Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mulungu Walonjeza Kuti Matenda a Maganizo Adzathelatu

Mulungu Walonjeza Kuti Matenda a Maganizo Adzathelatu

Kupitila m’Baibo, Mulungu amapeleka malangizo na cilimbikitso kwa anthu amene ali na matenda ovutika maganizo.

Koma iye wacita zambili kuposa pamenepa. Walonjeza kuti adzacotselatu zonse zimene zimabweletsa matenda a maganizo.

Mulungu akadzakwanilitsa lonjezo limeneli, sipadzakhalanso kuwawidwa mtima, kupanikizika maganizo, komanso zinthu zoipa zakale “sizidzakumbukilidwanso, ndipo sizidzabwelanso mumtima.”—Yesaya 65:17.

Mboni za Yehova ni zokonzeka kukuthandizani kudziŵa kuti ni liti komanso ni motani mmene Mulungu adzakwanilitsila lonjezo lolimbikitsa limeneli.