Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 14

Inu Akulu—Pitilizani Kutsanzila Mtumwi Paulo

Inu Akulu—Pitilizani Kutsanzila Mtumwi Paulo

“Muzitsanzila ine.”—1 AKOR. 11:1.

NYIMBO 99 Abale Miyanda Miyanda

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi citsanzo ca mtumwi Paulo cingawathandize bwanji akulu?

 MTUMWI Paulo anali kuwakonda abale ake. Iye anagwila nchito molimbika kuti awathandize. (Mac. 20:31) Pa cifukwa cimeneci, nawonso alambili anzake anali kum’konda ngako. Pa nthawi ina, akulu a ku Efeso “analila kwambili” atadziŵa kuti sadzamuonanso Paulo. (Mac. 20:37) Nawonso akulu odzipeleka amawakonda kwambili abale na alongo awo, ndipo amayesetsa kuwathandiza. (Afil. 2:16, 17) Koma nthawi zina, akulu amakumana na zovuta. N’ciyani cingawathandize kugonjetsa zovutazo?

2 Akulu ogwila nchito molimbika amenewa, angacite bwino kuganizila citsanzo ca Paulo. (1 Akor. 11:1) Iye sanali monga angelo, koma anali munthu wopanda ungwilo amene nthawi zina anali kuvutika kucita zoyenela. (Aroma 7:18-20) Pamwamba pa izi, anali kulimbana na mavuto ena. Koma Paulo sanalefuke kapena kutaya cimwemwe. Potengela citsanzo cake, akulu angagonjetse zovuta zimene amakumana nazo, na kukhalabe acimwemwe potumikila Yehova. Tiyeni tione mmene angacitile zimenezi.

3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino? Nanga tiphunzilenso ciyani?

3 M’nkhani ino, tikambilane zovuta zinayi zimene akulu amakumana nazo: (1) kulinganiza bwino nthawi yolalikila na kusamalila maudindo ena, (2) kupeza nthawi yocita ubusa, (3) kulimbana na zifooko za iwo eni, komanso (4) kucita na zophophonya za ena. Cina, tiphunzile mmene Paulo anagonjetsela zovutazi, ndiponso mmene akulu angatengele citsanzo cake.

KULINGANIZA BWINO NTHAWI YOLALIKILA NA KUSAMALILA MAUDINDO ENA

4. N’cifukwa ciyani nthawi zina kungakhale kovuta kwa akulu kutsogolela pa nchito yolalikila?

4 Cifukwa cake kungakhale kovuta. Akulu ali na maudindo ambili kuwonjezela pa kutsogolela pa nchito yolalikila. Mwacitsanzo, iwo amasinthana kukhala cheyamani pa msonkhano wamkati mwa mlungu, komanso kutsogoza Phunzilo la Baibo la Mpingo. Amakhalanso na nkhani zina zokakamba mu mpingo. Kuwonjezela apo, amaphunzitsanso atumiki othandiza nchito, komanso amakonda kupeleka cilimbikitso kwa abale na alongo awo. (1 Pet. 5:2) Akulu ena amagwila nchito yomanga Nyumba za Ufumu na zimango zina za gulu, komanso kuzikonza. Ngakhale n’telo, mofanana na onse mu mpingo, nchito yofunika ngako kwa mkulu aliyense ni yolalikila uthenga wabwino.—Mat. 28:19, 20.

5. Pokhala mlaliki, kodi Paulo anapeleka citsanzo cotani?

5 Citsanzo ca Paulo. Cimene cinam’thandiza kwambili kukwanitsa utumiki wake, cili pa Afilipi 1:10. Iye anati: “Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.” Paulo anatsatila malangizo ake amenewa. Iye anapatsidwa nchito yolalikila, ndipo kwa zaka zambili anaona nchitoyo kukhala cinthu cofunika kwambili. Anali kulalikila “poyela komanso kunyumba ndi nyumba.” (Mac. 20:20) Sanali kulalikila kamodzi pa tsiku, kapena kamodzi pa mlungu. Koma anali kulalikila pa mpata uliwonse wapezeka. Mwacitsanzo, pamene anali kuyembekezela mabwenzi ake ku Atene, analalikila kagulu ka anthu ochuka amene ena a iwo analabadila uthenga wake. (Mac. 17:16, 17, 34) Ngakhale pamene Paulo anali ‘womangidwa,’ analalikila anthu amene anabwela kwa iye.—Afil. 1:13, 14; Mac. 28:16-24.

6. Kodi Paulo anaphunzitsako ena zinthu zotani?

6 Paulo anali kugwilitsila nchito bwino nthawi yake. Kambili, anali kupita na ena mu ulaliki. Mwacitsanzo, pa ulendo wake wa umishonale woyamba, anapita na Yohane Maliko, ndipo pa ulendo waciŵili anapita na Timoteyo. (Mac. 12:25; 16:1-4) Mosakaikila, Paulo anaphunzitsa amuna amenewa mokhazikitsila mpingo, mocitila maulendo aubusa, komanso mmene angakhalile aphunzitsi aluso.—1 Akor. 4:17.

Tengelani citsanzo ca Paulo mwa kukhala okonzeka kulalikila (Onani ndime 7) *

7. Kodi akulu angatsatile bwanji malangizo a Paulo apa Aefeso 6:14, 15?

7 Phunzilo. Akulu angatengele citsanzo ca Paulo mwa kulalikila ku nyumba na nyumba, komanso pa mpata uliwonse wapezeka. (Ŵelengani Aefeso 6:14, 15.) Mwacitsanzo, iwo angalalikile akapita kokagula zinthu kapena kumalo anchito. Pamene akumanga zimango za gulu, angalalikile anthu okhala nawo pafupi ndiponso ocita malonda. Mofanana na Paulo, akulu angaphunzitseko ena pamene ali mu ulaliki, kuphatikizapo atumiki othandiza.

8. Kodi nthawi zina mkulu ayenela kucita ciyani?

8 Akulu sayenela kutangwanika kwambili na maudindo a mu mpingo kapena m’dela, cakuti n’kusoŵa nthawi yolalikila. Kuti azikhala na nthawi yocitako zinthu zina, nthawi zina mkulu angafunike kumakanako nchito zina. Pambuyo poganizila mwa pemphelo, iye angapeze kuti nchitoyo ingamudyele nthawi yocita zinthu zofunika kwambili. Zinthuzo ziphatikizapo kucititsa kulambila kwa pabanja mlungu uliwonse, kutengako mbali mokwanila pa nchito yolalikila, kapena kuphunzitsa ana awo molalikila. Akulu ena cimawavuta kukana maudindo ena owonjezela. Koma ayenela kudziŵa kuti Yehova amamvetsa colinga cawo cabwino cofuna kulinganiza bwino zinthu.

KUPEZA NTHAWI YOCITA UBUSA

9. Kodi akulu otangwanika angamavutike kucita ciyani?

9 Cifukwa cake kungakhale kovuta. Anthu a Yehova amakumana na mavuto ambili. M’masiku ano otsiliza, tonsefe timafunikila cilimbikitso, citonthozo, komanso thandizo. Ndipo nthawi zina, ena angafunike kuwalangiza kuti apewe khalidwe loipa. (1 Ates. 5:14) N’zoona kuti akulu, sangathetse mavuto onse amene anthu a Yehova amakumana nawo. Koma ngakhale n’telo, Yehova amafuna kuti akulu acite zimene angathe polimbikitsa nkhosa zake na kuziteteza. Kodi akulu otangwanika angapatule bwanji nthawi kuti athandize abale na alongo?

Muziyamikila ena na kuwalimbikitsa (Onani ndime 10, 12) *

10. Malinga na 1 Atesalonika 2:7, kodi Paulo anali kucita nawo zinthu motani anthu a Yehova?

10 Citsanzo ca Paulo. Iye anali kufuna-funa mipata yoyamikila abale ake na kuwalimbikitsa. Akulu ayenela kutengela citsanzo cake mwa kuwaonetsa cikondi anthu a Yehova. (Ŵelengani 1 Atesalonika 2:7.) Paulo anauza alambili anzake kuti iye komanso Yehova amawakonda. (2 Akor. 2:4; Aef. 2:4, 5) Iye anali kuwaona kuti ni mabwenzi ake, ndipo anali kuceza nawo. Anaonetsa kuti amawakhulupilila mwa kuwauza moona mtima nkhawa zake ndiponso zifooko zake. (2 Akor. 7:5; 1 Tim. 1:15) Komabe, sanali kungoganizila za mavuto ake. M’malo mwake, anali kufuna kuthandiza abale ake.

11. N’cifukwa ciyani Paulo anapatsa uphungu abale na alongo ake?

11 Nthawi zina, Paulo anafunika kupatsa uphungu abale na alongo ake. Koma sanali kucita zimenezo cifukwa cokhumudwa. Iye anawapatsa uphungu cifukwa cowakonda, ndipo anafuna kuteteza umoyo wawo wauzimu. Uphungu wake unali wosavuta kutsatila, cifukwa anali kufuna kuti anthuwo aulandile. Mwacitsanzo, Paulo anapeleka uphungu wamphamvu m’kalata yake yopita kwa Akorinto. Atalemba kalatayo, anawatumizila Tito cifukwa anali kufuna kudziŵa mmene Akhristuwo adzacitila na uphungu wa m’kalata yake. Iye anakondwela kwambili kudziŵa kuti iwo analabadila uphunguwo.—2 Akor. 7:6, 7.

12. Kodi akulu angawalimbikitse bwanji alambili anzawo?

12 Phunzilo. Akulu angatengele citsanzo ca Paulo mwa kupatula nthawi yoceza na alambili anzawo. Njila imodzi imene angacitile zimenezi, ni kufika mofulumila ku misonkhano ya mpingo, kuti akhale na maceza olimbikitsa na ena. Zimangotenga mphindi zocepa kuti mupeleke cilimbikitso kwa m’bale kapena mlongo. (Aroma 1:12; Aef. 5:16) Cina, mkulu amene amatengela citsanzo ca Paulo, amalimbitsa cikhulupililo ca alambili anzake poseŵenzetsa Mawu a Mulungu, na kuwatsimikizila kuti Mulungu amawakonda. Ndiponso, amaonetsa cikondi anthu amene akuwayang’anila. Iye amakambilana nawo kaŵili-kaŵili, na kufuna-funa mipata kuti awayamikile. Ndipo mkuluyo akafuna kupeleka uphungu, amazika uphunguwo m’Mawu a Mulungu. Amakamba mosapita m’mbali koma mokoma mtima, cifukwa amafuna kuti opatsidwa uphunguwo aulandile na kuuseŵenzetsa.—Agal. 6:1.

KULIMBANA NA ZIFOOKO ZA IWO ENI

13. Kodi mkulu angayambe kudziona motani cifukwa ca zifooko zake?

13 Cifukwa cake kungakhale kovuta. Akulu ni opanda ungwilo. Iwo amalakwitsa mofanana na munthu aliyense. (Aroma 3:23) Nthawi zina, cingakhale covuta kwa iwo kuona zophophonya zawo moyenela. Ena angamaike kwambili maganizo pa zolephela zawo moti n’kulefuka. Enanso angamaone kuti zophophonya zawo si zazikulu kwambili moti m’posafunikila kupanga masinthidwe.

14. Malinga n’kunena kwa Afilipi 4:13, kodi kudzicepetsa kunam’thandiza bwanji Paulo kulimbana na zifooko zake?

14 Citsanzo ca Paulo. Modzicepetsa, Paulo anazindikila kuti sakanakwanitsa kulimbana na zifooko zake pa iye yekha. Anafunikila thandizo la Mulungu. Poyamba, iye anali wokangalika pozunza Akhristu. Koma pambuyo pake, anavomeleza zolakwa zake, ndipo anali wofunitsitsa kusintha khalidwe lake. (1 Tim. 1:12-16) Na thandizo la Yehova, Paulo anakhala m’busa wacikondi, wacifundo, komanso wodzicepetsa. Anali kudziŵa kuti ali na zophophonya zambili, koma anakhulupilila kuti Yehova anam’khululukila, ndipo sanaike maganizo ake pa zophophonya zake. (Aroma 7:21-25) Sanayembekezele kukhala wangwilo. Koma anayesetsa kukulitsa makhalidwe acikhristu, ndipo modzicepetsa anadalila thandizo la Yehova kuti akwanilitse utumiki wake.—1 Akor. 9:27; ŵelengani Afilipi 4:13.

Yesetsani kugonjetsa zifooko za inu mwini (Onani ndime 14-15) *

15. N’cifukwa ciyani akulu ayenela kuona zophophonya zawo moyenela?

15 Phunzilo. Akulu ni anthu opanda ungwilo. Ndipo Yehova amafuna kuti iwo azivomeleza zophophonya zawo, komanso kukulitsa makhalidwe acikhristu. (Aef. 4:23, 24) Mkulu ayenela kudzisanthula poseŵenzetsa Mawu a Mulungu, na kupanga masinthidwe ofunikila. Akatelo, Yehova adzam’thandiza kukhala wacimwemwe komanso mkulu wabwino.—Yak. 1:25.

KUTHANA NA ZOPHOPHONYA ZA ENA

16. N’ciyani cingacitike ngati mkulu asumika maganizo pa zophophonya za ena?

16 Cifukwa cake kungakhale kovuta. Akulu akamacitila zinthu pamodzi na ofalitsa, amafika podziŵa bwino zophophonya za ofalitsawo. Komabe, ngati sangasamale, akulu angakhumudwe, angacite zinthu mopanda cifundo, kapena angayambe kuweluza ena. Paulo anacenjeza Akhristu kuti Satana amafuna kuti iwo azicita zimenezo.—2 Akor. 2:10, 11.

17. Kodi Paulo anali kuwaona motani abale na alongo ake?

17 Citsanzo ca Paulo. Iye anali kuona abale na alongo ake moyenelela. Anali kudziŵa bwino zophophonya zawo, ndipo nthawi zina anali kucita kumukhumudwa nazo. Ngakhale n’conco, iye anali kudziŵa kusiyana pakati pa khalidwe loipa na ŵanthu oipa. Anali kuwakonda abale ake, ndipo anali kuona zabwino mwa iwo. Pamene abale na alongo anali kuvutika kucita zoyenela, iye sanali kukaikila zolinga zawo, koma anali kuona kuti iwo angofunikila thandizo basi.

18. Kodi muphunzilapo ciyani mukaona mmene Paulo anacitila zinthu na Eodiya komanso Suntuke? (Afilipi 4:1-3)

18 Mwacitsanzo, ganizilani mmene Paulo anathandizila alongo aŵili mu mpingo wa ku Filipi. (Ŵelengani Afilipi 4:1-3.) Zioneka kuti Eodiya na Suntuke anasemphana maganizo, ndipo izi zinapangitsa kuti asakhalenso mabwenzi. Paulo sanacite nawo zinthu mwaukali kapena kuwaweluza, koma anasumika maganizo ake pa makhalidwe awo abwino. Iwo anali alongo okhulupilika amene anali na mbili yabwino. Paulo anadziŵa kuti Yehova anali kuwakonda. Kuona alongowa moyenelela, kunamusonkhezela kuwalimbikitsa kuti athetse kusamvana pakati pawo. Kunam’thandizanso kukhalabe wacimwemwe, ndiponso kukhala pa ubale wolimba na ena mu mpingo.

Pewani kuweluza ena (Onani ndime 19) *

19. (a) Kodi akulu angacite ciyani kuti aziona zabwino mwa ena? (b) Nanga muphunzilapo ciyani pa cithunzi ca mkulu amene akuyeletsa Nyumba ya Ufumu?

19 Phunzilo. Inu akulu, muziyang’ana pa makhalidwe abwino amene abale na alongo ali nawo. Aliyense ni wopanda ungwilo, koma ali na makhalidwe osililika. (Afil. 2:3) N’zoona kuti nthawi na nthawi, akulu angafunike kuwongolela maganizo a m’bale kapena mlongo. Koma monga Paulo, akulu ayenela kuyesetsa kupewa kusumika maganizo pa zokhumudwitsa zimene munthu angakambe kapena kucita. M’malo mwake, angacite bwino kuika maganizo pa cikondi cimene munthuyo ali naco pa Yehova, kupilila kwake potumikila Mulungu, komanso zabwino zimene amatha kucita. Akulu amene amaona zabwino mwa ena, amathandiza kuti mu mpingo mukhale cikondi.

PITILIZANI KUTENGELA CITSANZO CA PAULO

20. Kodi akulu angacite ciyani kuti apitilize kupindula na citsanzo ca Paulo?

20 Inu akulu, mudzapindula kwambili mukapitiliza kutengela citsanzo ca Paulo. Mwacitsanzo, mungaŵelenge nkhani yakuti, “Analankhula Molimba Mtima Chifukwa cha Mphamvu ya Yehova,” m’buku lakuti Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu. Poŵelenga nkhani ngati zimenezi, dzifunseni kuti, ‘Kodi citsanzo ca Paulo cinganithandize bwanji kukhalabe wacimwemwe pamene nikusamalila udindo wanga monga mkulu?’

21. Kodi akulu angakhale otsimikiza za ciyani?

21 Akulunu, kumbukilani kuti Yehova safuna kuti mukhale angwilo, koma afuna kuti mukhale okhulupilika. (1 Akor. 4:2) Iye anali kukondwela na Paulo kaamba kogwila nchito molimbika, komanso cifukwa ca kukhulupilika kwake. Inunso khalani otsimikiza kuti Mulungu amayamikila zimene mumacita pom’tumikila. Iye ‘sadzaiŵala nchito yanu na cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake, mwa kutumikila oyela ndipo mukupitiliza kuwatumikila.’—Aheb. 6:10.

NYIMBO 87 Bwelani Mutsitsimulidwe!

^ Timapindula kwambili na nchito zimene akulu acikondi amagwila mwakhama kuti atithandize. M’nkhani ino, tikambilane zovuta zinayi zimene iwo amakumana nazo. Tikambilanenso mmene citsanzo ca mtumwi Paulo, cingawathandizile kugonjetsa zovuta zimenezo. Cina, idzalimbikitsa tonsefe kuonetsa akulu cifundo na cikondi, komanso kuwacilikiza pa utumiki wawo.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale wakomboka kunchito, ndipo akulalikila mnzake wa kunchito.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mwacikondi mkulu akulimbikitsa m’bale amene wakhala payekha.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale akulangiza m’bale mnzake amene ni wokhumudwa na zimene zinacitika.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mkulu akupewa kudzudzula m’bale amene walekeza nchito imene wadzipeleka kugwila.