Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya malumbiro?

Lumbiro ndi mawu osonyeza “kulonjeza zinazake ndipo nthawi zambiri wolonjezayo, amatchula Mulungu monga . . . mboni yake.” Lumbiro lingakhale mawu ongolankhula kapena kuchita kulemba.

Anthu ena angamaganize kuti kulumbira sikoyenera chifukwa Yesu ananena kuti: “Usamalumbire n’komwe, . . . Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi, pakuti mawu owonjezera pamenepa achokera kwa woipayo.” (Mat. 5:33-37) Komatu Yesu ankadziwa kuti mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, nthawi zina anthu ankafunika kuchita malumbiro ndipo atumiki ena okhulupirika anachitapo malumbiro. (Gen. 14:22, 23; Eks. 22:10, 11) Ankadziwanso kuti Yehova anachitapo malumbiro osiyanasiyana. (Aheb. 6:13-17) Choncho, apa Yesu sankatanthauza kuti sitiyenera kuchita malumbiro. M’malomwake iye ankatichenjeza kuti sitiyenera kuchita malumbiro opanda tanthauzo kapena pa zinthu zosafunika kwenikweni. Tiziona kuti kuchita zinthu mogwirizana ndi mawu athu ndi nkhani yaikulu choncho tizichita zimene timalankhula.

Ndiye mungatani ngati mwauzidwa kuti mulumbire? Choyamba, muzitsimikiza kuti mungachitedi zomwe mukulumbirazo. Ngati mukukayikira, zingakhale bwino kuti musalumbire. Mawu a Mulungu amachenjeza kuti: “Kuli bwino kuti usalonjeze kusiyana ndi kulonjeza koma osakwaniritsa zimene walonjezazo.” (Mlal. 5:5) Chachiwiri, muziganizira mfundo za m’Malemba zokhudza lumbirolo ndipo kenako muzichita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chanu. Kodi zina mwa mfundo za m’Malemba zimenezi ndi ziti?

Malumbiro ena satsutsana ndi chifuniro cha Mulungu. Mwachitsanzo, a Mboni za Yehova amachita malonjezo pa ukwati wawo. Malonjezo amenewa amakhala malumbiro. Mkwati ndi mkwatibwi amalonjezana pamaso pa Mulungu ndi anthu kuti adzakondana, kusamalirana komanso kulemekezana “pa nthawi yonse imene [awiriwo] adzakhale ndi moyo.” (Anthu ena sanganene ndendende mawuwa akamakwatirana, komabe amachita malonjezo pamaso pa Mulungu.) Zikatero, iwo amakhala mwamuna ndi mkazi wake ndipo amafunika kukhala m’banjalo kwa moyo wawo wonse. (Gen. 2:24; 1 Akor. 7:39) Choncho malumbiro amenewa ndi oyenera ndipo ndi ogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.

Malumbiro ena amatsutsana ndi chifuniro cha Mulungu. Akhristu oona sachita malumbiro monga akuti, adzamenya nkhondo poteteza dziko lawo kapenanso akuti adzasiya kukhulupirira Mulungu chifukwa kuchita zimenezi kungakhale kuswa malamulo a Mulungu. Akhristu ‘sali mbali ya dzikoli’ choncho salowerera nawo m’mikangano komanso m’nkhondo za m’mayiko.​—Yoh. 15:19; Yes. 2:4; Yak. 1:27.

Malumbiro ena amayendera chikumbumtima cha munthu. Nthawi zina timafunika kuganizira mosamala malumbiro ena poganizira malangizo a Yesu akuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.”​—Luka 20:25.

Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti Mkhristu akufuna kukhala mzika ya dziko lina kapena kupeza pasipoti ndipo wazindikira kuti, kuti zimenezi zitheke akufunika kulumbira kuti adzakhala wokhulupirika kudzikolo. Ngati m’dzikolo kuchita lumbiroli kumatanthauza kuti munthu adzachita zinthu zosemphana ndi malamulo a Mulungu, chikumbumtima cha Mkhristu sichingamulole kuti alumbire, pokhapokha ngati aboma atamulola kusintha mawu ena ndi ena mulumbirolo kuti agwirizane ndi chikumbumtima chake.

Kuchita lumbiro loti adzakhala wokhulupirika, lomwe mawu ena asinthidwa, kungakhale kogwirizana ndi mfundo ya pa Aroma 13:1, yomwe imati: “Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.” Choncho, Mkhristu angaone kuti palibe cholakwika ndi lumbirolo chifukwa ndi zomwenso Mulungu amafuna kuti Akhristu azichita.

Chikumbumtima chingagwirenso ntchito ngati Mkhristu atauzidwa kugwiritsa ntchito chinachake kapena manja mwanjira inayake polumbira. Kale, Aroma komanso Asukuti ankagwiritsa ntchito malupanga awo polumbira posonyeza mphamvu za mulungu wawo wankhondo ndiponso kutsimikizira kuti munthu wolumbirayo adzakhala wokhulupirika. Agiriki ankaimika dzanja polumbira. Pochita zimenezi ankasonyeza kuti akuzindikira kuti pali winawake wamphamvu, amene akumva komanso kuona zomwe zikuchitikazo, yemwe anthu ayenera kuyankha kwa iye.

N’zoona kuti mtumiki wa Yehova sangalumbire pogwiritsa ntchito chizindikiro chilichonse cha dziko chogwirizana ndi kulambira konyenga. Koma bwanji ngati a khoti atakupemphani kuti mugwire Baibulo, polumbira kuti mudzapereka umboni woona? Pamenepo mungasankhe kutero, popeza m’Malemba muli zitsanzo za atumiki okhulupirika, omwenso polumbira anachita zinazake. (Gen. 24:2, 3, 9; 47:29-31) Mpofunika kukumbukira kuti mukamachita lumbiro ngati limenelo, mukulonjeza pamaso pa Mulungu kuti mulankhula zoona zokhazokha. Muyenera kukonzekera kuyankha moona mtima funso lililonse lomwe mungafunsidwe.

Popeza kuti timaona ubwenzi wathu ndi Yehova kukhala wamtengo wapatali, tiyenera kupemphera komanso kuganizira mosamala lumbiro lililonse limene tapemphedwa kuti tichite, n’cholinga choti titsimikizire kuti silikutsutsana ndi chikumbumtima chathu kapena mfundo za m’Baibulo. Mukasankha kuchita lumbiro linalake, muzionetsetsa kuti mukuchita zinthu mogwirizana ndi lumbirolo.​—1 Pet. 2:12.