Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 25

Yehova Amadalitsa Amene Amakhululukila Anzawo

Yehova Amadalitsa Amene Amakhululukila Anzawo

“Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.”—AKOL. 3:13.

NYIMBO 130 Khalani Wokhululuka

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Yehova amawatsimikizila ciyani anthu ocimwa olapa?

 NGAKHALE kuti Yehova ni Mlengi wathu, Wotipatsa Malamulo, komanso Woweluza wathu, iye alinso Atate wathu wacikondi wakumwamba. (Sal. 100:3; Yes. 33:22) Tikam’cimwila kenako n’kulapa mocokela pansi pamtima, amakhala wofunitsitsa kutikhululukila. (Sal. 86:5) Kupitila mwa mneneli Yesaya, Yehova mwacikondi anatitsimikizila kuti: “Ngakhale macimo anu atakhala ofiila kwambili, . . . adzayela ngati thonje.”—Yes. 1:18.

2. Kodi tiyenela kucita ciyani kuti tikhale pamtendele na anthu ena?

2 Cifukwa ca kupanda ungwilo, zokamba zathu komanso zocita zingakhumudwitse ena. (Yak. 3:2) Komabe, izi sizitanthauza kuti sitingakhale nawo pa ubale wolimba. Tingakhale nawo pa mtendele tikamawakhululukila. (Miy. 17:9; 19:11; Mat. 18:21, 22) Tikakhumudwitsana pa zinthu zazing’ono, Yehova amafuna kuti tizikhululukilana. (Akol. 3:13) Tiyenela kucita zimenezi, cifukwa Yehova “amakhululuka ndi mtima wonse.”—Yes. 55:7.

3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 M’nkhani ino, tikambilane mmene anthu opanda ungwilofe tingatengele Yehova pa nkhani yokhululuka. Ni macimo ati amene tiyenela kuuza akulu? N’cifukwa ciyani Yehova amafuna kuti tizikhululukila ena? Nanga tiphunzilapo ciyani kwa alambili anzathu amene anavutika kwambili cifukwa ca zolakwa za ena?

MKHRISTU AKACITA CHIMO LALIKULU

4. (a) Mtumiki wa Yehova akacita chimo lalikulu, kodi ayenela kucita ciyani? (b) Kodi akulu ali na udindo wotani akakumana na munthu amene anacita chimo?

4 Pakacitika chimo lalikulu, akulu ayenela kuuzidwa. Zitsanzo za macimo amenewo zachulidwa pa 1 Akorinto 6:9, 10. Macimo aakulu amakhala oti munthu waphwanya lamulo la Mulungu. Mkhristu akacita chimo ngati limeneli, ayenela kuuza Yehova m’pemphelo, komanso kukauza akulu a mpingo. (Sal. 32:5; Yak. 5:14) Kodi akulu ali na udindo wotani? Yehova yekha ndiye ali na udindo wokhululukila macimo kwathunthu, ndipo amacita zimenezi pa maziko a nsembe ya dipo. * Komabe, iye anapatsa akulu udindo wounika mwa Malemba kuti aone ngati wocimwayo angakhalebe mu mpingo. (1 Akor. 5:12) Mwa zina, amayesetsa kuyankha mafunso aya: Kodi munthuyo anacita chimolo mwadala? Kodi analibisa kwa ena? Kodi wakhala akucita chimolo kwa nthawi yaitali? Coposa zonse, kodi pali umboni wakuti iye ni wolapadi mocokela pansi pamtima? Kodi pali umboni woonetsa kuti Yehova anam’khululukila?—Mac. 3:19.

5. Kodi pamakhala mapindu otani pa nchito imene akulu amagwila?

5 Akulu akaonana na wolakwayo, colinga cawo ni kupanga cigamulo cimene cimakhala kuti capangidwa kale kumwamba. (Mat. 18:18) Kodi mpingo umapindula bwanji na makonzedwe amenewa? Phindu n’lakuti nkhosa za Yehova za mtengo wapatali zimatetezeka kwa ocimwa osalapa. (1 Akor. 5:6, 7, 11-13; Tito 3:10, 11) Makonzedwewo angathandizenso wocimwayo kulapa kuti Yehova am’khululukile. (Luka 5:32) Akulu amapemphelela wocimwayo amene walapa, na kupempha Yehova kuti am’thandize kucila kuuzimu.—Yak. 5:15.

6. Munthu akacotsedwa mu mpingo, kodi n’zotheka kum’khululukila? Fotokozani.

6 Bwanji ngati munthuyo si wolapa pamene akulu akuonana naye. Zikakhala conco, iye adzacotsedwa mu mpingo. Ngati anaphwanya lamulo la boma, akulu sadzamucinjiliza ku zotulukapo zake. Yehova amalola olamulila a boma kuweluza na kupeleka cilango kwa aliyense amene waphwanya lamulo, kaya ni wolapa kapena ayi. (Aroma 13:4) Komabe, munthuyo akazindikila kuti analakwadi, ndipo walapa mocokela pansi pamtima na kusintha, Yehova ni wokonzeka kum’khululukila. (Luka 15:17-24) Adzam’khululukilabe ngakhale kuti anacita macimo aakulu kwambili.—2 Mbiri. 33:9, 12, 13; 1 Tim. 1:15.

7. Kodi munthu amene anatilakwila tingam’khululukile m’lingalilo lotani?

7 Zili bwino kuti si udindo wathu kugamula kuti Yehova akhululukile wocimwa kapena ayi. Ngakhale n’conco, pali mbali imene tilipo na udindo. Kodi ni mbali iti? Nthawi zina, munthu angatilakwile kwambili. Komabe, iye angapepese kwa ife, na kupempha kuti tim’khululukile. Koma nthawi zina sangacite zimenezo. Zikakhala conco, tingam’khululukilebe m’lingalilo lakuti tingapewe kum’sungila cakukhosi kapena kumukwiyila. Kukamba zoona, izi zingatenge nthawi yaitali komanso khama, maka-maka ngati cimene anatilakwila cikutipweteka mtima kwambili. Nsanja ya Mlonda ya September 15, 1994 inati: “Mukakhululukila wocimwayo, zimenezo sizikutanthauza kuti mukulekelela chimolo. Mkhristu amene amakhululukila ena, amakhala na cidalilo cakuti Yehova adzaweluza nkhaniyo mwacilungamo. Iye ni Woweluza wolungama wa cilengedwe conse, ndipo adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika panthawi yake.” N’cifukwa ciyani Yehova amafuna kuti tizikhululuka, na kusiya zonse m’manja mwake?

CIFUKWA CAKE YEHOVA AMAFUNA KUTI TIZIKHULULUKA

8. Kodi kukhululuka kumaonetsa bwanji kuti timayamikila cifundo ca Yehova?

8 Kukhululuka kumaonetsa kuti ndife oyamikila. M’fanizo lina, Yesu anayelekezela Yehova na mbuye amene anakhululukila mmodzi wa akapolo ake cifukwa colephela kubweza nkhongole yaikulu imene anali nayo. Koma kapolo amene anakhululukidwayo analephela kucitila cifundo kapolo mnzake amene anam’kongola ndalama yocepa. (Mat. 18:23-35) Kodi Yesu anali kuphunzitsa mfundo yotani? Ngati timayamikiladi cifundo cacikulu cimene Yehova amationetsa, tidzalimbikitsidwa kukhululukila ena. (Sal. 103:9) Kalelo, nsanja ina ya mlonda inati: “Kaya takhululukila anzathu kwa nthawi yoculuka motani, sizingafanane na cikhululukilo komanso cifundo cimene Mulungu anationetsa kupitila mwa Khristu.”

9. Kodi Yehova amaonetsa ndani cifundo? (Mateyu 6:14, 15)

9 Tikamakhululukila ena, nafenso tidzakhululukidwa. Yehova amaonetsa cifundo kwa anthu acifundo. (Mat. 5:7; Yak. 2:13) Yesu anafotokoza momveka bwino mfundo imeneyi pamene anaphunzitsa ophunzila ake mopemphelela. (Ŵelengani Mateyu 6:14, 15.) Kalelo, Yehova ananena mfundo imodzimodziyo kwa mtumiki wake Yobu. Munthu wokhulupililika ameneyu anali atakhumudwa kwambili na mawu olasa a anzake atatu—Elifazi, Bilidadi, na Zofari. Yehova anauza Yobu kuti apemphelele anzakewo. Iye atacita zimenezo, Yehova anam’dalitsa.—Yobu 42:8-10.

10. N’cifukwa ciyani kusunga cakukhosi n’kovulaza? (Aefeso 4:31, 32)

10 Kusunga cakukhosi kumavulaza. Yehova amafuna kuti tipeze mpumulo umene umabwela tikapewa kusunga cakukhosi, kumene kuli ngati kunyamula cikatundu colema. (Ŵelengani Aefeso 4:31, 32.) Iye amatilimbikitsa kuti: “Usapse mtima ndipo pewa kukwiya.” (Sal. 37:8) Timapindula tikatsatila ulangizi umenewu. Kusunga cakukhosi kungativulaze kuthupi, na kutibweletsela matenda a maganizo. (Miy. 14:30) Mwacitsanzo, tikamwa poizoni, thanzi lathu n’limene limawonongeka, osati la wina. Mofananamo, tikasunga cakukhosi timadzivulaza ife eni, osati anthu amene anatikhumudwitsa. Conco, tikamakhululukila ena, timapindulitsa moyo wathu. (Miy. 11:17) Timakhala na mtendele wa maganizo, ndipo timapitiliza kutumikila Yehova.

11. Kodi Baibo imati ciyani pa nkhani ya kubwezela? (Aroma 12:19-21)

11 Kubwezela n’kwa Yehova. Si udindo wathu kubwezela wina akatilakwila. (Ŵelengani Aroma 12:19-21.) Popeza ndife opanda ungwilo, n’zosatheka kuweluza ena mwacilungamo, monga mmene Mulungu amacitila. (Aheb. 4:13) Ndipo nthawi zina, mkwiyo ungatilepheletse kucita zinthu mwanzelu. Yehova anauzila Yakobo kulemba kuti: “Mkwiyo wa munthu subala cilungamo ca Mulungu.” (Yak. 1:20) Tingakhale na cidalilo cakuti Yehova adzacita zoyenela, ndipo adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika panthawi yake.

Pewani kukwiya na kusunga cakukhosi. Siyani zonse m’manja mwa Mulungu. Iye adzathetsa mavuto onse obwela cifukwa ca ucimo (Onani ndime 12)

12. Kodi tingaonetse bwanji kuti timakhulupilila cilungamo ca Yehova?

12 Kukhululuka kumaonetsa kuti timakhulupilila cilungamo ca Yehova. Tikasiya zonse m’manja mwa Yehova, timaonetsa kuti timakhulupilila kuti iye adzathetsa zoipa zonse zimene ucimo wabweletsa. M’dziko lake latsopano limene anatilonjeza, kupwetekedwa mtima ‘sikudzakumbukilidwanso ndipo sikudzabwelanso mumtima.’ (Yes. 65:17) Koma bwanji ngati takhumudwa kwambili? Kodi n’zotheka kuthetsa mkwiyo komanso kuleka kusunga cakukhosi? Tiyeni tione mmene ena akwanitsila kucita zimenezi.

MADALITSO AMENE TIMAPEZA TIKAMAKHULULUKILA ENA

13-14. Kodi citsanzo ca Tony na José cakuphunzitsani ciyani pa nkhani yokhululuka?

13 Abale na alongo athu ambili anasankha kukhululuka olo kuti anakhumudwa kwambili na zocita za ena. Kodi iwo apeza madalitso otani cifukwa cocita zimenezi?

14 Zaka zambili kumbuyoku, Tony, * wa ku Philippines, anadziŵa kuti mkulu wake wina anaphedwa na munthu wina dzina lake José. Panthawiyo, Tony anali munthu wamkali komanso waciwawa, ndipo anali kufuna kubwezela. José anagwidwa na kuikidwa m’ndende cifukwa cocita zaupandu. Pambuyo pakuti iye watulutsidwa m’ndende, Tony analumbila kuti akadzam’peza adzamupha. Conco, iye anagula mfuti n’colinga cimeneco. Tony anayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. Iye anati: “Pamene n’nali kuphunzila Baibo, n’naona kuti n’nafunika kusintha khalidwe langa loipa, ndipo zimenezo zinaphatikizapo kuthetsa mkwiyo wanga.” Potsilizila pake Tony anabatizika, ndipo m’kupita kwa nthawi anakhala mkulu mu mpingo. Iye anadabwa kwambili atadziŵa kuti José nayenso anakhala mtumiki wa Yehova wobatizika. Aŵiliwo atakumana anakumbatilana mwacikondi, ndipo Tony anauza José kuti anam’khululukila. Tony anakamba kuti cifukwa cokhululuka, anapeza cimwemwe codzaza tsaya, moti sakanatha kucifotokoza. Ndithudi, Yehova anam’dalitsa Tony cifukwa cokhala wokonzeka kukhululuka.

Citsanzo ca Peter na mkazi wake Sue cionetsa kuti n’zotheka kuthetsa mkwiyo na kusasunga cakukhosi (Onani ndime 15-16)

15-16. Kodi citsanzo ca Peter na mkazi wake Sue cakuphunzitsani ciyani pa nkhani yokhululuka?

15 Mu 1985, pamene Peter na mkazi wake Sue anali pa msonkhano ku Nyumba ya Ufumu, bomba linaphulika mosayembekezeleka. Munthu wina anali atachela bomba m’Nyumba ya Ufumu. Bombalo litaphulika, Sue anavulala koopsa cakuti analeka kuona, kumva, na kununkhiza. Nthawi zambili Peter na mkazi wake Sue anali kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndani anacita zoipa zamtundu umenewu?’ Patapita zaka zambili, munthu wochela bombayo amene sanali mtumiki wa Yehova anagwidwa, ndipo anagamulidwa kuti akapike ndende moyo wake wonse. Peter na mkazi wake Sue atafunsidwa ngati anam’khulukila munthuyo, iwo anayankha kuti: “Yehova amatiphunzitsa kuti kusunga mkwiyo komanso cakukhosi kungativulaze kuthupi komanso kumatisoŵetsa mtendele wa maganizo. Conco, kucokela pamene bombalo linaphulika, tinapempha Yehova kuti atithandize kuthetsa mkwiyo na kusasunga cakukhosi kuti tipitilize kukhala na mtendele wamaganizo.”

16 Kodi cinali copepuka kwa iwo kum’khululukila munthuyo? Osati kweni-kweni. Iwo anapitiliza kuti: “Nthawi zina, mkazi wanga Sue akamavutika cifukwa ca kuvulala kumeneko, cimatiŵaŵa ngako. Koma cifukwa cakuti sitiika kwambili maganizo pa zimene zinacitikazo, mkwiyowo umatha mwamsanga. Kukamba zoona, ngati wochela bombayo angadzakhale m’bale tsiku lina, tingamulandile na manja aŵili. Cocitika cimeneci catiphunzitsa kuti mfundo za m’Baibo zimatimasula m’njila zambili, zimene sitinali kuziganizila. Cina, timatonthozedwa podziŵa kuti posacedwa, Yehova adzacotsapo mavuto onse.”

17. Kodi citsanzo ca mlongo Myra cakuphunzitsani ciyani pa nkhani yokhululuka?

17 Myra anaphunzila coonadi ataloŵa kale m’banja, apo n’kuti ali na ana aŵili ang’ono-ang’ono. Mwamuna wake sanali kufuna kuphunzila coonadi. M’kupita kwa nthawi, iye anacita cigololo n’kusiya banja lake. Myra anati: “Mwamuna wanga atanisiya pamodzi na ana athu aŵili, cinaniŵaŵa mofanana na mmene ambili amamvela wokondedwa wawo akacita zacinyengo. Sin’nayembekezele kuti angacite zimenezo. Sin’nakhulupilile, n’nali na cisoni, n’nadziimba mlandu, komanso n’nali wokwiya.” Ngakhale kuti ukwati unatha, cinali kumuŵaŵabe mu mtima. Myra anapitiliza kuti: “N’navutika na maganizo amenewo kwa miyezi, kenako n’nazindikila kuti maganizowo anali kukhudza ubale wanga na Yehova komanso anthu ena.” Myra tsopano amakamba kuti anakhululuka, ndipo samufunilanso zoipa mwamuna wake wakale. Iye amayembekezela kuti tsiku lina mwamunayo adzakhala bwenzi la Yehova. Mlongo Myra amaika maganizo ake pa za kutsogolo. Iye payekha anakwanitsa kukulitsa ana ake aŵiliwo na kukhala atumiki a Yehova. Pano tikamba, mlongo Myra akutumikila Yehova mwacimwemwe pamodzi na ana ake komanso mabanja awo.

YEHOVA AMAWELUZA MWACILUNGAMO

18. Kodi tingakhale na cidalilo cotani mwa Woweluza Wamkulu Yehova?

18 N’zolimbikitsa kudziŵa kuti tilibe udindo wosankha ciweluzo cimene munthu ayenela kulandila. Pokhala Woweluza Wamkulu, Yehova adzagwila nchito yofunika imeneyi. (Aroma 14:10-12) Tingakhale na cidalilo cakuti iye nthawi zonse amaweluza mogwilizana na mfundo zake zolungama za cabwino na coipa. (Gen. 18:25; 1 Maf. 8:32) Mulungu samacita zinthu mopanda cilungamo.

19. Kodi Yehova adzacita ciyani cifukwa ca cilungamo cake?

19 Timalakalaka kudzaona nthawi pamene Yehova adzacotsapo kothelatu zoipa zimene anthu opanda ungwilo abweletsa. Pa nthawiyo, kupwetekedwa mtima kudzathelatu. (Sal. 72:12-14; Chiv. 21:3, 4) Zonse sizidzakumbukilidwanso. Pamene tikuyembekezela nthawi yokondweletsa imeneyo, tiyamikila kwambili kuti Yehova amatithandiza kutengela citsanzo cake pa nkhani yokhululuka.

NYIMBO 18 Tikuyamikani Cifukwa ca Dipo

^ Yehova ni wofunitsitsa kukhululukila ocimwa olapa. Pokhala Akhristu, timafuna kutengela citsanzo cake wina akatikhumudwitsa. M’nkhani ino, tikambilane macimo a anthu ŵena amene ife tingakhululuke, komanso macimo amene tiyenela kuuza akulu. Tikambilanenso cifukwa cake Yehova amafuna kuti tizikhululukilana, ndiponso madalitso amene tidzapeza tikacita zimenezo.

^ Onani nkhani yakuti, “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga,” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1996.

^ Maina ena asinthidwa.