NKHANI YOPHUNZIRA 13

Kulambira Koona Kumachititsa Kuti Muzisangalala Kwambiri

Kulambira Koona Kumachititsa Kuti Muzisangalala Kwambiri

“Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu.”​—CHIV. 4:11.

NYIMBO NA. 31 Yendani ndi Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi n’chiyani chingachititse kuti Mulungu azivomereza kulambira kwathu?

 KODI mumaganizira chiyani mukamva mawu akuti “kulambira”? Mwina mumaganizira za m’bale wodzichepetsa yemwe wagwada pambali pa bedi lake, n’kumapemphera mochokera pansi pa mtima. Kapenanso mumaganizira za banja lomwe likusangalala kuphunzira mozama Baibulo.

2 Pa zochitika zonsezi, anthu amene atchulidwawo akulambira Mulungu. Kodi Yehova angavomereze kulambira kwawo? Angatero ngati akuchita zimenezo mogwirizana ndi chifuniro chake ndiponso ngati amamukonda komanso kumulemekeza. Timakonda kwambiri Yehova. Timadziwa kuti iye ndi woyenera kulambiridwa ndipo timafuna kuti tizimulambira m’njira yabwino kwambiri.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Munkhaniyi tikambirana kulambira kumene Yehova ankavomereza kalelo ndipo tionanso njira zina 8 zimene tingamulambirire movomerezeka masiku ano. Tikamachita zimenezi tiziganizira mmene ifeyo patokha tingamulambirire m’njira yabwino kwambiri. Tionanso chifukwa chake kulambira koona kumatithandiza kuti tizisangalala.

KULAMBIRA KUMENE YEHOVA ANKAVOMEREZA KALELO

4. Kodi anthu amene ankalambira Yehova Chikhristu chisanayambe anasonyeza bwanji kuti ankamulemekeza komanso kumukonda?

4 Chikhristu chisanayambe, amuna okhulupirika monga Abele, Nowa, Abulahamu ndi Yobu anasonyeza kuti ankalemekeza komanso kukonda Yehova. Kodi anachita bwanji zimenezi? Iwo anatero pokhala omvera, okhulupirika komanso popereka nsembe. Baibulo silifotokoza zonse zimene ankafunika kuchita polambira. Komabe iwo ankachita zonse zimene akanatha polemekeza Yehova ndipo iye ankavomereza kulambira kwawo. Kenako Yehova anapereka Chilamulo cha Mose kwa ana a Abulahamu. M’chilamulocho munali malamulo ambiri omwe ankafotokoza njira yolambirira imene Yehova ankavomereza.

5. Kodi ndi kusintha kotani kumene kunachitika pankhani ya kulambira koona pambuyo pa imfa ndi kuukitsidwa kwa Yesu?

5 Pambuyo pa imfa komanso kuukitsidwa kwa Yesu, Yehova sankafunanso kuti anthu azimulambira potsatira Chilamulo cha Mose. (Aroma 10:4) Akhristu ankafunika kutsatira chilamulo chatsopano, chomwe ndi “chilamulo cha Khristu.” (Agal. 6:2) Iwo akanasonyeza kuti akumvera “chilamulo” chimenecho osati poloweza ndandanda ya zimene ayenera kuchita ndi zimene sayenera kuchita, koma potsanzira Yesu ndi kugwiritsa ntchito zimene ankaphunzitsa. Masiku anonso Akhristu amayesetsa kutsanzira Khristu n’cholinga choti azisangalatsa Yehova komanso ‘kutsitsimulidwa.’​—Mat. 11:29.

6. Kodi nkhaniyi itithandiza bwanji?

6 Tikamakambirana chilichonse cha zimene timachita pa kulambira kwathu, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikuchita bwanji pankhani imeneyi?’ Mungadzifunsenso kuti, ‘Kodi ndingawonjezere zimene ndimachita polambira Mulungu?’ Muzisangalala ndi zimene mukukwanitsa kuchita bwino ndipo muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuona zimene mukufunika kuwonjezera kuchita.

KODI KULAMBIRA KWATHU KUMAPHATIKIZAPO ZINTHU ZITI?

7. Kodi Yehova amawaona bwanji mapemphero athu ochokera pansi pa mtima?

7 Timalambira Yehova tikamapemphera kwa iye. Malemba amayerekezera mapemphero athu ndi zofukiza zomwe zinkakonzedwa bwino n’kukaperekedwa kuchihema. (Sal. 141:2) Zofukizazo zinkatulutsa fungo labwino lomwe linkasangalatsa Mulungu. Mofanana ndi zimenezi mapemphero athu ochokera pansi pa mtima amakhala ‘osangalatsa’ kwa iye, ngakhale titagwiritsa ntchito mawu osavuta. (Miy. 15:8; Deut. 33:10) Tili ndi zifukwa zabwino zokhulupirira kuti Yehova amasangalala kumvetsera mapemphero athu osonyeza kuti timamukonda komanso kumuyamikira. Iye amafuna kuti tizimufotokozera nkhawa zathu, chikhulupiriro chathu komanso zimene timalakalaka. Ndiye musanapemphere kwa Yehova, bwanji osaganizira kaye zimene mukufuna kunena m’pemphero? Mukamachita zimenezi mudzapereka “zofukiza” zabwino kwambiri kwa Atate wanu wakumwamba.

8. Kodi tili ndi mwayi wapadera uti wotamanda Mulungu?

8 Timalambira Yehova tikamamutamanda. (Sal. 34:1) Timamutamanda tikamauza ena monyadira za makhalidwe ake odabwitsa komanso ntchito zake. Tingakhale ndi zabwino zambiri zolankhula zokhudza Yehova ngati timamuyamikira. Tikamapeza nthawi yoganizira ubwino wa Yehova pa zabwino zonse zimene amatichitira tingakhale ndi zifukwa zambiri zomutamandira. Ntchito yolalikira imatipatsa mwayi wabwino woti tizitamanda Mulungu ‘monga nsembe imene tikupereka kwa iye, yomwe ndi chipatso cha milomo yathu.’ (Aheb. 13:15) Mofanana ndi zimene timayenera kuchita poganizira kaye zimene tinganene popemphera kwa Yehova, tingachitenso bwino kuganizira zimene tinganene kwa anthu amene timawalalikira. Timafuna kuti “nsembe imene tikupereka” izikhala yabwino kwambiri. Choncho timalankhula ndi mtima wonse tikamauza ena mfundo za choonadi.

9. Mofanana ndi Aisiraeli, kodi timapindula bwanji chifukwa chosonkhana? Perekani chitsanzo cha zimene zinakuchitikirani.

9 Timalambira Yehova tikamapezeka pamisonkhano. Aisiraeli anauzidwa kuti: “Mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Mulungu adzasankhe.” (Deut. 16:16) Iwo ankafunika kusiya nyumba ndi mbewu zawo popanda woziyang’anira. Yehova anawalonjeza kuti: “Palibe aliyense adzasirira dziko lanu pamene mwachoka kukaona nkhope ya Yehova Mulungu wanu.” (Eks. 34:24) Popeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova, Aisiraeli oopa Mulunguwa ankapezeka pa zikondwererozi chaka chilichonse. Zimenezi zinkachititsa kuti azidalitsidwa kwambiri. Mwachitsanzo, ankamvetsa bwino Chilamulo cha Mulungu, kuganizira ubwino wake ndiponso ankalimbikitsidwa akasonkhana ndi olambira anzawo. (Deut. 16:15) Ifenso timapindula kwambiri ndi zinthu zimenezi tikamayesetsa kuti tikapezeke pamisonkhano. Komanso taganizirani mmene Yehova amasangalalira tikafika pamisonkhano titakonzekera kupereka ndemanga zachidule komanso zolimbikitsa.

10. N’chifukwa chiyani kuimba n’kofunika kwambiri pa kulambira kwathu?

10 Timalambira Yehova tikamaimba nawo nyimbo. (Sal. 28:7) Aisiraeli ankaona kuti kuimba nyimbo n’kofunika kwambiri pa kulambira. Mfumu Davide anasankha Alevi 288 kuti aziimba nyimbo pakachisi. (1 Mbiri 25:1, 6-8) Masiku ano tingasonyeze kuti timakonda Mulungu poimba nyimbo zomutamanda. Sikuti chofunika kwambiri ndi kukhala ndi luso loimba. Taganizirani chitsanzo ichi: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri” tikamalankhula koma zimenezi sizichititsa kuti tisamalankhule mumpingo komanso tikamalalikira. (Yak. 3:2) Mofanana ndi zimenezi, tikhozabe kumaimba nyimbo zotamanda Yehova ngakhale pamene tikuona kuti sitimaimba bwino.

11. Mogwirizana ndi Salimo 48:13, n’chifukwa chiyani tiyenera kumapeza nthawi yophunzira Baibulo ndi banja lathu?

11 Timalambira Yehova tikamaphunzira Mawu ake komanso kuphunzitsa ana athu zokhudza iye. Pa tsiku la Sabata, Aisiraeli sankagwira ntchito zawo za tsiku ndi tsiku ndipo zimenezi zinkawapatsa mwayi woganizira za ubwenzi wawo ndi Yehova. (Eks. 31:16, 17) Aisiraeli okhulupirika ankaphunzitsa ana awo zokhudza Yehova komanso ubwino wake. Ifeyo patokha timafunika kukonza nthawi yowerenga komanso kuphunzira Mawu a Mulungu. Imeneyi ndi mbali ya kulambira kwathu ndipo imatithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Sal. 73:28) Ndipo tikamaphunzira limodzi monga banja, tingathandize ana athu kuti akhale pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi wachikondi.—Werengani Salimo 48:13.

12. Kodi tikuphunzira chiyani pankhani ya mmene Yehova ankaonera ntchito yomanga chihema ndi zinthu zonse zokhudza chihemacho?

12 Timalambira Yehova tikamakonza komanso kumanga malo olambirira. Baibulo limanena kuti ntchito yokonza chihema ndi zonse zokhudza chihemacho zinali “zopatulika.” (Eks. 36:1, 4) Masiku anonso Yehova amaona kuti ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi nyumba zina za gulu ndi yopatulika. Abale ndi alongo ena amakhala akugwira ntchito zimenezi kwa nthawi yayitali. Kodi sitikuyenera kuyamikira zimene amachitazi zomwe ndi zofunika kwambiri pa ntchito ya Ufumu? Komabe iwo amagwiranso ntchito yolalikira. Enanso amafuna atachita upainiya. Akulu angasonyeze kuti akuthandiza pantchito ya zomangamanga, povomereza kuti abale ndi alongo akhamawa achite upainiya ngati akuyenerera. Kaya tili ndi luso la zomangamanga kapena ayi, tonsefe tingathandize pantchito yomanga ndi kukonza nyumba zolambirirazi.

13. Kodi tiziona bwanji zopereka zathu zothandizira pa ntchito za Ufumu?

13 Timalambira Yehova tikamathandiza pantchito ya Ufumu ndi zopereka zathu. Aisiraeli sankafunika kukaonekera pamaso pa Yehova chimanjamanja. (Deut. 16:16) Iwo ankafunika kubweretsa mphatso ina yake mogwirizana ndi mmene zinthu zinalili pa moyo wawo. Zimenezi zinkasonyeza kuti ankayamikira zonse zimene zinkakonzedwa kuti apindule mwauzimu. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova komanso kuti timayamikira zonse zimene akutichitira? Njira imodzi ndi kupereka ndalama zothandizira mpingo umene tikusonkhana komanso ntchito ya padziko lonse mogwirizana ndi m’mene zinthu zilili pa moyo wathu. Pa nkhaniyi mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Mphatso yochokera pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwera nayo, chifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apereke zimene angathe, osati zimene sangathe.” (2 Akor. 8:4, 12) Yehova amasangalala ndi ndalama zimene timapereka mochokera pansi pa mtima, ngakhale zitakhala zochepa bwanji.​—Maliko 12:42-44; 2 Akor. 9:7.

14. Mogwirizana ndi Miyambo 19:17, kodi Yehova amaona bwanji zimene timachita pothandiza abale ndi alongo athu?

14 Timalambira Yehova tikamathandiza Akhristu anzathu omwe akufunika kuthandizidwa. Yehova analonjeza kuti adzadalitsa Aisiraeli omwe ankathandiza osauka. (Deut. 15:7, 10) Ifenso tikamathandiza olambira anzathu Yehova amaona kuti tikupereka mphatso kwa iyeyo. (Werengani Miyambo 19:17.) Mwachitsanzo, pamene Akhristu a ku Filipi anatumiza mphatso kwa Paulo yemwe anali mkaidi, iye ananena kuti imeneyo inali “nsembe yovomerezeka yosangalatsa kwa Mulungu.” (Afil. 4:18) Mukaona abale ndi alongo a mumpingo mwanu muzidzifunsa kuti, ‘Kodi pali wina amene ndingamuthandize?’ Yehova amasangalala akaona kuti tikugwiritsa ntchito nthawi, mphamvu, luso ndi zinthu zathu pothandiza ena. Amaona kuti imeneyi ndi mbali ya kulambira kwathu.​—Yak. 1:27.

KULAMBIRA KOONA KUMATITHANDIZA KUKHALA OSANGALALA

15. Kulambira koona kumafuna nthawi komanso khama, koma n’chifukwa chiyani sikolemetsa?

15 Kulambira koona kumafuna nthawi komanso khama. Koma si chinthu cholemetsa. (1 Yoh. 5:3) N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa timalambira Yehova chifukwa chomukonda. Taganizirani za mwana wamng’ono amene akufuna kupatsa bambo ake chinachake. Mwina akhoza kutenga nthawi yaitali akujambula chithunzi kuti adzawapatse. Koma mwanayo sadandaula za kuchuluka kwa nthawi imene wakhala akujambula chithunzicho. Iye amakonda kwambiri bambo ake ndipo akusangalala kuwapatsa chithunzicho monga mphatso. Mofanana ndi zimenezi chifukwa chakuti timakonda Yehova, timasangalala kugwiritsa ntchito nthawi yathu komanso kuchita khama kuti tizimulambira movomerezeka.

16. Mogwirizana ndi Aheberi 6:10, kodi Yehova amaona bwanji zimene timachita pofuna kumusangalatsa?

16 Makolo achikondi sayembekezera kulandira mphatso zofanana kuchokera kwa ana awo. Iwo amazindikira kuti mwana aliyense ndi wosiyana ndi mnzake ndipo sangachite zinthu mofanana. Mofanana ndi zimenezi Atate wathu wakumwamba amamvetsa mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Mwina inu mukhoza kumachita zambiri kuposa anthu amene mukuwadziwa komanso amene mumawakonda. Kapenanso mungalephere kuchita zambiri ngati ena mwina chifukwa cha uchikulire, thanzi lanu, kapena maudindo a m’banja. Musamalole kuti zimenezi zikufooketseni. (Agal. 6:4) Yehova sadzaiwala ntchito yanu. Ngati mukuchita zimene mungakwanitse komanso muli ndi zolinga zoyenera, iye adzasangalala nanu. (Werengani Aheberi 6:10.) Ndipotu Yehova amaona zolinga za mtima wanu. Iye amafuna kuti muzisangalala komanso kukhala okhutira ndi zimene mukuchita pomulambira.

17. (a) Kodi tingatani ngati zikutivuta kuchita zinthu zina zokhudza kulambira? (b) Kodi njira zolambirira zomwe zasonyezedwa m’bokosi lakuti “Muziwonjezera Chimwemwe Chanu,” zakuthandizani bwanji?

17 Kodi tingatani ngati zimativuta kuchita nawo zinthu zina zokhudza kulambira monga kuphunzira patokha kapena kugwira ntchito yolalikira? Tikamachita zinthu zimenezi pafupipafupi, timazindikira kuti m’pamenenso timasangalala kwambiri komanso kupindula nazo. Tingayerekeze kulambira kwathu ndi zochitika zina monga kuchita masewera enaake kapenanso kuphunzira kuimba chida china chake. Ngati timachita zinthu zimenezi mwa apo ndi apo, sitingapite patsogolo. Koma bwanji ngati titamachita zimenezo tsiku lililonse? Tikhoza kuyamba ndi kuzichita nthawi yochepa kenako n’kumawonjezera nthawiyo pang’onopang’ono. Tikayamba kuona kuti tikuzichita bwino, tingayambe kumafunitsitsa kuti tizizichita nthawi zonse n’kumasangalala nazo. Izitu ndi zofanana ndi zimene zingachitike pa kulambira kwathu.

18. Kodi timakwaniritsa bwanji cholinga chimene tinalengedwera, nanga zotsatirapo zake n’zotani?

18 Timakwanitsa cholinga chimene Yehova anatilengera tikamamulambira kuchokera pansi pa mtima. Zimenezi zimatithandiza kuti tizikhala ndi moyo wosangalala komanso watanthauzo ndipo timakhala ndi chiyembekezo chodzamulambira mpaka kalekale. (Miy. 10:22) Panopa timakhala ndi mtendere wa m’maganizo chifukwa timadziwa kuti Yehova amathandiza anthu amene amamulambira akakumana ndi mavuto. (Yes. 41:9, 10) Choncho tili ndi zifukwa zabwino zokhalira osangalala tikamalambira Atate wathu wachikondi, amene ndi woyenera “kulandira ulemerero ndi ulemu” kuchokera kwa zinthu zonse zimene analenga.​—Chiv. 4:11.

NYIMBO NA. 24 Bwerani Kuphiri la Yehova

^ Monga Mlengi wa zinthu zonse, Yehova ndi woyenera kulambiridwa. Zimene timachita pomulambira zimakhala zovomerezeka kwa iye, tikamamvera malamulo ake komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake. Munkhaniyi tikambirana zinthu zosiyanasiyana 8, zimene timachita polambira Mulungu. Tiphunzira mmene tingamachitire bwino zinthu zimenezi kuti tizisangalala kwambiri.