Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 27

“Yembekezela Yehova”

“Yembekezela Yehova”

“Yembekezela Yehova. Limba mtima ndipo ucite zinthu mwamphamvu.”—SAL. 27:14.

NYIMBO 128 Pilila Mpaka Mapeto

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. (a) Kodi Yehova watipatsa ciyembekezo cotani? (b) Kodi ‘kuyembekezela Yehova’ kumatanthauza ciyani? (Onani mawu akuti “Kufotokozela Mawu Ena.”)

 YEHOVA anapeleka ciyembekezo cabwino kwa onse omukonda. Ndipo posacedwa iye adzacotsapo matenda, cisoni, na imfa. (Chiv. 21:3, 4) “Anthu ofatsa” amene akuyembekezela pa iye, adzawathandiza kukonza dziko lapansi kukhala paradaiso. (Sal. 37:9-11) Pa nthawiyo, aliyense wa ife adzakhala pa ubale wabwino kwambili na iye kuposa umene tili nawo pali pano. Ici n’ciyembekezo cabwino ngako! Koma n’cifukwa ciyani timakhulupilila kuti malonjezo a Mulungu adzakwanilitsidwa? Cifukwa Yehova salephela kukwanilitsa zimene walonjeza. Mwa ici, tili na cifukwa cabwino ‘coyembekezela Yehova.’ * (Sal. 27:14) Timaonetsa izi poyembekezela moleza mtima komanso mwacimwemwe kuti Mulungu adzakwanilitsa malonjezo ake.—Yes. 55:10, 11.

2. Kodi Yehova wacita kale ciyani?

2 Yehova waonetsa kale kuti amakwanilitsa malonjezo ake. Naci citsanzo codziŵika bwino: M’buku la Chivumbulutso, Yehova analonjeza kuti m’nthawi yathu ino, iye adzasonkhanitsa anthu kucokela ku dziko lililonse, fuko lililonse, komanso cinenelo ciliconse, kuti adzamulambile mogwilizana. Masiku ano, gulu lapadela limeneli limachedwa “khamu lalikulu.” (Chiv. 7:9, 10) Ngakhale kuti m’gulu limeneli muli amuna, akazi, komanso ana a zikhalidwe zosiyana-siyana, onse ni banja limodzi lamtendele ndiponso logwilizana la padziko lonse. (Sal. 133:1; Yoh. 10:16) A khamu lalikulu amenewa ni alaliki okangalika. Iwo ni okonzeka nthawi zonse kuuzako aliyense za ciyembekezo cawo ca dziko labwino. (Mat. 28:19, 20; Chiv. 14:6, 7; 22:17) Ngati ndinu wa khamu lalikulu, ndithudi muli na ciyembekezo ca tsogolo lowala.

3. Kodi colinga ca Satana n’ciyani?

3 Mdyelekezi amafuna kutitayitsa ciyembekezo cathu. Colinga cake ni kutipangitsa kukhulupilila kuti Yehova sasamala za ife, komanso kuti sadzasunga malonjezo ake. Satana akatitayitsa ciyembekezo cathu, sitingakhale olimba mtima ndipo tingaleke kutumikila Yehova. Monga tionele, Mdyelekezi anayesa kutayitsa Yobu ciyembekezo cake pofuna kum’tayitsa cikhulupililo mwa Yehova.

4. Tikambilane ciyani m’nkhani ino? (Yobu 1:9-12)

4 M’nkhani ino, tiona njila zimene Satana anaseŵenzetsa pofuna kutayitsa Yobu cikhulupililo cake. (Ŵelengani Yobu 1:9-12.) Tikambilanenso zimene tingaphunzile pa citsanzo ca Yobu, komanso cifukwa cake tiyenela kukumbukila kuti Mulungu amatikonda, ndiponso kuti adzakwanilitsa malonjezo ake.

SATANA ANAYESA KUMUTAYITSA CIYEMBEKEZO YOBU

5-6. N’ciyani cinacitika kwa Yobu m’kanthawi kocepa?

5 Zonse zinali kumuyendela bwino Yobu. Anali pa ubwenzi wolimba na Yehova. Banja lake linali lalikulu, logwilizana, ndiponso anali wolemela kwambili. (Yobu 1:1-5) Koma tsiku limodzi cabe, Yobu anataya pafupifupi zinthu zake zonse. Coyamba anatayikilidwa cuma cake conse. (Yobu 1:13-17) Kenako, ana ake okondedwa onse anafa. Tangoliganizilani tsoka limeneli! Makolo amasautsika na cisoni ngakhale atafeledwa mwana mmodzi cabe. Ndiye tangoganizani mmene Yobu na mkazi wake anasokonezekela maganizo, cisoni cosaneneka, komanso kutaya mtima atamva kuti ana awo onse 10 afa. N’zosadabwitsa kuti polila, Yobu anang’amba zovala zake n’kudzigwetsa pansi.—Yobu 1:18-20.

6 Cotsatila, Satana anadwalitsa Yobu matenda ozunza komanso ocititsa manyazi. (Yobu 2:6-8; 7:5) Izi zisanacitike, anthu anali kum’lemekeza kwambili Yobu, moti anali kupita kwa iye kukapemphako nzelu. (Yobu 31:18) Koma apa lomba anthu anayamba kum’pewa Yobu. Iye anakhala wodetsedwa, acibale ake pamodzi na anzake anam’kana, ngakhalenso anchito a pakhomo pake enieniwo.—Yobu 19:13, 14, 16.

Abale na alongo ambili masiku ano angamvetse mmene Yobu anamvela pamene anali kukumana na mavuto (Onani ndime 7) *

7. (a) Kodi Yobu anali kuona kuti mavuto ake akucokela kwa ndani? Ngakhale n’telo, kodi iye anakana kucita ciyani? (b) Ni mayeso otani amene Mkhristu angakumane nawo malinga na zimene tikuona pa pikica?

7 Colinga ca Satana cinali cakuti Yobu aziona kuti akuvutika cifukwa anakwiyitsa Yehova. Mwacitsanzo, Satana anagwilitsa nchito cimphepo camphamvu kugwetsa nyumba mmene ana onse 10 a Yobu anali kudya cakudya mosangalala. (Yobu 1:18, 19) Iye anapangitsanso moto kugwa kucokela kumwamba umene unapha ziŵeto zonse za Yobu, pamodzi na abusa amene anali kuziyang’anila. (Yobu 1:16) Popeza cimphepoco na moto zinacokela kumwamba, Yobu anaganiza kuti zacokela kwa Yehova Mulungu. Izi zinam’pangitsa kukhulupilila kuti anali atakwiyitsa Yehova mwa njila ina yake. Ngakhale n’telo, iye anakana kunyoza Atate wake wakumwamba. Yobu sanaiŵale kuti zabwino zonse zimene analandila pa zaka zonsezo, ni Yehova anam’patsa. Conco, anaganiza kuti ngati anali kukondwela kulandila zabwino, ayenelanso kucivomeleza kulandila zoipa. Ndiye cifukwa cake Yobu ananena kuti: “Dzina la Yehova lipitilize kutamandidwa.” (Yobu 1:20, 21; 2:10) Ngakhale kuti Yobu anali atatayikilidwa cuma, ana ake, ngakhale thanzi lake, iye anakhalabe nganganga kwa Yehova. Koma Satana anali asanathane naye Yobu.

8. Kodi Satana anacitanso ciyani kwa Yobu?

8 Satana anagwilitsanso nchito anzake atatu acinyengo a Yobu kuti amupangitse kudzimva wopanda pake. Amuna amenewa anakamba kuti Yobu anali kuvutika cifukwa ca zoipa zina zake zimene anacita. (Yobu 22:5-9) Iwo anayesanso kum’pangitsa kukhulupilila kuti ngakhale kuti sanali kucita zoipa, zonse zimene anacita pofuna kukondweletsa Mulungu zinangopita pacabe. (Yobu 4:18; 22:2, 3; 25:4) M’ceniceni, iwo anali kuyesa kupangitsa Yobu kukayikila zoti Mulungu anali kum’konda, anali kumusamalila, komanso kuti kum’tumikila kunalibe phindu lililonse. Mawu awo akanapangitsa Yobu kuona kuti alibenso ciyembekezo.

9. N’ciyani cinathandiza Yobu kukhala wolimba mtima?

9 Yelekezani kuti mukumuona Yobu ali khale paphulusa uku akumva ululu waukulu. (Yobu 2:8) Anzake atatu akumunena kuti iye si munthu wabwino, komanso kuti zonse zimene anacita n’zopanda phindu. Mavuto amukulila msinkhu, ndipo ali na cisoni cacikulu cifukwa cotayikilidwa ana ake. Poyamba, Yobu sakukamba ciliconse. (Yobu 2:13–3:1) Ngati anzakewo akuganiza kuti kukhala cete kwa Yobu kukutanthauza kuti iye akufuna kusiya Yehova, ndiye kuti alemba m’madzi. Kenako, Yobu akuŵelamutsa mutu na kuyang’ana anzakewo aciphamaso n’kunena kuti: “Mpaka ine kumwalila, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.” (Yobu 27:5) N’ciyani cinathandiza Yobu kukhala wolimba mtima conco pokumana na mavuto onsewa? Ngakhale pamene anali wolefuka kothelatu, iye sanataye ciyembekezo cakuti Mulungu wake wacikondi adzathetsa mavuto ake. Anadziŵa kuti ngakhale amwalile, Yehova adzamuukitsa.—Yobu 14:13-15.

KODI TINGATENGELE BWANJI CITSANZO CA YOBU?

10. Kodi nkhani ya Yobu itiphunzitsa ciyani?

10 Nkhani ya Yobu itiphunzitsa kuti Satana sangatikakamize kusiya Yehova, komanso kuti Yehova amadziŵa zonse zimene zimaticikila pa umoyo wathu. Zimene zinacitikila Yobu zimatithandiza kumvetsa zonse zolowetsedwamo pamene tikuvutika. Tiyeni tione ena mwa maphunzilo amene tingatengepo pa citsanzo ca Yobu.

11. Kodi tingakhale otsimikiza za ciyani ngati tidalilabe Yehova? (Yakobo 4:7)

11 Yobu anaonetsa kuti ngati tidalilabe Yehova, tingathe kupilila mayeso alionse na kum’tsutsa Satana. Kodi pamakhala zotulukapo zotani? Malemba amatitsimikizila kuti Mdyelekezi adzatithaŵa.—Ŵelengani Yakobo 4:7.

12. Kodi ciyembekezo ca ciukitso cinamulimbikitsa bwanji Yobu?

12 Cina, tiyenela kugwila zolimba ciyembekezo ca ciukitso. Monga tinaonela m’nkhani yapita, Satana amaseŵenzetsa msampha woopa imfa pofuna kutikanganula kwa Yehova. Satana anakamba kuti Yobu pofuna kupulumutsa moyo wake, akanatha kucita ciliconse, ngakhale kuleka kutumikila Yehova. Koma limeneli linali bodza lamkunkhuniza. Ngakhale pamene Yobu anamva fungo la imfa, iye anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Pokhulupilila kuti Yehova ni wabwino, komanso pokhala na ciyembekezo cakuti iye adzakonza zinthu, kunam’thandiza Yobu kupilila. Yobu anali kudziŵa bwino lomwe kuti ngati Yehova sadzakonza zinthu pamene iye ali moyo, ndiye kuti adzacitapo kanthu ndithu m’tsogolo mwa kumuukitsa. Kwa iye ciyembekezo ca ciukitso cinali ceniceni. Nafenso tikamaona kuti ciyembekezoci n’ceniceni, kuopa imfa sikudzatitayitsa cikhululupililo cathu.

13. N’cifukwa ciyani m’pofunika kuwadziŵa bwino macenjela amene Satana anagwilitsa nchito pa Yobu?

13 Tiyenela kuwadziŵa bwino macenjela amene Satana anagwilitsa nchito pa Yobu, cifukwa ni amenenso amagwilitsa nchito pa ife. Onani cinenezo ca Satana ici: “Munthu [osati Yobu cabe] angalolele kupeleka ciliconse cimene ali naco kuti apulumutse moyo wake.” (Yobu 2:4, 5) M’mawu ena, Satana anatanthauza kuti ife sitim’konda kwenikweni Yehova Mulungu, komanso kuti tingaleke kum’tumikila pofuna kupulumutsa moyo wathu. Anatanthauzanso kuti Mulungu satikonda, komanso kuti sayamikila zimene timayesetsa kucita pofuna kum’kondweletsa. Oyembekezela Yehovafe macenjela a Satana timawadziŵa bwino. Conco sayenela kutipusitsa nawo.

14. Kodi mayeso angatithandize kudziŵa ciyani za ife eni? Fotokozani citsanzo.

14 Tiziona mayeso kuti ni mwayi wodziunika ife eni. Mayeso amene Yobu anakumana nawo anam’thandiza kudziŵa zofooka zake, na kuwongolela. Mwacitsanzo, iye anaona kuti anafunika kukhala wodzicepetsa kwambili. (Yobu 42:3) Nafenso tingadziŵe mbali zofunika kuwongolela tikakumana na mayeso. M’bale Nikolay, * amene anaikidwa m’ndende ngakhale kuti anali kudwala kwambili anati: “Ndende ili ngati makina a ekiselo (X-ray). Imakuthandiza kuona makhalidwe acikhristu amene uyenela kukulitsa.” Tikadziŵa zofooka zathu, tiyenela kuyesetsa kugwililapo nchito.

15. Kodi tiyenela kumvetsela ndani? Ndipo n’cifukwa ciyani?

15 Tizimvetsela kwa Yehova osati adani athu. Yobu anamvetsela mwachelu pamene Yehova anali kukamba naye. Mulungu polankhula kwa Yobu, zinali monga akumuuza kuti: ‘Kodi ukuziona mphamvu zanga za kulenga? Nidziŵa zonse zimene zakucitikila. Kodi uganiza siningakwanitse kukusamalila?’ Yobu anayankha modzicepetsa komanso moyamikila kwambili pa ubwino wa Yehova. Iye anati: “Ndinkangomva za inu, koma tsopano diso langa lakuonani.” (Yobu 42:5) N’kutheka kuti Yobu pokamba mawu amenewa anali paphulusa, thupi lake lili zilonda zokha-zokha, akulila ana ake. Ngakhale zinali conco, Yehova anam’tsimikizila Yobu kuti amam’konda komanso kuti akumuyanjabe.—Yobu 42:7, 8.

16. Malinga n’kunena kwa Yesaya 49:15, 16, kodi tizikumbukila ciyani pokumana na mayeso?

16 Masiku anonso, anthu angatinyoze na kutiyesa opanda pake. Iwo angatisemele cinyau aliyense payekha kapena monga gulu, ndipo “angatinamizile zoipa zilizonse.” (Mat. 5:11) Nkhani ya Yobu, itiphunzitsa kuti Yehova ali na cidalilo mwa ife cakuti tidzakhalabe okhulupilika pokumana na mayeso. Yehova amatikonda, ndipo sadzawasiya anthu amene amamuyembekezela. (Ŵelengani Yesaya 49:15, 16.) Tisamamvetsele zimene adani a Mulungu amatineneza. M’bale James wa ku Turkey, amene banja lake linakumana na mayeso aakulu, anati: “Tinazindikila kuti kumvetsela mabodza oneneza anthu a Mulungu kungatikhwethemule. Conco, tinaika maganizo pa ciyembekezo ca Ufumu, ndipo tinakhalabe okangalika mu utumiki wathu kwa Yehova. Zotulukapo zake, tinakhalabe acimwemwe.” Mofanana na Yobu, timamvetsela Yehova. Mabodza a adani athu satitayitsa ciyembekezo cathu.

CIYEMBEKEZO CANU CIDZAKUTHANDIZANI KUPILILA

Yobu anadalitsidwa cifukwa ca kukhulupilika kwake. Iye na mkazi wake anasangalala na madalitso a Yehova kwa moyo wawo wonse (Onani ndime 17) *

17. Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca amuna na akazi okhulupilika ochulidwa m’caputala 11 ca Aheberi?

17 Yobu ni citsanzo cimodzi cabe ca atumiki a Yehova amene anakhalabe olimba pokumana na mayeso. M’kalata yake kwa Aheberi, mtumwi Paulo anakambanso za ena ambili, powachula kuti “mtambo wa mboni waukulu.” (Aheb. 12:1) Onsewo anakumanapo na mayeso aakulu, koma anakhalabe okhulupilika kwa Yehova. (Aheb. 11:36-40) Kodi kupilila kwawo komanso kugwila nchito kwawo molimbika kunangopita pacabe? Kutalitali! Ngakhale kuti iwo sanaone kukwanilitsidwa kwa malonjezo onse a Mulungu m’nthawi yawo , anayembekezelabe Yehova. Ndipo cifukwa anali kudziŵa bwino lomwe kuti Yehova anali kuwayanja, iwo anali na cidalilo cakuti adzaona kukwanilitsidwa kwa malonjezo ake. (Aheb. 11:4, 5) Citsanzo cawo cimatilimbikitsa kuti tisaleke kuyembekezela Yehova.

18. Kodi ndinu ofunitsitsa kucita ciyani? (Aheberi 11:6)

18 Masiku ano, tikukhala m’dziko limene zinthu zikungoipilaipila. (2 Tim. 3:13) Satana akali kuwayesa anthu a Mulungu. Mosasamala kanthu na zopinga zimene tingakumane nazo kutsogolo, tiyeni tigwilebe nchito ya Yehova molimbika, tili na cidalilo cakuti “ciyembekezo cathu cili mwa Mulungu wamoyo.” (1 Tim. 4:10) Tisaiŵale kuti madalitso amene Mulungu anapatsa Yobu pamapeto pake, anaonetsa kuti “Yehova ndi wacikondi cacikulu ndi wacifundo.” (Yak. 5:11) Tiyeni tikhalebe okhulupilika kwa Yehova, tili na cidalilo cakuti iye “amapeleka mphoto kwa anthu omufuna-funa ndi mtima wonse.”—Ŵelengani Aheberi 11:6.

NYIMBO 150 Funani Cipulumutso ca Mulungu

^ Tikaganizila za munthu amene anapilila mayeso aakulu, nthawi zambili amene amabwela m’maganizo mwathu ni Yobu. Kodi tingaphunzilepo ciyani pa zimene zinacitikila munthu wokhulupilika ameneyu? Tiphunzilapo kuti Satana sangatikakamize kum’siya Yehova. Tiphunzilaponso kuti Yehova amadziŵa zonse zimene zimaticikila pa umoyo. Tsiku lina, iye adzacotsapo mavuto athu onse monga anacitila kwa Yobu. Tiyenela kuonetsa mwa zocita zathu kuti timakhulupililadi mfundo zimenezi. Mwa kutelo, timaonetsa kuti ‘tikuyembekezela Yehova.’

^ KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Liwu la Ciheberi limene analimasulila kuti “ciyembekezo” limatanthauza kuyembekezela cina cake mwacidwi. Lingatanthauzenso kukhulupilila munthu wina kapena kum’dalila.—Sal. 25:2, 3; 62:5.

^ Maina ena asinthidwa.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yobu na mkazi wake akulila ana awo amene afa.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yobu anapilila mayeso ake mpaka kumapeto. Iye na mkazi wake akuganizila madalitso amene Yehova waapatsa pamodzi na banja lawo.