Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 30

Ulosi Wamakedzana Umene Umakukhudzani

Ulosi Wamakedzana Umene Umakukhudzani

“Ndidzaika cidani pakati pa iwe ndi mkaziyo.”—GEN. 3:15.

NYIMBO 15 Tamandani Woyamba Kubadwa wa Yehova

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Yehova anacita ciyani Adamu na Hava atangocimwa? (Genesis 3:15)

 ADAMU na Hava atangocimwa, Yehova anapeleka ciyembekezo ku mbadwa zake kupitila mu ulosi wofunika kwambili. Zimene anakamba zinalembedwa pa Genesis 3:15.—Ŵelengani.

2. N’cifukwa ciyani ulosi wa pa Genesis 3:15 ni wofunika kwambili?

2 Ulosi umenewu timaupeza m’buku loyamba la m’Baibo. Koma mabuku ena onse a m’Baibo amagwilizana na ulosiwu m’njila ina yake. Monga mmene msana wa buku umamangilizila masamba onse pamodzi, nawonso mawu a pa Genesis 3:15 amamangiliza mabuku onse a m’Baibo kuti akhale uthenga umodzi wogwilizana. Uthengawo ni wakuti Mpulumutsi adzatumizidwa kuti awononge Mdyelekezi komanso onse omutsatila. * Zimenezi zidzakhala zokondweletsa kwa onse okonda Yehova!

3. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 M’nkhani ino, tiyankha mafunso otsatilawa onena za ulosi wa pa Genesis 3:15: Ndani amene akuchulidwa mu ulosi umenewu? Kodi ulosiwu ukukwanilitsidwa bwanji? Nanga timapindula motani na ulosi umenewu?

NDANI AMENE AKUCHULIDWA MU ULOSIWU?

4. Kodi “njokayo” ndani? Nanga tidziŵa bwanji zimenezi?

4 Amene akuchulidwa m’nkhani ya pa Genesis 3:14, 15, ni “njoka,” “mbewu” ya njokayo, “mkazi,” ndiponso “mbewu” ya mkaziyo. Baibo imatithandiza kuwadziŵa bwino onsewa. * Tiyeni tiyambe na njoka. Njoka yeniyeni sikanamva zimene Yehova anakamba m’munda wa Edeni. Conco, Yehova ayenela kuti anali kukamba na colengedwa cokhala na nzelu popeleka ciweluzo cake. Kodi colengedwaco cinali ndani maka-maka? Chivumbulutso 12:9 iyankha funso limeneli. Pa lembali, “njoka yakale ija” imachulidwa kuti Satana Mdyelekezi. Koma kodi mbewu ya njokayo ndani?

NJOKA

Ni Satana Mdyelekezi, amene Chivumbulutso 12:9 imamuchula kuti “njoka yakale ija” (Onani ndime 4)

5. Kodi mbewu ya njokayo ndani?

5 Nthawi zina, Baibo imagwilitsa nchito mawu akuti mbewu mophiphilitsa, potanthauza aja amene amaganiza na kucita zinthu monga tate wawo wophiphilitsa. Conco, mbewu ya njokayo imaphatikizapo zolengedwa zauzimu komanso anthu oipa, ndipo imatsutsa Yehova Mulungu na anthu ake, monga mmene Satana amacitila. Zolengedwa zauzimuzo ni angelo amene anasiya mautumiki awo kumwamba m’nthawi ya Nowa. Ndipo anthu oipawo ni aja amene amacita zinthu potengela tate wawo Mdyelekezi.—Gen. 6:1, 2; Yoh. 8:44; 1 Yoh. 5:19; Yuda 6.

MBEWU YA NJOKAYO

Ni zolengedwa zauzimu komanso anthu amene amatsutsa Yehova Mulungu na anthu ake (Onani ndime 5)

6. N’cifukwa ciyani ‘mkazi’ wochulidwa mu ulosiwu sangakhale Hava?

6 Tsopano, tiyeni tikambilane za “mkaziyo.” Iye ayenela kuti sanali Hava. N’cifukwa ciyani tikutelo? Taonani cifukwa cimodzi ici. Ulosiwo unakamba kuti mbewu ya mkaziyo “idzaphwanya” mutu wa njokayo. Monga taonela kale, njokayo ni Satana amene ni colengedwa cauzimu. Ndipo mbewu ya munthu wopanda ungwilo, Hava, sikanatha kuphwanya mutu wake. Conco panafunikila wina wake amene akanatha kucita zimenezo.

7. Mogwilizana na Chivumbulutso 12:1, 2, 5, 10, kodi mkazi wochulidwa pa Genesis 3:15 ndani?

7 Buku lothela m’Baibo limamufotokoza bwino mkazi wochulidwa pa Genesis 3:15. (Ŵelengani Chivumbulutso 12:1, 2, 5, 10.) Ameneyu si mkazi wamba. Iye ali na mwezi kunsi kwa mapazi ake, ndipo kumutu kwake kuli cisoti cacifumu cokhala na nyenyezi 12. Mkaziyu anabeleka mwana wophiphilitsa, amene ni Ufumu wa Mulungu. Ufumuwo uli kumwamba, conco nayenso mkaziyu ayenela kukhala wakumwamba. Iye ni gulu la Yehova lakumwamba la angelo onse okhulupilika.—Agal. 4:26.

MKAZI

Ni gulu la Yehova lakumwamba la angelo onse okhulupilika (Onani ndime 7)

8. Kodi mbali yoyamba ya mbewu ya mkaziyo ndani? Nanga ni liti pamene anakhala mbewuyo? (Genesis 22:15-18)

8 Mawu a Mulungu amatithandiza kudziŵanso amene ali mbali yoyamba ya mbewu ya mkaziyo. Mbewuyo anayenela kukhala mbadwa ya Abulahamu. (Ŵelengani Genesis 22:15-18.) Malinga na ulosi, Yesu ndiye anali mbadwa yeniyeni ya munthu wokhulupilika ameneyo. (Luka 3:23, 34) Koma mbewuyo anayenela kukhala wamphamvu kuposa munthu, cifukwa adzaphwanya Satana Mdyelekezi kuti asadzakhalekonso. Conco, Yesu atafika zaka pafupifupi 30 anadzozedwa na mzimu woyela monga Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. Pamene iye anadzozedwa, anakhala mbewu yofunika kwambili ya mkazi. (Agal. 3:16) Yesu atafa na kuukitsidwa, Mulungu ‘anamuveka ulemelelo ndi ulemu monga cisoti cacifumu,” ndipo anam’patsa “ulamulilo wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.” Anam’patsanso ulamulilo wakuti “awononge nchito za Mdyerekezi.”—Aheb. 2:7; Mat. 28:18; 1 Yoh. 3:8.

MBEWU YA MKAZIYO

Ni Yesu Khristu pamodzi na olamulila anzake odzozedwa a 144,000 (Onani ndime 8-9)

9-10. (a) Ndani ena amene alinso mbewu ya mkaziyo? Nanga ni liti pamene amakhala mbewuyo? (b) Kodi tikambilane ciyani tsopano?

9 Koma pali amene akupanga mbali yaciŵili ya mbewu ya mkaziyo. Mtumwi Paulo anawachula pamene anauza Ayuda na Akhristu odzozedwa a mitundu ina kuti: “Ngati muli a Khristu, ndinudi mbewu ya Abulahamu, olandila colowa mogwilizana ndi lonjezolo.” (Agal. 3:28, 29) Yehova akadzoza Mkhristu na mzimu woyela, munthuyo amakhala mbali ya mbewu ya mkaziyo. Conco, mbewu imeneyi imaphatikizapo Yesu Khristu na olamulila anzake a 144,000. (Chiv. 14:1) Onsewa amatengela citsanzo ca Atate wawo, Yehova Mulungu.

10 Popeza tadziŵa onse ochulidwa pa Genesis 3:15, tiyeni lomba tikambilane mmene Yehova wakhala akukwanilitsila ulosi umenewu, komanso mmene tikupindulila nawo.

KODI ULOSIWU WAKHALA UKUKWANILITSIDWA MOTANI?

11. Kodi mbewu ya mkaziyo inavulazidwa “cidendene” cake m’lingalilo lanji?

11 Malinga na ulosi wa pa Genesis 3:15, njoka inali kudzavulaza “cidendene” ca mbewu ya mkazi. Ulosiwu unakwanilitsidwa pamene Satana, anasonkhezela Ayuda na Aroma kuti aphe Mwana wa Mulungu. (Luka 23:13, 20-24) Munthu akadzipweteka cidendene, kwa kanthawi amalephela kuyenda. Mofananamo, Yesu atafa n’kuikidwa m’manda, sanathe kucita ciliconse kwa masiku atatu.—Mat. 16:21.

12. Kodi mutu wa njokayo udzaphwanyidwa motani? Nanga zimenezi zidzacitika liti?

12 Kuti ulosi wa pa Genesis 3:15 ukwanilitsidwe, Yesu anafunika kuukitsidwa. Cifukwa ciyani? Cifukwa malinga na ulosi, mbewu ya mkazi imeneyi inafunika kuphwanya mutu wa njokayo. Izi zinafuna kuti cilonda cake ku cidendene cipole. Ndipo cinapoladi! Pa tsiku lacitatu Yesu anaukitsidwa monga colengedwa cauzimu cosakhoza kufa. Nthawi ya Mulungu ikadzakwana, Yesu adzaphwanya Satana kuti asadzakhalekonso. (Aheb. 2:14) Awo amene adzalamulila na Khristu, adzagwila naye nchito yowononga adani onse a Mulungu, omwe ni mbewu ya njoka.—Chiv. 17:14; 20:4, 10. *

KODI ULOSI UMENEWU TIKUPINDULA NAWO MOTANI?

13. Kodi tikupindula motani na kukwanilitsidwa kwa ulosi umenewu?

13 Ngati ndinu mtumiki wa Mulungu wodzipatulila, ndiye kuti mukupindula na kukwanilitsidwa kwa ulosi umenewu. Yesu anabwela padziko monga munthu, ndipo anaonetsa bwino makhalidwe a Atate ake. (Yoh. 14:9) Conco mwa kuphunzila za Yesu, tafika pom’dziŵa bwino Yehova Mulungu, na kuyamba kum’konda. Tapindulanso na ziphunzitso za Yesu, komanso citsogozo cake pa mpingo wacikhristu masiku ano. Iye watiphunzitsa mmene tingakhalile na umoyo wokondweletsa Yehova. Ndipo tonsefe tingapindule cifukwa ca imfa ya Yesu, kapena kuti kuvulazidwa kwa cidendene cake. Motani? Yesu ataukitsidwa, anapeleka mtengo wa magazi ake monga nsembe yangwilo ‘yotiyeletsa ku ucimo wonse.’—1 Yoh. 1:7.

14. Kodi tidziŵa bwanji kuti zimene Yehova analosela mu Edeni sizinakwanitsidwe nthawi yomweyo? Fotokozani.

14 Mawu a ulosi amene Yehova anakamba mu Edeni, anaonetsa kuti padzapita nthawi kuti akwanilitsidwe kwathunthu. Panafunika nthawi kuti mkazi abeleke mbewu yolonjezedwa, kuti Mdyelekezi asonkhanitse otsatila ake, komanso kuti cidani cionekele pakati pa magulu aŵili amenewa. Kumvetsa ulosi umenewu kumatipindulila, cifukwa umanenelatu kuti dziko lolamulidwa na Satana limazonda alambili a Yehova. Patapita nthawi, Yesu anauza ophunzila ake zofanana na zimenezi. (Maliko 13:13; Yoh. 17:14) Takhala tikuona kukwanilitsidwa kwa mbali ya ulosi umenewu maka-maka pa zaka 100 zapitazo. Kodi wakwanilitsidwa motani?

15. N’cifukwa ciyani cidani ca anthu m’dzikoli cakula kwambili pa ife? Nanga n’cifukwa ciyani sitiyenela kumuopa Satana?

15 Yesu atangokhala Mfumu Yaumesiya mu 1914, anapitikitsa Satana kumwamba. Pano tikamba, iye ali pano padziko lapansi, kuyembekezela ciwonongeko. (Chiv. 12:9, 12) Koma sikuti akungoyembekezela popanda kucitapo kanthu. Iye ali pa kalikiliki, ni wokwiya ndipo akukhuthulila mkwiyo wakewo pa anthu a Mulungu. (Chiv. 12:13, 17) Pa cifukwa cimeneci, cidani ca anthu m’dzikoli cakulilatu pa anthu a Mulungu akulitsa. Koma palibe cifukwa coopela Satana na otsatila ake. M’malo mwake, timakhala na cidalilo monga ca mtumwi Paulo, amene analemba kuti: “Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?” (Aroma 8: 31) Conco, tiyenela kukhala na cidalilo conse mwa Yehova, cifukwa monga taonela, mbali yaikulu ya ulosi wa pa Genesis 3:15 inakwanilitsidwa kale.

16-18. Kodi Curtis, Ursula, komanso Jessica, apindula bwanji cifukwa comvetsetsa Genesis 3:15?

16 Lonjezo la Yehova la pa Genesis 3:15 lingatithandize kuthana na mayeso alionse amene tingakumane nawo. Mmishonale wina dzina lake Curtis, amene akutumikila ku Guam, anati: “Nthawi zina, nimakumana na mayeso amene amayesa kukhulupilika kwanga kwa Yehova. Koma kusinkhasinkha ulosi wa pa Genesis 3:15, kwanithandiza kukhulupililabe Atate wanga wakumwamba.” M’bale Curtis amayembekezela mwacidwi nthawi pamene Yehova adzacotsapo mavuto onse.

17 Mlongo wina wa ku Bavaria dzina lake Ursula, anakamba kuti kumvetsa ulosi wa pa Genesis 3:15 kunam’thandiza kukhulupilila kuti Baibo ni youzilidwa na Mulungu. Iye anacita cidwi kwambili poona kuti maulosi ena onse amagwilizana na ulosi umenewu. Iye anakambanso kuti: “N’nalimbikitsidwa ngako n’tadziŵa kuti Yehova anacitapo kanthu mwamsanga kuti mtundu wa anthu ukhale na ciyembekezo.”

18 Mlongo Jessica wa ku Micronesia anati: “Nimakumbukilabe mmene n’namvela nthawi yoyamba n’tazindikila kuti napeza coonadi. N’naona kuti ulosi wa pa Genesis 3:15 ukukwanilitsidwa. Izi zanithandiza kukumbukila kuti sicinali colinga ca Yehova kuti anthufe tizikumana na mavuto. Ulosi umenewu, walimbitsanso cikhulupililo canga cakuti kutumikila Yehova kumatithandiza kukhala na umoyo wabwino koposa pali pano, ngakhalenso m’tsogolo.”

19. N’cifukwa ciyani tingakhale otsimikiza kuti mbali yothela ya ulosi umenewu idzakwanilitsidwa?

19 Monga taonela, ulosi wa pa Genesis 3:15 ukukwanilitsidwa. Tadziŵa amene ali mbewu ya mkazi komanso mbewu ya njoka. Yesu, amene ndiye mbali yoyamba ya mbewu ya mkaziyo anacila cilonda ca cidendene cake, ndipo pano tikamba, iye ni Mfumu yamphamvu yosakhoza kufa. Yehova watsala pang’ono kutsiliza kusankha amene adzalamulile pamodzi na Mwana wake. Iwonso ni mbewu ya mkazi. Poti mbali yoyamba ya ulosi umenewu inakwanilitsidwa kale, ndife otsimikiza kuti nayonso mbali yothela, imene ni kuphwanya mutu wa njoka, idzakwanilitsidwa. Atumiki a Mulungu okhulupilika adzakondwela kwambili Satana akadzawonongedwa. Pamene tikuyembekezela nthawiyo, conde tisafooke. Mulungu wathu ni wokhulupilika. Kupitila mwa mbewu ya mkazi, iye adzadalitsa “mitundu yonse ya padziko lapansi.”—Gen. 22:18.

NYIMBO 23 Ulamulilo wa Yehova Wayamba

^ Kuti tiumvetsetse bwino uthenga wa m’Baibo, tiyenela kumvetsa ulosi wa pa Genesis 3:15. Kuphunzila ulosi umenewu kungalimbitse cikhulupililo cathu mwa Yehova, na kutithandiza kukhala otsimikiza kuti iye adzakwanilitsa malonjezo ake onse.

^ Onani mutu wakuti, “Uthenga wa m’Baibulo” m’kabuku kakuti, Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu.

^ Onani bokosi lakuti, “Ochulidwa pa Genesis 3:14, 15.”