Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Ndani adzaukitsidwa pano padziko lapansi? Nanga ciukitso cawo cidzakhala cotani?

Onani mmene Baibo imayankhila mafunso amenewa.

Machitidwe 24:15 imatiuza kuti kudzakhala “kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” Olungama ni anthu amene anali kumvela Mulungu asanamwalile, ndipo maina awo analembedwa m’buku la moyo. (Mal. 3:16) Osalungama amaphatikizapo anthu amene analibe nthawi yokwanila yophunzila za Yehova asanamwalile, ndipo maina awo mulibe m’buku la moyo.

Yohane 5:28, 29 imachula za magulu aŵili a anthu amene amachulidwanso pa Machitidwe 24:15. Yesu anakamba kuti “amene anali kucita zabwino adzauka kuti alandile moyo. Amene anali kucita zoipa adzauka kuti aweluzidwe.” Anthu olungama anali kucita zinthu zabwino asanafe. Iwo adzauka kuti alandile moyo cifukwa maina awo akalimo m’buku la moyo. Koma anthu osalungama anali kucita zoipa asanafe. Iwo adzauka kuti aweluzidwe. Maina awo ni osalembedwa m’buku lamoyo, ndipo khalidwe lawo lidzafunika kulisanthula coyamba. Pa nthawiyo, iwo adzakhala na mwayi wophunzila za Yehova, ndipo maina awo adzalembedwa m’buku la moyo.

Chivumbulutso 20:12, 13 imafotokoza kuti onse oukitsidwa, adzafunika kumvela “zolembedwa m’mipukutu,” kutanthuza malamulo atsopano amene Mulungu adzatipatsa m’dziko latsopano. Awo amene sadzamvela adzawonongedwa.—Yes. 65:20.

Danieli 12:2 inalosela kuti ena mwa amene anagona mu imfa, adzauka kuti ‘alandile moyo wosatha, koma ena adzalandila citonzo ndipo adzadedwa mpaka kale-kale.’ Vesi limeneli limafotokoza cimene cidzacitika pamapeto pake pambuyo pa ciukitso cawo, kaya kulandila “moyo wosatha” kapena ‘kudedwa mpaka kale-kale.’ Conco, kumapeto kwa zaka Cikwi ena adzalandila moyo wosatha, koma ena adzawonongedwa moti sadzakhalakonso.—Chiv. 20:15; 21:3, 4.

Ganizilani citsanzo ici. Zimene zidzacitike ku magulu aŵili a anthu odzaukitsidwa, tingaziyelekezele na zimene zimacitika kwa alendo ofuna kukakhala ku dziko lina. Olungama ali ngati anthu amene anapatsidwa cikalata colola munthu kugwila nchito kapena kukhala m’dziko mpaka kale-kale. Mosiyana na zimenezi, osalungama ali ngati alendo amene angapatsidwe cilolezo cokhalila m’dziko kwakanthawi cabe. Koma asanaloledwe kupitiliza kukhala m’dzikomo, alendo otelo adzafunika kuonetsa kuti akutsatila malamulo a dzikolo. Mofananamo, anthu osalungama amene adzaukitsidwa adzafunika kumvela malamulo a Yehova, na kuonetsa kuti ni olungama kuti akhalebe m’Paradaiso. Kaya alendowo analandila cilolezo cotani poloŵa m’dziko lina, pothela pake ena angalandile unzika, pamene ena angathamangitsidwe m’dzikolo. Cigamulo ca boma cimeneci cimadalila khalidwe limene iwo amaonetsa m’dzikolo. Mofananamo, ciweluzo ca Mulungu pa anthu amene adzaukitsidwe, cidzadalila kukhulupilika kwawo, na khalidwe limene adzaonetse m’dziko latsopano.

Yehova ni Mulungu wacikondi , komanso wokonda cilungamo. (Deut. 32:4; Sal. 33:5) Iye adzaonetsa cikondi cake poukitsa olungama na osalungama omwe. Pa nthawi imodzimodziyo, iye adzayembekezela onse kutsatila malamulo ake a makhalidwe abwino. Ndipo okhawo amene adzaonetsa kuti amam’konda, na kutsatila malamulo akewo, adzaloledwa kukhalabe m’dziko latsopano.