Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 16

Pezani Cimwemwe Popatsa Yehova Zabwino Zimene Mungathe Pacanu

Pezani Cimwemwe Popatsa Yehova Zabwino Zimene Mungathe Pacanu

“Aliyense payekha ayese nchito yake.”—AGAL. 6:4.

NYIMBO 37 Kutumikila Yehova na Moyo Wonse

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. N’ciyani cimatibweletsela cimwemwe cacikulu?

 YEHOVA amafuna kuti tikhale acimwemwe. Tidziŵa zimenezi cifukwa cimwemwe ni cipatso ca mzimu wake woyela. (Agal. 5:22) Popeza kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila, timakhala na cimwemwe cacikulu tikamatengako mbali mokwanila mu utumiki wacikhristu, komanso tikamathandiza abale athu m’njila zosiyana-siyana.—Mac. 20:35.

2-3. (a) Malinga na Agalatiya 6:4, ni zinthu ziŵili ziti zimene zingatithandize kukhalabe acimwemwe potumikila Yehova? (b) Nanga tikambilane ciyani m’nkhani ino?

2 Malinga na Agalatiya 6:4, mtumwi Paulo anachula zinthu ziŵili zimene zingatithandize kukhalabe acimwemwe. (Ŵelengani.) Coyamba, colinga cathu cizikhala kupatsa Yehova zabwino koposa zimene ife tingathe pacathu. Tikamamupatsa zimene ife tingathe pacathu, tidzakhala acimwemwe. (Mat. 22:36-38) Caciŵili, tizipewa kudzilinganiza na anthu ŵena. Tiyenela kuyamikila Yehova pa zimene timakwanitsa kucita, maphunzilo athu, kapena maluso athu. Paja zonse zimene tili nazo zinacokela kwa iye. Komabe, ngati ena amatiposa pa mbali zina za utumiki, tiyenela kusangalala kuti iwo akuseŵenzetsa maluso awo potamanda Yehova, osati kuti adzichukitse kapena kudzipezela ulemelelo. M’malo mopikisana nawo, tiziphunzila kwa iwo.

3 M’nkhani ino, tikambilane zimene zingatithandize tikalefuka cifukwa colephela kucita zambili mu utumiki wa Mulungu mmene tikufunila. Tikambilanenso mmene tingaseŵenzetsele bwino maluso athu, komanso zimene tingaphunzile ku zitsanzo za ena.

TIKAONA KUTI SITINGATHE KUCITA ZAMBILI

Kucita zimene tingathe pa msinkhu uliwonse kumakondweletsa Yehova (Onani ndime 4-6) b

4. N’ciyani cingapangitse ena kulefuka? Fotokozani citsanzo.

4 Atumiki ena a Yehova, sakwanitsa kucita zambili mu utumiki cifukwa ca ukalamba kapena matenda. Umu ni mmene zinalili kwa mlongo Carol. Iye anali na mwayi wotumikila kumalo osoŵa. Pa nthawiyo, anali kutsogoza maphunzilo a Baibo 35, ndipo anathandiza angapo kudzipatulila na kubatizika. Utumiki wake unali kuyenda bwino kwambili! Koma anadwala matenda aakulu, moti nthawi zambili anali kungokhala panyumba. Iye anati: “Cifukwa ca kudwala kwanga, nimalephela kucita zambili poyelekeza na anthu ŵena, moti nimaona kuti ndine wolephela. Nimalefuka poona kuti siningathenso kucita zambili mmene nimafunila.” Mlongo Carol amayesetsa kupatsa Yehova zimene amakwanitsa. Izi n’zoyamikilika kwambili. Sitikaikila kuti Mulungu wathu wacifundo, amayamikila zimene mlongoyu amakwanitsa kucita.

5. (a) Kodi tiyenela kukumbukila ciyani tikalefuka cifukwa cosakwanitsa kucita zambili? (b) Malinga n’zimene tikuona pa cithunzi, kodi m’baleyu wakhala akupatsa Yehova zimene angathe motani?

5 Ngati nthawi zina mumalefuka na zimene simukwanitsa kucita, dzifunseni kuti, ‘Kodi Yehova amafuna ciyani kwa ine?’ Iye amafuna kuti muzim’patsa zimene mungakwanitse malinga na mikhalidwe yanu. Ganizilani citsanzo ici: Mlongo amene ali m’zaka za m’ma 80 amalefuka akaona kuti sakwanitsa kucita zambili mu ulaliki poyelekeza na zimene anali kucita ali m’zaka za m’ma 40. Iye amaona monga Yehova sakondwela na zimene amayesetsa kum’patsa. Koma kodi zimenezi n’zoona? Ganizilani izi. Ngati mlongoyu anali kupatsa Mulungu zabwino koposa ali m’zaka za m’ma 40, ndipo akali kupitilizabe kucita zimenezo ngakhale ali na zaka za m’ma 80, ndiye kuti sanaleke kum’patsa zabwino. Tikayamba kuona kuti zimene timacita si zokwanila kwa Yehova, tizikumbukila kuti iye ndiye amaika mlingo wa zimene zimam’kondweletsa. Tikamayesetsa kucita zimene tingathe, Yehova adzati kwa ife: ‘Mwacita bwino kwambili!’—Yelekezelani na Mateyu 25:20-23.

6. Tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca mlongo Maria?

6 Tidzakhala acimwemwe tikamasumika maganizo pa zimene tingakwanitse kucita, osati zimene sitingakwanitse. Ganizilani citsanzo ca mlongo Maria. Iye ali na matenda amene amamulepheletsa kucita zambili mu ulaliki. Poyamba, anali wopsinjika maganizo ndipo anadziona wacabe-cabe. Koma pambuyo pake, iye anaganizila za mlongo wina mu mpingo mwawo amene anali kukhala cigonele cifukwa ca matenda. Mlongo Maria anaganiza zomuthandiza. Anati: “N’nakonza zakuti nilalikile na mlongo wodwalayo pa foni komanso m’makalata. Nthawi iliyonse nikalalikila naye, n’nali kufika panyumba nili wacimwemwe komanso wokhutila cifukwa cothandiza mlongo wanga.” Nafenso tingawonjezele cimwemwe cathu tikamasumika maganizo pa zimene timakwanitsa kucita, osati pa zimene sitingakwanitse. Koma bwanji ngati timacita zambili, kapena timacita bwino pa mbali zina mu utumiki wa Yehova?

NGATI MULI NA MPHATSO, “IGWILITSENI NCHITO”

7. Ni malangizo othandiza ati amene mtumwi Petulo anapatsa Akhristu?

7 M’kalata yake yoyamba youzilidwa, mtumwi Petulo analimbikitsa abale ake kugwilitsila nchito mphatso na maluso awo kuti alimbikitse Akhristu anzawo. Iye analemba kuti: “Molingana ndi mphatso imene aliyense walandila, igwilitseni nchito potumikilana monga oyang’anila abwino amene alandila kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” (1 Pet. 4:10) Conco, tisazengeleze kuseŵenzetsa mphatso zathu mokwanila poopa kuti ena angaticitile nsanje kapena kuti tingawalefule. Tikatelo, ndiye kuti sitikupatsa Yehova zabwino zimene ifeyo tingathe.

8. Malinga na 1 Akorinto 4:6, 7, n’cifukwa ciyani tiyenela kupewa kudzitama na mphatso zathu?

8 Tiziseŵenzetsa mphatso zathu mokwanila. Koma tiyenela kukhala osamala kuti tisadzitame. (Ŵelengani 1 Akorinto 4:6, 7.) Mwacitsanzo, mungakhale kuti muli na mphatso yoyambitsa maphunzilo a Baibo. Musadodome kuseŵenzetsa mphatso imeneyo. Komabe, muzikumbukila kuti simuyenela kudzitama. Tiyelekeze kuti ulaliki unakuyendelani bwino moti munayambitsa phunzilo la Baibo. Conco, mukufunitsitsa kuuzako a m’kagulu kanu ka ulaliki. Pamene mufika ku kaguluko, mupeza kuti mlongo wina akufotokoza mmene ulaliki wake unamuyendela bwino moti anatha kugaŵila magazini imodzi. Iye anagaŵila magazini, koma imwe munayambitsa phunzilo. Kodi mudzacita ciyani? Mudziŵa kuti anthu a m’kagulu kanu adzalimbikitsidwa na cocitika canu. Koma mungacite bwino kuyembekeza kuti mukacifotokoze nthawi ina, kuti musapangitse mlongo wogaŵila magaziniyo kuona kuti munacita bwino kuposa iye. Kucita zimenezo kungakhale kumulemekeza. Koma musaleke kuyambitsa maphunzilo a Baibo. Muli na mphatso, conco igwilitsileni nchito.

9. Kodi mphatso zathu tiyenela kuziseŵenzetsa motani?

9 Tizikumbukila kuti maluso alionse amene tingakhale nawo, ni mphatso zocokela kwa Mulungu. Tiyenela kuseŵenzetsa mphatso zimenezo kuti tilimbikitse mpingo, osati kuti tichuke nazo. (Afil. 2:3) Ngati tiseŵenzetsa mphamvu zathu na maluso athu kucita cifunilo ca Mulungu, tidzakhala na cimwemwe osati cifukwa timaposa ena, koma cifukwa timaseŵenzetsa mphatso zathu kuti tipeleke citamando kwa Yehova.

10. N’cifukwa ciyani si bwino kudziyelekezela na anthu ena?

10 Ngati sangasamale, munthu angagwele mu msampha woyelekezela zimene iye amacita bwino na zimene ena sacita bwino. Mwacitsanzo, m’bale angakhale kuti amakamba bwino nkhani za anthu onse. Ili ndilo luso lake. Koma mu mtima mwake, iye angamaone m’bale amene amavutika kupeleka nkhani za onse kuti ni wolephela. Komabe, m’baleyo angakhale kuti amacita bwino pa mbali zina monga kuceleza, kuphunzitsa bwino ana ake, kapena kulalikila mokangalika. Timayamikila ngako kuti tili na abale na alongo ambili amene amaseŵenzetsa mphatso zawo potumikila Yehova, na kuthandiza ena!

PHUNZILANI KU ZITSANZO ZA ENA

11. N’cifukwa ciyani tiyenela kuyesetsa kutengela citsanzo ca Yesu?

11 Ngakhale kuti tiyenela kupewa kudziyelekezela na ena, tingapindule mwa kuphunzila ku zitsanzo za anthu ena okhulupilika. Citsanzo cabwino koposa n’ca Yesu. Olo kuti iye anali wangwilo, tingatengele makhalidwe ake abwino, komanso zimene anacita. (1 Pet. 2:21) Tikamayesetsa kutengela citsanzo cake mosamala kwambili, tidzakhala atumiki abwino a Yehova komanso aluso mu ulaliki.

12-13. Tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Mfumu Davide?

12 M’mawu a Mulungu, muli zitsanzo zambili za amuna na akazi okhulupilika amene tingatengele citsanzo cawo olo kuti anali opanda ungwilo. (Aheb. 6:12) Ganizilani za Mfumu Davide amene Yehova anamucha kuti “munthu wapamtima panga” kapena “munthu amene amanisangalatsa kwambili,” malinga na kumasulila kwa Baibo ina. (Mac. 13:22) Koma Davide anali wopanda ungwilo. Ndipo iye anacita macimo aakulu. Ngakhale n’conco, iye ni citsanzo cabwino kwa ife. Cifukwa ciyani? Cifukwa atapatsidwa uphungu, iye sanadzilungamitse. M’malo mwake, analandila uphungu wamphamvu umenewo, na kulapa mocokela pansi pa mtima. Mwa ici, Yehova anamukhululukila.—Sal. 51:3, 4, 10-12.

13 Tingaphunzile kwa Davide mwa kudzifunsa kuti: ‘Kodi nimacita ciyani nikapatsidwa uphungu? Kodi nimavomeleza kulakwa kwanga mwamsanga, kapena nimayesa kudzilungamitsa? Kodi nimafulumila kukankhila ena mlandu? Kodi nimayesetsa kuti nisadzabwelezenso zolakwazo?’ Mungadzifunsenso mafunso ngati amenewa mukamaŵelenga nkhani zina za amuna na akazi okhulupilika ochulidwa m’Baibo. Kodi iwo anakumanapo na mavuto ofanana na anu? Kodi anaonetsa makhalidwe abwino ati? Pa zimene mwaŵelengazo dzifunseni kuti: ‘Kodi ningatengele bwanji citsanzo ca mtumiki uyu wa Yehova wokhulupilika?’

14. Kodi tingapindule bwanji poona mmene Akhristu anzathu akucitila?

14 Tingapindulenso mwa kutengela citsanzo ca okhulupilila anzathu—acicepele komanso acikulile. Mwacitsanzo, kodi mungaganizileko wina mu mpingo mwanu amene akupilila mayeso mokhulupilika, mwina ni matenda, kutunthiwa na anzake, kapena kutsutsidwa na acibale ake? Kodi mumaona makhalidwe abwino mwa munthuyo amene mungakonde kuwakulitsa? Kuganizila pa citsanzo cake, kungakuthandizeni kupilila mayeso amene mukukumana nawo. Ni mwayi waukulu cotani nanga kukhala na Akhristu okhulupilika amene tingatengeleko citsanzo cawo kuti tikhale acimwemwe.—Aheb. 13:7; Yak. 1:2, 3.

KHALANI ACIMWEMWE POTUMIKILA YEHOVA

15. Kodi mtumwi Paulo anapeleka uphungu wotani wotithandiza kupitiliza kutumikila Yehova mwacimwemwe?

15 Kuti tilimbikitse mtendele na mgwilizano mu mpingo, aliyense payekha ayenela kupatsa Mulungu zimene angakwanitse. Ganizilani za Akhristu a m’nthawi ya atumwi. Iwo anali na mphatso komanso ma utumiki osiyana-siyana. (1 Akor. 12:4, 7-11) Koma izi sizinawapangitse kuyamba kupikisana kapena kubweletsa magaŵano pakati pawo. M’malo mwake, Paulo analimbikitsa aliyense kucita zimene zikanathandiza kuti “amange thupi la Khristu.” Iye analembela Aefeso kuti: “Thupi lonselo limakula podzimanga lokha mwacikondi, pokhala lolumikizika bwino ndi logwilizana mwa mfundo iliyonse yogwila nchito yake yofunikila.” (Aef. 4:1-3, 11, 12, 16) Amene anacita zimenezo analimbikitsa mtendele na mgwilizano, zimene timaona m’mipingo masiku ano.

16. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciyani? (Aheberi 6:10)

16 Muziyesetsa kupewa kudziyelekezela na ena. M’malo mwake, phunzilani kwa Yesu na kuyesetsa kutengela makhalidwe ake. Pindulani na zitsanzo za m’Baibo komanso zamakono za anthu okhulupilika. Pamene mukupitiliza kucita zimene mungathe, khalani wotsimikiza kuti Yehova “si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu.” (Ŵelengani Aheberi 6:10.) Pitilizani kutumikila Yehova mwacimwemwe, podziŵa kuti iye amayamikila kufunitsitsa kwanu kuti mum’kondweletse.

NYIMBO 65 Pita Patsogolo!

a Tonsefe tingapindule na zitsanzo za ena mu mpingo. Koma tiyenela kupewa kudzilinganiza na iwo. Nkhani ino, itithandiza kukhalabe acimwemwe, na kupewa kudzikuza kapena kulefuka cifukwa coyelekezela nchito zathu na nchito za ena.

b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: M’bale akutumikila pa Beteli ali wacinyamata. Pambuyo pake, anakwatila ndipo anayamba upainiya na mkazi wake. Atakhala na ŵana, anawaphunzitsa kulalikila. Tsopano m’zaka zake zaukalamba, akupitiliza kucita zimene angathe pocita ulaliki wa m’makalata.