Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 28

Ufumu wa Mulungu Ukulamulila!

Ufumu wa Mulungu Ukulamulila!

“Ufumu wa dziko wakhala Ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake.”—CHIV. 11:15.

NYIMBO 22 Ufumu Ulamulila—Ubwele!

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi ndife otsimikiza za ciyani? Nanga cifukwa ciyani?

 TIKAYANG’ANA mmene zinthu zikuyendela m’dzikoli, kodi sizikuwonjezela nkhawa kwa inu? Anthu m’mabanja sakondana. M’dzikoli anthu akuipilaipila pa kukhala ankhanza, odzikonda, ndiponso aciwawa. Ndipo ambili cimawavuta kukhulupilila anthu audindo. Koma zocitika zimenezi zingatipatse cidalilo cakuti zinthu zidzakhala bwino. N’cifukwa ciyani tikutelo? Cifukwa zimene anthu amacita n’zogwilizana ndendende na zimene Baibo inakambilatu ponena za “masiku otsiliza.” (2 Tim. 3:1-5) Kukwanilitsidwa kwa ulosi umenewu, kumene palibe munthu angatsutse, ni umboni wakuti Khristu Yesu akulamulila monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Kuwonjezela pa ulosi umenewu, palinso maulosi ena ambili okamba za Ufumu. Cikhulupililo cathu cidzalimba tikaona maulosi ena amene akwanilitsidwa m’zaka za posacedwa.

Monga mmene telala amalumikizila zidutswa zansalu n’kusoka covala, nawonso maulosi m’buku la Danieli na Chivumbulutso amatithandiza kudziŵa bwino pamene tafika na zocitika pa pulogilamu ya Yehova (Onani ndime 2)

2. Tikambilane ciyani m’nkhani ino? Nanga n’cifukwa ciyani? (Fotokozani cithunzi pacikuto.)

2 M’nkhani ino, tikambilane (1) ulosi umene umatithandiza kudziŵa pamene Ufumu unakhazikitsidwa, (2) maulosi amene amatithandiza kudziŵa kuti Yesu ni mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba, ndiponso (3) maulosi oonetsa mmene adani a Ufumu wa Mulungu adzawonongedwele. Monga mmene telala amalumikizila zidutswa zansalu n’kusoka covala, nawonso maulosi osiyana-siyana amene tikambilane, amatithandiza kudziŵa bwino pamene tafika na zocitika pa pulogilamu ya Yehova.

MMENE TIMADZIŴILA PAMENE UFUMUWO UNAKHAZIKITSIDWA

3. Kodi ulosi wa pa Danieli 7:13, 14, umatitsimikizila ciyani ponena za Mfumu ya Ufumu wa Mulungu?

3 Ulosi wa pa Danieli 7:13, 14, umatitsimikizila kuti Khristu Yesu adzakhala Wolamulila wabwino mu Ufumu wa Mulungu. Ndipo anthu a mitundu yonse adzasangalala ‘kumutumikila.’ Iye sadzaloŵedwa m’malo na Wolamulila wina. Ulosi wina wa m’buku la Danieli unakambilatu kuti Yesu adzalandila Ufumu wake kumapeto kwa nyengo yochedwa nthawi zokwanila 7. Kodi n’zotheka kudziŵa nthawi pamene cocitika cosangalatsaci cinacitika?

4. Fotokozani mmene Danieli 4:10-17 imatithandizila kudziŵa caka cimene Khristu anakhala Mfumu. (Onaninso mawu am’munsi.)

4 Ŵelengani Danieli 4:10-17. “Nthawi zokwanila 7” ziimila nyengo ya zaka 2,520. Nyengo imeneyo inayamba mu 607 B.C.E. pamene Ababulo anacotsa mfumu yothela pa mpando wacifumu wa Yehova ku Yerusalemu. Inatha mu 1914 C.E. pamene Yehova anaika Yesu, “amene ali woyenelela mwalamulo,” kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. *Ezek. 21:25-27.

5. Kodi ulosi wokamba za “nthawi zokwanila 7” ungatipindulile motani?

5 Kodi ulosi umenewu umatipindulila bwanji? Kudziŵa bwino “nthawi zokwanila 7” zimenezi, kumatipatsa cidalilo cakuti Yehova adzakwanilitsa malonjezo ake pa nthawi yake. Monga mmene anaikilatu nthawi yokhazikitsa Ufumu wake, iye adzaonetsetsanso kuti maulosi ena onse akwanilitsidwa pa nthawi yake yoikika. Inde, tsiku la Yehova ‘silidzacedwa.’—Hab. 2:3.

MMENE TIMADZIŴILA KUTI KHRISTU NI MFUMU YA UFUMU WA MULUNGU

6. (a) Ni umboni uti umene uonetsa kuti Khristu akulamulila kumwamba? (b) Kodi ulosi wa pa Chivumbulutso 6:2-8 umatsimikizila motani umboni umenewo?

6 Cakumapeto kwa utumiki wake padziko lapansi, Yesu anakambilatu zocitika padziko zimene zinali kudzathandiza ophunzila ake kudziŵa kuti iye wayamba kulamulila kumwamba. Mwa zina, anachula nkhondo, njala, na zivomezi. Anachulanso kuti kudzakhala milili, kapena kuti matenda “m’malo osiyana-siyana,” ndipo citsanzo ni mlili wa COVID-19. Baibo imachula zocitika zimenezi kuti “cizindikilo” ca kukhalapo kwa Khristu. (Mat. 24:3, 7; Luka 21:7, 10, 11) Patapita zaka zoposa 60 pambuyo pakuti Yesu wafa na kubwelela kumwamba, iye anatsimikizila mtumwi Yohane kuti zinthu zimenezi zidzacikadi. (Ŵelengani Chivumbulutso 6:2-8.) Zinthuzo zakhala zikucitika cicokeleni pamene Yesu anakhala Mfumu mu 1914.

7. N’cifukwa ciyani padziko lapansi pakucitika zinthu zoipa kwambili kucokela pamene Yesu anakhala Mfumu?

7 N’cifukwa ciyani zinthu padzikoli zinaipilatu Yesu atakhala Mfumu? Chivumbulutso 6:2 imapeleka yankho. Coyambilila cimene Yesu anacita atangokhala Mfumu ni kumenya nkhondo. Kumenyana na ndani? Na Mdyelekezi komanso ziŵanda zake. Malinga na Chivumbulutso caputala 12, Satana sanapambane nkhondoyo, ndipo iye pamodzi na ziŵanda zake anaponyedwa ku dziko lapansi. Popeza ali na mkwiyo waukulu, Satana akufuzila mkwiyo wakewo pa anthu. Zimenezi zabweletsa “tsoka [pa] dziko lapansi.”—Chiv. 12:7-12.

Sitikondwela kumva nkhani zoipa. Koma pamene tikuona maulosi a m’Baibo akukwanilitsidwa, timatsimikizila kuti Ufumu wa Mulungu ukulamuliladi (Onani ndime 8)

8. Timapindula bwanji tikamaona kukwanilitsidwa kwa maulosi okamba za Ufumu?

8 Kodi maulosi amenewa amatipindulila bwanji? Zocitika padzikoli komanso kusintha kwa makhalidwe a anthu, kumatithandiza kudziŵa kuti Yesu anakhala Mfumu. Conco, tisamakhumudwe tikaona anthu akucita zinthu modzikonda komanso mwankhanza. M’malo mwake, tizikumbukila kuti zocita zawozo zikukwanilitsa ulosi wa m’Baibo. Ufumu wa Mulungu ukulamulila. (Sal. 37:1) Ndipo zinthu pa dzikoli ziziipilaipila pamene Aramagedo ikuyandikila. (Maliko 13:8; 2 Tim. 3:13) Timamuyamikila kwambili Atate wathu wakumwamba potithandiza kudziŵa cifukwa cake padzikoli pali mavuto ambili.

MMENE ADANI A UFUMU WA MULUNGU ADZAWONONGEDWELA

9. Kodi ulosi wa pa Danieli 2:28, 31-35, umaufotokoza motani ulamulilo wothela padziko lonse? Nanga unayamba liti kulamulila?

9 Ŵelengani Danieli 2:28, 31-35. Ulosi umenewu ukukwanilitsidwa masiku ano. Loto la Nebukadinezara lionetsa zimene zinali kudzacitika “m’masiku otsiliza,” pambuyo pakuti Khristu wayamba kulamulila. Adani a Yesu padziko lapansi aphatikizapo ulamulilo wothela wamphamvu padziko lonse umene Baibo inakambilatu. Ulamulilowo ukuimilidwa na ‘mapazi acitsulo cosakanizika na dongo.’ Ulamulilo wa padziko lonse umenewu ukulamulila pali pano. Unayamba kulamulila pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, pamene Britain na America anapanga mgwilizano wapadela. Cifanizilo cimene Nebukadinezara analota, cinaonetsa zinthu ziŵili zokhudza ulamulilo wamphamvu padziko lonse umenewu. Zinthu ziŵilizo zikusiyanitsa ulamulilo umenewu na maufumu ena a kumbuyoku.

10. (a) Kodi ulosi wa Danieli unaonetsa motani mgwilizano wa Britain na America? (b) Kodi tiyenela kupewa ciyani? (Onani bokosi lakuti, “ Samalani Nalo Dongo!”)

10 Coyamba, mosiyana na maulamulilo amphamvu padziko lonse a m’mbuyomu ochulidwa m’masomphenya, mgwilizano wa Britain na America ukuimilidwa na msakanizo wa citsulo na dongo, osati golide kapena siliva. Dongo liimila “ana a anthu” kapena kuti anthu wamba. (Dan. 2:43) Monga mmene tikuonela masiku ano, anthu akhala na mphamvu kwambili pocita masankho, makampeni omenyela maufulu a anthu, zionetselo zazikulu, komanso kukhazikitsa mabungwe a anchito. Izi zacepetsa mphamvu za ulamulilo umenewu kuti ukwanilitse zofuna zake.

11. Kodi Ulamulilo wa Padziko Lonse wa Britain na America, umalimbitsa bwanji cidalilo cathu cakuti tikukhala m’nthawi ya mapeto?

11 Caciŵili, Britain na America amene akuimilidwa na mapazi a cifanizilo cacikulu cija, ndiwo ulamulilo wothela wamphamvu padziko lonse umene Baibo inakambilatu. Ndipo sudzaloŵedwa m’malo na ulamulilo wina wa anthu. M’malo mwake, ulamulilowu pamodzi na maboma ena onse a anthu udzawonongedwa na Ufumu wa Mulungu pa Aramagedo. *Chiv. 16:13, 14, 16; 19:19, 20.

12. Kodi ulosi wa Danieli umapeleka umboni winanso uti umene umatilimbikitsa na kutipatsa ciyembekezo?

12 Kodi ulosi umenewu umatipindulila bwanji? Ulosi wa Danieli umapeleka umboni winanso woonetsa kuti tikukhala m’nthawi ya mapeto. Zaka zoposa 2,500 zapitazo, Danieli anakambilatu kuti ufumu wa Babulo ukadzatha, maulamulilo ena anayi amphamvu padziko lonse adzakhudza kwambili zocita za anthu a Mulungu. Kuwonjezela apo, iye anaonetsa kuti ulamulilo wa Britain na America udzakhala wothela pa maulamulilo amenewa. Izi zimatilimbikitsa na kutipatsa ciyembekezo cakuti posacedwa, Ufumu wa Mulungu udzaseselatu maboma onse a anthu, ndipo udzalamulila dziko lonse lapansi.—Dan. 2:44.

13. Kodi “mfumu ya 8” komanso “mafumu 10” zochulidwa pa Chivumbulutso 17:9-12 ziimila ciyani? Ndipo kodi ulosi umenewu wakwanilitsidwa motani?

13 Ŵelengani Chivumbulutso 17:9-12. Zimene zinawonongedwa pa nkhondo yoyamba yapadziko lonse, zinakwanilitsa ulosi winanso wa m’Baibo wokamba za masiku otsiliza. Olamulila andale anafuna kubweletsa mtendele padziko lonse. Conco mu January 1920, iwo anakhazikitsa bungwe la League of Nations, limene linadzaloŵedwa m’malo na bungwe la United Nations mu October 1945. Bungwe limeneli limachedwa “mfumu ya 8.” Koma izi sizitanthauza kuti nawonso ni ulamulilo wamphamvu padziko lonse. Bungweli limatenga mphamvu ku maulamulilo andale amene ni mamembala ake. Mophiphilitsa, Baibo imachula maulamulilo amenewa kuti “mafumu 10.”

14-15. (a) Kodi Chivumbulutso 17:3-5 imati ciyani za “Babulo Wamkulu”? (b) Fotokozani zimene zikucitikila zipembedzo zonyenga.

14 Ŵelengani Chivumbulutso 17:3-5. M’masomphenya ocokela kwa Mulungu, mtumwi Yohane anaona hule, “Babulo Wamkulu,” amene aimila ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conyenga. Kodi masomphenya amenewa akwanilitsidwa motani? Kwa nthawi yaitali, zipembedzo zonyenga zakhala zikugwilizana kwambili na maulamulilo andale, ndipo zikudalitsa maulamulilo amenewo. Komabe, posacedwa Yehova adzaika m’mitima ya maulamulilo andale amenewa zakuti ‘acite monga mwa maganizo ake.’ Kodi padzakhala zotulukapo zotani? Maulamulilo andale amenewo, kapena kuti “mafumu 10,” adzaukila zipembedzo zonyenga na kuziwononga.—Chiv. 17:1, 2, 16, 17.

15 Tidziŵa bwanji kuti mapeto a Babulo Wamkulu ayandikila? Cingatithandize kuyankha funso limeneli ni kukumbukila kuti mzinda wamakedzana wa Babulo unali wotetezeka na madzi a mtsinje waukulu wa Firate. Buku la Chivumbulutso limayelekezela anthu mamiliyoni amene amacilikiza Babulo Wamkulu na “madzi” oteteza. (Chiv. 17:15) Koma imaonetsanso kuti madziwo ‘adzauma,’ kutanthauza kuti anthu ambili adzaleka kucilikiza zipembedzo zonyenga. (Chiv. 16:12) Ulosi umenewu ukukwanilitsidwa masiku ano cifukwa anthu ambili akutuluka m’zipembedzo zonyenga, ndipo akupita kwina kukafuna-funa thandizo pa mavuto awo.

16. Kodi kumvetsa tanthauzo la maulosi okamba za bungwe la United Nations na kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu kumatipindulila bwanji?

16 Kodi maulosi amenewa amatipindulila bwanji? Kukhazikitsidwa kwa bungwe la United Nations, komanso kuleka kwa anthu kucilikiza zipembedzo zonyenga, ni umboni winanso wakuti tili m’masiku otsiliza. Pamene madzi ophiphilitsa a Babulo Wamkulu akuuma, kodi ndiko kudzakhala kuwonongedwa kwa zipembedzo zonyenga? Ayi. Monga takambila kale, Yehova adzapangitsa “mafumu 10,” kutanthauza maulamulilo andale amene amacilikiza bungwe la United Nations, ‘kuti acite monga mwa maganizo ake.’ Babulo Wamkulu adzawonongedwa modzidzimutsa na maulamulilo andale amenewa, ndipo dziko lonse lidzadabwa. * (Chiv. 18:8-10) Kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu kudzawakhudza kwambili anthu padziko, ndipo kungadzabweletse mavuto. Koma anthu a Mulungu adzakhala na zifukwa ziŵili zokhalila acimwemwe. Cipembedzo conyenga, cimene cakhala mdani wa Yehova Mulungu kwa zaka zambili sicidzakhalaponso. Ndipo cipulumutso cathu cidzakhala citayandikila.—Luka 21:28.

KHALANI NA CIDALILO CAKUTI YEHOVA ADZATITETEZA M’TSOGOLOMU

17-18. Kodi tingatani kuti tilimbitsebe cikhulupililo cathu? (b) Kodi tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

17 Danieli analosela kuti anthu “adzadziŵa zinthu zambili zoona.” Ndipo zimenezi n’zoona. Tamvetsa maulosi ambili okhudza nthawi yathu ino. (Dan. 12:4, 9, 10) Maulosi amenewo ni olondola, ndipo amatipangitsa kumulemekeza kwambili Yehova komanso Mawu ake ouzilidwa. (Yes. 46:10; 55:11) Conco, pitilizani kulimbitsa cikhulupililo canu mwa kuphunzila Malemba mwakhama, ndiponso kuthandiza ena kukhala pa ubale wabwino na Yehova. Iye amateteza anthu amene amamudalila kwathunthu, na kuwapatsa “mtendele wosatha.”—Yes. 26:3.

18 M’nkhani yotsatila, tidzakambilana maka-maka maulosi okamba za mpingo wacikhristu m’nthawi ya mapeto. Monga tidzaphunzilila, maulosi amenewo adzapelekanso umboni wakuti tikukhala m’masiku otsiliza. Tidzaonanso umboni wina wakuti Yesu ni Mfumu yathu amene tsopano akutsogolela otsatila ake okhulupilika.

NYIMBO 61 Patsogolo!Inu Mboni Zake

^ Tikukhala m’nthawi yocititsa cidwi kwenikweni m’mbili yonse ya anthu. Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa, malinga na zimene maulosi ambili a m’Baibo anakambilatu. M’nkhani ino, tikambilane ena mwa maulosi amenewo n’colinga cakuti tizamitse cikhulupililo cathu mwa Yehova, komanso kuti atithandize kukhala osatekeseka ndi acidalilo pali pano ndiponso m’tsogolo.

^ Onani phunzilo 32 mfundo 4 m’buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!, ndiponso onelelani vidiyo pa jw.org yakuti Ufumu wa Mulungu Unayamba Kulamulila mu 1914.

^ Kuti mudziŵe zambili ponena za ulosi wa Danieli, onani Nsanja ya Olonda, ya June 15, 2012, mas. 14-19.

^ Kuti mudziŵe zambili zakutsogolo, onani mutu 21 m’buku lakuti Ufumu wa Mulungu Ukulamulila!