NKHANI YOPHUNZIRA 25

Yehova Amadalitsa Anthu Omwe Amakhululuka

Yehova Amadalitsa Anthu Omwe Amakhululuka

“Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.”​—AKOL. 3:13.

NYIMBO NA. 130 Muzikhululuka

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yehova amawatsimikizira chiyani anthu ochimwa omwe alapa?

 KUWONJEZERA pa kukhala Mlengi wathu, Wotipatsa malamulo komanso Woweruza wathu, Yehova ndi Atate wathu wachikondi. (Sal. 100:3; Yes. 33:22) Tikamuchimwira n’kulapa mochokera pansi pa mtima iye amatikhululukira, ndipo amachita zimenezi mofunitsitsa. (Sal. 86:5) Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova amatitsimikizira mwachikondi kuti: “Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.”​—Yes. 1:18.

2. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tikufuna kuti tizikhala mwamtendere ndi ena?

2 Chifukwa choti si ife angwiro, tonsefe nthawi zina timalankhula kapena kuchita zimene zingakhumudwitse ena. (Yak. 3:2) Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti sitingathe kumagwirizana nawo. Titha kumagwirizana nawo ngati titayesetsa kukhala ndi mtima wokhululuka. (Miy. 17:9; 19:11; Mat. 18:21, 22) Yehova amafuna kuti tizikhululukirana pa zinthu zing’onozing’ono zomwe timalakwirana. (Akol. 3:13) Tili ndi chifukwa chomveka chochitira zimenezi. Pajatu iye amatikhululukira “ndi mtima wonse.”​—Yes. 55:7.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Munkhaniyi, tiona mmene anthu ochimwafe tingatsanzirire Yehova pa nkhani ya kukhululuka. Kodi ndi machimo ati omwe tiyenera kudziwitsa akulu? N’chifukwa chiyani Yehova amatilimbikitsa kuti tizikhululukira ena? Nanga tingaphunzire chiyani kwa Akhristu ena omwe anakumanapo ndi mavuto aakulu chifukwa cha machimo a anthu ena?

MKHRISTU AKACHITA TCHIMO LALIKULU

4. (a) Kodi mtumiki wa Yehova ayenera kuchita chiyani akachita tchimo lalikulu? (b) Kodi akulu akakumana ndi munthu yemwe wachita tchimo udindo wawo umakhala wotani?

4 Tiyenera kudziwitsa akulu munthu wina akachita tchimo lalikulu. Ena mwa machimowa ndi omwe atchulidwa pa 1 Akorinto 6:9, 10. Munthu yemwe wachita tchimo lalikulu amakhala kuti wachita zoipa kwambiri zosemphana ndi malamulo a Mulungu. Zikatere munthuyo ayenera kupemphera kwa Yehova Mulungu komanso kukauza akulu. (Sal. 32:5; Yak. 5:14) Kodi akulu amakhala ndi udindo wotani? Yehova yekha ndiye ali ndi udindo wokhululukira machimo, ndipo amachita zimenezo pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo. * Komabe iye anapatsa akulu udindo wosankha pogwiritsa ntchito Malemba, ngati munthu wochimwa akufunika kukhalabe mumpingo. (1 Akor. 5:12) Mwa zina, akulu amafunika kupeza mayankho a mafunso awa: Kodi munthuyo anachita kukonzekera kuti achite tchimolo? Kodi ankabisira tchimolo anthu ena? Kodi wakhala akuchita tchimolo kwa nthawi yaitali? Ndipo funso lofunika kwambiri ndi lakuti, kodi pali umboni wosonyeza kuti walapa mochokera pansi pa mtima? Kodi pali umboni woti Yehova wamukhululukira?​—Mac. 3:19.

5. Kodi zimene akulu amachita zimakhala ndi zotsatirapo zabwino ziti?

5 Akulu akakumana ndi munthu yemwe wachita tchimo amafuna asankhe zinthu mogwirizana ndi zomwe zasankhidwa kale kumwamba. (Mat. 18:18) Kodi kuchita zimenezi kumathandiza bwanji mpingo? Mpingo umakhala wotetezeka chifukwa anthu osalapa omwe angasokoneze nkhosa za Yehova za mtengo wapatali amachotsedwa. (1 Akor. 5:6, 7, 11-13; Tito 3:10, 11) Zingathandizenso wochimwa kuti alape ndiponso kuti Yehova amukhululukire. (Luka 5:32) Akulu amapempherera munthu yemwe walapa ndipo amapempha Yehova kuti amuthandize kuchira mwauzimu.​—Yak. 5:15.

6. Kodi Yehova amakhululukirabe munthu yemwe wachotsedwa? Fotokozani.

6 Tiyerekeze kuti munthu sakusonyeza kulapa pamene wakumana ndi akulu. Zikatero amachotsedwa mumpingo. Ngati waphwanya malamulo a boma, akulu sangamuteteze kuti asakumane ndi zotsatira za zoipa zomwe wachitazo. Yehova amalola akuluakulu a boma kuweruza komanso kupereka chilango kwa aliyense amene waphwanya malamulo, kaya munthuyo analapa kwa akulu kapena ayi. (Aroma 13:4) Komabe ngati munthuyo nzeru zamubwerera, ndipo walapa kuchokera pansi pa mtima, Yehova amakhala wofunitsitsa kumukhululukira. (Luka 15:17-24) Amamukhululukirabe ngakhale kuti anachita machimo akuluakulu kwambiri.​—2 Mbiri 33:9, 12, 13; 1 Tim. 1:15.

7. Kodi tingasonyeze bwanji kuti takhululukira munthu yemwe watilakwira?

7 N’zosangalatsa kudziwa kuti sitinapatsidwe udindo wosankha kuti Mulungu akhululukire munthu kapena ayi. Komabe pali chinthu china chimene timafunika kusankha. Kodi timafunika kusankha chiyani? Nthawi zina munthu angatilakwire, mwinanso kutilakwira kwambiri, kenako n’kupepesa komanso kutipempha kuti timukhululukire. Koma nthawi zina sangachite zimenezi. Ngakhale zili choncho, tingasankhe kumukhululukira posapitiriza kumusungira chakukhosi komanso kumukwiyira. Kunena zoona kuti tichite zimenezi pangafunike nthawi komanso khama, makamaka ngati munthuyo watilakwira kwambiri. Nsanja ya Olonda ya September 15, 1994 inanena kuti: “Tikakhululukira munthu sizitanthauza kuti tikusangalala ndi tchimo lomwe anachitalo. Kwa Mkhristu, kukhululuka kumatanthauza kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova n’kumakhulupirira kuti achitapo kanthu. Iye ndi Woweruza wachilungamo m’chilengedwe chonse, ndipo adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika pa nthawi yake.” N’chifukwa chiyani iye amatilimbikitsa kuti tizikhululuka n’kumakhulupirira kuti iye aweruza nkhaniyo mwachilungamo?

CHIFUKWA CHAKE YEHOVA AMATILIMBIKITSA KUTI TIZIKHULULUKA

8. Kodi timasonyeza bwanji kuti timayamikira chifundo cha Yehova?

8 Kukhululuka kumasonyeza kuti ndife oyamikira. M’fanizo lina, Yesu anayerekezera Yehova ndi mbuye, yemwe anakhululukira kapolo wake ngongole yaikulu yomwe sakanatha kubweza. Komabe kapoloyo analephera kusonyeza chifundo kapolo mnzake amene anamukongoza ndalama zochepa kwambiri. (Mat. 18:23-35) Kodi Yesu ankafuna kutiphunzitsa chiyani pamenepa? Ngati timayamikiradi chifundo chachikulu chomwe Yehova amatisonyeza, tidzakhala ofunitsitsa kukhululukira ena. (Sal. 103:9) Zaka zambiri zapitazo, Nsanja ya Olonda ina inanena kuti: “Kaya takhala tikukhululukira anthu kambirimbiri bwanji, sitingafike pa mlingo umene Mulungu amatikhululukira komanso kutisonyeza chifundo kudzera mwa Khristu.”

9. Kodi Yehova amasonyeza chifundo kwa ndani? (Mateyu 6:14, 15)

9 Okhululukira ena nawonso adzakhululukidwa. Yehova amachitira chifundo anthu omwenso ndi achifundo. (Mat. 5:7; Yak. 2:13) Yesu anafotokoza mfundo imeneyi momveka bwino pamene ankaphunzitsa ophunzira ake kupemphera. (Werengani Mateyu 6:14, 15.) Timaphunziranso mfundo imeneyi pa zimene Yehova anauza mtumiki wake Yobu. Munthu wokhulupirikayu anali atakhumudwa kwambiri ndi mawu opweteka omwe Elifazi, Bilidadi ndi Zofari anamulankhula. Yehova anumuuza Yobu kuti awapempherere. Iye atachita zimenezi Yehova anamudalitsa.​—Yobu 42:8-10.

10. Kodi timadzivulaza bwanji tikasunga chakukhosi? (Aefeso 4:31, 32)

10 Timadzivulaza tokha tikamasunga chakukhosi. Yehova amafuna tizisangalala komanso kupepukidwa mumtima chifukwa chosasunga chakukhosi. (Werengani Aefeso 4:31, 32.) Iye amatilimbikitsa kuti ‘tisamapse mtima ndipo tizipewa kukwiya.’ (Sal. 37:8) Kutsatira malangizo amenewa n’kothandiza kwambiri. Kusunga chakukhosi kungawononge thanzi lathu komanso maganizo athu. (Miy. 14:30) Kusunga chakukhosi sikuvulaza munthu yemwe watilakwirayo, ngati mmene zingakhalire titamwa poizoni n’kumayembekezera kuti avulale ndi mnzathuyo. Choncho tikakhululukira ena zimakhala ngati tadzipatsa mphatso. (Miy. 11:17) Timakhala ndi mtendere wa mumtima ndi m’maganizo ndipo timapitirizabe kutumikira Yehova.

11. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani yobwezera? (Aroma 12:19-21)

11 Yehova ndi amene ali woyenera kubwezera. Yehova sanatipatse udindo wobwezera munthu wina akatilakwira. (Werengani Aroma 12:19-21.) Popeza sitiona moyenera zinthu chifukwa choti si ife angwiro, sitingaweruze bwino nkhani ngati mmene Mulungu angachitire. (Aheb. 4:13) Ndipo nthawi zina tingalephere kuweruza bwino chifukwa chosokonezedwa ndi mmene tikumvera. Yehova anauzira Yakobo kulemba kuti: “Mkwiyo wa munthu subala chilungamo cha Mulungu.” (Yak. 1:20) Tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzachita zoyenera ndipo adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika.

Tisamakwiye komanso kusunga chakukhosi. Tizisiya nkhaniyo m’manja mwa Mulungu. Iye adzathetsa mavuto onse obwera chifukwa cha uchimo (Onani ndime 12)

12. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira kuti Yehova adzachita chilungamo?

12 Kukhululuka kumasonyeza kuti timakhulupirira kuti Yehova adzachita chilungamo. Tikamasiya nkhani m’manja mwa Yehova, timasonyeza kuti tikukhulupirira kuti iye adzachotsa zoipa zonse zobwera chifukwa cha uchimo. M’dziko latsopano zinthu zopweteka “sizidzakumbukiridwanso, ndipo sizidzabweranso mumtima” ngakhale pang’ono. (Yes. 65:17) Komabe munthu wina akatikhumudwitsa kwambiri, kodi n’zotheka kusiya kumukwiyira komanso kusamusungira chakukhosi? Tiyeni tione zimene zathandiza ena kuchita zimenezi.

MADALITSO OBWERA CHIFUKWA CHOKHULULUKA

13-14. Kodi mwaphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Tony ndi José pa nkhani ya kukhululuka?

13 Abale ndi alongo athu ambiri anasankha kukhululuka pamene ena anawachitira zinthu zopweteka kwambiri. Ndiye kodi iwo apeza madalitso otani?

14 Asanaphunzire choonadi, Tony * yemwe amakhala ku Philippines, anamva kuti mmodzi mwa azichimwene ake anaphedwa ndi munthu wina dzina lake José. Pa nthawiyo, Tony anali munthu wachiwawa ndipo ankafuna kubwezera. José anamangidwa n’kuikidwa m’ndende chifukwa cha mlandu wakewo. Atatulutsidwa m’ndende, Tony anatsimikiza mtima kuti amusakasaka mpaka kumupha ndipo anagula mfuti. Kenako iye anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Tony anati, “Pamene ndinkaphunzira Baibulo, ndinazindikira kuti ndikufunika kusintha moyo wanga, zomwe zinkaphatikizapo kusiya kukhala wokwiya.” Patapita nthawi, Tony anabatizidwa ndipo kenako anakhala mkulu. Ndiye tangoganizani mmene iye anadabwira atamva kuti José anabatizidwa n’kukhala mtumiki wa Yehova. Awiriwa atakumana anakumbatirana, ndipo Tony anauza José kuti anali atamukhululukira. Tony ananena kuti kukhululukira José kunamuthandiza kukhala ndi chimwemwe chosaneneka. Kunena zoona, Yehova anamudalitsa chifukwa chokhala ndi mtima wofunitsitsa kukhala wokhululuka.

Chitsanzo cha Peter ndi Sue chikusonyeza kuti tikhoza kusiya kukhala okwiya komanso kusunga chakukhosi (Onani ndime 15-16)

15-16. Kodi zimene zinachitikira Peter ndi Sue zakuphunzitsani chiyani pa nkhani yokhululuka?

15 Mu 1985, Peter ndi Sue ankachita misonkhano ku Nyumba ya Ufumu pomwe mwadzidzidzi kunaphulika bomba. Munthu wina anali ataika bombalo m’Nyumba ya Ufumuyo. Pa nthawiyo Sue anavulala kwambiri zomwe zinachititsa kuti asamaone komanso kumva. Iye anasiyanso kumva fungo. Nthawi zambiri Peter ndi Sue ankadzifunsa kuti, ‘Ndi munthu wotani yemwe angachite choipa chachikulu chonchi?’ Patapita zaka zambiri, Munthu amene anaphulitsa bomba lija, yemwe sankatumikira Yehova anagamulidwa kuti akakhale kundende moyo wake wonse. Atafunsidwa ngati anakhululukira munthuyo, Peter ndi Sue ananena kuti: “Yehova amatiphunzitsa kuti kupitiriza kukwiya komanso kusunga chakukhosi kungawononge thanzi ndi maganizo athu. Choncho zimene zija zitangochitika tinapempha Yehova kuti atithandize kuti tisakwiye komanso kusunga chakukhosi.”

16 Kodi zakhala zophweka kuti akhululukire munthu uja? Osati nthawi zonse. Iwo anapitiriza kuti: “Nthawi zina tikamakumana ndi mavuto chifukwa cha kuvulala kwa Sue, zimayamba kutiwawa mumtima. Koma timasiya kuganizira nkhaniyo ndipo zikatero mkwiyowo umatha. Ndipo tinganene mochokera pansi pa mtima kuti ngati tsiku lina munthuyo adzakhale m’bale wathu, tidzamulandira. Zimene zinatichitikirazi, zatiphunzitsa kuti mfundo za m’Baibulo zimatimasula kuposa mmene tingaganizire. Timalimbikitsidwanso podziwa kuti posachedwapa Yehova athetsa mavuto onse.”

17. Kodi mwaphunzira chiyani pa nkhani ya kukhululuka pa zimene zinachitikira Myra?

17 Myra anaphunzira choonadi ali kale pabanja komanso ali ndi ana awiri ang’onoang’ono. Koma mwamuna wake sanavomere kuphunzira Baibulo. Patapita nthawi, mwamunayo anachita chigololo n’kusiya banjalo. Myra ananena kuti: “Mwamuna wanga atandisiya limodzi ndi anawo, ndinamva ngati mmene anthu ambiri amamvera akachitiridwa zinthu zopanda chilungamo ndi munthu amene amamukonda, monga kukhumudwa kwambiri, osakhulupirira kuti zikuchitikadi, kumva chisoni, kunong’oneza bondo, kudziimba mlandu komanso kukwiya.” Ngakhale kuti ukwatiwo unatha, ndinkamvabe kuti ndagwiritsidwa fuwa lamoto. Myra ananenanso kuti: “Ndinapitiriza kumva choncho kwa miyezi yambiri, ndipo kenako ndinazindikira kuti zimenezi zinkasokoneza ubwenzi wanga ndi Yehova komanso anthu ena.” Panopa iye amanena kuti anasiya kukhala wokwiya ndipo sasungiranso chakukhosi mwamuna wake wakaleyo. Iye amayembekezera kuti tsiku lina mwamunayo adzayamba kutumikira Yehova. Myra amaganizira kwambiri zam’tsogolo. Iye analera yekha ana ake awiri omwe panopa akutumikira Yehova ndipo akusangalala kutumikira ndi ana akewo limodzi ndi mabanja awo.

YEHOVA NDI WOWERUZA WABWINO KWAMBIRI

18. N’chifukwa chiyani tingadalire Yehova yemwe ndi Woweruza Wamkulu?

18 Timapepukidwa mumtima chifukwa chodziwa kuti sitinapatsidwe udindo wovuta wosankha mmene anthu ayenera kuweruzidwira. Monga Woweruza Wamkulu, Yehova ndi amene adzagwire ntchito yofunikayi. (Aroma 14:10-12) Timakhala otsimikiza kuti iye nthawi zonse adzaweruza mogwirizana ndi mfundo zake zokhudza chabwino ndi choipa. (Gen. 18:25; 1 Maf. 8:32) Iye sadzachita zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.

19. Kodi Yehova adzachita zinthu ziti chifukwa choti amaweruza mwachilungamo?

19 Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene Yehova adzathetse mavuto obwera chifukwa chakuti anthufe ndi ochimwa. Pa nthawiyo, mavuto onse omwe anakhudza thanzi lathu komanso maganizo adzathetsedwa. (Sal. 72:12-14; Chiv. 21:3, 4) Sitidzakumbukiranso mavuto amenewa. Pamene tikuyembekezera kuti nthawi yosangalatsayi ifike, timathokoza kwambiri Yehova chifukwa amatithandiza kuti tizimutsanzira pa nkhani yokhululuka.

NYIMBO NA. 18 Tikuthokoza Chifukwa cha Dipo

^ Yehova amafunitsitsa kukhululukira anthu ochimwa omwe alapa. Monga Akhristu, timafunika kutengera chitsanzo chake ena akatilakwira. Munkhaniyi tikambirana machimo omwe tikhoza kungokhululuka patokha komanso machimo amene tiyenera kudziwitsa akulu. Tionanso chifukwa chake Yehova amafuna kuti tizikhululukirana komanso madalitso omwe timapeza tikamachita zimenezi.

^ Onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1996.

^ Mayina ena asinthidwa.