NKHANI YOPHUNZIRA 27

“Yembekezera Yehova”

“Yembekezera Yehova”

“Yembekezera Yehova. Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu.”​—SAL. 27:14.

NYIMBO NA. 128 Tipirire Mpaka Mapeto

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. (a) Kodi Yehova watipatsa chiyembekezo chotani? (b) Kodi ‘kuyembekezera Yehova’ kumatanthauza chiyani? (Onani “Tanthauzo la Mawu Ena.”)

 YEHOVA wapereka chiyembekezo chabwino kwambiri kwa onse omwe amamukonda. Posachedwapa athetsa matenda, zopweteka komanso imfa. (Chiv. 21:3, 4) Iye adzathandiza “ofatsa” omwe akumuyembekezera kukonza dzikoli kukhala paradaiso. (Sal. 37:9-11) Adzathandizanso aliyense wa ife kukhala naye pa ubwenzi wabwino kuposa panopa. Chimenechitu ndi chiyembekezo chabwino kwambiri. Koma kodi n’chifukwa chiyani timakhulupirira kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwadi? Nthawi zonse iye amakwaniritsa malonjezo ake. Choncho tili ndi chifukwa chomveka chotichititsa ‘kuyembekezera Yehova.’ * (Sal. 27:14) Timachita zimenezi poyembekezera moleza mtima komanso mosangalala kuti Mulungu akwaniritse cholinga chake.​—Yes. 55:10, 11.

2. Kodi Yehova wachita kale zinthu ziti?

2 Yehova wasonyeza kale kuti amakwaniritsa malonjezo ake. Taganizirani chitsanzo chimodzi ichi. M’buku la Chivumbulutso, iye analonjeza kuti m’masiku athu ano adzachititsa kuti anthu a mitundu, zikhalidwe komanso zilankhulo zosiyanasiyana azimulambira mogwirizana. Masiku ano gulu la anthu lapaderali limadziwika kuti “khamu lalikulu.” (Chiv. 7:9, 10) Ngakhale kuti m’gululi muli amuna, akazi komanso ana ochokera m’mitundu, zilankhulo komanso zikhalidwe zosiyanasiyana, iwo ali m’banja la padziko lonse logwirizana. (Sal. 133:1; Yoh. 10:16) Anthu a m’khamu lalikululi amagwiranso mwakhama ntchito yolalikira. Nthawi zonse amakhala okonzeka kuuza aliyense yemwe angamvetsere za chiyembekezo chawo chodzakhala m’dziko labwino. (Mat. 28:19, 20; Chiv. 14:6, 7; 22:17) Ngati inunso muli m’khamu lalikululi, n’zosakayikitsa kuti chiyembekezo choti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolomu ndi chamtengo wapatali kwa inu.

3. Kodi Satana amafuna chiyani?

3 Mdyerekezi safuna kuti muziyembekezera zinthu za m’tsogolo. Amafuna muzikhulupirira kuti Yehova sakuganizirani ndipo sadzakwaniritsa zimene analonjeza. Ngati Satana angapambane, sitingakhalenso olimba mtima ndipo mwinanso tingasiye kutumikira Yehova. Monga mmene tionere, Mdyerekezi anayesa kuchititsa Yobu kuti asakhale ndi chiyembekezo komanso asiye kutumikira Yehova.

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi? (Yobu 1:9-12)

4 Munkhaniyi, tikambirana njira zimene Satana anagwiritsa ntchito poyesetsa kuchititsa Yobu kuti asakhale wokhulupirika. (Werengani Yobu 1:9-12.) Tikambirananso zimene tingaphunzire pa chitsanzo cha Yobu komanso chifukwa chake tiyenera kumakumbukira kuti Mulungu amatikonda ndipo adzakwaniritsa malonjezo ake.

SATANA ANAYESA KUCHITITSA YOBU KUTI ASAKHALE NDI CHIYEMBEKEZO

5-6. Kodi n’chiyani chinachitikira Yobu m’kanthawi kochepa?

5 Zinthu zinkamuyendera bwino kwambiri Yobu. Iye anali pa ubwenzi ndi Yehova. Anali ndi banja lalikulu komanso logwirizana ndipo anali ndi chuma chambiri. (Yobu 1:1-5) Koma m’tsiku limodzi lokha iye anataya pafupifupi chilichonse. Choyamba, anataya chuma chake chonse. (Yobu 1:13-17) Kenako ana ake onse anafa. Taganizirani nkhani yokhudza kufa kwa ana akeyi. Makolo amamva chisoni kwambiri mwana wawo akamwalira. Ndiye tangoganizani mmene Yobu ndi mkazi wake anamvera kupweteka atamva zoti ana awo onse 10 afa. Mpake kuti iye anang’amba zovala zake akulira n’kudzigwetsa pansi.​—Yobu 1:18-20.

6 Kenako Satana anadwalitsa Yobu matenda opweteka kwambiri komanso ochititsa manyazi. (Yobu 2:6-8; 7:5) Pa nthawi ina anthu a m’dera lake ankamulemekeza kwambiri ndipo ankabwera kudzamupempha malangizo. (Yobu 31:18) Koma tsopano anayamba kumupewa. Iye anayamba kukanidwa ndi abale ake, anzake ngakhalenso antchito ake enieni.​—Yobu 19:13, 14, 16.

A Mboni ambiri masiku ano angamvetse mmene Yobu anamvera atakumana ndi mavuto (Onani ndime 7) *

7. (a) Kodi Yobu ankakhulupirira kuti n’chiyani chinkachititsa mavuto ake, koma anakana kuchita chiyani? (b) Kodi Mkhristu angamve bwanji atakumana ndi mayesero ofanana ndi zimene zikuoneka pachithunzipa?

7 Satana ankafuna kuti Yobu azikhulupirira kuti akukumana ndi mavuto chifukwa choti Yehova sakumukondanso. Mwachitsanzo, Satana anachititsa mphepo ya mphamvu kuomba nyumba imene ana onse 10 a Yobu ankachitiramo phwando. (Yobu 1:18, 19) Anachititsanso moto kutsika kuchoka kumwamba nkuwononga, osati ziweto zokha, koma ngakhalenso antchito omwe ankazisamalira. (Yobu 1:16) Popeza kuti mphepoyo komanso motowo zinachokera kumwamba, Yobu ankaona ngati Yehova ndi amene akuchititsa ndipo ankaganiza kuti mwina wamukhumudwitsa mwa njira ina yake. Ngakhale zinali choncho, iye anakana kutukwana Atate wake wakumwamba. Yobu ankadziwa kuti kwa zaka zambiri anakhala akulandira zinthu zabwino kuchokera kwa Yehova. Choncho ankaganiza kuti ngati ankasangalala kulandira zinthu zabwino, ankayeneranso kukhala wokonzeka kulandira zinthu zoipa. Ndiye anati: “Dzina la Yehova lipitirize kutamandidwa.” (Yobu 1:20, 21; 2:10) Pofika pa nthawiyi Yobu anali adakali wokhulupirika kwa Yehova ngakhale kuti chuma chake chinali chitatha, ana ake atamwalira komanso anali akudwala kwambiri. Koma Satana anali asanathane naye.

8. Kodi kenako Satana anagwiritsa ntchito njira iti poyesa Yobu?

8 Kenako Satana anagwiritsa ntchito anthu atatu omwe ankati ndi anzake a Yobu kuti amuchititse kudziona ngati wachabechabe. Anthu amenewa ankanena kuti mavuto omwe Yobu anakumana nawo ankasonyeza kuti iye anachita zoipa zambiri. (Yobu 22:5-9) Iwo anayesetsanso kumuchititsa kukhulupirira kuti ngakhale zikanakhala kuti sankachita zoipa, zonse zomwe ankachita pofuna kusangalatsa Mulungu zinali zopanda phindu. (Yobu 4:18; 22:2, 3; 25:4) Pamenepatu iwo ankayesa kumuchititsa kukayikira kuti Mulungu amamukonda, angamusamalire, komanso kuti aziona kuti kumutumikira n’kosathandiza. Zimene ankalankhulazo zikanachititsa kuti Yobu ataye mtima.

9. N’chiyani chinathandiza Yobu kuti akhale wolimba?

9 Yerekezani kuti mukuona zomwe zikuchitika. Yobu wakhala paphulusa ndipo akumva ululu kwambiri. (Yobu 2:8) Anzake aja akupitirizabe kunena kuti iye si munthu wabwino ndiponso kuti zonse zomwe anachita n’zopanda phindu. Mayesero ake akumulemera ngati miyala ikuluikulu pomwe akupitiriza kumva chisoni kwambiri chifukwa cha imfa ya ana ake. Poyamba Yobu sakulankhulapo chilichonse. (Yobu 2:13–3:1) Ngati anzake a Yobuwo akuganiza kuti iye wakhala chete posonyeza kuti wasiya Mlengi wake, akudzinamiza. Pa nthawi ina Yobu, mwina podzutsa mutu n’kuyang’ana anzake abodzawo, akunena kuti: “Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.” (Yobu 27:5) N’chiyani chinathandiza Yobu kupitirizabe kukhala wolimba pa mavuto onse omwe anakumana nawo? Ngakhale pamene zinthu zinafika povuta kwambiri sanasiye kuyembekezera kuti Mulungu wake wachikondi amuthandiza. Ankadziwa kuti ngakhale atamwalira, Yehova adzamuukitsa.​—Yobu 14:13-15.

KODI TINGATSANZIRE BWANJI YOBU?

10. Kodi nkhani ya Yobu imatiphunzitsa chiyani?

10 Nkhani ya Yobu imatiphunzitsa kuti Satana sangatikakamize kuti tisiye kutumikira Yehova, komanso kuti Yehovayo amadziwa chilichonse chimene chikutichitikira. Zimene zinamuchitikirazi zingatithandizenso kumvetsa nkhani zina zomwe zinkachitika. Taganizirani mfundo zina zothandiza zomwe tingaphunzire kwa Yobu.

11. Ngati titapitiriza kukhulupirira Yehova, kodi tingakhale otsimikiza za chiyani? (Yakobo 4:7)

11 Zimene Yobu anachita zimasonyeza kuti tikamapitiriza kukhulupirira Yehova tikhoza kupirira mayesero aliwonse komanso kutsutsa Satana. Kodi zotsatira zake zingakhale zotani? Malemba amatitsimikizira kuti Mdyerekezi adzatithawa.​—Werengani Yakobo 4:7.

12. Kodi kukhala ndi chiyembekezo choti adzauka kunamulimbikitsa bwanji Yobu?

12 Tiyenera kumakhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka. Monga mmene nkhani yapita ija inafotokozera, nthawi zambiri Satana amagwiritsa ntchito mantha omwe timakhala nawo pa nkhani ya imfa pofuna kutichititsa kuti tisakhale okhulupirika. Satana ananena kuti Yobu akhoza kuchita chilichonse ngakhalenso kusiya kukhala wokhulupirika kwa Yehova, kuti ateteze moyo wake. Komatu limeneli linali bodza. Ngakhale pamene zinafika poipa kwambiri moti zinkaoneka kuti amwalira, Yobu sanasiye kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Anapitirizabe kupirira chifukwa chokhulupirira ubwino wa Yehova komanso kuyembekezera kuti Mulungu akonza zinthu. Ankakhulupirira kuti ngati Yehova sangakonze zinthu iye adakali ndi moyo, adzamuukitsa m’tsogolo. Yobu ankakhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka. Ngati ifenso timakhulupirira kwambiri zimenezi, sitingasiye kukhala okhulupirika kwa Yehova ngakhale pamene zikuoneka kuti tikhoza kufa.

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala tcheru ndi njira zomwe Satana anagwiritsa ntchito poyesa Yobu?

13 Tiyenera kukhala tcheru ndi njira zomwe Satana anagwiritsa ntchito poyesa Yobu chifukwa amazigwiritsanso ntchito masiku ano. Taonani zimene iye ananena: “Munthu [osati Yobu yekha] angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.” (Yobu 2:4, 5) Izi zikusonyeza kuti Satana amanena kuti sititumikira Mulungu mochokera pansi pa mtima, ndipo tikhoza kulolera kusiya kumutumikira kuti tipulumutse moyo wathu. Iye amanenanso kuti Mulungu satikonda ndipo zonse zomwe timachita kuti timusangalatse alibe nazo ntchito. Popeza tinachenjezedwa, ife amene timayembekezera Yehova sitimapusitsidwa ndi mabodza a Satanawa.

14. Kodi mayesero angatithandize bwanji? Perekani chitsanzo.

14 Tiziona mayesero omwe takumana nawo monga mwayi wathu wodziwira mmene tilili. Mayesero omwe Yobu anakumana nawo anamuthandiza kudziwa zinthu zomwe ankafunika kukonza pa moyo wake. Mwachitsanzo iye anazindikira kuti ankafunika kukulitsa khalidwe la kudzichepetsa. (Yobu 42:3) Ifenso tikakumana ndi mayesero tingadziwe zambiri zokhudza mmene tilili. M’bale wina dzina lake Nikolay, * yemwe anaikidwa m’ndende ngakhale kuti ankadwala kwambiri ananena kuti: “Ndende ili ngati mashini oonera mkati mwa thupi a X-ray, ndipo ingathandize kuona makhalidwe omwe Mkhristu ali nawo.” Tikadziwa zofooka zathu tikhoza kuzikonza.

15. Kodi tiyenera kumvera ndani, nanga n’chifukwa chiyani?

15 Tiyenera kumvera Yehova osati adani athu. Yobu anamvetsera mwatcheru pamene Yehova ankamulankhula. Mulungu anamuthandiza kuganizira nkhaniyo, zomwe zinali ngati akumuuza kuti: ‘Kodi ukutha kuona kuti ndili ndi mphamvu zolenga zinthu? Ndikudziwa chilichonse chomwe chakuchitikira. Kodi ukuganiza kuti sindingathe kukusamalira?’ Yobu anayankha modzichepetsa komanso anayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha ubwino wake. Iye anati: “Ndinkangomva za inu, koma tsopano diso langa lakuonani.” (Yobu 42:5) Yobu ayenera kuti analankhula zimenezi adakali pa phulusa pompaja, thupi lake lili zilonda zokhazokha komanso akulirabe ana ake omwe anamwalira aja. Ngakhale zinali choncho Yehova anamutsimikizira kuti ankamukonda komanso ankamuonabe kuti ndi bwenzi lake.​—Yobu 42:7, 8.

16. Mogwirizana ndi Yesaya 49:15, 16, kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikakumana ndi mayesero?

16 Masiku anonso anthu angatinyoze kapena kutichitira zinthu ngati kuti ndife opanda pake. Angayese kuipitsa mbiri yathu kapena ya gulu lathu komanso “kutinamizira zoipa zilizonse.” (Mat. 5:11) Pa zomwe zinachitikira Yobu, timaphunzira kuti Yehova sakayikira kuti tidzakhalebe okhulupirika tikakumana ndi mayesero. Iye amatikonda ndipo sangasiye anthu omwe amamuyembekezera. (Werengani Yesaya 49:15, 16.) Musamamvetsere zinthu zabodza zomwe adani a Mulungu amanena. M’bale wina wa ku Turkey dzina lake James, yemwe banja lake linakumana ndi mayesero aakulu ananena kuti: “Tinazindikira kuti kumvetsera mabodza omwe anthu amanenera anthu a Mulungu kungatifooketse. Choncho tinkaganizira kwambiri za chiyembekezo chathu cha Ufumu wa Mulungu komanso kuchita zambiri pomutumikira. Izi zinatithandiza kuti tipitirizebe kukhala osangalala.” Mofanana ndi Yobu timamvera Yehova. Mabodza amene adani athu amanena sangatichititse kutaya chiyembekezo chathu.

CHIYEMBEKEZO CHANU CHINGAKUTHANDIZENI KUKHALA OLIMBA

Yobu anadalitsidwa chifukwa chokhala ndi mtima wosagawanika. Iye ndi mkazi wake anasangalala kwa nthawi yaitali ndi madalitso a Yehova (Onani ndime 17) *

17. Kodi tikuphunzira chiyani kwa amuna ndi akazi okhulupirika otchulidwa pa Aheberi 11?

17 Yobu ndi mmodzi chabe wa atumiki a Yehova omwe anakhalabe olimba pokumana ndi mayesero. M’kalata imene analembera Aheberi, mtumwi Paulo anafotokozamo za enanso ambiri omwe anawatchula kuti “mtambo wa mboni waukulu.” (Aheb. 12:1) Onsewa anakumana ndi mayesero akuluakulu, koma anakhalabe okhulupirika kwa Yehova. (Aheb. 11:36-40) Ndiye kodi kupirira komanso khama lawo zinapita pachabe? Ayi ndithu. Ngakhale kuti munthawi yawo sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova, anapitirizabe kumuyembekezera. Ndipo popeza ankakhulupirira kuti Yehova akusangalala nawo, sankakayikira kuti adzaona malonjezowo akukwaniritsidwa. (Aheb. 11:4, 5) Chitsanzo chawo chingatithandize kukhala otsimikiza kwambiri kuti tiziyembekezera Yehova.

18. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani? (Aheberi 11:6)

18 Panopa tikukhala m’dziko limene likuipiraipirabe. (2 Tim. 3:13) Satana sanasiye kuyesa anthu a Mulungu. Kaya tikumana ndi mavuto otani m’tsogolomu, tiyeni titsimikize mtima kuti tizichita khama potumikira Yehova, n’kumakhulupirira kuti “chiyembekezo chathu chili mwa Mulungu wamoyo.” (1 Tim. 4:10) Tizikumbukira kuti zimene Mulungu anachitira Yobu pambuyo pake zimasonyeza “kuti Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.” (Yak. 5:11) Ifenso tiyeni tipitirize kukhala okhulupirika kwa Yehova ndipo tisamakayikire kuti adzapereka mphoto kwa “anthu omufunafuna ndi mtima wonse.”​—Werengani Aheberi 11:6.

NYIMBO NA. 150 Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke

^ Tikamaganizira za munthu yemwe anapirira mayesero aakulu, nthawi zambiri timaganizira za Yobu. Kodi timaphunzira chiyani pa zimene zinamuchitikira? Timaphunzira kuti Satana sangatikakamize kusiya kutumikira Yehova, komanso kuti Yehovayo amadziwa chilichonse chomwe chikutichitikira. Ndipo mofanana ndi mmene anathetsera mavuto a Yobu, tsiku lina adzathetsanso mavuto athu onse. Zochita zathu zikamasonyeza kuti timakhulupirira kwambiri mfundozi, timakhala m’gulu la anthu omwe ‘amayembekezera Yehova.’

^ TANTHAUZO LA MAWU ENA: Mawu a Chiheberi omwe anawamasulira kuti “chiyembekezo” kwenikweni amatanthauza “kudikira” chinachake mwachidwi. Angatanthauzenso kukhulupirira wina wake kapena kumudalira.​—Sal. 25:2, 3; 62:5.

^ Mayina ena asinthidwa.

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yobu ndi mkazi wake aferedwa ana awo.

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yobu anapirira mpaka pamene mayesero ake anatha. Iye ndi mkazi wake akuganizira madalitso omwe Yehova wapatsa banja lawo