Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi ndi anthu ati omwe adzaukitsidwire padzikoli, nanga kuuka kwake kudzakhala kotani?

Tiyeni tione mmene Baibulo limayankhira mafunso amenewa.

Pa Machitidwe 24:15 Baibulo limatiuza kuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” Olungama ndi anthu omwe asanamwalire ankamvera Mulungu choncho mayina awo analembedwa m’buku la moyo. (Mal. 3:16) Osalungama akuphatikizapo anthu omwe asanamwalire analibe mwayi wophunzira za Yehova choncho mayina awo sanalembedwe m’buku la moyo.

Lemba la Yohane 5:28, 29 limanena za magulu awiri a anthu omwewa, omwe atchulidwanso pa Machitidwe 24:15. Yesu ananena kuti “amene anali kuchita zabwino adzauka kuti alandire moyo, amene anali kuchita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.” Olungamawo ankachita zabwino asanamwalire. Iwo adzauka kuti alandire moyo chifukwa mayina awo adakali m’buku la moyo. Osalungamawanso ankachita zoipa asanamwalire choncho adzauka kuti aweruzidwe. Popeza kuti mayina awo sanalembedwe m’bulu la moyo, iwo adzapatsidwa nthawi yoti aweruzidwe kapena kuti kuonedwa kaye ngati asintha. Pa nthawiyo adzakhala ndi mwayi wophunzira za Yehova komanso kuti mayina awo alembedwe m’buku la moyo.

Lemba la Chivumbulutso 20:12, 13 limafotokoza kuti anthu onse omwe adzaukitsidwe adzafunika kumvera “zolembedwa m’mipukutuyo,” zomwe ndi malamulo atsopano omwe Mulungu adzatipatse m’dziko la tsopano. Anthu omwe sadzamvera adzawonongedwa.​—Yes. 65:20.

Lemba la Danieli 12:2 linaneneratu kuti ena omwe anamwalira adzauka kuti ‘alandire moyo wosatha koma ena adzalandira chitonzo ndipo adzadedwa mpaka kalekale.’ Vesili limanena za chiweruzo chomaliza chomwe oukitsidwawa adzalandire chomwe ndi kulandira “moyo wosatha” kapena “kudedwa mpaka kalekale.” Pamapeto pa zaka 1,000, ena adzalandira moyo wosatha pomwe ena adzawonongedwa.​—Chiv. 20:15; 21:3, 4.

Taganizirani chitsanzo ichi. Magulu awiri a anthu oukitsidwawa tingawayerekezere ndi anthu amene akufuna kukakhala m’dziko lina. Olungama ali ngati anthu amene apita m’dziko lina ndipo apatsidwa zikalata zowalola kukhala kapena kugwira ntchito m’dzikolo kwa nthawi yayitali komanso kukhala ndi ufulu wochita zinthu zina. Mosiyana ndi zimenezi osalungama ali ngati anthu omwe apita m’dziko lina ndipo apatsidwa zikalata zongowalola kukhala m’dzikolo monga alendo komanso kwa nthawi yochepa. Alendo oterowo angafunike kuti asonyeze mwa zochita zawo ngati angaloledwe kuti apitirizebe kukhala m’dzikolo. Mofanana ndi zimenezi, osalungama omwe adzaukitsidwe adzafunika kumamvera malamulo a Yehova komanso kusonyeza mwa zochita zawo kuti ndi olungama kuti apitirize kukhala m’Paradaiso. Ndipotu kaya anthu amene apita m’dziko lina apatsidwa zikalata zotani, ena n’kupita kwa nthawi amaloledwa kukhala nzika za dzikolo pomwe ena amabwezedwa kwawo. Zimenezi zimatengera zochita komanso khalidwe lawo m’dziko limene apitalo. Mofanana izi, chiweruzo chimene oukitsidwa onse adzapatsidwe, chidzadalira pa chikhulupiriro chawo komanso zochita zawo m’dziko latsopano.

Sikuti Yehova wangokhala Mulungu wachikondi koma ndi Mulungunso wachilungamo. (Deut. 32:4; Sal. 33:5) Adzasonyeza chikondi chake poukitsa olungama ndi osalungama omwe. Koma pa nthawi imodzimodziyo, adzafuna kuti anthuwo azidzamvera mfundo zake zokhudza chabwino ndi choipa. Anthu okhawo omwe adzasonyeze kuti amamukonda komanso kumvera mfundo zake, ndi amene adzaloledwe kupitirizabe kukhala m’dziko latsopano.