Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 2

“Sandulikani mwa Kusintha Maganizo Anu”

“Sandulikani mwa Kusintha Maganizo Anu”

“Sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikile cimene cili cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.”—AROMA 12:2.

NYIMBO 88 N’dziŵitseni Njila Zanu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1-2. Kodi tiyenela kupitiliza kucita ciyani pambuyo pa ubatizo? Fotokozani.

 KODI mumasesamo kangati m’nyumba mwanu? Mwina musanasamukile m’nyumbayo, munaiyeletsa bwino kwambili. Koma bwanji ngati pambuyo pake mwaleka kuiyeletsa? Mosakayikila, posapita nthawi m’nyumbamo mungakhale fumbi na dothi. Kuti nyumba yanu ikhalebe yaukhondo, muyenela kumaiyeletsa nthawi zonse.

2 Mofananamo, tiziyesetsa kuwongolela kaganizidwe kathu na umunthu wathu. N’zoona kuti tisanabatizike, tinayesetsa kupanga masinthidwe ofunikila mu umoyo wathu kuti ‘tidziyeletse na kucotsa cinthu ciliconse coipitsa thupi kapena mzimu.’ (2 Akor. 7:1) Ngakhale n’telo, tiyenela kutsatila uphungu wa mtumwi Paulo wakuti “pitilizani kukhala atsopano.” (Aef. 4:23 NWT) N’cifukwa ciyani sitiyenela kuleka kuyesetsa kucita zimenezi? Cifukwa posapita nthawi, m’maganizo mwathu mungaloŵe fumbi na dothi la m’dzikoli. Kuti tipewe zimenezi na kukhalabe oyela pamaso pa Yehova, tiyenela kupitiliza kusanthula maganizo athu, umunthu wathu, na zikhumbo zathu.

PITILIZANI ‘KUSINTHA MAGANIZO ANU MWA KUSANDULIKA’

3. Kodi “kusintha maganizo anu” kumatanthauza ciyani? (Aroma 12:2)

3 Kodi tiyenela kucita ciyani kuti tisinthe maganizo athu? (Ŵelengani Aroma 12:2.) Mawu a Cigiliki amene anawamasulila kuti “kusintha maganizo anu,” angamasulidwenso kuti “kukonzanso maganizo anu.” Conco, izi zitanthauza kuti pamafunika zambili, osati kucita nchito zabwino zocepa cabe. Tiyenela kusanthula umunthu wathu wamkati, na kupanga masinthidwe alionse ofunikila kuti umoyo wathu ukhale wogwilizana na cifunilo ca Yehova. Tizicita izi nthawi zonse, osati kamodzi kokha.

Kodi zisankho zanu pa nkhani ya maphunzilo na nchito zimaonetsa kuti mukuika zinthu za Ufumu patsogolo? (Onani ndime 4-5) c

4. Kodi tingateteze bwanji maganizo athu kuti asaumbidwe na dzikoli?

4 Tikadzakhala angwilo, nthawi zonse tizikondweletsa Yehova m’zocita zathu zonse. Koma palipano, timafunika kulimbikila kuti tikondweletse Yehova. Onani mmene Paulo anagwilizanitsila kusintha maganizo athu na kucita cifunilo ca Mulungu pa Aroma 12:2. M’malo molola dzikoli kutiumba, tiyenela kudzisanthula kuti tione ngati timalola maganizo a Yehova kutsogolela zolinga zathu, na zisankho zathu.

5. Kodi tingasanthule bwanji maganizo athu za mmene timaonela kuyandikila kwa tsiku la Yehova? (Onani cithunzi.)

5 Ganizilani citsanzo ici. Yehova amafuna kuti ‘tizikumbukila nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.’ (2 Pet. 3:12) Dzifunseni kuti: ‘Kodi zocita zanga pa umoyo zimaonetsa kuti nikudziŵa bwino kuti tili kumapeto kwenikweni kwa dongosolo lino la zinthu? Kodi zisankho zanga pa nkhani ya maphunzilo komanso nchito, zimaonetsa kuti kutumikila Yehova ndiko kofunika kwambili pa umoyo wanga? Kodi nimakhulupilila kuti Yehova adzanisamalila pamodzi na banja langa, kapena nimangokhalila kudela nkhawa zinthu zakuthupi?’ Yehova amakondwela kwambili akamationa tikuyesetsa kukhala umoyo wogwilizana na cifunilo cake.—Mat. 6:25-27, 33; Afil. 4:12, 13.

6. Tisaleke kucita ciyani?

6 Tiyenela kusanthula kaganizidwe kathu nthawi na nthawi, na kupanga masinthidwe alionse ofunikila. Paulo anauza Akorinto kuti: “Pitilizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’cikhulupililo. Pitilizani kudziyesa kuti mudziŵe kuti ndinu munthu wotani.” (2 Akor. 13:5) Kukhala “m’cikhulupililo” kumaphatikizapo zambili osati cabe kupezeka ku misonkhano yacikhristu na kulalikila. Kumaphatikizaponso kaganizidwe kathu, zokonda zathu, komanso zolinga zathu. Conco, tiyenela kupitiliza kusintha maganizo athu mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu, kuyesetsa kuganiza mmene iye amaganizila, na kucita zonse zotheka kuti tikhale umoyo wogwilizana na cifunilo cake.—1 Akor. 2:14-16.

‘VALANI UMUNTHU WATSOPANO’

7. Malinga na Aefeso 4:31, 32, n’ciyani cina cimene tiyenela kucita? Nanga n’cifukwa ciyani kucita zimenezi kungakhale kovuta?

7 Ŵelengani Aefeso 4:31, 32. Kuwonjezela pa kupanga masinthidwe m’kaganizidwe kathu, tiyenela ‘kuvala umunthu watsopano.’ (Aef. 4:24) Kuti izi zitheke tiyenela kulimbikila. Mwa zina, tiyenela kuyesetsa kucotsa makhalidwe oipa mwa ife, monga kuwawidwa mtima kwanjilu, kupsa mtima, na mkwiyo. N’cifukwa ciyani kucita izi kungakhale kovuta. Cifukwa makhalidwe ena oipa anazika mizu kwambili. Mwacitsanzo, Baibo imakamba kuti anthu ena ‘amakonda kukwiya,’ komanso ‘amakonda kupsa mtima. (Miy. 29:22) Munthu wa makhalidwe ozika mizu ngati amenewa, angafunike kupitiliza kulimbikila kuti asinthe ngakhale pambuyo pa ubatizo. Citsanzo cotsatila citsimikizila zimenezi.

8-9. Kodi cocitika ca m’bale Stephen cionetsa bwanji kufunika kopitiliza kuvula umunthu wakale?

8 M’bale wina dzina lake Stephen anali na vuto la kusaugwila mtima. Iye anati: “Ngakhale pambuyo pa ubatizo, n’nafunika kuyesetsa kuthetsa mkwiyo wanga. Mwacitsanzo, nthawi ina pamene n’nali kulalikila nyumba na nyumba, n’napitikitsa mbala imene inaba wailesi ya m’galimoto yanga. N’tatsala pang’ono kuigwila, inataya wailesiyo n’kuthaŵa. Pamene n’nafotokozela anzanga zimene zinacitika, mmodzi wa akulu ananifunsa kuti, ‘M’bale Stephen, ukanaigwila ukanaicita ciyani?’ Funso limenelo linanicititsa kuganiza kwambili, ndipo linanithandiza kuti nipitilize kuyesetsa kukhala mwamtendele na ena.” b

9 Cocitika ca m’bale Stephen cionetsa kuti khalidwe loipa lokhudza umunthu wathu lingaonekelenso mosayembekezela, ngakhale pamene tikuona kuti khalidwelo tinalithetsa. Izi zikakucitikilani musalefuke, ndipo musadzione kuti ndinu Mkhristu wolephela. Ngakhale mtumwi Paulo anavomeleza kuti: “Pamene ndikufuna kucita cinthu cabwino, coipa cimakhala cili ndi ine.” (Aroma 7:21-23) Akhristu onse ni opanda ungwilo. Conco, onse amalimbana na makhalidwe ena oipa amene amapitilizabe kubwela mu umoyo wawo wacikhristu mofanana na fumbi na dothi m’nyumba. Tiyenela kuyesetsa kukhalabe oyela. Tingacite bwanji zimenezi?

10. Kodi makhalidwe oipa tingalimbane nawo bwanji? (1 Yohane 5:14, 15)

10 Pemphelani kwa Yehova za khalidwe limene mukulimbana nalo, muli na cidalilo cakuti adzakumvelani na kukuthandizani. (Ŵelengani 1 Yohane 5:14, 15.) Ngakhale kuti Yehova sadzathetsa khalidwelo mozizwitsa, angakupatseni mphamvu kuti musafooke. (1 Pet. 5:10) Citani zinthu mogwilizana na mapemphelo anu, popewa kucita zinthu zimene zingapangitse umunthu wanu wakale kubwelanso. Mwacitsanzo, pewani kuonelela mafilimu, mapulogilamu a pa TV, kapena kuŵelenga nkhani zimene zimalimbikitsa makhalidwe oipa amene mukuyesetsa kuwathetsa. Ndipo musalole maganizo anu kukhazikika pa zilakolako zoipa.—Afil. 4:8; Akol. 3:2

11. Kodi tiyenela kucita ciyani kuti tisalekeze kuvala umunthu watsopano?

11 Mukavula umunthu wakale, muyenela kuvala umunthu watsopano. Mungacite bwanji zimenezo? Cipangeni kukhala colinga canu kutengela citsanzo ca Yehova pamene muphunzila za makhalidwe ake. (Aef. 5:1, 2) Mwacitsanzo, mukaŵelenga nkhani ya m’Baibo yoonetsa khalidwe la kukhululuka la Yehova, dzifunseni kuti, ‘Kodi nimakhululukila ena?’ Mukaŵelenga za mmene Yehova anaonetsela cifundo kwa anthu ovutika, dzifunseni kuti, ‘Kodi inenso nimaonetsa cifundo mwa zocita zanga kwa alambili anzanga ovutika?’ Pitilizani kusintha maganizo anu, mwa kuvala umunthu watsopano, ndipo dzilezeleni mtima pocita zimenezo.

12. Kodi citsanzo ca m’bale Stephen cionetsa bwanji kuti Baibo ili na mphamvu zokhoza kusintha munthu?

12 M’bale Stephen amene tam’chula uja, anazindikila kuti anali kuvala munthu watsopano mwapang’ono-pang’ono. Iye anati: “Kucoka panthawi imene n’nabatizika, nakumana na zinthu zambili zimene zikananipangitsa kucita ciwawa. Anthu ena akanikhumudwitsa, nimayesetsa kusakwiya msanga ndipo nthawi zina nimangocokapo. Mkazi wanga limodzi na anthu ena amaniyamikila kaamba ka kuyesetsa kwanga. Ndine wokondwa cifukwa umoyo wanga tsopano, unasintha. Sinidzitama kuti n’nasintha khalidwe langa, koma nimakhulupilila kuti ni umboni wakuti Baibo ili na mphamvu zokhoza kusintha munthu.”

MUSALEKE KULIMBANA NAZO ZILAKOLAKO ZOIPA

13. N’ciyani cidzatithandiza kukhala na zikhumbo zabwino? (Agalatiya 5:16)

13 Ŵelengani Agalatiya 5:16. Pofuna kutithandiza kuti tipambane pa nkhondo yolimbana na zilakolako zoipa, Yehova mowolowa manja amatipatsa mzimu wake woyela. Tikamaŵelenga Mawu a Mulungu, timalola mzimu woyela kutsogolela zocita zathu. Timalandilanso mzimu woyela tikamapezeka ku misonkhano. Pa misonkhano imeneyo, timakhala na nthawi yoceza na abale na alongo, amene mofanana na ife amayesetsa kucita zabwino, ndipo izi zimatilimbikitsa. (Aheb. 10:24, 25; 13:7) Cina, tikamacondelela Yehova mocokela pansi pa mtima kuti atithandize kugonjetsa zifooko, iye adzatigaŵila mzimu wake woyela umene udzatipatsa mphamvu zopitiliza kumenya nkhondoyo. N’zoona kuti kucita zimenezi sikungathetse zilakolako zoipa. Koma kudzatithandiza kupewa kucita zinthu motsatila zilakolako zimenezo. Malinga na zimene Agalatiya 5:16 imakamba, anthu amene amayenda mwa mzimu, ‘sadzatsatila cilakolako ca thupi ngakhale pang’ono.’

14. N’cifukwa ciyani tiyenela kupitiliza kukulitsa zikhumbo zabwino?

14 Tikangokhazikitsa pulogilamu yocita zauzimu, tiyenela kumamatilabe pulogilamu imeneyo na kupitiliza kukulitsa zikhumbo zabwino. Cifukwa ciyani? Cifukwa pali mdani wathu wina amene sagona. Mdani ameneyo ni mayeselo akuti ticite zoipa. Ngakhale pambuyo pa ubatizo, tingamakopedwe na zinthu zimene tiyenela kuzipewa, monga kuchova njuga, kumwa moŵa mwaucidakwa, kapena kupenyelela zamalisece. (Aef. 5:3, 4) M’bale wina wacinyamata anati: “Vuto lalikulu limene nakhala nikulimbana nalo, ni cikhumbo cofuna kugonana na mwamuna mnzanga. N’nali kuona kuti vutoli n’la kanthawi cabe. Koma mpaka pano nikali kulimbana nalo.” N’ciyani cingakuthandizeni ngati cilakolako coipa n’camphamvu?

Mukayesedwa na cilakolako coipa, musafooke podziŵa kuti ena analimbanapo na cilakolako ngati canu, ndipo anacigonjetsa. (Onani ndime 15-16)

15. N’cifukwa ciyani n’zolimbikitsa kudziŵa kuti enanso amalimbana na zilakolako zoipa? (Onani cithunzi.)

15 Ngati mukulimbana na cilakolako coipa camphamvu, dziŵani kuti simuli nokha. Baibo imati: “Palibe mayeselo amene mwakumana nawo osiyana ndi amene amagwela anthu ena.” (1 Akor. 10:13a) Palembali, Baibo ina inati: “Palibe mayeselo aakulu msinkhu amene mwakumanapo nawo kuposa amene amagwela anthu onse.” Mawu amenewa analembela abale na alongo a ku Korinto. Ena a iwo kale anali acigololo, amathanyula, komanso zidakwa. (1 Akor. 6:9-11) Kodi muganiza kuti pambuyo pobatizika, iwo analeka kulimbana na zilakolako zawo? Ayi, anali kulimbanabe nazo. N’zoona kuti iwo anali Akhristu odzozedwa. Koma ngakhale n’telo, anali anthu opanda ungwilo. Pa cifukwa cimeneci, iwo nthawi zina anali kulimbana na zilakolako zoipa. Izi n’zolimbikitsa kwa ife. Cifukwa ciyani? Cifukwa izi zionetsa kuti zilakolako zilizonse zoipa zimene mukugwebana nazo, ena anadzigonjetsapo kale. Ndithudi, mungakhalebe ‘olimba m’cikhulupililo podziŵa kuti anzanunso m’gulu lonse la abale anu m’dzikoli akukumana na masautso ngati omwewo.’—1 Pet. 5:9.

16. Kodi tiyenela kupewa maganizo otani? Nanga n’cifukwa ciyani?

16 Pewani kuganiza kuti palibe angamvetse vuto limene mukulimbana nalo. Kuganiza mwanjila imeneyi kungakupangitseni kuona kuti vuto lanu silingathe, na kuti palibe zimene mungacite kuti mugonjetse zilakolako zoipazo. Baibo imati: “Mulungu ndi wokhulupilika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile, koma pamene mukukumana ndi mayeselowo iye adzapeleka njila yopulumukila kuti muthe kuwapilila.” (1 Akor. 10:13b) Conco, ngakhale cilakolako coipa cikhale camphamvu motani, n’zotheka kukhalabe okhulupilika kwa Yehova. Ndipo mwa thandizo lake, tidzapewa kucita zinthu motsatila zilakolako zathu.

17. Ngakhale kuti n’zosatheka kuletselatu zilakolako zoipa kubwela m’maganizo mwathu, kodi tiyenela kupewa ciyani?

17 Nthawi zonse muzikumbukila mfundo iyi: Pokhala anthu opanda ungwilo, sitingaletse zilakolako zoipa kubwela m’maganizo mwathu. Koma zikabwela m’maganizo mwanu, muyenela kuzicotsa mwamsanga, monga anacitila Yosefe kuthaŵa mkazi wa Potifara mwamsanga. (Gen. 39:12) Musazitsatile zilakolako zanu zoipazo.

LIMBIKILANIBE

18-19. Kodi tiyenela kudzifunsa mafunso ati pamene tikuyesetsa kusintha maganizo athu?

18 Kusintha maganizo athu kumafuna kulimbikilabe kuti maganizowo na zocita zathu zigwilizane na cifunilo ca Yehova. Conco nthawi na nthawi, muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zocita zanga zimaonetsa kuti nikudziŵa kuti tikukhala m’nthawi ya mapeto? Kodi nikupita patsogolo pa nkhani ya kuvala umunthu watsopano? Kodi nimalola mzimu wa Yehova kunitsogolela pa umoyo wanga kuti nizikana kucita zinthu motsatila zilakolako za thupi?’

19 Mukamadzisanthula, ikani maganizo pa kupita kwanu patsogolo, osati pa kufuna kucita zinthu mwangwilo. Mukaona kuti pali mbali zofunika kuwongolela, musalefuke. M’malo mwake, tsatilani langizo la pa Afilipi 3:16 lakuti: “Mulimonse mmene tapitila patsogolo, tiyeni tipitilize kupita patsogolo mwa kuyenda moyenela m’njila yomweyo.” Mukatelo, dziŵani kuti Yehova adzadalitsa kuyesetsa kwanu kuti musinthe maganizo anu.

NYIMBO 36 Titeteze Mitima Yathu

a Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kusalola dongosolo lino la zinthu kuumba kaganizidwe kawo. Uwu ni uphungu wabwino ngakhale kwa ife masiku ano. Tiyenela kuyesetsa kusalola maganizo oipa a dzikoli kuumba kaganizidwe kathu mwa njila ina iliyonse. Kuti izi zitheke, tiyenela kupitiliza kuwongolela kaganizidwe kathu, nthawi zonse tikazindikila kuti sikogwilizana na cifunilo ca Mulungu. M’nkhani ino, tikambilane mmene tingacitile zimenezi.

b Onani nkhani yakuti, “Umoyo Wanga Unali Kuipilaipilabe” mu Nsanja ya Mlonda ya September 1, 2015.

c MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale wacinyamata akuganizila zimene ayenela kusankha pakati pa maphunzilo apamwamba na utumiki wa nthawi zonse.