Mulungu Akulonjeza Kuti Kuvutika Maganizo Kudzatheratu

Mulungu Akulonjeza Kuti Kuvutika Maganizo Kudzatheratu

Kudzera m’Baibulo, Mulungu amapereka malangizo komanso amatonthoza anthu amene akuvutika ndi matenda amaganizo.

Kuwonjezera pamenepo, iye akulonjeza kuti adzathetseratu zinthu zimene zimachititsa kuti anthu azivutika ndi matenda amaganizo.

Mulungu akadzakwaniritsa lonjezo limeneli, sitidzamvanso kuwawa kulikonse, kuvutika ndi nkhawa kapena maganizo oipa chifukwa “zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.”​—Yesaya 65:17.

A Mboni za Yehova adzasangalala kukuthandizani kudziwa nthawi imene Mulungu adzakwaniritse lonjezo lokhazika mtima pansi limeneli komanso mmene adzachitire zimenezi.