Kodi ‘kunyansidwa ndi choipa’ kumatanthauza chiyani?

12 Yehova amafuna kuti ‘tizinyansidwa ndi choipa.’ (Aroma 12:9) Mawu akuti ‘kunyansidwa,’ amafotokoza za kuipidwa kwambiri ndi chinthu chinachake. Taganizirani mmene mungamvere ngati mutauzidwa kuti mudye chakudya chowola. Kungoganizira kokha zimenezi kungachititse kuti musamamve bwino. Mofanana ndi zimenezi, ngakhale maganizo ofuna kuchita zinthu zimene Yehova amanena kuti n’zoipa, ayenera kukhala chinthu chonyansa kwa ife.

13. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuteteza maganizo athu?

13 Muziteteza maganizo anu. Anthufe timachita zimene timaganiza. N’chifukwa chake Yesu anaphunzitsa kuti tizikana maganizo omwe angachititse kuti tichite tchimo lalikulu. (Mat. 5:21, 22, 28, 29) Timafuna kusangalatsa Atate wathu wakumwamba. Choncho n’zofunika kwambiri kuti tizichotsa mwamsanga maganizo alionse oipa omwe tingakhale nawo.

14. Kodi zimene timalankhula zimasonyeza chiyani zokhudza ifeyo, nanga ndi mafunso ati amene tiyenera kudzifunsa?

14 Muzilamulira lilime lanu. Yesu anati: “Zotuluka m’kamwa zimachokera mumtima.” (Mat. 15:18) Zimenetu ndi zoona, chifukwa zimene timalankhula zimasonyeza kuti ndife anthu otani. Choncho muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndimapewa kunama ngakhale kuti kunena zoona kungachititse kuti ndikumane ndi mavuto? Ngati ndili pa banja, kodi ndimapewa kukopana ndi anthu amene si amuna kapena akazi anzanga? Kodi ndimapeweratu kulankhula mawu otukwana? Kodi ndimalankhula modekha munthu wina akandikhumudwitsa?’ Ndi zothandiza kwambiri kumaganizira mafunso ngati amenewa. Zimene mumalankhula zili ngati ulusi umene umalumikiza nsalu za chovala. Mukamayesetsa kupewa mawu oipa, kunama kapena kulankhula mawu otukwana mukamalankhula ndi ena, mudzaona kuti n’zosavuta kuvula umunthu wakale.

15. Kodi kupachika umunthu wathu wakale “pamtengo” kumatanthauza chiyani?

15 Muzikhala ofunitsitsa kuchita zoyenera. Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo chabwino kwambiri chosonyeza kuti tiyenera kutsimikiza mtima kusintha zinthu pa moyo wathu. Iye analemba kuti tiyenera kupachika umunthu wathu wakale “pamtengo.” (Aroma 6:6) M’mawu ena, tiyenera kutsanzira Khristu. Tifunika kuthetseratu maganizo ndi makhalidwe amene Yehova amadana nawo. Tikamatsatira malangizo amenewa ndi pamene tingakhale ndi chikumbumtima chabwino komanso chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha. (Yoh. 17:3; 1 Pet. 3:21) Tizikumbukira kuti Yehova sangasinthe mfundo zake n’cholinga chofuna kungotisangalatsa. M’malomwake, ifeyo tiyenera kusintha kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake.​—Yes. 1:16-18; 55:9.

16. N’chifukwa chiyani muyenera kutsimikiza mtima kuti mupitirizebe kulimbana ndi zofooka zanu?

16 Tisasiye kulimbana ndi zofooka zathu. Ngakhale pamene mwabatizidwa mumafunika kupitiriza kulimbana ndi zilakolako zoipa. Taganizirani chitsanzo cha Maurício. Ali wamng’ono, anayamba kuchita khalidwe logonana ndi amuna anzake. Kenako anakumana ndi anthu a Yehova ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. Atasintha zinthu pa moyo wake, anabatizidwa mu 2002. Ngakhale kuti wakhala akutumikira Yehova kwa zaka zambiri, Maurício ananena kuti: “Ndivomereze kuti nthawi zina ndimalimbanabe ndi zilakolako zoipa.” Koma iye samalola kuti zimenezi zimufooketse. M’malomwake iye anati: “Ndimalimbikitsidwa kudziwa kuti ndikasankha kusachita zimene ndikulakalakazo, ndikhoza kusangalatsa Yehova.” *

17. Kodi zimene zinachitikira Nabiha zakulimbikitsani bwanji?

17 Tizipempha Yehova kuti atithandize ndipo tizidalira mzimu wake osati mphamvu zathu. (Agal. 5:22; Afil. 4:6) Tiyenera kukhala otsimikiza mtima kuti tivule umunthu wakale ndiponso kuti tisauvalenso. Taganizirani chitsanzo cha mayi wina dzina lake Nabiha. Bambo ake anamuthawa ali ndi zaka 6 zokha. Iye anati: “Zimenezi zinachititsa kuti ndizivutika kwambiri maganizo.” Pamene ankakula, Nabiha ankangokhala wolusa ndipo sankachedwa kupsa mtima. Iye ankazembetsa mankhwala osokoneza bongo ndipo anamangidwa n’kukakhala m’ndende zaka zingapo. A Mboni ena amene anapita kundende imene iye anali, anayamba kuphunzira naye Baibulo. Nabiha anayamba kusintha kwambiri zinthu pa moyo wake. Iye anati: “Zoipa zina zomwe ndinkachita sizinandivute kuzisiya. Koma ndinavutika kwambiri kuti ndisiye kusuta.” Nabiha anavutika kwa chaka chathunthu ndipo kenako anakwanitsa kusiya chizolowezi chimenechi. Kodi n’chiyani chinamuthandiza? Iye anati: “Koposa zonse, kupemphera kwambiri kwa Yehova ndi kumene kunandithandiza.” Panopa iye amauza ena kuti: “Ndine wotsimikiza kuti ngati ineyo ndinakwanitsa kusintha kuti ndizisangalatsa Yehova, ndiye kuti aliyense angakwanitse.” *

INUNSO MUNGAKHALE WOYENERA KUBATIZIDWA

18. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 6:9-11, kodi atumiki ambiri a Mulungu akwanitsa kuchita chiyani?

18 Munthawi ya atumwi, amuna ndi akazi ena omwe Yehova anawasankha kuti akalamulire limodzi ndi Khristu, pa nthawi ina anali oti ankachita makhalidwe oipa. Mwachitsanzo, iwo ankachita zachiwerewere, kugonana amuna kapena akazi okhaokha komanso ankaba. Koma mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, anakwanitsa kusintha makhalidwe awo. (Werengani 1 Akorinto 6:9-11.) Masiku anonso Baibulo lathandiza anthu ambiri kusintha zinthu pa moyo wawo. * Iwo akwanitsa kusiya makhalidwe oipa omwe anali ovuta kwambiri kuti awasiye. Chitsanzo chawo chikusonyeza kuti inunso mukhoza kusintha komanso kusiya makhalidwe oipa n’kukhala woyenera kubatizidwa.

19. Kodi nkhani yotsatira ifotokoza chiyani?

19 Kuwonjezera pa kuyesetsa kuti avule umunthu wakale, amene akufuna kubatizidwa ayeneranso kuchita khama kuti avale umunthu watsopano. Nkhani yotsatira ifotokoza mmene tingachitire zimenezi komanso mmene ena angatithandizire.

NYIMBO NA. 41 Mulungu Imvani Pemphero Langa

^ ndime 5 Kuti tifike pobatizidwa, timafunika kusintha makhalidwe athu. Nkhaniyi itithandiza kudziwa kuti ndi makhalidwe ati amene amapanga umunthu wakale, chifukwa chake tiyenera kuwasiya komanso mmene tingachitire zimenezo. Nkhani yotsatira idzafotokoza zimene tingachite kuti tipitirize kuvala umunthu watsopano ngakhale pamene tabatizidwa.

^ ndime 3 TANTHAUZO LA MAWU ENA: ‘Kuvula umunthu wakale,’ kumatanthauza kusiya makhalidwe ndi zizolowezi zimene sizisangalatsa Yehova ndipo tiyenera kuchita zimenezi tisanabatizidwe.​—Aef. 4:22.

^ ndime 10 Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti, “Baibulo Limasintha Anthu​—‘Ndinazindikira Kuti Ndiyenera Kubwerera kwa Yehova,’” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2012.

^ ndime 16 Kuti mudziwe zambiri onani nkhani yakuti, “Baibulo Limasintha Anthu​—‘Anandikomera Mtima Kwambiri,’” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2012.

^ ndime 17 Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti, “Baibulo Limasintha Anthu​—‘Ndinali Munthu Waukali Komanso Wosachedwa Kupsa Mtima,’” mu Nsanja ya Olonda October 1, 2012.

^ ndime 18 Onani bokosi lakuti, “ Baibulo Limasintha Anthu.”

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kusiya maganizo ndi makhalidwe oipa kuli ngati kuvula chovala chakale.