Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi mtumwi Paulo anatanthauza ciyani pamene anati iye ni “khanda lobadwa masiku asanakwane”? (1 Akorinto 15:8)

Pa 1 Akorinto 15:8, Paulo anati: “Pomalizila pake anaonekela kwa ine, ngati khanda lobadwa masiku asanakwane.” Kale, tinali kufotokoza kuti zioneka kuti Paulo anali kukamba zimene zinam’citikila ataona Yesu m’masomphenya mu ulemelelo wake kumwamba. Zinali ngati kuti iye anapatsidwa mwayi wobadwanso, kapena woukitsidwa ku moyo wauzimu nthawi isanakwane, kukali zaka mahandiledi ambili kuti ciukitso cimeneci cisanacitike. Komabe, pambuyo poisanthula mozama vesi limeneli, kwakhala kofunika kusintha kafotokozedwe kake.

N’zoona kuti pa vesili, Paulo anali kufotokoza zimene zinacitika pamene anatembenuka kukhala Mkhristu. Koma kodi anatanthauza ciyani pamene anakamba kuti iye ni “khanda lobadwa masiku asanakwane”? Mwina n’cifukwa ca mbali zotsatilazi.

Kutembenuka kwake kunacitika mwadzidzidzi komanso modabwitsa. Nthawi zambili, anthu samayembekezela kuti mwana angabadwe masiku asanakwane. Pamene Saulo (amene pambuyo pake anadzacedwa Paulo) anali pa ulendo wopita ku Damasiko kuti akazunze Akhristu, sanayembekezele kuti adzaona Yesu woukitsidwayo m’masomphenya. Paulo iye mwini, komanso Akhristu amene anali kufuna kukawazunza, sanayembekezele kuti iye angatembenuke n’kukhala Mkhristu. Kuwonjezela apo, cocitikaci cinali codzidzimutsa kwambili cakuti Paulo anali ataleka kuona kwakanthawi.—Mac. 9:1-9, 17-19.

Kutembenuka kwake kunacitika “pa nthawi yosayenelela.” Liwu loyambilila lacigiriki limene analimasulila kuti “khanda lobadwa masiku asanakwane,” lingatanthauzenso kuti “khanda lobadwa pa nthawi yosayenelela.” Baibo ya Jerusalem Bible inamasulila vesili kuti: “Zinali ngati kuti kubadwa kwanga anthu sanakuyembekezele.” Pa nthawi imene Paulo anali kutembenuka, Yesu anali atabwelela kale kumwamba. Mosiyana na anthu amene anachula m’mavesi a pambuyo, Paulo analibe mwayi woona Yesu woukitsidwayo asanakwele kumwamba. (1 Akor. 15:4-8) Yesu ataonekela kwa Paulo mosayembekezeleka, Paulo anakhala na mwayi woona Yesu woukitsidwayo, olo kuti zinaoneka ngati zinacitika “pa nthawi yosayenelela.”

Anali kukamba za iye mwini poonetsa kudzicepetsa. Akatswili ena a Baibo amati mawu amene Paulo anaseŵenzetsa pa vesili, angapeleke lingalilo la kutsitsa munthu. Ngati izi n’zimene Paulo anali kutanthauza, ndiye kuti iye anali kukamba kuti sanali woyenela kukhala mtumwi. Iye anati: “Ndine wamng’ono kwambili mwa atumwi onse, ndipo si ine woyenela kuchedwa mtumwi, cifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu. Koma mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili monga ndililimu.”—1 Akor. 15:9, 10.

Conco, apa zioneka kuti Paulo anali kunena za nthawi pamene Yesu anaonekela kwa iye mosayembekezeleka komanso modzidzimutsa, kutembenuka kwake kwadzidzidzi, kapena kusayenelela kwake mwauzimu kukhala mtumwi. Mulimonsemo, Paulo anayamikila kwambili cocitika cimeneco. Cinam’tsimikizila kuti Yesu anaukadi kwa afuka. N’cifukwa cake, polalikila kwa ena za kuuka kwa Yesu, iye anali kufotokoza za kutembenuka kwakeko kumene kunacitika mosayembekezela.—Mac. 22:6-11; 26:13-18.