NKHANI YOPHUNZIRA 1

Musamakayikire Kuti ‘Mawu a Mulungu Ndi Choonadi’

Musamakayikire Kuti ‘Mawu a Mulungu Ndi Choonadi’

LEMBA LA CHAKA CHA 2023: “Mawu anu onse Ndi choonadi chokhachokha.”​—SAL. 119:160.

NYIMBO NA. 96 Buku la Mulungu Ndi Chuma

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. N’chifukwa chiyani anthu ambiri masiku ano sakhulupirira Baibulo?

 ANTHU ambiri masiku ano sadziwa yemwe angamukhulupirire. Iwo amakayikira ngati anthu omwe amawalemekeza monga andale, asayansi ndi amalonda amafunadi kuwathandiza. Kuwonjezera pamenepo, iwo sakhulupirira atsogoleri a zipembedzo zomwe zimati ndi za Chikhristu. Choncho n’zosadabwitsa kuti sakhulupirira Baibulo, buku lomwe atsogoleriwo amati amatsatira mfundo zake.

2. Mogwirizana ndi Salimo 119:160, kodi tisamakayikire chiyani?

2 Monga atumiki a Yehova, sitikayikira kuti iye ndi “Mulungu wachoonadi” komanso kuti nthawi zonse amatifunira zabwino. (Sal. 31:5; Yes. 48:17) Timadziwa kuti tingakhulupirire zomwe timawerenga m’Baibulo, chifukwa “mawu onse [a Mulungu] ndi choonadi chokhachokha.” (Werengani Salimo 119:160.) Timavomereza zimene katswiri wina wa Baibulo analemba kuti: “Pa zimene Mulungu ananena palibe chilichonse chabodza kapena zimene sizingachitike mpang’ono pomwe. Anthu a Mulungu amakhulupirira chilichonse chomwe iye wanena chifukwa samukayikira ngakhale pang’ono.”

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Kodi tingathandize bwanji ena kuti nawonso azikhulupirira Mawu a Mulungu? Tiyeni tione zifukwa zitatu zomwe zimatichititsa kukhulupirira Baibulo. Tikambirana za kulondola kwa Mawu ake, kukwaniritsidwa kwa maulosi ake komanso mphamvu zomwe Baibulo lili nazo zotha kusintha moyo wa munthu.

UTHENGA WA M’BAIBULO NDI WOLONDOLA NDIPO SUNASINTHIDWE

4. N’chifukwa chiyani anthu ena amakayikira ngati Baibulo lili lolondola?

4 Yehova Mulungu anagwiritsa ntchito amuna okhulupirika 40 kuti alembe mabuku a m’Baibulo. Komabe, palibe mipukutu yoyambirira ya Baibulo yomwe ilipobe mpaka pano. Zolemba zomwe zilipo masiku ano ndi zomwe zinachita kukoperedwa. Zimenezi zimachititsa anthu ena kukayikira ngati zimene timawerenga m’Baibulo masiku ano zilidi zomwe zinalembedwa pamipukutu yoyambirira. Kodi munayamba mwaganizirapo kuti tingatsimikizire bwanji ngati zili zomwezodi?

Akatswiri okopera Malemba a Chiheberi anayesetsa kuchita zimenezo mosamala kwambiri kuti Mawu a Mulungu omwe anakopera akhale olondola (Onani ndime 5)

5. Kodi kukopera Malemba a Chiheberi kunkachitika bwanji? (Onani chithunzi chapachikuto.)

5 Pofuna kuteteza uthenga wake wouziridwa, Yehova anauza anthu ake kuti aziukopera. Iye analamula mafumu a Chiisiraeli kuti azikopera Chilamulo ndipo anauza Alevi kuti aziphunzitsa anthu Chilamulocho. (Deut. 17:18; 31:24-26; Neh. 8:7) Ayuda atachoka ku ukapolo ku Babulo, akatswiri ena odziwa kukopera Chilamulo anakopera kambirimbiri Malemba a Chiheberi. (Ezara 7:6) Pokopera iwo anachita zinthu mosamala. M’kupita kwa nthawi, akatswiriwa sankangowerenga mawu okha koma ankawerenganso zilembo kuti atsimikizire kuti akopera chilichonse molondola. Chifukwa choti sanali angwiro, zolakwika zina zing’onozing’ono zinapezeka m’mawu a m’Baibulo omwe ankakoperawo. Koma popeza panali zolembedwa zambirimbiri zomwe zinakoperedwa, zolakwika zija zinkatha kudziwika mosavuta. Motani?

6. Kodi zinthu zomwe zinalakwika pokopera Baibulo zimadziwika bwanji?

6 Akatswiri a Baibulo masiku ano ali ndi njira zodalirika zodziwira zinthu zomwe zinakoperedwa molakwika. Tayerekezerani kuti anthu 100 auzidwa kuti akopere pamanja zolembedwa zomwe zili patsamba lina la buku. Ndiye wina walakwitsa pang’ono penapake. Njira imodzi yomwe ingatithandize kudziwa zolakwikazo ndi kuyerekezera zimene munthuyo wakopera ndi zimene ena onsewo akopera. Mofanana ndi zimenezi poyerekezera mipukutu yosiyanasiyana ya Baibulo, akatswiri amatha kudziwa zimene wokopera wina analakwitsa kapena kuchotsamo.

7. Kodi timadziwa bwanji kuti okopera Baibulo anachita zimenezo molondola?

7 Anthu omwe ankakopera mipukutu ya Baibulo anayesetsa kuti achite zimenezo molondola. Taganizirani chitsanzo chosonyeza kuti izi ndi zoona. Mpukutu wakale kwambiri wa Malemba a Chiheberi wotchedwa Leningrad Codex unamalizidwa kulembedwa cha m’ma 1008 kapena 1009 C.E. Komabe m’zaka zaposachedwapa kwapezeka mipukutu yambiri ya Baibulo komanso mbali zake zomwe zinalembedwa pafupifupi zaka 1,000 m’mbuyomo, mpukutu umenewu usanalembedwe. Ndiye wina angaganize kuti pambuyo pokopera mobwerezabwereza uthenga wa m’mipukutuyi kwa zaka zoposa 1,000, n’kutheka kuti uthenga wa mumpukutu wa Leningrad Codex ungakhale wosiyana kwambiri ndi womwe uli m’mipukutu yakaleyi. Komatu izi si zoona. Akatswiri omwe anayerekezera mipukutu yakaleyi ndi yatsopano anapeza kuti ngakhale kuti panali tinthu tina tomwe tinalembedwa mosiyana, uthenga wa m’Baibulo unakoperedwa molondola.

8. Kodi Malemba a Chigiriki amasiyana bwanji ndi zolemba zina zakale?

8 Akhristu oyambirira ankatsanzira zimene okopera Malemba a Chiheberi anachita. Mosamala, iwo anakopera mabuku 27 a Malemba a Chigiriki, omwe ankagwiritsa ntchito pamisonkhano komanso polalikira. Atayerekezera mipukutu ya Chigiriki yomwe inapezeka ndi zolemba zina zomwe zinalembedwa pa nthawiyo, katswiri wina anati: “Masiku ano pali mipukutu yambiri ya Malemba a Chigiriki yomwe ilipo kuposa zolemba zina ndipo zikuoneka kuti ndi yokwanira.” Buku lina linanena kuti: “Munthu sangakayikire kuti zimene akuwerenga m’Baibulo [la Malemba a Chigiriki] lomasuliridwa bwino masiku ano, ndi zimenedi olemba mipukutu yoyambirira analemba.”​—Anatomy of the New Testament.

9. Mogwirizana ndi Yesaya 40:8, kodi ndi mfundo iti yoona yokhudza uthenga wa m’Baibulo?

9 Zimene okopera akhala akuchita pokopera Malemba mosamala kwa zaka zambiri, n’zomwe zachititsa kuti Baibulo lomwe timawerenga komanso kuphunzira masiku ano likhale lolondola. b N’zosakayikitsa kuti Yehova ndi amene wakhala akuthandiza kuti uthenga wake usungidwe molondola. (Werengani Yesaya 40:8.) Komabe ena anganene kuti mfundo yakuti uthenga wa m’Baibulo sunasinthe, si umboni wakuti linauziridwa ndi Mulungu. Ndiye tiyeni tione umboni wotsimikizira kuti Baibulo ndi louziridwa.

MAULOSI A M’BAIBULO NDI ODALIRIKA

Left: C. Sappa/​DeAgostini/​Getty Images; right: Image © Homo Cosmicos/​Shutterstock

Maulosi a m’Baibulo anakwaniritsidwa m’mbuyomu ndipo akukwaniritsidwanso masiku ano (Onani ndime 10-11) d

10. Perekani chitsanzo cha ulosi umene unakwaniritsidwa womwe umasonyeza kuti lemba la 2 Petulo 1:21 ndi loona. (Onani zithunzi.)

10 M’Baibulo muli maulosi ambiri amene anakwaniritsidwa, ndipo ena anakwaniritsidwa patapita zaka mahandiredi kuchokera pamene analembedwa. Mbiri imatitsimikizira kuti maulosiwa anakwaniritsidwadi. Izi sizimatidabwitsa chifukwa timadziwa kuti maulosi a m’Baibulo anauziridwa ndi Yehova. (Werengani 2 Petulo 1:21.) Taganizirani za maulosi onena za kugonjetsedwa kwa mzinda wa Babulo. Cha m’ma 700 B.C.E., mneneri Yesaya anauziridwa kulosera kuti mzindawu womwe unali wamphamvu, udzagonjetsedwa. Ananena ngakhale dzina la yemwe adzaugonjetse kuti ndi Koresi ndipo ananeneratu mwatsatanetsatane mmene mzindawo udzagonjetsedwere. (Yes. 44:27–45:2) Yesaya ananeneratunso kuti mzindawo ukadzawonongedwa simudzakhalanso anthu. (Yes. 13:19, 20) Izi ndi zomwe zinachitikadi. Amedi ndi Aperisiya anagonjetsa Babulo mu 539 B.C.E., ndipo panopa pamalo omwe panali mzinda wamphamvuwu, ndi milu ya miyala yokhayokha.​—Onerani vidiyo yakuti Baibulo Linaneneratu Kuti Mzinda wa Babulo Udzagonjetsedwa, mu buku lapazipangizo zamakono lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, phunziro 03 mfundo 5.

11. Fotokozani mmene lemba la Danieli 2:41-43 likukwaniritsidwira masiku ano.

11 Sikuti maulosi a m’Baibulo anangokwaniritsidwa m’mbuyo mokhamu, panopa tikuwaonanso akukwaniritsidwa. Mwachitsanzo, taganizirani za ulosi wochititsa chidwi wa Danieli, wonena za ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. (Werengani Danieli 2:41-43.) Ulosiwu unanena molondola kuti “pa zinthu zina [ulamulirowu] udzakhala wolimba” ngati chitsulo, ndipo “pa zinthu zina udzakhala wosalimba” ngati dongo. Izitu ndi zoona. Ulamuliro wa Britain ndi America wakhala ukusonyeza kuti ndi wamphamvu ngati chitsulo, popambana pa nkhondo zonse za padziko lonse komanso popitiriza kukhala ndi gulu la nkhondo lamphamvu. Komabe mphamvu zawo zakhala zikuchepetsedwa ndi nzika, zomwe zimamenyera ufulu wawo kudzera m’mabungwe a ogwira ntchito komanso popanga zionetsero zotsutsana ndi boma. Katswiri wina pa nkhani zandale posachedwapa anati: “Palibe ulamuliro wina wa demokalase womwe ndi wogawikana kwambiri pa nkhani zandale kuposa wa United States.” Nalonso dziko la Britain lomwe ndi mbali ya ulamulirowu, m’zaka zaposachedwapa lakhala logawikana pa nkhani ya mgwirizano womwe lingakhale nawo ndi mayiko a m’bungwe la European Union. Kugawikana kumeneku kwachititsa kuti ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America uzilephera kuchita zinthu zina.

12. Kodi maulosi a m’Baibulo amatitsimikizira chiyani?

12 Maulosi ambiri a m’Baibulo omwe akwaniritsidwa kale amatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. Timamva ngati mmene anamvera wolemba masalimo wina yemwe anapemphera kwa Yehova kuti: “Ine ndafooka chifukwa cholakalaka chipulumutso chanu, pakuti ndayembekezera mawu anu.” (Sal. 119:81) Kudzera m’Baibulo, mokoma mtima Yehova amatipatsa “chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino.” (Yer. 29:11) Chiyembekezo chathu sichidalira pa zimene munthu angachite, koma pa malonjezo a Yehova. Tiyeni tipitirize kukhulupirira kwambiri Mawu a Mulungu pophunzira mwakhama maulosi a m’Baibulo.

MALANGIZO A M’BAIBULO AKUTHANDIZA ANTHU AMBIRI

13. Mogwirizana ndi Salimo 119:66, 138, kodi ndi umboni wina uti womwe ungatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri Baibulo?

13 Umboni wina wotithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Baibulo ndi woti limathandiza kwambiri anthu omwe amatsatira malangizo ake. (Werengani Salimo 119:66, 138.) Mwachitsanzo, mabanja ena omwe anali atatsala pang’ono kutha panopa akukhalabe limodzi mosangalala. Ana awo amasangalala kuleredwa m’banja la Chikhristu momwe amadzimva kukhala otetezeka komanso okondedwa.​—Aef. 5:22-29.

14. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene kugwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo kungathandizire munthu kusintha moyo wake.

14 Ngakhale zigawenga zoopsa zasintha moyo wawo chifukwa chotsatira malangizo anzeru a m’Baibulo. Taganizirani mmene malangizo ake anathandizira mkaidi wina dzina lake Jack. c Iye anali wachiwawa ndipo ankadziwika kuti anali mmodzi wa akaidi oopsa omwe anagamulidwa kuti aphedwe. Koma tsiku lina Jack anakhala nawo paphunziro la Baibulo. Kukoma mtima kwa abale omwe ankachititsa phunzirolo kunamukhudza kwambiri ndipo nayenso anayamba kuphunzira. Atayamba kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo anasintha zochita ndi khalidwe lake n’kukhala munthu wabwino. Patapita nthawi, Jack anakhala wofalitsa wosabatizidwa ndipo kenako anabatizidwa. Ankalalikira mwakhama za Ufumu wa Mulungu kwa akaidi anzake ndipo anathandiza pafupifupi akaidi 4 kuphunzira choonadi. Pamene linkafika tsiku loti akaphedwe iye anali atasinthiratu. Mmodzi wa maloya ake anati: “Umu si mmene ndinkamudziwira Jack zaka 20 zapitazo. Zimene a Mboni za Yehova akhala akumuphunzitsa zamuthandiza kusintha moyo wake.” Ngakhale kuti iye anaphedwa, chitsanzo chake chikusonyeza kuti tingathe kukhulupirira Mawu a Mulungu komanso kuti ali ndi mphamvu yotha kusintha munthu.​—Yes. 11:6-9.

Malangizo a m’Baibulo athandiza anthu ambiri ochokera m’mitundu yosiyanasiyana kusintha moyo wawo (Onani ndime 15) e

15. Kodi kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo kumasiyanitsa bwanji anthu a Yehova ndi anthu ena masiku ano? (Onani chithunzi.)

15 Anthu a Yehova ndi ogwirizana chifukwa chakuti amatsatira mfundo za m’Baibulo. (Yoh. 13:35; 1 Akor. 1:10) Mtendere ndi mgwirizano wathu zimaonekera bwino, mosiyana ndi anthu a m’dzikoli omwe ndi ogawikana chifukwa cha ndale, kusiyana mitundu komanso mmene amapezera zinthu. Wachinyamata wina dzina lake Jean anakhudzidwa kwambiri poona mgwirizano wa anthu a Mulungu. Iye anakulira m’dziko lina ku Africa. M’dzikolo mutayamba nkhondo ya pachiweniweni, Jean analowa usilikali koma kenako anathawira m’dziko loyandikana nalo. Ali kumeneko anakumana ndi a Mboni za Yehova. Jean anati: “Ndinaphunzira kuti anthu amene ali m’chipembedzo choona salowerera ndale ndiponso si ogawikana, m’malomwake amakondana.” Iye anapitiriza kuti: “M’mbuyomu ndinadzipereka kumenyera nkhondo dziko langa, koma nditaphunzira choonadi cha m’Baibulo ndinadzipereka kuti ndizitumikira Yehova.” Jean anasinthiratu moyo wake. M’malo momenyana ndi anthu osiyana ndi iyeyo, panopa amauza aliyense amene angakumane naye choonadi cha m’Baibulo chomwe chimagwirizanitsa anthu. Mfundo yoti malangizo a m’Baibulo amathandiza anthu a mitundu yonse, ndi umboni wamphamvu woti tingathe kukhulupirira Mawu a Mulungu.

PITIRIZANI KUKHULUPIRIRA MAWU MULUNGU OMWE NDI CHOONADI

16. N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti tizikhulupirira Mawu a Mulungu?

16 Pamene zinthu m’dzikoli zikuipiraipira, kukhulupirira kwathu choonadi kudzayesedwa. Anthu ena adzayesa kutichititsa kuti tiyambe kukayikira ngati Baibulo lili loona kapenanso ngati Yehova anasankha anthu oti azitsogolera anthu ake masiku ano. Koma ngati timakhulupirira kuti Mawu a Yehova nthawi zonse ndi oona tidzatha kukana misampha yoyesa chikhulupiriro chathuyi. ‘Tidzatsimikiza mtima kutsatira malangizo [a Yehova] mpaka kalekale, ndithu kwa moyo wathu wonse.’ (Sal. 119:112) ‘Sitidzachita manyazi’ kuuza ena zokhudza choonadi komanso kuwalimbikitsa kuti azichita zinthu mogwirizana ndi choonadicho. (Sal. 119:46) Tidzatha kupirira ‘moleza mtima ndiponso mwachimwemwe’ mavuto aakulu, kuphatikizapo kuzunzidwa.​—Akol. 1:11; Sal. 119:143, 157.

17. Kodi lemba lathu la chaka lizitikumbutsa chiyani?

17 Timayamikira kwambiri kuti Yehova watithandiza kudziwa choonadi. Choonadichi chimatithandiza kukhala odekha ndiponso chimatiphunzitsa mmene tiyenera kukhalira m’dzikoli lomwe anthu ndi osokonezeka kwambiri kuposa kale. Ndiponso chimatipatsa chiyembekezo cha tsogolo labwino mu Ufumu wa Mulungu. Choncho lemba la chaka cha 2023, litithandize kuti tizikhulupirira kwambiri kuti Mawu a Mulungu ndi choonadi chokhachokha.​—Sal. 119:160.

NYIMBO NA. 94 Timayamikira Mulungu Potipatsa Mawu Ake

a Lemba la chaka cha 2023 lomwe lasankhidwa lingatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Lembali limati: “Mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha.” (Sal. 119:160) N’zosakayikitsa kuti mungavomereze mfundo ya palembali. Koma anthu ambiri sakhulupirira kuti Baibulo limanena zoona komanso kuti lingatipatse malangizo odalirika. Munkhaniyi tiona maumboni atatu omwe tingagwiritse ntchito pothandiza anthu oona mtima kuti azikhulupirira Baibulo ndi malangizo ake.

b Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya mmene Baibulo lasungidwira, pitani pa jw.org ndipo lembani pamalo ofufuzira kuti “Mbiri Komanso Baibulo.”

c Mayina ena asinthidwa.

d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mogwirizana ndi zomwe Mulungu ananena, mzinda wokongola wa Babulo, m’kupita kwa nthawi unawonongedwa.

e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’malo momenyana ndi anthu, wachinyamata wina anaphunzira m’Baibulo mmene angakhalire mwamtendere komanso mmene angathandizire ena kuti azichita zomwezo.