Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi mtumwi Paulo ankatanthauza chiyani pomwe anadzitchula kuti anali ngati “khanda lobadwa masiku asanakwane”? (1 Akorinto 15:8)

Pa 1 Akorinto 15:8, Paulo ananena kuti: “Pomalizira pake anaonekera kwa ine, ngati khanda lobadwa masiku asanakwane.” Poyamba tinkafotokoza kuti zimaoneka kuti pamenepa Paulo ankanena za zomwe zinachitika pa nthawi yomwe anaona masomphenya a Yesu mu ulemerero wake kumwamba. Zinali ngati wapatsidwa mwayi wobadwa, kapena kuti kuukitsidwa mwauzimu, mtundu wa kuuka womwe unali kudzachitika zaka zambiri m’tsogolo. Komabe kufufuza mfundo zowonjezereka pavesili, kwasonyeza kuti pakufunika kusintha mmene tinkafotokozera lembali.

N’zoona kuti Paulo ankafotokoza za zomwe zinachitika pa nthawi yomwe anatembenuka kukhala Mkhristu. Koma kodi ankatanthauza chiyani pomwe ananena kuti anali ngati “khanda lobadwa masiku asanakwane”? N’kutheka kuti ankatanthauza zinthu zingapo.

Kutembenuka kwake kunachitika mwadzidzidzi komanso mosayembekezereka. Nthawi zambiri kuti mwana abadwe masiku asanakwane zimachitika mwadzidzidzi. Saulo (yemwe kenako anayamba kudziwika kuti Paulo) akupita ku Damasiko kuti akazunze Akhristu, sankayembekezera kuti aona masomphenya a Yesu Khristu yemwe anali ataukitsidwa. Kutembenuka kwa Paulo sikunali kodabwitsa kwa iye yekha, koma kunalinso kodabwitsa kwa Akhristu omwe amafuna kukawazunza mumzindawo. Kuwonjezera pamenepo, zomwe zinamuchitikirazi zinali zochititsa mantha moti mpaka anasiya kuona kwa kanthawi.​—Mac. 9:1-9, 17-19.

Iye anatembenuka “pa nthawi yolakwika.” Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti ‘kubadwa masiku asanakwane,’ angamasuliridwenso kuti “kubadwa pa nthawi yolakwika.” Baibulo lina linamasulira mawuwa kuti: “Zinali ngati ndabadwa pa nthawi yomwe palibe amene amayembekezera.” (The Jerusalem Bible.) Pa nthawi yomwe Paulo ankatembenuka, Yesu anali atabwerera kale kumwamba. Mosiyana ndi anthu omwe Paulo anawatchula m’mavesi oyambirira, iye sanaone Yesu asanapite kumwamba. (1 Akor. 15:4-8) Kuonekera mwadzidzidzi kumene Yesu anachita kunamupatsa Paulo mwayi woona Yesu ngakhale kuti zingaoneke ngati zinachitika “pa nthawi yolakwika.”

Ankafotokoza zokhudza iyeyo modzichepetsa. Malinga ndi zimene akatswiri ena amanena, mawu amene Paulo anagwiritsa ntchitowa angasonyeze kudzipeputsa. Ngati umu ndi mmene iye ankaganizira, ndiye kuti ankavomereza kuti sanali woyenera kupatsidwa mwayi umenewu. Ndipotu anapitiriza kunena kuti: “Ineyo ndine wamng’ono kwambiri mwa atumwi onse, ndipo si ine woyenera kutchedwa mtumwi, chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu. Koma mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili monga ndililimu.”​—1 Akor. 15:9, 10.

Choncho zikuoneka kuti Paulo ankanena za zimene zinachitika pamene Yesu anaonekera kwa iye mwadzidzidzi, kutembenuka kwake pa nthawi yosayembekezereka kapenanso kuti anali wosayenerera mwauzimu kuti aone masomphenya ochititsa chidwiwa. Mulimonsemo, Paulo ankaona kuti zimene zinamuchitikirazi zinali zamtengo wapatali. Zinamuthandiza kuti asamakayikire ngakhale pang’ono kuti Yesu anaukitsidwa. N’zosadabwitsa kuti nthawi zambiri ankatchula zomwe zinamuchitikirazi akamalalikira kwa ena zokhudza kuukitsidwa kwa Yesu.​—Mac. 22:6-11; 26:13-18.