Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 17

Zimene Azimayi Angaphunzire kwa Yunike

Zimene Azimayi Angaphunzire kwa Yunike

“Usasiye malamulo a mayi ako, pakuti zimenezi zili ngati nkhata ya maluwa yokongola pamutu pako, ndi mkanda wokongola m’khosi mwako.”​—MIY. 1:8, 9.

NYIMBO NA. 137 Akazi Achikhristu Okhulupirika

ZIMENE TIPHUNZIRE *

Pamene Timoteyo akubatizidwa, mayi ake a Yunike ndi agogo ake aakazi a Loisi akuoneka osangalala komanso onyadira (Onani ndime 1)

1-2. (a) Kodi a Yunike anali ndani, nanga anakumana ndi vuto lotani monga mayi? (b) Fotokozani chithunzi chapachikuto.

 NGAKHALE kuti Baibulo silifotokoza mmene zinalili pa nthawi imene Timoteyo ankabatizidwa, n’zosavuta kuganizira chimwemwe chimene mayi ake, a Yunike anali nacho pa tsikulo. (Miy. 23:25) Yerekezerani kuti mukuwaona akumuyang’ana monyadira pomwe waima m’madzi omulekeza m’chiuno. Iwo akumwetulira pamene agogo ake a Timoteyo a Loisi awagwira ataima nawo pafupi. Akupumira m’mwamba pomwe Timoteyo akumizidwa m’madzi. Potuluka m’madzimo, Timoteyo akumwetulira kwambiri ndipo mayi ake sakuchitira mwina koma kugwetsa misozi ya chisangalalo. Apatu a Yunike akwanitsa kuthandiza mwana wawo kuti azikonda Yehova ndi Mwana wake Yesu Khristu, ngakhale kuti kuchita zimenezi kunali kovuta. Kodi ndi mavuto otani omwe anapirira kuti zimenezi zitheke?

2 Timoteyo analeredwa m’banja limene makolo ake anali osiyana zipembedzo. Bambo ake anali Mgiriki, pomwe mayi ake ndi agogo ake anali Ayuda. (Mac. 16:1) Iye ayenera kuti anali wachinyamata pomwe a Yunike ndi a Loisi anayamba Chikhristu. Koma bambo ake sanalowe nawo chipembedzochi. Ndiye kodi Timoteyo akanakhala mbali iti? Iye anali wamkulu ndithu moti akanatha kusankha yekha zochita. Kodi akanakhala mbali ya bambo ake omwe anali osakhulupirira? Kapena kodi akanapitiriza kutsatira miyambo ya Chiyuda yomwe anaphunzitsidwa kuyambira ali mwana? Kapenanso kodi akanavomera kukhala wotsatira wa Yesu Khristu?

3. Mogwirizana ndi Miyambo 1:8, 9, kodi Yehova amaona bwanji zimene azimayi amachita pothandiza ana awo kuti akhale anzake?

3 Masiku anonso akazi a Chikhristu amakonda mabanja awo. Kuposa chilichonse, iwo amafunitsitsa kuthandiza ana awo kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ndipo Mulungu wathu amayamikira kwambiri khama lawo. (Werengani Miyambo 1:8, 9.) Yehova wathandiza amayi ambiri kuphunzitsa ana awo choonadi.

4. Kodi azimayi amakumana ndi mavuto otani masiku ano?

4 Mwachibadwa, nthawi zina mayi angamadzifunse ngati ana ake adzasankhe kutumikira Yehova ngati mmene anachitira Timoteyo. Ndipotu makolo amadziwa mavuto amene ana amakumana nawo m’dziko la Satanali. (1 Pet. 5:8) Kuwonjezera pamenepo, vuto lina ndi lakuti azimayi ambiri amalera okha ana kapenanso amuna awo salambira Yehova. Mlongo wina dzina lake Christine * ananena kuti: “Mwamuna wanga anali bambo wabwino komanso wokonda banja lake. Koma sankandilola kuphunzitsa ana anga mfundo zimene a Mboni za Yehova amatsatira. Ndinakhala ndikulira kwa zaka zambiri. Ndipo ndinkadzifunsa ngati ana anga adzayambe kulambira Yehova.”

5. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

5 Ngati ndinu mayi wa Chikhristu, inunso mungathandize ana anu kuti azikonda komanso kutumikira Yehova mofanana ndi mmene a Yunike anachitira. Munkhaniyi, tikambirana mmene mungawatsanzirire pophunzitsa ana anu kudzera mu zolankhula ndi zochita zanu. Tionanso mmene Yehova angakuthandizireni.

MUZIPHUNZITSA ANA ANU MWA ZOLANKHULA ZANU

6. Mogwirizana ndi 2 Timoteyo 3:14, 15, kodi n’chiyani chinamuthandiza Timoteyo kuti akhale Mkhristu?

6 Timoteyo ali kamnyamata, mayi ake anayesetsa kumuphunzitsa “malemba oyera,” monga mmene Ayuda ankawatchulira. N’zoona kuti iwo sankadziwa zinthu zambiri chifukwa sankadziwa chilichonse chokhudza Yesu Khristu. Komabe zimene Timoteyo anaphunzira m’Malemba zikanamuthandiza kuti avomereze kukhala Mkhristu. Koma kodi iye akanatero? Monga wachinyamata, iye anali ndi ufulu wosankha kuti akhale Mkhristu. N’zosakayikitsa kuti Timoteyo ‘anakhulupirira pambuyo pokhutira’ ndi choonadi chonena za Yesu chifukwa cha khama la mayi ake. (Werengani 2 Timoteyo 3:14, 15.) A Yunike ayenera kuti anasangalala kwambiri chifukwa choti anakwanitsa kuphunzitsa mwana wawo zokhudza Yehova. Iwotu anachita zinthu mogwirizana ndi dzina lawo lomwe limatanthauza “kugonjetsa.”

7. Kodi a Yunike akanathandiza bwanji mwana wawo kupita patsogolo mwauzimu pambuyo pobatizidwa?

7 Kubatizidwa kunali chinthu chofunika kwambiri pa moyo wa Timoteyo. Koma sikuti nkhawa ya a Yunike inathera pomwepo. Iwo ankaganiza kuti kodi mwana wawo akanasankha kuchita zotani pa moyo wake? Kodi mwina akanayamba kugwirizana ndi anthu a makhalidwe oipa? Kodi akanapita kukaphunzira ku Atene n’kuyamba kukhulupirira nzeru za anthu osaopa Mulungu? Kodi akanawononga nthawi komanso mphamvu zake posakasaka chuma? Amayi ake sakanamusankhira zochita koma akanatha kumuthandiza. Motani? Iwo anakachita zimenezi popitiriza mwakhama kuthandiza mwana wawo kuti azikonda kwambiri Yehova komanso kuyamikira Mwana wake. Sikuti ndi anthu a m’banja losiyana zipembedzo okha omwe amakumana ndi mavuto pothandiza ana kuti azikonda Yehova. Ngakhale pamene makolo onse ali m’choonadi, zikhoza kukhala zovuta kuphunzitsa ana mowafika pa mtima kuti akhale atumiki a Yehova okhulupirika. Ndiye kodi makolo angaphunzire chiyani pa chitsanzo cha a Yunike?

8. Kodi mayi angathandize bwanji mwamuna wake yemwe ndi Mkhristu pophunzitsa ana awo zokhudza Yehova?

8 Muziphunzira Baibulo ndi ana anu. Alongonu, ngati amuna anu ali m’choonadi, Yehova amafuna kuti muziwathandiza pophunzitsa ana anu zokhudza iye. Njira imodzi imene mungachitire zimenezo, ndi kuyesetsa kuthandiza banja lanu kuti lizichita Kulambira kwa Pabanja. Muzilankhula zabwino zokhudza pulogalamuyi ndipo muziganizira zimene mungachite kuti kulambirako kuzikhala kosangalatsa. Mwinanso mungathandize mwamuna wanu kukonza zinthu zinazake zapadera zimene mungafunike kuphunzira. Kuwonjezera pamenepo, ngati mukuona kuti ana ena ndi okulirapo ndipo akufunika kuphunzira nawo Baibulo paokha pogwiritsa ntchito buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, mwina mungathandizane ndi mwamuna wanu powaphunzitsa.

9. Kodi mlongo yemwe mwamuna wake si wa Mboni angapeze kuti thandizo?

9 Alongo ena amafunika kuphunzira Baibulo ndi ana awo chifukwa choti akulera okha anawo kapenanso amuna awo si a Mboni. Ngati umu ndi mmene zilili m’banja lanu, musade nkhawa kwambiri. Yehova adzakuthandizani. Muzigwiritsa ntchito zinthu zophunzitsira zimene wapereka m’gulu lake pophunzira ndi ana anu. Bwanji osafunsa makolo ena odziwa zambiri kuti akuthandizeni kudziwa mmene mungagwiritsire ntchito zinthu zophunzitsirazi pa Kulambira kwa Pabanja? * (Miy. 11:14) Yehova angakuthandizeninso kuti muzilankhulana bwino ndi ana anu. Muzimupempha kuti akuthandizeni kudziwa zimene zili mumtima ndi m’maganizo mwawo. (Miy. 20:5) Kufunsa funso losavuta ngati lakuti, ‘Kodi ndi vuto lotani lomwe umakumana nalo kawirikawiri kusukulu?’ kungakuthandizeni kuti mudziwe zambiri.

10. Kodi ndi njira ina iti imene mungathandizire ana anu kuphunzira za Yehova?

10 Muzikonza mipata yophunzitsira ana anu zokhudza Yehova. Muziuza ana anu zinthu zabwino zokhudza Yehova ndi zinthu zambiri zimene wakuchitirani. (Deut. 6:6, 7; Yes. 63:7) Zimenezi n’zofunika makamaka ngati simungathe kuphunzira ndi ana anu pafupipafupi kunyumba. Christine, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Panalibe mipata yambiri yokambirana ndi ana anga zokhudza Yehova, choncho ndinkagwiritsa ntchito mwayi uliwonse umene wapezeka. Tinkatha kupita kukayenda kapena kukakwera bwato, n’kumakambirana za zinthu zodabwitsa zimene Yehova analenga komanso zinthu zina zambiri zimene zikanawathandiza kukhala mabwenzi ake. Atayamba kukula, ndinayamba kuwalimbikitsa kuti aziphunzira Baibulo paokha.” Kuwonjezera pamenepo, muzilankhula zabwino zokhudza gulu la Yehova komanso abale ndi alongo. Musamalankhule zosonyeza kuti mukuimba mlandu akulu. Zimene mumalankhula zingachititse kuti akakumana ndi mavuto aziwadalira n’kuwapempha malangizo kapena ayi.

11. Mogwirizana ndi Yakobo 3:18, n’chifukwa chiyani n’zofunika kumalimbikitsa mtendere m’banja?

11 Muzilimbikitsa mtendere m’banja mwanu. Nthawi zonse muzisonyeza kuti mumakonda mwamuna ndi ana anu. Muzilankhula mokoma mtima komanso mwaulemu zokhudza mwamuna wanu, ndipo muziphunzitsa ana anu kuchita zomwezo. Mukamatero mungathandize kuti m’banja mwanu mukhale mtendere ndipo zingakhale zosavuta kwa ana anu kuphunzira za Yehova. (Werengani Yakobo 3:18.) Taganizirani chitsanzo cha Jozsef, yemwe akutumikira monga mpainiya wapadera ku Romania. Ali mwana, bambo ake ankaletsa iyeyo, mayi ake ndi abale ake kutumikira Yehova. Jozsef anati: “Mayi anga ankayesetsa kwambiri kuti tizikhala mwamtendere m’banja mwathu. Bambo anga akamachita ukali kwambiri, m’pamene mayi anga ankasonyeza kukoma mtima kwambiri. Akaona kuti zikutivuta kulemekeza komanso kumvera bambo athu, ankakambirana nafe Aefeso 6:1-3. Kenako ankatifotokozera makhalidwe abwino a bambo athu komanso kutithandiza kumvetsa chifukwa chake tiyenera kuwakonda. Zimenezi zinkathandiza kuti tizikhala mwamtendere.”

MUZIPHUNZITSA ANA ANU MWA ZOCHITA ZANU

12. Mogwirizana ndi 2 Timoteyo 1:5, kodi chitsanzo cha a Yunike chinathandiza bwanji Timoteyo?

12 Werengani 2 Timoteyo 1:5. A Yunike ankapereka chitsanzo chabwino kwa Timoteyo. Iwo ayenera anamuphunzitsa kuti chikhulupiriro chenicheni chimaphatikizapo zochita za munthu. (Yak. 2:26) Mosakayikira, Timoteyo ankaona kuti zochita za mayi ake zinkasonyeza kuti ankakonda kwambiri Yehova. Ankaonanso kuti kutumikira Yehova kunkawathandiza mayi akewo kukhala osangalala. Ndiye kodi chitsanzo cha a Yunike chinamuthandiza bwanji? Monga mmene mtumwi Paulo anafotokozera, iye anakhala ndi chikhulupiriro cholimba ngati cha mayi ake. Komatu izi sizinangochitika mwamwayi. Timoteyo ankaona chitsanzo cha mayi ake ndipo ankafunitsitsa kuwatsanzira. Mofanana ndi zimenezi, masiku ano alongo ambiri athandiza anthu a m’banja mwawo kuyamba kutumikira Yehova, “osati ndi mawu” koma zochita. (1 Pet. 3:1, 2) Inunso mungachite zimenezi. Motani?

13. N’chifukwa chiyani mayi ayenera kumaona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri?

13 Muziona kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri. (Deut. 6:5, 6) Mofanana ndi azimayi ambiri, mumalolera kudzimana zinthu zambiri. Mumasala tulo ndipo mumagwiritsa ntchito nthawi, ndalama ndi zinthu zina kuti muzipezera ana anu zinthu zofunika pa moyo. Koma simuyenera kutanganidwa kwambiri ndi zinthu zimenezi mpaka kusoweratu nthawi yolimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Nthawi zonse muzipeza nthawi yopemphera pa nokha, kuphunzira Baibulo komanso kusonkhana. Mukamachita zimenezi, mudzalimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova komanso kupereka chitsanzo chabwino kwa anthu a m’banja lanu ndi anthu ena.

14-15. Kodi mukuphunzira chiyani pa zitsanzo za Leanne, Maria ndi João?

14 Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo za achinyamata, omwe anaphunzira kukonda komanso kukhulupirira Yehova poona zitsanzo za mayi awo. Mwana wa Christine, dzina lake Leanne ananena kuti: “Sizinkatheka kuti tiziphunzira Baibulo poyera, koma amayi nthawi zonse ankapezeka pamisonkhano. Ngakhale kuti sitinkadziwa zambiri zokhudza Baibulo, chitsanzo chawo chinatithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Tinkadziwa kuti a Mboni amaphunzitsa choonadi tisanayambe n’komwe kupita kumisonkhano.”

15 Maria, yemwe nthawi zina bambo ake ankalanga banja lonse likapita kumisonkhano, anati: “Mayi anga ndi mmodzi mwa alongo olimba mtima kwambiri. Ndili mwana, nthawi zina ndinkakana kuchita zinthu zina chifukwa choopa zimene anthu ena anganene. Koma kuona kulimba mtima kwawo komanso kuti nthawi zonse ankaika Yehova pamalo oyamba pa moyo wawo, zinandithandiza kuti ndisamaope anthu.” João, yemwe bambo ake ankaletsa banja lawo kuti lisamakambirane za Yehova panyumba pawo, anati: “Chomwe chinkandilimbikitsa kwambiri n’chakuti mayi anga ankalolera kuchita chilichonse kuti asangalatse bambo anga kupatulapo kusiya kukonda Yehova.”

16. Kodi chitsanzo cha mlongo yemwe ali ndi ana chingathandize bwanji ena?

16 Alongo omwe muli ndi ana, kumbukirani kuti chitsanzo chanu chimathandizanso ena. Ganizirani mmene chitsanzo cha a Yunike chinathandizira mtumwi Paulo. Iye ankadziwa kuti chikhulupiriro chopanda chinyengo cha Timoteyo ‘chinayamba kukhazikika mwa a Yunike.’ (2 Tim. 1:5) Kodi ndi liti pamene Paulo anaona kwa nthawi yoyamba chikhulupiriro cha a Yunike? N’kutheka kuti ndi pa ulendo wake woyamba waumishonale pomwe anakumana ndi a Loisi ndi a Yunike ku Lusitara ndipo mwina anawathandiza kukhala Akhristu. (Mac. 14:4-18) Tangoganizani, pamene Paulo ankalembera Timoteyo kalata patatha zaka 15, ankakumbukirabe ntchito zosonyeza chikhulupiriro za a Yunike ndipo anawagwiritsa ntchito ngati chitsanzo choyenera kutengera. N’zosakayikitsa kuti chikhulupiriro chawo chinalimbikitsa kwambiri mtumwi Paulo komanso Akhristu ena. Ngati mukulera nokha ana kapena muli m’banja losiyana zipembedzo, dziwani kuti kukhulupirika kwanu kumathandiza komanso kulimbikitsa ena.

Kuthandiza mwana kuti azikonda Yehova kumatenga nthawi, choncho musamataye mtima (Onani ndime 17)

17. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mutaona kuti mwana wanu sakufuna kutumikira Yehova ngakhale kuti mwayesetsa kumuphunzitsa?

17 Koma bwanji ngati mutaona kuti zimene mukuchita pofuna kuthandiza mwana wanu sizikuphula kanthu? Muzikumbukira kuti kuphunzitsa mwana kumatenga nthawi yaitali. Monga mmene chithunzichi chikusonyezera, mukadzala mbewu nthawi zina mungayambe kukayikira ngati idzakule n’kubereka zipatso. Ngakhale sikumudziwa ngati mbewuyo ingabereke zipatso, mumapitirizabe kuthirira kuti ikule. (Maliko 4:26-29) Mofanana ndi zimenezi, monga mayi nthawi zina mungamakayikire ngati mukuwafika pamtima ana anu. N’zoona kuti simungawasankhire zochita. Koma mukamapitiriza kuchita zonse zimene mungathe powaphunzitsa, mumawapatsa mwayi woti akhale pa ubwenzi ndi Yehova.​—Miy. 22:6.

MUZIDALIRA YEHOVA KUTI AKUTHANDIZENI

18. Kodi Yehova angathandize bwanji ana anu kuti akhale mabwenzi ake?

18 Kuyambira kale, Yehova wakhala akuthandiza achinyamata ambiri kuti akhale mabwenzi ake. (Sal. 22:9, 10) Iye angathandizenso ana anu kukhala naye pa ubwenzi ngati iwowo akufuna. (1 Akor. 3:6, 7) Ngakhale zitaoneka kuti sakumutumikira ndi mtima wonse, iye adzapitiriza kuwakonda. (Sal. 11:4) Akadzangosonyeza ngakhale pang’ono “maganizo abwino” iye adzawathandiza. (Mac. 13:48; 2 Mbiri 16:9) Adzakuthandizani kulankhula zoyenera pa nthawinso yoyenera pamene ana anu akufunikira kwambiri kumva zimenezo. (Miy. 15:23) Kapenanso angalimbikitse m’bale kapena mlongo wina mumpingo kuti awasonyeze chidwi. Ngakhale anawo atakula, Yehova angawathandize kukumbukira zimene munawaphunzitsa m’mbuyomu. (Yoh. 14:26) Yehova adzakudalitsani kwambiri mukamapitiriza kuphunzitsa ana anu mwa zolankhula ndi zochita zanu.

19. N’chifukwa chiyani simuyenera kukayikira kuti Yehova akusangalala nanu?

19 Sikuti chikondi cha Yehova kwa inu chimadalira pa zimene ana anu asankha. Iye amakukondani chifukwa chakuti inuyo mumamukonda. Ngati mukulera nokha ana, Yehova akulonjeza kuti adzakhala Atate wa ana anu komanso Mtetezi wanu. (Sal. 68:5) Simungachititse kuti ana anu asankhe kutumikira Yehova kapena ayi. Koma mukapitiriza kumudalira n’kumachita zonse zomwe mungathe powathandiza, iye adzasangalala nanu.

NYIMBO NA. 134 Ana Ndi Mphatso Yochokera kwa Yehova

^ Nkhaniyi ifotokoza zimene akazi a Chikhristu omwe ali ndi ana angaphunzire kwa mayi ake a Timoteyo, a Yunike ndiponso mmene angathandizire ana awo kudziwa komanso kukonda Yehova.

^ Mayina ena asinthidwa.

^ Mwachitsanzo, onani phunziro 50 m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, komanso nkhani yakuti, “Njira Zopangira Kulambira kwa Pabanja Kapena Kuphunzira Baibulo Patokha” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2011, tsamba 6-7.