Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 37

N’zotheka Kuti Muziwadalila Abale Anu

N’zotheka Kuti Muziwadalila Abale Anu

“Cikondi . . . cimakhulupilila zinthu zonse, cimayembekezela zinthu zonse.”—1 AKOR. 13:4, 7.

NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciyani n’zosabwitsa kuti anthu m’dzikoli sakhulupililana?

 M’DZIKO la Satanali, n’cinthu covuta kwa anthu kukhulupilila aliyense. Izi zili conco cifukwa nthawi zambili iwo amagwilitsidwa mwala na azamalonda, andale, komanso atsogoleli acipembedzo. Zimenezi zapangitsanso ena kuleka kukhulupilila anzawo, maneba awo, ngakhale a m’banja mwawo. Sitiyenela kudabwa na zimenezi cifukwa Baibo inakambilatu kuti: ‘M’masiku otsiliza . . . anthu adzakhala . . . osakhulupilika, . . . onenela anzawo zoipa, . . . aciwembu.’ M’mawu ena, anthu amatengela maganizo a mulungu wa nthawi ino amene sitingam’khulupilile olo pang’ono.—2 Tim. 3:1-4; 2 Akor. 4:4.

2. (a) Ndani amene tiyenela kum’dalila na mtima wonse? (b) Nanga ena angakayikile ciyani?

2 Ife Akhristu timadziŵa kuti tiyenela kudalila Yehova na mtima wonse. (Yer. 17:7, 8) Timatsimikiza kuti iye amatikonda, komanso kuti ‘sadzasiya’ mabwenzi ake. (Sal. 9:10) Timadalilanso Khristu Yesu cifukwa anapeleka moyo wake kaamba ka ife. (1 Pet. 3:18) Ndipo tadzionela tokha kuti Baibo imapeleka citsogozo codalilika. (2 Tim. 3:16, 17) Conco, n’zosacita kufunsa kuti timadalila Yehova, Yesu, komanso Baibo. Koma ena angayike ngati abale na alongo mu mpingo nawonso angawadalile nthawi zonse. Ngati timakayikila, n’cifukwa ciyani m’pofunika kuti tiziwadalila?

ABALE NA ALONGO NI OFUNIKA KWA IFE

Kuzungulila dziko lonse, tili na abale na alongo amenenso amam’konda Yehova mmene ife timacitila (Onani ndime 3)

3. Ni mwayi wapadela uti umene tili nawo? (Maliko 10:29, 30)

3 Yehova anatisankha kukhala m’banja la padziko lonse la alambili ake. Umenewu ni mwayi wapadela kwambili, ndipo umabweletsa madalitso osaneneka. (Ŵelengani Maliko 10:29, 30.) Kuzungulila dziko lonse, tili na abale na alongo amenenso amam’konda Yehova mmene ife timacitila. Ndipo amayesetsa kumvela malamulo ake pa umoyo wawo. Olo kuti timasiyana zinenelo, zikhalidwe, na mavalidwe, timawakonda abale athu ngakhale taonana nawo kwa nthawi yoyamba. Timakondwela maka-maka tikamatamanda nawo limodzi Atate wathu wacikondi wakumwamba, na kum’lambila.—Sal. 133:1.

4. N’cifukwa ciyani abale na alongo ni ofunika kwa ife?

4 Tiyenela kukhalabe ogwilizana na abale na alongo athu kuposa kale lonse. Nthawi zina, iwo amatithandiza kunyamula zofooka zathu. (Aroma 15:1; Agal. 6:2) Cina, amatilimbikitsa kukhalabe okangalika potumikila Yehova, komanso kukhala olimba mwauzimu. (1 Ates. 5: 11; Aheb. 10:23-25) Tangoganizilani mmene zikanakhalila kwa ife popanda abale na alongo otithandiza kucilimika pogwebana na adani athu, omwe ni Satana Mdyerekezi na dziko lake loipa. Posacedwa, Satana pamodzi na anthu ake adzaukila atumiki a Mulungu. Pa nthawiyo, tikasangalala kwambili kuona kuti abale na alongo ali pambali pathu kutithandiza.

5. N’cifukwa ciyani ena cimawavuta kudalila abale na alongo?

5 Komabe, ena cimawavuta kudalila abale na alongo, mwina cifukwa cakuti Mkhristu mnzawo anaulula nkhani yawo ya cinsinsi. Kapena wina mu mpingo anakamba kapena kucita zinthu zimene zinawakhumudwitsa kwambili. Zaconco zikacitika, cingakhale covuta kudalila ena. Ndiye n’ciyani cingatithandize kuti tiziwadalila abale na alongo?

CIKONDI CIMATITHANDIZA KUWADALILA ABALE ATHU

6. Kodi cikondi cingatithandize bwanji kudalila ena? (1 Akorinto 13:4-8)

6 Cikondi ndiwo maziko a kudalilana wina na mnzake. 1 Akorinto caputala 13, imafotokoza mmene cikondi cimatithandizila kudalila abale athu, kapena kuyambilanso kuwadalila. (Ŵelengani 1 Akorinto 13:4-8.) Mwacitsanzo, vesi 4 imati “cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima.” Yehova amaleza nafe mtima ngakhale pamene tam’cimwila. Mofananamo, tiyenela kuwalezela mtima abale athu akatikhumudwitsa m’mawu kapena m’zocita. Vesi 5 imati: “[Cikondi] sicikwiya. Sicisunga zifukwa.” Conco, tizipewa kusunga zolakwa za abale athu mumtima, na colinga cakuti akakalakwitsanso, tikawakumbutse. Ndipo Mlaliki 7:9 imati ‘tisamafulumile kukwiya mumtima mwathu.’ Conco, ni bwino kutsatila mawu a pa Aefeso 4:26 akuti: “Dzuŵa lisaloŵe muli cikwiyile.”

7. Kodi mfundo za pa Mateyu 7:1-5, zimatithandiza bwanji kudalila ena?

7 Cina cingatithandize kudalila abale na alongo athu, ni kuwaona mmene Yehova amawaonela. Iye amawakonda, ndipo sawasungila zifukwa akalakwa. Ifenso tiyenela kucita cimodzimodzi. (Sal. 130:3) M’malo moyang’ana pa zophophonya zawo, tiziyang’ana pa makhalidwe awo abwino, komanso zabwino zimene iwo angathe kucita. (Ŵelengani Mateyu 7:1-5.) Tiyeni tiziwadalilabe, cifukwa cikondi “cimakhulupilila zinthu zonse.” (1 Akor. 13:7) Mawuwa satanthauza kuti Yehova amafuna kuti tizidalila ena mwacimbuli-mbuli ayi. Koma amafuna tiziwadalila cifukwa amaonetsa kuti ni okhulupilika. *

8. Kodi tingacite ciyani kuti tiziwadalila abale athu?

8 Ulemu umabwela wokha. N’cimodzimodzinso kuti anthu ayambe kutidalila, ndipo izi zimatenga nthawi. Kodi tingacite ciyani kuti tiyambe kuwadalila abale athu? Tiyenela kuwadziŵa bwino. Tingacite zimenezi mwa kuceza nawo pa misonkhano ya mpingo, na kumalalikila nawo. Ndipo tizileza nawo mtima kuti tiwapatse mwayi woonetsa kuti ni okhulupilika. Mwacitsanzo, munthu amene mwangoyamba kumene kudziŵana naye, simungamuuze nkhani zanu zonse zacinsinsi. Koma pamene mwafika pom’dziŵa bwino munthuyo, pang’ono-m’pang’ono mungayambe kumasuka kumuuzako nkhani za inu mwini. (Luka 16:10) Nanga mungacite ciyani ngati m’bale kapena mlongo anaulula cinsinsi canu? Musafulumile kuthetsa ubwenzi wanu. Ndipo musalole kuti zophophonya za ocepa zikupangitseni kuleka kudalila abale na alongo. Pa nkhani imeneyi, tiyeni tikambilane zitsanzo za atumiki angapo a Yehova okhulupilika amene anagwilitsidwapo mwala, koma sanaleke kudalila abale awo.

PHUNZILANI KWA ANTHU AMENE SANALEKE KUDALILA ENA

Hana saneleke kudalila anthu oimilako Yehova, olo kuti poyamba Eli anamudzudzula kuti waledzela (Onani ndime 9)

9. (a) Kodi Hana anapitiliza bwanji kudalila makonzedwe a Yehova mosayang’ana zolakwa za anthu omuimilako? (b) Kodi citsanzo ca Hana citiphunzitsa ciyani pa nkhani yodalila makonzedwe a Yehova? (Onani cithunzi.)

9 Kodi munayamba mwakhumudwapo na zocita za m’bale wapaudindo? Ngati n’conco, mungapindule poganizila citsanzo ca Hana. Pa nthawiyo, Mkulu wa Ansembe Eli ndiye anali kutsogolela pa kulambila Yehova mu Isiraeli. Koma banja lake silinali citsanzo cabwino. Ana ake amene anali na maudindo apadela, nthawi zambili anali kucita zaciwelewele, limene ni khalidwe lonyansa. Komanso atate wawo sanali kuwadzudzula mwamphamvu. Yehova sanacotse Eli pa udindo wake nthawi yomweyo. Ngakhale n’telo, Hana posafuna kunyanyala makonzedwe a Mulungu, sanaleke kupita ku cihema kukalambila pamene Eli anali mkulu wa ansembe. Eli ataona Hana akupemphela ali wopsinjika maganizo, iye anamudzudzula kuti waledzela. M’malo mofunsa coyamba kuti adziŵe zoona zake, iye anafikila kumuimba mlandu mkazi wopsinjika maganizo ameneyu. (1 Sam. 1:12-16) Ngakhale n’conco, Hana analonjeza kuti akadzakhala na mwana, adzam’peleka ku cihema kumene adzakhala pansi pa uyang’anilo wa Eli. (1 Sam. 1:11) Kodi ana a Eli anafunika kupatsidwa cilango pa zolakwa zawo? Inde, ndipo pa nthawi yake Yehova anacitapo kanthu. (1 Sam. 4:17) M’kupita kwa nthawi, Mulungu anadalitsa Hana na mwana wamwamuna, dzina lake Samueli.—1 Sam. 1:17-20.

10. Kodi Mfumu Davide anapitiliza bwanji kudalila ena ngakhale kuti anthu ena anam’cita zaciyengo?

10 Kodi mnzanu wapamtima anayamba wakucitam’poni cinyengo? Ngati n’conco, ganizilani za Mfumu Davide. Mnzake wina wapamtima anali Ahitofeli. Koma pamene Abisalomu mwana wa Davide anakonza ciwembu cofuna kulanda ufumu wa atate ake, Ahitofeli anagwilizana naye pa ciwembu cimeneco. Tangoganizani mmene zinam’pweteka mtima Davide, poona kuti mwana wake weniweni, komanso munthu amene anali kumuona kuti ni bwenzi lake am’pandukila. Ngakhale kuti anam’citila zaciyengo conco, Davide sanaleke kudalila ena. Iye anapitiliza kudalila mnzake wina wokhulupilika, Husai, amene sanagwilizane nawo pa kupandukila mfumu. Davide anali na zifukwa zomveka zomukhulupilila Husai. Iye anaonetsa kuti anali bwenzi labwino, ndipo anaika ngakhale moyo wake pa ciwopsezo kuti athandize Davide.—2 Sam. 17:1-16.

11. Ni m’njila iti imene mtumiki wina wa Nabala anaonetsela kuti anali kudalila ena?

11 Ganizilaninso citsanzo ca mmodzi wa atumiki a Nabala. Davide na asilikali ake mokoma mtima anateteza atumiki a Mwisiraeli wina dzina lake Nabala. Nthawi ina, Davide anapempha Nabala munthu wolemela kuti am’thandize cakudya limodzi na asilikali ake. Nabala atakana kuwapatsa cakudya, Davide anakwiya kwambili cakuti anaganiza zokapha mwamuna aliyense m’nyumba ya Nabala. Abigayeli, mkazi wa Nabala, analandila lipoti lokhudza nkhaniyi kwa mmodzi wa atumiki ake. Popeza anali wa m’nyumba ya Nabala, mtumikiyo anadziŵa kuti moyo wake unali m’manja mwa Abigayeli. M’malo mothaŵa, iye anali na cidalilo conse kuti Abigayeli adzakonza zinthu. Anatelo podziŵa kuti iye anali mkazi wanzelu. Zimene zinacitika zionetsa kuti iye anali na zifukwa zabwino zokhulupilila Abigayeli. Abigayeli anacita zinthu molimba mtima kuti apangitse Davide kusintha colinga cake. (1 Sam. 25:2-35) Iye anakhulupilila kuti Davide adzacita zinthu moganiza bwino.

12. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kuwadalila ophunzila ake, ngakhale kuti iwo anali kulakwitsa zinthu zina?

12 Ngakhale kuti ophunzila a Yesu anali kulakwitsa zinthu zina, iye anali kuwadalilabe. (Yoh. 15:15, 16) Pamene Yakobo na Yohane anapempha Yesu kuti akawapatse malo apamwamba mu Ufumu wa Mulungu, iye sanakayikile zolinga zawo potumikila Yehova, kapena kuwacotsa pa utumwi. (Maliko 10:35-40) Patapita nthawi, ophunzila ake onse anathaŵa n’kumusiya yekha usiku wakuti aphedwa maŵa lake. (Mat. 26:56) Ngakhale n’conco, Yesu sanaleke kuwadalila. Anali kudziŵa kuti iwo anali opanda ungwilo, koma “anawakonda mpaka pa mapeto a moyo wake.” (Yoh. 13:1) Ndipo Yesu ataukitsidwa, anapatsa ophunzila ake 11 okhulupilika udindo waukulu wotsogolela pa nchito yopanga ophunzila, na kusamalila nkhosa zake za mtengo wapatali. (Mat. 28:19, 20; Yoh. 21:15-17) Iye anali na zifukwa zabwino zowadalila ophunzila ake opanda ungwilo. Onse anatumikila mokhulupilika mpaka mapeto a moyo wawo wa padziko lapansi. Kukamba zoona, Hana, Davide, mtumiki wa Nabala, Abigayeli, komanso Yesu, ni zitsanzo zabwino pa nkhani yodalila anthu opanda ungwilo.

KUYAMBANSO KUDALILA ABALE ATHU

13. N’cifukwa ciyani cingakhale covuta kwa ife kudalila ena?

13 Kodi munayamba mwauzako wina nkhani yacinsinsi, kenako n’kudzatulukila kuti anaululila ena nkhaniyo? Izi zingakhale zopweteka mtima kwambili. Mlongo wina anauza mkulu nkhani yacinsinsi. Tsiku lotsatila, mkazi wa mkuluyo anatumila foni mlongoyo kuti am’limbikitse. Mlongoyo anadziŵa kuti inali nkhani imene anauza mkuluyo mseli, ndipo cinakhala covuta kwa iye kum’dalila mkuluyo. Koma mlongoyo anapita kukapempha thandizo kwa mkulu wina, cimene cinali cinthu cabwino. Ndipo anam’thandiza kuyambanso kuwadalila akulu.

14. N’ciyani cinathandiza m’bale wina kuyambanso kudalila ena?

14 M’bale wina anasungila akulu aŵili cakukhosi kwa nthawi yaitali. Iye sanali kuwadalila akuluwo. Koma anayamba kuganizila zimene m’bale amene iye amam’lemekeza kwambili anakamba. Mfundo imene inamugwila mtima m’baleyo inali yakuti: “Satana ndiye mdani, osati abale athu.” M’baleyo anaiganizila mofatsa mfundo imeneyi, ndipo anapemphela kwa Yehova. Pambuyo pake, anakhazikitsa mtendele na akulu aŵili amenewo.

15. N’cifukwa ciyani zingatenge nthawi yaitali kuti tiyambenso kudalila ena? Fotokozani citsanzo.

15 Kodi munayamba mwatayikidwapo mwayi wa utumiki? Ici cingakhale cinthu covuta kwa inu. Mlongo Grete pamodzi na amayi ake anali Mboni zokhulupilika panthawi ya ulamulilo wa Nazi ku Germany m’ma 1930, pamene nchito yathu inaletsedwa. Mlongo Grete anali kusangalala na utumiki wokopela Nsanja ya Mlonda kwa okhulupilila anzake. Koma pamene abale anadziŵa kuti atate ake amatsutsa coonadi, mlongo Grete analandidwa utumikiwo, poopa kuti atate akewo angaulule zinsinsi zokhudza mpingo kwa a boma. Mayeso a Grete sanathele pamenepa. Pa nthawi yonse ya nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, abale sanapatsenso Grete na amayi ake mwayi wokopela Nsanja ya Mlonda, ndipo anali kukana ngakhale kuwapatsa moni. Izi zinam’pweteka mtima kwambili mlongo Grete, cakuti zinatenga nthawi yaitali kuti awakhululukile na kuyambanso kuwadalila. Koma m’kupita kwa nthawi, anazindikila kuti Yehova anawakhululukila abalewo, ndipo iyenso anayenela kucita cimodzimodzi. *

“Satana ndiye mdani, osati abale athu.”

16. N’cifukwa ciyani tiyenela kuyesetsa kuwadalila abale na alongo athu?

16 Ngati zaconco zinakucitikilam’poni, yesetsani kuti muyambenso kuwadalila abale anu. Koma mungafunike nthawi, ndipo khama lanu silidzapita pacabe. Mwacitsanzo, ngati cakudya cinacake cakudwalitsani m’mimba, mudzakhala wosamala kwambili na zimene mumadya. Koma simungalekeletu kudya, cabe cifukwa cakudya cimodzi cinakudwalitsani. Mofananamo, sitiyenela kuleka kuwadalila abale na alongo athu amene timadziŵa kuti ni opanda ungwilo, cabe cifukwa ca cocitika cimodzi cimene cinatikhumudwitsa. Tikayambanso kuwadalila abale athu, timakhala na cimwemwe cowilikiza. Komanso, timakhala pa malo abwino oona zimene ifeyo tingacite kuti tilimbikitse mzimu wodalilana mu mpingo.

17. N’cifukwa ciyani kudalila ena n’kofunika ngako? Nanga tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

17 M’dziko la Satanali, kudalilana n’cinthu cosoŵa kwambili. Koma ife timawadalila abale na alongo athu cifukwa timawakonda. Iwonso amatikonda. Kudalilana kotelo kumatithandiza kukhala acimwemwe komanso ogwilizana, ndipo kudzatiteteza podzakumana na mavuto m’tsogolomu. Kodi muyenela kucita ciyani ngati wina wakugwilitsani mwala ndipo mwaleka kum’dalila? Muziona zinthu mmene Yehova amazionela, muzigwilitsa nchito mfundo za m’Baibo, kulitsani cikondi canu pa abale na alongo, komanso tengelani zitsanzo za anthu ochulidwa m’Baibo. Inde, n’zothekadi kucotsa mkwiyo umene tingakhale nawo, na kuyambanso kuwadalila abale athu. Tikatelo, tidzakhala na mabwenzi osaŵelengeka, ‘amene amamatilila kuposa m’bale wathu.’ (Miy. 18:24) Koma Cinyanja cimati, lende n’kukankhana. Conco, ifenso tiyenela kukhala odalilika kwa abale athu. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zimene tingacite kuti abale athu azitidalila.

NYIMBO 99 Abale Miyanda Miyanda

^ Tiyenela kuwadalila abale athu. Koma kucita izi si kopepuka cifukwa nthawi zina iwo angatigwilitse mwala. M’nkhani ino, tikambilane mmene kugwilitsa nchito mfundo za m’Baibo kungatithandizile kuti tiziwakhulupilila kwambili Akhristu anzathu, kapena kuyambanso kuwakhulupilila ngati iwo anatigwilitsapo mwala.

^ Baibo imacenjeza kuti anthu ena mu mpingo sitingawadalile. (Yuda 4) Nthawi zina, abale na alongo onyenga angakambe “zinthu zopotoka” pofuna kusoceletsa ena. (Mac. 20:30) Sitiyenela kuwakhulupilila kapena kumvetsela zokamba zawo.

^ Kuti mudziŵe zambili zokhudza mlongo Grete, onani buku la m’Cizungu lakuti, Yearbook of Jehovah’s Witnesses la 1974, mas. 129-131.