Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi Baibo imati ciyani pa nkhani ya kucita malumbilo?

Lumbilo limatanthauza “kulengeza kapena kulonjeza mwalamulo kuti udzacita zimene walonjezazo, ndipo nthawi zambili umachula Mulungu kukhala mboni.” Munthu angacite lumbilo pakamwa kapena mocita kulemba.

Ena angaganize kuti kucita lumbilo n’kulakwa cifukwa Yesu anati: “Usamalumbile n’komwe . . . Tangotsimikizani kuti mukati ‘Inde’ akhaledi Inde, ndipo mukati ‘Ayi,’ akhaledi Ayi, pakuti mawu owonjezela pamenepa acokela kwa woipayo.” (Mat. 5:33-37) Yesu anadziŵa kuti Cilamulo ca Mose cinafuna kuti alambili okhulupilika a Mulungu azicita malumbilo pa zocitika zina. (Gen. 14:22, 23; Eks. 22:10, 11) Anadziŵanso kuti Yehova iye mwini analumbilapo. (Aheb. 6:13-17) Apa Yesu sanatanthauze kuti sitiyenela kucita malumbilo. M’malo mwake, iye anali kucenjeza anthu kupewa kucita malumbilo pa zinthu zosafunika, kapena kulumbila kopanda tanthauzo. Conco, nthawi zonse tizicita zimene talonjeza cifukwa n’zimene Yehova amafuna.

Nanga mungacite ciyani ngati akuuzani kuti mucite malumbilo? Coyamba, tsimikizani kuti mudzacitadi zimene mufuna kulumbilila. Ngati simuli wotsimikiza, ni bwino kusacita malumbilo amenewo. Mawu a Mulungu amaticenjeza kuti: “Kuli bwino kuti usalonjeze kusiyana ndi kulonjeza koma osakwanilitsa zimene walonjezazo.” (Mlal. 5:5) Cotsatila, ganizilani mfundo za m’Malemba zogwilizana na zimene mufuna kulumbilila, kenako pangani cisankho motsatila cikumbumtima canu cophunzitsidwa Baibo. Kodi zina mwa mfundo za m’Malemba n’ziti?

Malumbilo ena amagwilizana na cifunilo ca Mulungu. Mwacitsanzo, Mboni za Yehova zimalumbililana pomanga ukwati. Malumbilowo amakhala malonjezo. Mwamuna na mkazi amalonjezana pamaso pa Mulungu komanso pamaso pa anthu, kuti adzakondana na kulemekezana “ku nthawi yonse imene [aŵiliwo] adzakhala na moyo.” (Okwatilana ena sacita kukamba malumbilo pamaso pa anthu, koma amalumbilabe pamaso pa Mulungu.) Ndiyeno, amawalengeza kuti tsopano iwo ni banja, ndipo ukwati wawo umakhala mgwilizano wa moyo wonse. (Gen. 2:24; 1 Akor. 7:39) Malumbilo aukwati amenewo ni oyenelela, ndipo ni ogwilizana na cifunilo ca Mulungu.

Malumbilo ena sagwilizana na cifunilo ca Mulungu. Mkhristu woona sayenela kucitako malumbilo olonjeza kuti adzateteza dziko lawo pogwilitsila nchito zida za nkhondo, kapena kulumbilila kuti sadzakhulupililanso mwa Mulungu. Kucita zimenezo n’kuphwanya malamulo a Mulungu. Akhristu sayenela kukhala “mbali ya dzikoli.” Conco, sitingatengeko mbali m’mikangano yawo.—Yoh. 15:19; Yes. 2:4; Yak. 1:27.

Malumbilo ena amakhala nkhani ya cikumbumtima. Nthawi zina, tingafunike kupenda mosamala lumbilo lathu poseŵenzetsa uphungu wa Yesu wakuti: “Pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.”—Luka 20:25.

Mwacitsanzo, tinene kuti Mkhristu akusaina mapepala kuti akhale nzika ya dzikolo, kapena kuti atenge pasipoti. Iye wadziŵa kuti, kuti zimenezo zitheke ayenela kulumbilila kuti adzacita zinthu mokhulupilika. Ngati kulumbilako kuloŵetsamo kucita cina cake cosemphana na malamulo a Mulungu, cikumbumtima ca Mkhristu cophunzitsidwa Baibo sicingamulole kucita zimenezo. Komabe, boma lingamulole kusinthako mawu a lumbilolo, kuti iye acite zinthu na cikumbumtima coyela.

Kucita lumbilo lakuti adzacita zinthu mokhulupilika, limene mawu ake awasinthako, kungakhale kogwilizana na mfundo ya pa Aroma 13:1, imene imati: “Munthu aliyense azimvela olamulila akulu-akulu.” Conco, Mkhristu angaone kuti palibe kulakwika kulikonse akalumbilila kucita cinthu cimenenso Mulungu amafuna kuti Akhristu azicita.

Imakhalanso nkhani ya cikumbumtima mukauzidwa kuti munyamule cina cake m’manja, kapena kupanga gesica ina yake pocita malumbilo. M’nthawi zakale, Aroma komanso Asukuti, pocita malumbilo, anali kunyamula malupanga amene anali cizindikilo ca mulungu wa nkhondo. Cinalinso citsimikizo cakuti msilikaliyo adzakhala wokhulupilika. Agiriki anali kukweza manja awo m’mwamba polumbila. Anali kucita izi poona kuti kuli Mulungu amene amamva zokamba zawo, kuona zocita zawo, komanso kuti anthu adzayankha mlandu kwa iye.

N’zoona kuti pocita malumbilo, mtumiki wa Yehova sanganyamule cizindikilo ciliconse ca dziko monga mbendela cokhudzananso na kulambila konyenga. Koma bwanji ngati m’khoti akuuzani kuti munyamule Baibo, na kulumbila kuti mupeleke umboni wa zoona? Zikakhala conco, mungasankhe kucita zimenezo cifukwa Malemba amachulako anthu okhulupilika amene polumbila anapanga gesica ina yake.(Gen. 24:2, 3, 9; 47:29-31) M’pofunika kukumbukila kuti pocita lumbilo limenelo, mukulonjeza pamaso pa Mulungu kuti mudzakambadi zoona. Muyenela kukhala wokonzeka kuyankha moona mtima mafunso onse amene angakufunseni.

Cifukwa ubale wathu na Yehova ni wamtengo wapatali, mwapemphelo tiyenela kuganizila lumbilo lililonse limene tifuna kucita, na kuonetsetsa kuti silidzapondeleza cikumbumtima cathu, kapena kupwanya mfundo za m’Baibo. Mukasankha kucita malumbilo, tsimikizani kuti mudzasunga lonjezo lanu.—1 Pet. 2:12.