Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 12

Kodi Mumatha Kuona Zimene Zekariya Anaona?

Kodi Mumatha Kuona Zimene Zekariya Anaona?

“‘Koma mzimu wanga,’ watelo Yehova wa makamu.”—ZEK. 4:6.

NYIMBO 73 Tilimbitseni Mtima

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Ayuda omasulidwa mu ukapolo anali kuyembekezela cinthu cokondweletsa citi?

 AYUDA anakondwela ngako pamene Yehova “analimbikitsa mtima wa Koresi mfumu ya Perisiya,” kumasula Aisiraeli amene anali mu ukapolo ku Babulo kwa zaka zambili. Mfumuyo inalengeza kuti Ayuda abwelele kudziko la kwawo, “n’kukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli.” (Ezara 1:1, 3) Cinali cilengezo cokondweletsa kwambili! Izi zinatanthauza kuti kulambila Mulungu woona kunali kudzabwezeletsedwa m’dziko limene iye anapatsa anthu ake.

2. Kodi cinthu coyamba cimene Ayuda ocoka ku ukapolo anacita cinali ciyani?

2 Mu 537 B.C.E., Ayuda amene anayambilila kucoka ku ukapolo anafika ku Yerusalemu, limene linali likulu la ufumu wa kum’mwela wa Yuda. Posakhalitsa, Ayuda obwelelawo anayamba kumanga kacisi, ndipo podzafika mu 536 B.C.E., anali atatsiliza kale kuyala maziko a kacisiyo.

3. Kodi Ayuda anakumana na citsutso cotani?

3 Komabe, Ayudawo atangoyamba kumanganso kacisi, anayamba kutsutsidwa kwambili. Anthu owazungulila “anakhala akufooketsa manja a anthu a ku Yuda ndi kuwagwetsa ulesi pa nchito yomanga.” (Ezara 4:4) Izi zinali zovuta kwambili kwa iwo. Koma zinaposa pamenepo. Mu 522 B.C.E., Aritasasita, mfumu yatsopano ya Perisiya anayamba kulamulila. * Otsutsawo anaona kuti kusintha kwa ulamulilo kumeneko, unali mwayi wawo wakuti aletseletu nchito yomangayo ‘poyambitsa mavuto mwa kupanga malamulo.’ (Sal. 94:20) Conco mwa zina, iwo anauza Mfumu Aritasasita kuti Ayuda akufuna kupandukila ulamulilo wake. (Ezara 4:11-16) Mfumuyo inakhulupilila mabodza awo, ndipo inaika ciletso pa nchito yomanga kacisi. (Ezara 4:17-23) Cifukwa ca ciletso cimeneco, Ayuda analeka kumanga kacisi.—Ezara 4:24.

4. Kodi Yehova anacita ciyani anthu otsutsa ataletsa nchito yomanga kacisi? (Yesaya 55:11)

4 Anthu a m’dzikolo osalambila Yehova, komanso anthu ena mu ufumu wa Perisiya anayesetsa kuletsa nchito yomanganso kacisi. Koma Yehova anafuna kuti nchitoyo ipitilizebe, ndipo iye nthawi zonse amakwanilitsa cifunilo cake. (Ŵelengani Yesaya 55:11.) Conco, anasankha mneneli wolimba mtima Zekariya, na kumuonetsa masomphenya 8 ocititsa cidwi. Kenako, Zekariya anali kudzafotokozela Ayuda masomphenyawo kuti awalimbikitse. Masomphenya olimbikitsa amenewo, anawathandiza kuona kuti sanayenela kuopa anthu owatsutsa, komanso anawalimbikitsa kupitiliza kugwila nchito ya Yehova. M’masomphenya acisanu, Zekariya anaona coikapo nyale na mitengo iŵili ya maolivi.

5. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

5 Tonsefe timalefulidwa nthawi zina. Koma tingapindule na cilimbikitso cimene Yehova anapatsa Aisiraeli kupitila m’masomphenya acisanu a Zekariya. M’nkhani ino, tikambilane mmene kumvetsa masomphenyawo kungatithandizile kutumikila Yehova mokhulupilika tikamatsutsidwa, zinthu zikasintha pa umoyo wathu, komanso tikalandila malangizo amene sitinawamvetsetse.

TIKAMATSUTSIDWA

Zekariya anaona masomphenya a mitengo iŵili ya maolivi, imene inali kuthila mafuta pa coikapo nyale cokhala na nyale 7 (Onani ndime 6)

6. Kodi masomphenya a coikapo nyale na mitengo iŵili ya maolivi ochulidwa pa Zekariya 4:1-3, anawalimbikitsa bwanji Ayuda? (Onani cithunzi pacikuto.)

6 Ŵelengani Zekariya 4:1-3. Masomphenya a coikapo nyale na mitengo iŵili ya maolivi, inathandiza Ayuda kugonjetsa citsutso. Motani? Kodi mwaona kuti coikapo nyaleco cinali kulandilabe mafuta a nyale? Mitengo iŵili ya maolivi inali kuthila mafuta m’mbale yoloŵa. Ndiyeno mbaleyo inali kuthila mafutawo ku nyale 7 zimene zinali pa coikapo nyale cija. Mafutawo anali kupangitsa kuti nyalezo zipitilize kuyaka. Zekariya anafunsa kuti: “Kodi zimenezi zikuimila ciyani?” Mngelo anayankha na mawu a Yehova akuti: “‘Sipakufunika gulu lankhondo, kapena mphamvu, koma mzimu wanga,’ watelo Yehova wa makamu.” (Zek. 4:4, 6) Mafuta ocokela ku mitengo, aimila mzimu woyela wamphamvu wa Yehova umene sumatha. Magulu onse ankhondo mu ufumu wa Perisiya sanali kanthu powayelekezela na mphamvu ya mzimu wa Mulungu. Pokhala na Yehova kumbali yawo, omanga kacisiwo akanatha kugonjetsa citsutso ciliconse, na kutsiliza nchito yawo. Uwu unali uthenga wolimbikitsa ngako! Zimene Ayuda anayenela kucita ni kudalila Yehova, na kubwelela ku nchito yawo. Izi n’zimene iwo anacita olo kuti ciletso cinali cikalipobe.

7. N’kusintha kotani kunabweletsa mpumulo kwa omanga kacisi?

7 Kusintha kunabweletsa mpumulo kwa omanga kacisi. N’kusintha kotani? Mu 520 B.C.E., Dariyo Woyamba anakhala mfumu ya Perisiya. M’caka caciŵili ca ulamulilo wake, iye anazindikila kuti ciletso cimene cinaikidwa pa nchito yomanga kacisi n’cosagwilizana na malamulo. Conco, analamula Ayuda kuti atsilize nchito yawo. (Ezara 6:1-3) Nkhaniyo inadabwitsa aliyense. Koma mfumuyo inacita zoposa pamenepo. Inalamula kuti anthu owazungulila aleke kusokoneza nchito yomangayo, komanso kuti apeleke ndalama na zinthu zina zothandizila pa nchitoyo. (Ezara 6:7-12) Cotulukapo n’cakuti Ayuda anatsiliza kumanga kacisi mu 515 B.C.E., pambuyo pa zaka zinayi.—Ezara 6:15.

Dalilani mphamvu za Yehova mukamatsutsidwa (Onani ndime 8)

8. N’cifukwa ciyani muyenela kukhala wolimba mtima pamene mukutsutsidwa?

8 Masiku anonso, atumiki a Yehova ambili amatsutsidwa. Mwacitsanzo, ena amakhala ku maiko amene nchito yathu ni yoletsedwa. M’maiko otelo, abale athu angamangidwe na ‘kuwatengela kwa abwanamkubwa na mafumu,’ kuti ukhale umboni kwa iwo. (Mat. 10:17, 18) Nthawi zina, kusintha kwa ulamulilo kungabweletse mpumulo. Kapena woweluza wokoma mtima angapeleke ciweluzo cimene cingakomele abale athu. Mboni zina zimakumana na citsutso cosiyanako. Zimatsutsidwa na a m’banja mwawo amene akuyesetsa kuwaletsa kutumikila Mulungu, ngakhale kuti m’dziko limene akukhala muli ufulu wolambila Yehova. (Mat. 10:32-36) Nthawi zambili, otsutsawo amaleka kutsutsa abale awo akaona kuti alephela kuwaletsa kutumikila Mulungu wawo. Ndipo nthawi zina, aja amene anali otsutsa kwambili afika pokhala Mboni zokangalika. Motelo, mukakumana na citsutso, musafooke. Khalani wolimba mtima, cifukwa Yehova na mzimu wake woyela wamphamvu ali ku mbali yanu. Conco, palibe cifukwa coopela.

ZINTHU ZIKASINTHA

9. N’cifukwa ciyani Ayuda ena sanakondwele ataona maziko a kacisi watsopano?

9 Maziko a kacisi watsopano atayalidwa, Ayuda ena okalamba analila. (Ezara 3:12) Iwo anaona kuti kacisi amene Solomo anamanga, anali waulemelelo kusiyana na kacisi watsopano amene anali kudzamangidwa. (Hag. 2:2, 3) Iwo sanakondwele na kacisi watsopanoyo poyelekezela na wakale. Koma masomphenya a Zekariya anawathandiza kukhalanso acimwemwe. Motani?

10. Kodi mawu a pa Zekariya 4:8-10, anawathandiza bwanji Ayuda kukhalanso acimwemwe?

10 Ŵelengani Zekariya 4:8-10. Kodi mngelo anatanthauza ciyani pamene anati Ayuda “adzasangalala ndi nchito imeneyi ndipo adzaona cingwe ca mmisili womanga nyumba m’dzanja la [bwanamkubwa waciyuda] Zerubabele”? Cingwe ca mmisili womanga ni cida cimene amaseŵenzetsa kuti apime ngati cinthu n’coongoka bwino-bwino. Conco, mngelo anali kutsimikizila anthu a Mulungu kuti ngakhale kuti kacisi sadzakhala waulemelelo monga wa poyamba, adzamalizidwa kumangidwa, ndipo adzakhala mmene Yehova akufunila. Popeza iye anali kudzasangalala na kacisiyo, nawonso Ayuda anafunika kucita cimodzimodzi. Cinali cofunika kwambili kwa Yehova n’cakuti kulambila kumene kunali kucitika pa kacisi watsopanoyo, kukhale kogwilizana na mmene iye amafunila. Ayuda akanasumika maganizo awo pa kulambila Yehova m’njila imene iye amavomeleza, komanso pa kupeza ciyanjo cake, akanakhalanso acimwemwe.

Khalani na kapenyedwe koyenela zinthu zikasintha (Onani ndime 11-12) *

11. N’ciyani cakhala covuta kwa alambili ena a Yehova?

11 Zinthu zikasintha pa umoyo wathu, cimakhala covuta kwa ambili a ife kucilandila. Ena amene akhala mu utumiki wanthawi zonse wapadela, utumiki wawo wasintha. Cifukwa ca ukalamba, enanso asiya utumiki umene amaukonda. N’cibadwa kusakondwela ngati masinthidwe a conco nafenso atikhudza. Poyamba, sitingamvetsetse masinthidwe amenewo kapena kuwavomeleza. Tingamayewe mmene zinthu zinalili utumiki usanasinthe. Ndipo mwina tingalefuke, na kuganiza kuti sitingacite zambili kwa Yehova m’mikhalidwe yathu yatsopano. (Miy. 24:10) Kodi masomphenya a Zekariya angatithandize bwanji kupitiliza kupatsa Mulungu zabwino mmene tingathele?

12. Kodi masomphenya a Zekariya angatithandize bwanji kukhala acimwemwe zinthu zikasintha?

12 Kuona zinthu mmene Yehova amazionela kungatithandize kuzolowela kusintha kumeneko. Iye akucita zinthu zazikulu masiku ano, ndipo tili na mwayi wapadela wokhala anchito anzake. (1 Akor. 3:9) Utumiki wathu ungasinthe, koma cikondi ca Yehova pa ife sicisintha. Conco, ngati masinthidwe a m’gulu akukhudzani inuyo panokha, pewani kumangokhalila kuganizila zifukwa zimene anapangila masinthidwewo. M’malo moyewa masiku ‘akale,’ mwapemphelo onani zabwino pa masinthidwewo. (Mlal. 7:10) Cina, pewani kuganizila zinthu zimene simungathenso kucita, koma ganizilani zimene mungathe kucita. Pa masomphenya a Zekariya, tiphunzilapo za kufunika kokhala na maganizo oyenela. Tikatelo, tidzakhalabe acimwemwe komanso okhulupilika, ngakhale pamene zinthu zasintha.

CIKAKHALA COVUTA KUTSATILA MALANGIZO

13. N’cifukwa ciyani Aisiraeli ena anaona kuti malangizo akuti ayambenso kumanga kacisi anali osathandiza?

13 Nchito yomanganso kacisi inali italetsedwa. Komabe, amuna oikidwa kuti atsogolele—Mkulu wa Ansembe Yesuwa (Yoswa), komanso Bwanamkubwa Zerubabele—‘anayamba kumanganso nyumba ya Mulungu.’ (Ezara 5:1, 2) Mwina Ayuda ena anaona kuti kucita zimenezo kunali kosathandiza. Nchito yomanga kacisi sikanabisika kwa adani, amene anayesetsa kucita zonse zotheka kuti ailepheletse basi. Amuna aŵiliwo apaudindo, Yoswa na Zerubabele, anayenela kukhala na citsimikizo cakuti Yehova adzawathandiza. Ndipo iwo anakhala naco. Motani?

14. Malinga n’kunena kwa Zekariya 4:12, 14, kodi Mkulu wa Ansembe Yoswa komanso Bwanamkubwa Zerubabele analandila citsimikizo cotani?

14 Ŵelengani Zekariya 4:12, 14. M’masomphenya Zekariya amenewa, mngelo anauza mneneli wa Mulungu wokhulupilika kuti mitengo iŵili ya maolivi ikuimila “odzozedwa aŵili,” amene ni Yoswa na Zerubabele. Amuna aŵiliwa mophiphilitsa ‘anaimilila kumbali iyi ndi mbali inayi ya Ambuye wa dziko lonse lapansi,’ Yehova. Uwu unali udindo wapadela kwambili! Yehova anali kuwakhulupilila. Motelo, Aisiraeli anali na cifukwa comveka cokhulupilila malangizo a amunawo na citsogozo ca Yehova, cifukwa ndiye anawasankha kuti awatsogolele.

15. Tingaonetse bwanji kuti timalemekeza malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu?

15 Njila imodzi imene Yehova amapelekela malangizo kwa anthu ake masiku ano, ni kupitila m’Mawu ake Baibo. M’buku lake limeneli, iye amatiuza mmene tingamulambilile. Kodi tingaonetse bwanji kuti timalemekeza malangizo amene timalandila m’Mawu a Mulungu? Ni mwa kuwaŵelenga mosamala na kuwamvetsetsa. Dzifunseni kuti, ‘Nikamaŵelenga Baibo kapena zofalitsa zathu, kodi nimaima na kusinkhasinkha zimene naŵelengazo? Kodi nimafufuza mfundo zina za coonadi zimene ni “zovuta kuzimvetsa”? Kapena kodi nimangoŵelenga mfundozo mwa patali-patali?’ (2 Pet. 3:16) Tikamapatula nthawi yosinkhasinkha zimene Yehova amatiphunzitsa, tidzakwanitsa kutsatila malangizo ake, na kukwanilitsa nchito yathu yolalikila.—1 Tim. 4:15, 16.

Khulupililani malangizo amene mumalandila kwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” (Onani ndime 16) *

16. Ngati sitinamvetsetse malangizo amene timalandila kwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” n’ciyani cingatithandize kuwatsatilabe?

16 Yehova amapelekanso malangizo kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Nthawi zina, kapoloyo angapeleke malangizo amene sitingawamvetsetse. Mwacitsanzo, mwina tingapatsidwe malangizo acindunji otithandiza kukapulumuka ngozi yacilengedwe, imene tingaone kuti singacitike kudela lathu. Kapena mwina tingaone kuti kapolo akuumitsa kwambili zinthu pa nthawi ya mlili. Kodi tingacite ciyani tikaona kuti malangizo amene tapatsidwa ni osathandiza? Tiyenela kuganizila mmene Aisiraeli anapindulila cifukwa colabadila malangizo amene anapatsidwa kupitila mwa Yoswa na Zerubabele. Tingaganizilenso nkhani zina za m’Baibo zimene timaŵelenga. Nthawi zina, anthu a Mulungu amalandila malangizo amene mkaonedwe kathu ka umunthu angaoneke osathandiza. Koma pambuyo pake, amakhala opulumutsa moyo.—Ower. 7:7; 8:10.

MUZITHA KUONA ZIMENE ZEKARIYA ANAONA

17. Kodi Ayuda anapindula motani na masomphenya a coikapo nyale na mitengo iŵili ya maolivi?

17 Masomphenya acisanu amene Zekariya anaona anali acidule, koma anathandiza kwambili Ayuda kupitiliza nchito yawo, komanso kulambila kwawo. Ndipo ataseŵenzetsa zimene anaphunzila pa masomphenyawo, anaona kuti Yehova akuwathandiza na kuwatsogolela. Kupitila mwa mzimu wake woyela wamphamvu, iye anawathandiza kupitiliza kugwila nchito yawo na kukhalanso acimwemwe.—Ezara 6:16.

18. Kodi masomphenya a Zekariya angakuthandizeni bwanji?

18 Inunso mungapindule kwambili na masomphenya a Zekariya a coikapo nyale na mitengo iŵili ya maolivi. Monga taonela, angakuthandizeni kupeza mphamvu kuti mulimbane na ŵanthu otsutsa, kukhalabe acimwemwe zinthu zikasintha pa umoyo wanu, komanso kukhulupilila na kumvela malangizo amene simunawamvetsetse. Mungacite ciyani ngati mukukumana na mavuto pa umoyo? Coyamba, onani zimene Zekariya anaona—umboni wakuti Yehova akusamalila anthu ake. Kenako, citani zimene mukuonazo mwa kukhulupilila Yehova na kupitiliza kumulambila na mtima wanu wonse. (Mat. 22:37) Mukatelo, iye adzakuthandizani kuti mum’tumikile na cimwemwe kwamuyaya.—Akol. 1:10, 11

NYIMBO 7 Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

^ Yehova anaonetsa Zekariya masomphenya angapo ocititsa cidwi. Zimene Zekariya anaona, zinapatsa iye komanso anthu a Yehova mphamvu yogonjetsa zovuta zimene anakumana nazo pokhazikitsanso kulambila koyela. Masomphenyawo nafenso angatithandize kutumikila Yehova mokhulupilika ngakhale tikumane na mavuto. M’nkhani ino, tikambilane maphunzilo amene titengapo pa masomphenya a Zekariya a coikapo nyale komanso mitengo ya maolivi.

^ Patapita zaka, m’masiku a Bwanamkubwa Nehemiya, wolamulila wina dzina lake Aritasasita anakomela mtima Ayuda.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale waona kufunika kozoloŵela pamene zinthu zasintha cifukwa ca ukalamba na kufooka kwa thanzi.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo akusinkhasinkha mmene Yehova amathandizila “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” monga anacitila kwa Yoswa na Zerubabele.