Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 15

Kodi Ndinu “Citsanzo . . . M’kalankhulidwe”?

Kodi Ndinu “Citsanzo . . . M’kalankhulidwe”?

“Ukhale citsanzo kwa okhulupilika m’kalankhulidwe.” —1 TIM. 4:12.

NYIMBO 90 Tilimbikitsane Wina na Mnzake

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi kulankhula ni mphatso yocokela kwa ndani?

 KULANKHULA ni mphatso yocokela kwa Mulungu wathu wacikondi. Munthu woyamba Adamu atangolengedwa, anali kugwilitsila nchito mawu pokambilana na Atate wake wakumwamba. Cina, anali na luso lopeka mawu atsopano. Adamu anaseŵenzetsa luso limeneli popatsa nyama zonse maina. (Gen. 2:19) Ndipo iye anakondwela ngako kukambilana na munthu mnzake kwa nthawi yoyamba—mkazi wake wokongolayo, Hava.—Gen. 2:22, 23.

2. Kodi anthu kalelo komanso masiku ano, aigwilitsila nchito bwanji molakwika mphatso ya kulankhula?

2 Posakhalitsa, mphatso ya kulankhula inagwilitsidwa nchito molakwika. Satana Mdyelekezi ananamiza Hava, ndipo bodzalo linapangitsa anthu kukhala ocimwa komanso opanda ungwilo. (Gen. 3:1-4) Adamu anaseŵenzetsa lilime lake molakwika pamene anaimba mlandu Hava, ngakhalenso Yehova, pa zimene iye mwini analakwitsa. (Gen. 3:12) Kaini ananena bodza kwa Yehova atapha m’bale wake Abele. (Gen. 4:9) Patapita nthawi, mbadwa ya Kaini Lameki, analemba ndakatulo imene inaonetsa kuti anthu anali aciwawa m’nthawi yake. (Gen. 4:23, 24) Nanga masiku ano zinthu zili bwanji? Timaona atsogoleli andale akukamba manyozo mopanda manyazi pagulu la anthu. Kuwonjezela apo, n’covuta kupeza filimu imene mulibe mawu onyoza kapena otukwana. Cinanso, ana a sukulu amamva mawu otukwana kusukulu, ngakhalenso akulu-akulu ku malo anchito. Inde, mawu olaula amene anthu amakonda kukamba, aonetselatu kuti makhalidwe abwino aloŵa pansi kwambili m’dzikoli.

3. Kodi tiyenela kukhala osamala za ciyani? Nanga tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 Tikaleka kusamala, tingazolowele kwambili kumva mawu oipa moti nafenso tingayambe kumawakamba. Pokhala Akhristu, timafuna kukondweletsa Yehova, ndipo kucita izi kumafuna zambili kuposa kungopewa mawu otukwana. Timafuna kuseŵenzetsa mphatso ya mtengo wapatali ya kulankhula m’njila yabwino, imene ni kutamanda Mulungu wathu. M’nkhani ino, tikambilane mmene tingacitile zimenezi (1) mu ulaliki, (2) pa misonkhano ya mpingo, komanso (3) poceza na anthu ŵena. Koma coyamba, tiyeni tikambilane cifukwa cake makambidwe athu amam’khudza Yehova.

MAKAMBIDWE ATHU AMAM’KHUDZA YEHOVA

Kodi zokamba zanu zimaonetsa kuti ndinu munthu wotani? (Onani ndime 4-5) d

4. Malinga na Malaki 3:16, n’cifukwa ciyani makambidwe athu amam’khudza Yehova?

4 Ŵelengani Malaki 3:16. Kodi mungaganizile cifukwa cimene Yehova analolela kuti maina a anthu, amene zokamba zawo zinaonetsa kuti amamuopa na kuganizila za dzina lake, alembedwe mu “buku [lake] la cikumbutso”? Zokamba zathu zimavumbula zimene zili mu mtima mwathu. Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima.” (Mat. 12:34) Nkhani zimene timakamba, zimaonetsa mlingo wa cikondi cathu pa Yehova. Ndipo iye afuna kuti anthu amene amam’konda akasangalale na moyo kwamuyaya m’dziko latsopano.

5. (a) Kodi malankhulidwe athu amakhudza bwanji kulambila kwathu? (b) Malinga na zimene tikuona pa cithunzi, kodi tiyenela kudziŵa ciyani za malankhulidwe athu?

5 Makambidwe athu angapangitse kuti Yehova alandile kulambila kwathu kapena ayi. (Yak. 1:26) Anthu osakonda Mulungu amakamba mwaukali, mwankhadzulila, komanso monyada. (2 Tim. 3:1-5) Sitifuna kukhala monga iwo olo pang’ono. Timafunitsitsa kukondweletsa Yehova mwa mawu athu. Koma kodi Yehova angakondwele ngati timakamba mokoma mtima ndiponso mwacifundo pa misonkhano yacikhristu, kapena mu ulaliki, koma n’kumakamba nkhadzulila komanso mopanda cikondi kunyumba?—1 Pet. 3:7.

6. Kodi panakhala zotulukapo zabwino zotani cifukwa ca makambidwe abwino a Kimberly?

6 Tikamagwilitsila nchito bwino mphatso ya kulankhula, ena amatidziŵa kuti ndife alambili a Yehova. Timathandiza anthu okhala nafe pafupi kuona bwino-bwino kusiyana “pakati pa munthu amene akutumikila Mulungu ndi amene sanatumikilepo Mulungu.” (Mal. 3:18) Izi n’zimene zinacitika kwa mlongo wina dzina lake Kimberly. b Iye na mnzake wa m’kalasi anapatsidwa nchito ya pasukulu yoti agwilile pamodzi. Pambuyo pogwila nchitoyo, mnzake wa m’kalasi anaona kuti Kimberly anali kusiyana na ana ena pasukulupo. Iye sanali kukambila ena zoipa, kapena kuseŵenzetsa mawu acipongwe. Koma anali kukamba mokoma mtima. Mnzake wa m’kalasi wa Kimberly anacita cidwi, ndipo anavomela kuphunzila Baibo. Yehova amakondwela kwambili ngati makambidwe athu amakopa anthu kuti aphunzile coonadi.

7. Kodi mumafuna kugwilitsila nchito motani mphatso ya kulankhula imene Mulungu anakupatsani?

7 Tonsefe timafuna kuti makambidwe athu azilemekeza Yehova, komanso kuti abale athu azitikonda. Lomba, tiyeni tikambilane zimene tingacite kuti tipitilize kukhala “citsanzo . . . m’kalankhulidwe.”

KHALANI CITSANZO MU ULALIKI

Kukamba na anthu mokoma mtima mu ulaliki kumakondweletsa Yehova (Onani ndime 8-9)

8. Kodi Yesu anatipatsa citsanzo cotani pa nkhani yoseŵenzetsa mphatso ya kulankhula mu ulaliki?

8 Muzikamba mokoma mtima komanso mwaulemu ena akakukhumudwitsani. Pa utumiki wake, Yesu anaimbidwa mlandu wabodza wakuti anali cidakwa, wosusuka, wanchito wa Mdyelekezi, wonyozela Sabata, ndiponso kuti anali wonyoza Mulungu. (Mat. 11:19; 26:65; Luka 11:15; Yoh. 9:16) Ngakhale n’conco, iye sanabwezele mwa kukamba mwaukali. Mofanana na Yesu, ena akatikambila mawu onyoza tizipewa kubwezela. (1 Pet. 2:21-23) Komabe, kudziletsa kotelo kumakhala kovuta. (Yak. 3:2) Nanga n’ciyani cingatithandize?

9. N’ciyani cingatithandize kulamulila lilime lathu mu ulaliki?

9 Musakhumudwe ngati mwininyumba wakunyozani mu ulaliki. M’bale wina dzina lake Sam anati: “Nimakumbukila mfundo yakuti uthengawo ni wofunikila kwa mwininyumbayo, komanso kuti iye akhoza kusintha.” Nthawi zina, mwininyumba amakhala wokwiya cifukwa tamufikila panthawi yolakwika. Tikapeza munthu wokwiya mu ulaliki, tingacite zimene mlongo wina dzina lake Lucia amacita. Tingapeleke pemphelo lacidule, kupempha Yehova kuti atithandize kukhalabe odekha kuti tipewe kukamba mwaukali kapena mopanda ulemu.

10. Malinga n’kunena kwa 1 Timoteyo 4:13, tiyenela kukhala na colinga cotani?

10 Khalani mphunzitsi wogwila mtima kwambili. Timoteyo anali mlaliki waluso, koma anafunika kupitiliza kunola luso lake la kuphunzitsa. (Ŵelengani 1 Timoteyo 4:13.) Kodi tingacite ciyani kuti tikhale aphunzitsi ofika munthu pamtima mu ulaliki? Tizikonzekela bwino lomwe. Tiyamikila kuti tili na zida zosiyana-siyana zotithandiza kukhala aphunzitsi abwino. Mudzapeza mfundo zothandiza mukafufuza m’bulosha yakuti, Citani Khama pa kuŵelenga na Kuphunzitsa, komanso pa mbali yakuti “Citani Khama mu Ulaliki,” yopezeka mu Kabuku ka Umoyo na Utumiki. Kodi mumaseŵenzetsa zida zimenezi mokwanila? Tikakonzekela bwino, mantha amacepa ndipo timakamba mwacidalilo.

11. N’ciyani cathandiza Akhristu ena kukhala aphunzitsi abwino?

11 Cina cingatithandize kukhala aphunzitsi abwino, ni kuphunzilako kwa ena mu mpingo. M’bale Sam amene tam’chula, amafuna kudziŵa cimene cathandiza Akhristu ena kukhala aphunzitsi abwino. Iye amaona mmene iwo amaphunzitsila, ndipo amatengela citsanzo cawo. Mlongo wina dzina lake Talia, amamvetsela mosamalitsa kwa akambi aluso akamapeleka nkhani za onse mu mpingo. Mwa kutelo, waphunzila luso la kukambilana bwino nkhani zimene anthu amafunsapo kaŵili-kaŵili mu ulaliki.

KHALANI CITSANZO PA MISONKHANO

Kuimba na mtima wonse pa msonkhano kumakondweletsa Yehova (Onani ndime 12-13)

12. Kodi ena cimawavuta kucita ciyani?

12 Tonsefe tingatengeko mbali pa misonkhano ya mpingo tikamaimba, na kupeleka ndemanga zokonzekela bwino. (Sal. 22:22) Ena cimawavuta kuimba nyimbo kapena kupeleka ndemanga pagulu. Kodi na imwe cimakuvutani? Ngati n’conco, onani cimene cathandiza ena kuthetsa mantha amenewo.

13. N’ciyani cingakuthandizeni kuimba na mtima wonse pa msonkhano?

13 Muziimba mocokela pansi pamtima. Tikamaimba nyimbo za Ufumu, colinga cathu cacikulu ni kutamanda Yehova. Mlongo wina dzina lake Sara amaona kuti sadziŵa kuimba bwino. Koma amafuna kutamanda Yehova m’nyimbo. Conco, iye wapeza kuti n’kothandiza kukonzekela nyimbozo ali ku nyumba, monga mmene amakonzekelela mbali zina za msonkhano. Amaziyeseza nyimbozo na kuona mmene mawu ake akugwilizanila na mfundo zimene adzaphunzila ku msonkhano. Iye anati: “Izi zimanithandiza kusumika maganizo anga pa mawu, osati mmene nikuimbila.”

14. N’ciyani cingakuthandizeni kuyankhapo pa misonkhano mukamacita mantha?

14 Muziyankhapo kaŵili-kaŵili. Izi zingakhale zovuta kwa ena. Mlongo Talia amene tam’chula uja anati: “Nikamayankha pagulu, nimacita mantha kwambili olo kuti ena samaona zimenezo, cifukwa mawu anga amamveka odekha. Koma cimanivuta kuyankhapo.” Ngakhale n’telo, mlongo Talia saleka kupelekapo ndemanga. Akamakonzekela misonkhano, iye amakumbukila kuti yankho loyamba liyenela kukhala lacidule komanso lacindunji. Anati: “Zimenezi zili bwino kwa ine, ndiiko komwe, wotsogoza amayamikila yankho loyamba litakhala lalifupi, losavuta kumva, ndiponso loyankha funso mwacindunji.”

15. Tiyenela kukumbukila ciyani cokhudza ndemanga zathu?

15 Ngakhale Akhristu amene alibe manyazi nthawi zina sapeleka ndemanga pa misonkhano. Cifukwa ciyani? Mlongo wina dzina lake Juliet anati: “Nthawi zina, nimazengeleza kuyankhapo cifukwa nimaona kuti yankho lake ni lacidule kwambili cakuti sinikhutila kuti nayankhapo.” Komabe, tizikumbukila kuti Yehova amafuna kuti tiziyesetsa kupeleka ndemanga zabwino mmene tingathele. c Iye amayamikila kwambili kufunitsitsa kwathu kum’tamanda pa misonkhano, posalola mantha kutilepheletsa kucita zimenezo.

KHALANI CITSANZO MUKAMACEZA NA ANTHU ŴENA

16. Kodi tiyenela kupewa makambidwe otani?

16 Muzipewa kukamba “mawu acipongwe” alionse. (Aef. 4:31) Monga takambila kale, pakamwa pa Mkhristu pasamatuluke mawu otukwana alionse. Ndiponso, pali makambidwe ena amene angamveke monga si acipongwe. Naonso tiyenela kuwapewa. Mwacitsanzo, tizipewa kuyelekezela cikhalidwe ca anthu ena, mtundu wawo, kapena dziko lawo. Cina, tiyenela kupewelatu kukhumudwitsa ena powakambila mawu olasa. M’bale wina anati: “Nthawi zina, nakambapo mawu olasa amene nimaona kuti ni nthabwala cabe komanso kuti alibe vuto, koma osadziŵa kuti wina anakhumudwa nawo mawuwo. Kwa zaka, mkazi wanga wakhala akunithandiza kwambili poniuza mseli nikakamba mawu amene iye na anthu ŵena akhumudwa nawo.”

17. Mogwilizana na Aefeso 4:29, kodi ena tingawalimbikitse bwanji?

17 Muzikamba mawu olimbikitsa. Khalani wofulumila kuyamikila ena, m’malo mosuliza kapena kudandaula. (Ŵelengani Aefeso 4:29.) Aisiraeli anali na zifukwa zambili zokhalila oyamikila, koma mobweleza-bweleza anali kudandaula. Mzimu wodandaula umayambukila anthu ŵena. Kumbukilani kuti lipoti loipa limene azondi 10 anabweletsa, linapangitsa ‘ana onse a Isiraeli “kudandaula za Mose.” (Num. 13:31–14:4) Kumbali ina, ciyamikilo cingathandize ena kupitiliza kucita zabwino. Sitikaikila kuti mwana wamkazi wa Yefita, analimbikitsidwa kwambili kupitiliza utumiki wake cifukwa ca ziyamikilo zimene anali kulandila kwa atsikana anzake. (Ower. 11:40) Mlongo Sara amene tam’chula anati: “Tikamayamikila ena, timawapangitsa kumva kuti Yehova amawakonda komanso kuti ali na malo m’gulu lake.” Conco, muziyesa kupeza mipata yoyamikila ena mocokela pansi pa mtima.

18. Malinga na Salimo 15:1, 2, n’cifukwa ciyani tiyenela kukamba zoona nthawi zonse? Nanga izi ziphatikizapo ciyani?

18 Muzikamba zoona nthawi zonse. Sitingakondweletse Yehova ngati timanama. Iye amadana na bodza la mtundu uliwonse. (Miy. 6:16, 17) Ngakhale kuti anthu ambili masiku ano amaona kuti kunama kulibe vuto kwenikweni, ife timaona bodza mmene Yehova amalionela. (Ŵelengani Salimo 15:1, 2.) Mwa ici, timapewelatu bodza lililonse, ngakhalenso kupeleka mwadala cithunzi colakwika.

Kusintha maceza oipa kuti akhale abwino kumapangitsa kuti Yehova atiyanje (Onani ndime 19)

19. N’ciyani cina cimene tiyenela kusamala naco?

19 Pewani kufalitsa mijedo yovulaza. (Miy. 25:23; 2 Ates. 3:11) Mlongo Juliet amene tam’chula uja, anafotokoza mmene amamvelela akamva mijedo yoipa. Anati: “Nimakhumudwa nikamvetsela mijedo yoipa, komanso nimataya cikhulupililo mwa munthu amene akukamba mijedo ameneyo. Ndiiko komwe, ningakhulupilile bwanji kuti iye sadzanikambilanso misece kwa anthu ena?” Mukaona kuti makambilano anu akuyamba kukhala misece, conde sinthani nkhani.—Akol. 4:6.

20. Kodi mudzayesetsa kucita ciyani mwa zokamba zanu?

20 Popeza tikukhala m’dziko limene makambidwe oipa ni ofala, tiyenela kuyesetsa kuti zokamba zathu zizikondweletsa Yehova. Kumbukilani kuti kulankhula ni mphatso yocokela kwa Yehova, ndipo mmene timaigwilitsila nchito zimam’khudza. Iye adzatidalitsa tikamayesetsa kukamba mawu olimbikitsa mu ulaliki, pa misonkhano, komanso poceza na anthu ŵena. Cisonkhezelo coipa ca dzikoli cikadzatha, cidzakhala cosavuta kulemekeza Yehova mwa mawu athu. (Yuda 15) Koma pali pano, yesetsani kukondweletsa Yehova na “mawu a pakamwa [panu].”—Sal. 19:14.

NYIMBO 121 Kudziletsa N’kofunika

a Yehova anatipatsa mphatso yabwino kwambili—mphatso ya kulankhula. Koma n’zacisoni kuti anthu ambili saiseŵenzetsa bwino mphatsoyi mmene iye afunila. N’ciyani cingatithandize kuti mawu athu azikhala abwino, komanso olimbikitsa m’dzikoli limene makhalidwe akungoipilaipila? Kodi tingam’kondweletse bwanji Yehova mwa mawu athu tikakhala mu ulaliki, pa misonkhano ya mpingo, komanso poceza na ena? Nkhani ino iyankha mafunso amenewa.

b Maina ena asinthidwa.

c Kuti mudziŵe zambili pa nkhani yopeleka ndemanga, onani nkhani yakuti, “Tamandani Yehova Pakati pa Mpingo,” mu Nsanja ya Mlonda ya January 2019.

d MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale akuyankha mwaukali kwa mwininyumba amene ni wokwiya. M’bale sakuimba nyimbo pa msonkhano wa mpingo. Mlongo akukamba misece yovulaza.