Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 13

Kulambila Koona Kudzawonjezela Cimwemwe Canu

Kulambila Koona Kudzawonjezela Cimwemwe Canu

“Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo ndi ulemu.”—CHIV. 4:11.

NYIMBO 31 Uziyenda na Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. N’ciyani cimapangitsa Mulungu kuvomeleza kulambila kwathu?

 N’CIYANI cimabwela m’maganizo mwanu mukamva liwu lakuti “kulambila”? Mwina m’maganizila za m’bale amene modzicepetsa wagwada m’cipinda cake, ndipo akupemphela mocokela pansi pamtima. Kapena m’maganizila za banja lacimwemwe limene limacita kulambila kwa pabanja nthawi zonse.

2 Pa zocitika ziŵilizi, onse akulambila. Kodi Yehova adzavomeleza kulambila kwawo? Inde, malinga ngati n’kogwilizana na colinga cake, komanso ngati kukucitika cifukwa comukonda na kumulemekeza. Timam’konda ngako Yehova! Ndipo tidziŵa kuti iye ni woyenela kum’lambila, komanso timafuna kuti tizimulambila m’njila yabwino koposa.

3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 M’nkhani ino, tikambilane kulambila kumene Yehova anavomeleza m’nthawi yakale, komanso mbali 8 zokhudza kulambila kumene iye amavomeleza masiku ano. Pamene tikutelo, ganizilani mmene inuyo panokha mungawongolele zimene mumacita pa kulambila kwanu. Tikambilanenso cifukwa cake kulambila koona kumatipangitsa kukhala acimwemwe.

KULAMBILA KUMENE YEHOVA ANAVOMELEZA M’NTHAWI YAKALE

4. Kodi alambili a Yehova akale anaonetsa bwanji ulemu na cikondi kwa iye?

4 M’nthawi yakale, amuna okhulupilika monga Abele, Nowa, Abulahamu, komanso Yakobo, anaonetsa ulemu na cikondi kwa Yehova. Motani? Mwa kumumvela, kuika cikhulupililo cawo mwa iye, na kupeleka nsembe. Baibo sitiuza zonse zimene iwo anacita pa kulambila kwawo. Koma anacita zimene akanatha kuti alemekeze Yehova, ndipo iye anavomeleza kulambila kwawo. Iye anapatsa mbadwa za Abulahamu Cilamulo ca Mose. Malamulowo anali na malangizo okhudza kulambila Yehova m’njila imene iye amavomeleza.

5. Kodi panakhala kusintha kotani pa nkhani ya kulambila koona Yesu atafa na kuukitsidwa?

5 Yesu atafa na kuukitsidwa, Yehova sanafunenso kuti anthu azimulambila motsatila Cilamulo ca Mose. (Aroma 10:4) Akhristu anayenela kutsatila cilamulo catsopano, kutanthauza “cilamulo ca Khristu.” (Agal. 6:2) Iwo anayenela kumvela “cilamulo” cimeneci, osati mwa kuciloweza pamtima kapena kutsatila mndandanda wa zoyenela kucita komanso zosayenela, koma mwa kutengela citsanzo ca Yesu na kucita zimene iye anaphunzitsa. Masiku anonso, Akhristu amacita zimene angathe potsatila Khristu kuti akondweletse Yehova, komanso kuti ‘atsitsimulidwe.’—Mat. 11:29.

6. Tingacite ciyani kuti tipindule na nkhani ino?

6 Pokambilana mbali iliyonse ya kulambila kwathu, dzifunseni kuti, ‘Kodi napita bwanji patsogolo pa mbali imeneyi? Ni mbali iti imene ningawongolele pa kulambila kwanga?’ Muyenela kukondwela na mmene mwapitila patsogolo. Koma muyenelanso kupempha Yehova kuti akuthandizeni pa mbali zofunika kuwongolela.

KODI TIMALAMBILA MULUNGU M’NJILA ZITI?

7. Kodi Yehova amawaona bwanji mapemphelo athu ocokela pansi pa mtima?

7 Timalambila Yehova tikamapemphela kwa iye. Malemba amayelekezela mapemphelo athu na nsembe zofukiza zimene zinali kupelekedwa pa cihema, komanso patapita nthawi, pa kacisi. (Sal. 141:2) Zofukiza zimenezo zinali kutulutsa fungo lokoma lokondweletsa mtima wa Mulungu. Mofananamo, mapemphelo athu ocokela pansi pa mtima ‘amamusangalatsa’ Mulungu, ngakhale pamene taseŵenzetsa mawu wamba osavuta. (Miy. 15:8; Deut. 33:10) Conco, sitikaikila kuti Yehova amakondwela kumva mawu athu oonetsa kuti timam’konda na kumuyamikila. Iye amafuna kuti tizimuuza nkhawa zathu, komanso zimene timafuna. Musanayambe kupemphela kwa Yehova, bwanji osaganizila mofatsa zimene mudzakamba m’pemphelo? Mukatelo, mudzapeleka ‘nsembe yofukiza’ yabwino koposa kwa Atate wanu wakumwamba.

8. Kodi tili na mpata wabwino uti wotamanda Mulungu?

8 Timalambila Yehova tikamam’tamanda. (Sal. 34:1) Timatamanda Yehova tikamauzako ena za makhalidwe ake abwino komanso nchito zake. Citamando cathu cimacokela mu mtima. Conco, tikamapatula nthawi yosinkhasinkha ubwino wa Yehova, kutanthauza zonse zimene waticitila, tidzakhala na zifukwa zambili zomutamandila. Nchito yolalikila imatipatsa mpata wabwino ‘wotamanda Mulungu monga nsembe imene tikupeleka kwa [iye], yomwe ni cipatso ca milomo yathu.’ (Aheb. 13:15) Monga mmene timasankhila bwino mawu tisanapemphele kwa Yehova, tiyenela kucitanso cimodzimodzi pa zimene tidzakamba kwa anthu amene timawalalikila. Tifuna kuti nsembe yathu yacitamando ikhale yabwino koposa. Ndiye cifukwa cake, timauzako ena coonadi mocokela mu mtima.

9. Mofanana na Aisiraeli, kodi timapindula bwanji tikamasonkhana pamodzi? Fotokozani citsanzo ca inu mwini.

9 Timalambila Yehova tikamapezeka ku misonkhano. Kalelo, Mulungu anauza Aisiraeli kuti: “Mwamuna aliyense pakati panu azikaonekela katatu pa caka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Mulungu adzasankhe.” (Deut. 16:16) Iwo anayenela kusiya nyumba zawo na minda yawo popanda wozilondela. Yehova anawalonjeza kuti: “Palibe aliyense adzasilila dziko lanu pamene mwacoka kukaona nkhope ya Yehova Mulungu wanu.” (Eks. 34:24) Cifukwa cokhulupilila kwambili Yehova, Aisiraeli oopa Mulungu amenewo anali kupezeka ku zikondwelelo za pacaka. Akatelo, iwo anali kupindula kwambili. Anali kuwonjezela cidziŵitso cawo pa Cilamulo ca Mulungu, kusinkhasinkha ubwino wake, komanso kukhala na maceza olimbikitsa na okhulupilila anzawo. (Deut. 16:15) Nafenso timapindula mofananamo tikamayesetsa kupezeka ku misonkhano yacikhristu. Ndipo ganizilani cimwemwe cimene Yehova amakhala naco tikabwela okonzekela na kupeleka ndemanga zacidule komanso zogwila mtima.

10. N’cifukwa ciyani kuimba nyimbo n’kofunika kwambili pa kulambila kwathu?

10 Timalambila Yehova tikamaimba nyimbo za Ufumu. (Sal. 28:7) Aisiraeli anaona kuti kuimba nyimbo ni mbali yofunika kwambili pa kulambila kwawo. Mfumu Davide anasankha Alevi 288 kuti aziimba pa kacisi. (1 Mbiri 25:1, 6-8) Masiku ano, tingaonetse kuti timakonda Mulungu mwa kuimba nyimbo zacitamando. Kamvekedwe ka mawu athu si ndiko kofunika kwambili. Ganizilani izi: Tikamalankhula, “timapunthwa nthawi zambili.” Koma sitileka kupeleka nkhani mu mpingo komanso kulalikila. (Yak. 3:2) Mofananamo, tisalole mamvekedwe a mawu athu kutilepheletsa kuimba nyimbo zotamanda Yehova.

11. Mogwilizana na Salimo 48:13, n’cifukwa ciyani tiyenela kupatula nthawi yoŵelenga Baibo monga banja?

11 Timalambila Yehova tikamaŵelenga Mawu ake, na kuphunzitsa ana athu za iye. Sabata linapatsa Aisiraeli mpata wakuti aombole nthawi yolimbitsa ubale wawo na Yehova. (Eks. 31:16, 17) Aisiraeli okhulupilika anali kuphunzitsa ana awo za Yehova na ubwino wake. Nafenso, tiyenela kupatula nthawi yoŵelenga Mawu a Mulungu. Iyi ni mbali ya kulambila Yehova, ndipo imatithandiza kumuyandikila. (Sal. 73:28) Tikamaphunzila pamodzi monga banja, tingathandize ana athu kukhala pa ubale wabwino na Atate wathu wacikondi wakumwamba.—Ŵelengani Salimo 48:13.

12. Tiphunzilapo ciyani za mmene Yehova anaonela nchito ya aja amene anapanga cihema na kucikongoletsa?

12 Timalambila Yehova tikamamanga malo olambilila na kuwasamalila. Baibo imakamba kuti nchito yomanga cihema colambilila na kucikongoletsa, inali ‘nchito yopatulika.’ (Eks. 36:1, 4) Masiku anonso, Yehova amaona nchito yomanga Nyumba za Ufumu na zimango zina za gulu kukhala yopatulika. Abale na alongo ena amataila maola oculuka pogwila nchito zimenezi. Timawayamikila kwambili abale athu amene amadzipeleka pocilikiza nchito ya Ufumu. Cina, iwo amagwilanso nchito yolalikila. Ndipo ena a iwo angafune kuyamba upainiya. Akulu mu mpingo angacilikize nchito ya mamangidwe mwa kusazengeleza kuika abale na alongo athu akhama amenewa kukhala apainiya ngati iwo ayenelela. Kaya tili na luso la mamangidwe kapena ayi, tonsefe tingatengeko mbali posamalila malo athu olambilila ndiponso kuti akhale mumkhalidwe wabwino.

13. Kodi copeleka cathu cocilikiza nchito ya Ufumu tiyenela kuciona motani?

13 Timalambila Yehova tikamacilikiza nchito ya Ufumu mwa zopeleka zathu. Aisiraeli sanaloledwe kukaonekela kwa Yehova cimanja-manja. (Deut. 16:16) Anayenela kupeleka mphatso malinga na mmene zinthu zinalili kwa iwo. Mwa kutelo, iwo anaonetsa ciyamikilo cawo pa makonzedwe amene anakhazikitsidwa kuti awapindulitse mwauzimu. Kodi tingaonetse bwanji kuti timam’konda Yehova, komanso kuti timayamikila zinthu zauzimu zimene timalandila? Njila imodzi ni kupanga copeleka cocilikiza mpingo wathu, komanso nchito ya padziko lonse mmene tingakwanitsile. Mtumwi Paulo anakamba kuti: “Mphatso yocokela pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwela nayo, cifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apeleke zimene angathe, osati zimene sangathe.” (2 Akor. 8:4, 12) Yehova amayamikila copeleka ciliconse cimene tingapange mocokela pansi pa mtima, kaya cikhale cocepa motani.—Maliko 12:42-44; 2 Akor. 9:7.

14. Malinga na Miyambo 19:17, kodi Yehova amaliona bwanji thandizo limene timapeleka kwa abale athu?

14 Timalambila Yehova tikamathandiza Akhristu anzathu ofunikila thandizo. Yehova analonjeza kuti adzabwezela Aisiraeli amene anali kucitila cifundo osauka. (Deut. 15:7, 10) Inde, nthawi iliyonse tikathandiza Mkhristu mnzathu, Yehova amaona kuti thandizolo ni mphatso kwa iye. (Ŵelengani Miyambo 19:17.) Mwacitsanzo, Akhristu a ku Filipi atatumiza mphatso kwa Paulo mkaidi, iye anacha mphatsoyo kuti “nsembe yovomelezeka yosangalatsa kwa Mulungu.” (Afil. 4:18) Ganizilani anthu a mu mpingo mwanu, na kudzifunsa kuti, ‘Kodi pali wina amene ningathandize?’ Yehova amakondwela kwambili tikamaseŵenzetsa nthawi yathu, mphamvu zathu, maluso athu, komanso zinthu zathu zakuthupi pothandiza ena. Iye amaona zimenezo kuti ni mbali ya kulambila kwathu.—Yak. 1:27.

KULAMBILA KOONA KUMATIBWELETSELA CIMWEMWE

15. Kulambila koona kumafuna nthawi komanso khama. Koma n’cifukwa ciyani si kolemetsa?

15 Kulambila koona kumafuna nthawi komanso khama. Koma si kolemetsa. (1 Yoh. 5:3) Cifukwa ciyani? Cifukwa timalambila Yehova kaamba komukonda. Ganizilani mwana wamng’ono amene akufuna kupatsa atate ake mphatso. Iye angathele nthawi yoculuka kujambula pikica yakuti awapatse. Mwanayo sakudandaula na nthawi imene wataila pojambula pikicayo. Iye amawakonda atate ake, ndipo ni wokondwa kuwapatsa mphatso imeneyo. Mofananamo, cifukwa cokonda Yehova, timayesetsa kuseŵenzetsa nthawi yathu na mphamvu zathu kuti titengeko mbali pa kulambila koona.

16. Malinga n’kunena kwa Aheberi 6:10, kodi Yehova amamvela bwanji akaona kuyesetsa kwathu kuti tim’kondweletse?

16 Makolo acikondi sayembekezela kulandila mphatso yofanana kwa mwana aliyense. Iwo amadziŵa kuti mwana aliyense ni wosiyana na mnzake. Mofananamo, Atate wathu wakumwamba amadziŵa zimene aliyense wa ife angathe kucita. Mwina inu mungacite zambili kupambana anzanu. Kapena simungathe kucita zambili mofanana na ena, mwina cifukwa ca ukalamba, matenda, kapena maudindo anu m’banja. Koma musalefuke. (Agal. 6:4) Yehova sadzaiŵala nchito yanu. Iye adzakondwela ngati mukumupatsa zimene mungathe na colinga cabwino. (Ŵelengani Aheberi 6:10.) Yehova amaona ngakhale zolinga za mtima wanu. Amafuna kuti mukhale acimwemwe komanso okhutila na zimene mumatha kucita pom’lambila.

17. (a) Ngati cimativuta kucita zinthu zokhudza kulambila kwathu, kodi tiyenela kucita ciyani? (b) Kodi mwapindula bwanji na zina mwa mbali za kulambila kwathu zimene zili pa bokosi lakuti, “ Wonjezelani Cimwemwe Canu”?

17 Bwanji ngati cimativuta kucita zinthu zokhudza kulambila, monga kucita phunzilo la munthu mwini kapena ulaliki wapoyela? Tikamacita zinthu zimenezi kaŵili-kaŵili, m’pamenenso tidzasangalala nazo kwambili, komanso kupindula nazo. Kulambila kwathu tingakuyelekezele na maseŵelo ena ake, kapena kuphunzila moseŵenzetsela cipangizo coimbila. Ngati tingamacite zimenezi mwa apo na apo, sitingapite kwambili patsogolo. Koma bwanji ngati timacita pulakatisi tsiku lililonse? Poyamba, tingamacite zimenezi kwa mphindi zocepa, kenako n’kumawonjezela pang’ongo-pang’ono. Tikamaona zotulukapo zabwino cifukwa ca khama lathu, tiziyembekezela mwacidwi kucita zinthuzo. N’zimenenso tiyenela kucita pa kulambila kwathu.

18. Kodi timakwanilitsa bwanji colinga ca kukhalapo kwathu na moyo? Nanga padzakhala mapindu otani?

18 Tidzakwanilitsa colinga ca kukhalapo kwathu na moyo, ngati tilambila Yehova na mtima wonse. Tikatelo, tidzakhala na cimwemwe, umoyo waphindu, komanso ciyembekezo codzalambila Yehova kwamuyaya. (Miy. 10:22) Tili na mtendele wamaganizo cifukwa timadziŵa kuti Yehova amathandiza alambili ake akakumana na mavuto. (Yes. 41:9, 10) Ndipo tili na zifukwa zabwino zokhalila acimwemwe polambila Atate wathu wacikondi, amene ni woyenela kulandila “ulemelelo ndi ulemu” kucokela ku zolengedwa zake zonse.—Chiv. 4:11.

NYIMBO 24 Bwelani ku Phili la Yehova

^ Pokhala Mlengi wa zinthu zonse, Yehova ni woyenela kum’lambila. Iye amavomeleza kulambila kwathu tikamamvela malamulo ake, na kutsatila mfundo zake. M’nkhani ino, tikambilane mbali 8 zokhudza kulambila. Pamene tikambilana, onani mmene tingawongolele pa mbalizo, komanso mmene zidzawonjezela cimwemwe cathu.